Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga

N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimati nambala ya 144,000 yotchulidwa m’buku la Chivumbulutso ndi yeniyeni osati yophiphiritsira?

Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndinamva chiŵerengo cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anayi mphambu anayi.” (Chivumbulutso 7:4) Baibulo limasonyeza kuti “iwo osindikizidwa chizindikiro” ndi gulu la anthu amene anasankhidwa kuti akakhale ndi Kristu kumwamba ndipo azidzalamulira dziko lapansi laparadaiso likubweralo. (2 Akorinto 1:21, 22; Chivumbulutso 5:9, 10; 20:6) Nambala yawo ya 144,000 imaonedwa kuti ndi yeniyeni pa zifukwa zingapo. Chifukwa choyamba ndicho zinthu zina zomwe zatchulidwa m’chaputala chomwecho cha Chivumbulutso 7.

Mtumwi Yohane atatha kuuzidwa mwa masomphenya za gulu la anthu 144,000 limeneli, anasonyezedwa gulu lina. Yohane anafotokoza kuti gulu lachiŵirili ndi ‘khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.’ Khamu lalikulu limeneli ndi anthu amene adzapulumuke “chisautso chachikulu” chimene chikubweracho, chimene chidzawononge dziko loipali.​—Chivumbulutso 7:9, 14.

Koma taonani mmene Yohane anasiyanitsira vesi 4 ndi vesi 9 la Chivumbulutso chaputala 7. Iye anati gulu loyambalo, “iwo osindikizidwa chizindikiro,” alipo okwana nambala yodziŵika. Koma gulu lachiŵirilo, a “khamu lalikulu,” ndi osadziŵika nambala yawo. Poganizira zimenezo, m’pomveka kunena kuti nambala ya 144,000 ndi yeniyeni. Nambala ya 144,000 ikanakhala yophiphiritsira yoimira gulu la anthu limene nambala yake siikudziŵika, kusiyana kwa mavesi aŵiriŵa sikukanaoneka. Choncho nkhani ya m’chaputala chimenechi ikusonyeza mosapita m’mbali kuti nambala ya 144,000 iyenera kukhala yeniyeni.

Akatswiri a Baibulo osiyanasiyana, akale ndi aposachedwapa, nawonso pomalizira pake anafika pa mfundo yomweyo, yoti nambalayo ndi yeniyeni. Mwachitsanzo, pothirirapo ndemanga pa lemba la Chivumbulutso 7:4, 9, mlembi wa buku lina lotanthauzira mawu wa ku Britain dzina lake Dr. Ethelbert W. Bullinger ananena mawu otsatiraŵa zaka pafupifupi 100 zapitazo: “Ndi mfundo yosavuta kumvetsa: nambala yodziŵika akuisiyanitsa ndi nambala yosadziŵika m’chaputala chimodzi chomwechi.” (The Apocalypse or “The Day of the Lord,” tsamba 282) Chaposachedwapa, Robert L. Thomas, Jr., pulofesa wa Chipangano Chatsopano pasukulu ina yotchedwa Master’s Seminary ku United States analemba kuti: “Mfundo yoti nambalayo ndi yophiphiritsira ilibe maziko enieni.” Iye anawonjezera kuti: “[Pa Chivumbulutso 7:4] pali nambala yodziŵika mosiyana ndi nambala yosadziŵika ya pa [Chivumbulutso] 7:9. Ngati tinena kuti nambala imeneyi ndi yophiphiritsira, ndiye kuti palibe nambala iliyonse m’bukuli imene tinganene kuti ndi yeniyeni.”​—Revelation: An Exegetical Commentary, Voliyumu 1, tsamba 474.

Anthu ena amati popeza m’buku la Chivumbulutso muli mawu ophiphiritsira kwambiri, manambala onse amene ali m’bukuli, kuphatikizapo nambala ya 144,000, ayenera kukhala ophiphiritsira. (Chivumbulutso 1:1, 4; 2:10) Koma zimenezo mwachionekere si zoona. N’zoona kuti m’buku la Chivumbulutso muli manambala ophiphiritsira ambiri, koma mulinso manambala enieni. Mwachitsanzo, Yohane ananena za “mayina khumi ndi aŵiri a atumwi khumi ndi aŵiri a Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 21:14) Mwachionekere, nambala ya khumi ndi aŵiri yotchulidwa m’vesi limeneli ndi yeniyeni, osati yophiphiritsira. Kuwonjezera apo, Yohane analemba za “zaka chikwi” za ulamuliro wa Kristu. Nambala imeneyo iyeneranso kuonedwa monga yeniyeni malinga ndi zimene timapeza tikaŵerenga mosamala zimene Baibulo limanena. * (Chivumbulutso 20:3, 5-7) Choncho, kuti tinene kuti nambala ya m’buku la Chivumbulutso ndi yeniyeni kapena yophiphiritsira zimadalira nkhani imene vesi limene muli nambalayo likufotokoza.

Mfundo yoti nambala ya 144,000 ndi yeniyeni ndipo imaimira anthu oŵerengeka, amene ali kagulu kakang’ono poyerekezera ndi “khamu lalikulu,” imagwirizananso ndi mbali zina za Baibulo. Mwachitsanzo, popitiriza ndi masomphenya amene Yohane anaona, a 144,000 akufotokozedwa kuti ‘anagulidwa mwa anthu zipatso zoundukula.’ (Chivumbulutso 14:1, 4) Mawu akuti “zipatso zoundukula” amatanthauza zinthu zapang’ono zoimira zinthu zina. Ndipo Yesu ali padziko lapansi analankhula za anthu amene adzalamulire naye mu Ufumu wake wakumwamba ndipo anawatcha ‘kagulu ka nkhosa.’ (Luka 12:32; 22:29) Zoonadi, anthu amene adzalamulire kumwamba ndi ochepa poyerekezera ndi anthu amene adzakhale padziko lapansi laparadaiso limene likubweralo.

Choncho, nkhani imene ikufotokozedwa m’chaputala 7 cha Chivumbulutso ndiponso maumboni ena opezeka m’mbali zina za Baibulo zikutsimikizira kuti nambala ya 144,000 iyenera kuonedwa kuti ndi yeniyeni. Imaimira anthu amene adzakhale kumwamba ndi Kristu kulamulira dziko lapansi laparadaiso, limene lidzadzazidwe ndi anthu ambiri achimwemwe osadziŵika nambala yawo olambira Yehova Mulungu.​—Salmo 37:29.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Kuti mumve zambiri zokhudza Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu, onani buku la Revelation​—Its Grand Climax At Hand! masamba 289-90, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 31]

Nambala ya anthu amene adzalamulire kumwamba ndi 144,000 basi

[Chithunzi patsamba 31]

“Khamu lalikulu” silikudziŵika nambala yake

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Stars: Courtesy of Anglo-Australian Observatory, photograph by David Malin