Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunafuna Moyo Wachimwemwe

Kufunafuna Moyo Wachimwemwe

Kufunafuna Moyo Wachimwemwe

ZAKA zingapo zapitazo, anthu a ku France, Germany, Great Britain, ndi United States anawafunsa funso loti, “Kodi chimafunika n’chiyani kuti munthu akhale wachimwemwe?” Pa anthu amene anafunsidwawo, anthu 89 mwa anthu 100 alionse ananena kuti chimafunika ndi thanzi labwino; anthu 79 mwa anthu 100 alionse anatchula kukhala ndi ukwati kapena mnzawo wokhala naye wabwino; anthu 62 mwa anthu 100 alionse anatchula za kukoma kokhala kholo; ndipo anthu 51 mwa anthu 100 alionse anaganiza kuti kukhala ndi ntchito yabwino n’kumene kumafunika kuti munthu akhale wachimwemwe. Ndipo ngakhale kuti anthu ambiri amadziŵa kuti kukhala ndi ndalama sikutanthauza kuti munthu akhala ndi chimwemwe, anthu 47 mwa anthu 100 alionse amene anafunsidwa funsolo ankakhulupirira kuti ndalama n’zimene zimabweretsa chimwemwe. Kodi zochitika zenizeni zimasonyeza chiyani?

Choyamba, taganizirani za kugwirizana kumene akuti kulipo pakati pa ndalama ndi moyo wachimwemwe. Kafukufuku amene anachitika pa anthu 100 olemera kwambiri a ku United States anasonyeza kuti anthu ameneŵa si achimwemwe kwambiri kuposa anthu ena onse. Kuwonjezera apo, ngakhale kuti anthu ambiri a ku United States awonjezera katundu amene ali naye pafupifupi kuŵirikiza kaŵiri m’zaka 30 zapitazi, iwo sikuti ndi achimwemwe kwambiri panopa kuposa mmene analili kale, malinga ndi zimene akatswiri a za maganizo anena. M’malo mwake, lipoti lina linati: “Pa zaka [30] zomwezomwezo, anthu odwala matenda ovutika maganizo awonjezeka kwambiri. Achinyamata amene akudzipha awonjezeka katatu. Maukwati amene akutha awonjezeka kaŵiri.” M’mayiko ena okwana pafupifupi 50, ochita kafukufuku amene anafufuza kugwirizana kwa ndalama ndi moyo wachimwemwe anafika pa mfundo yakuti ndalama sizingagule chimwemwe.

Chachiŵiri, kodi zinthu monga thanzi labwino, ukwati wabwino, ndi ntchito yabwino n’zofunika bwanji kuti munthu akhale ndi moyo wachimwemwe? Zikanakhala kuti zinthu zimenezi n’zofunika kwambiri kuti munthu akhale wachimwemwe, bwanji za anthu ambirimbiri amene alibe thanzi labwino ndi ena ambiri amene alibe ukwati wabwino? Nanga bwanji za anthu okwatirana amene alibe ana ndi amuna ndi akazi ambirimbiri amene alibe ntchito yabwino? Kodi anthu onse oterowo ndiye kuti moyo wawo wonse adzakhala opanda chimwemwe? Ndipo kodi anthu amene amati ndi achimwemwe panopa chifukwa ali ndi thanzi labwino ndi banja labwino sangapitirizebe kukhala achimwemwe zinthu zitasintha pamoyo wawo?

Kodi Tikugwiritsa Ntchito Njira Zoyenera Pofunafuna Chimwemwe?

Aliyense amafuna kukhala wachimwemwe. Zimenezi n’zosadabwitsa chifukwa Mlengi wa munthu amafotokozedwa kuti ndi “Mulungu wolemekezeka [“wachimwemwe,” NW]” ndipo munthu anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu. (1 Timoteo 1:11; Genesis 1:26, 27) Choncho m’pomveka kuti anthu amafunafuna moyo wachimwemwe. Komabe, anthu ambiri azindikira kuti kukhala wachimwemwe n’kovuta mofanana ndi mmene kulili kovuta kufumbata mchenga m’manja. Ziŵiri zonsezi sizichedwa kutayika.

Koma kodi n’kutheka kuti anthu ena akuyesetsa mopitirira muyeso kuti akhale achimwemwe? Katswiri wa maganizo ndi kakhalidwe ka anthu Eric Hoffer anaganiza choncho. Iye anati: “Kufunafuna moyo wachimwemwe n’chifukwa chachikulu chimene anthu amakhalira opanda chimwemwe.” Zimenezo zimakhaladi choncho ngati tikufunafuna chimwemwe m’njira zolakwika. Ngati tikutero, ndiye kuti mosalephera tidzagwiritsidwa mwala. Kuyesetsa kukhala munthu wolemera, kufuna kutchuka kapena kudziŵika, kufuna kukhala ndi udindo pandale, kufuna kukhala munthu wolemekezeka, kufuna kukhala munthu wopeza bwino; kapena kumangodzikhalira n’kumaganizira za moyo wako wokha basi ndiponso kumafuna kupeza nthaŵi yomweyo zinthu zimene ukulakalaka, zonsezi sizibweretsa chimwemwe. Choncho n’zosadabwitsa kuti anthu ena ayamba kuyendera mfundo yodabwitsa imene mlembi wina ananena, yoti: “Tikanangosiya kaye kufuna kukhala achimwemwe, tikanakhala osangalala ndithu”!

N’zochititsa chidwi kuti kafukufuku amene tinamutchula koyambirira kwa nkhani ino uja anasonyezanso kuti anthu 4 mwa anthu 10 alionse anaganiza kuti kuchita zinthu zabwino ndi kuthandiza ena n’kumene kumabweretsa chimwemwe. Ndipo munthu mmodzi mwa anthu 4 alionse anatsindika kuti kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso kukhala munthu wopembedza kumathandiza kwambiri kuti munthu akhale wachimwemwe. N’zachionekere kuti tiyenera kuona bwinobwino zimene zimafunika kuti munthu akhaledi wachimwemwe. Nkhani yotsatirayi itithandiza kuchita zimenezi.

[Zithunzi patsamba 3]

Anthu ambiri amaganiza kuti ndalama, banja labwino, kapena ntchito yabwino n’zimene zimabweretsa chimwemwe. Kodi mukugwirizana nawo?