Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Takhala ndi Moyo Watanthauzo ndi Wosangalala Chifukwa Chodzipereka

Takhala ndi Moyo Watanthauzo ndi Wosangalala Chifukwa Chodzipereka

Mbiri ya Moyo Wanga

Takhala ndi Moyo Watanthauzo ndi Wosangalala Chifukwa Chodzipereka

YOSIMBIDWA NDI MARIAN NDI ROSA SZUMIGA

Lemba la Salmo 54:6 limati: “Ine mwini ndidzapereka nsembe kwa Inu.” Lemba limeneli ndi limene Marian Szumiga ndi mkazi wake Rosa, amene amakhala ku France, akhala akuyendera pa moyo wawo. Posachedwapa iwo anafotokoza zina mwa zinthu zomwe zawachitikira pa moyo wawo wautali ndi watanthauzo wotumikira Yehova.

MARIAN: Makolo anga anali Akatolika ochokera ku Poland. Bambo anga analibe mwayi wopita kusukulu. Komabe, pa nthaŵi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, iwo anaphunzira kuŵerenga ndi kulemba akugwira ntchito yausilikali m’mayenje amene asilikali amabisalamo kunkhondo. Bambo anali munthu woopa Mulungu, koma tchalitchi nthaŵi zambiri chinawakhumudwitsa.

Pali chochitika chimodzi makamaka chimene sanachiiwale. Tsiku lina, panthaŵi yankhondoyo, wansembe anabwera kudzayendera gulu la asilikali limene Bambo anali. Bomba litaphulika chapafupi, wansembeyo anathaŵa atachita mantha, ndipo anamenya hatchi yake ndi mtanda wake kuti ithamange kwambiri. Bambo anadabwa kwambiri kuona kuti munthu “woimira” Mulungu anagwiritsa ntchito chinthu “choyera” kuti athaŵe msanga. Ngakhale kuti anaona zinthu ngati zimenezo ndi zinthu zoopsa za kunkhondo, chikhulupiriro cha Bambo mwa Mulungu sichinafooke. Nthaŵi zambiri ankanena kuti ndi Mulungu amene anawathandiza kuti abwereko amoyo kunkhondoko.

“Poland Wamng’ono”

M’chaka cha 1911, bambo anga anakwatira mtsikana wa m’mudzi woyandikana ndi wawo. Dzina lake linali Anna Cisowski. Nkhondo itangotha kumene, mu 1919, Bambo ndi Mayi anasamuka ku Poland kupita ku France, kumene Bambo anapeza ntchito mu mgodi wa malasha. Ineyo ndinabadwa mu March 1926 m’tawuni yotchedwa Cagnac-les-Mines, kum’mwera chakumadzulo kwa France. Kenaka makolo anga anasamukira m’dera lokhala anthu a ku Poland la Loos-en-Gohelle, pafupi ndi tawuni ya Lens kumpoto kwa France. Wogulitsa buledi anali wa ku Poland, wogulitsa nyama anali wa ku Poland, ndipo wansembe anali wa ku Poland. N’zosadabwitsa kuti dera limeneli linkatchedwa Poland Wamng’ono. Makolo anga ankagwira nawo ntchito zosiyanasiyana za m’mudzimo. Nthaŵi zambiri Bambo ankakonza zionetsero zimene zinkaphatikizapo seŵero ndi kuimba nyimbo. Ankakambirananso zinthu nthaŵi zambiri ndi wansembe, koma wansembeyo nthaŵi zambiri sankawafika pamtima chifukwa ankangoti, “Pali zinsinsi zambiri.”

Tsiku lina mu 1930, azimayi aŵiri anagogoda pachitseko chathu. Anali Ophunzira Baibulo, monga momwe Mboni za Yehova zinkadziŵikira masiku amenewo. Bambo anga analandira Baibulo kuchokera kwa iwo, buku limene kwa zaka zambiri ankafuna kuliŵerenga. Iwo ndi Mayi anaŵerenganso mwachidwi mabuku ena ofotokoza za m’Baibulo amene azimayiwo anawasiyira. Makolo anga anakhudzidwa kwambiri ndi zimene anaŵerenga m’mabuku ameneŵa. Ngakhale kuti anali anthu otanganidwa, makolo anga anayamba kumapita ku misonkhano yokonzedwa ndi Ophunzira Baibulowo. Bambo akamakambirana ndi wansembe uja anapitirizabe kutsutsana, mpaka tsiku lina wansembeyo anawauza makolo anga kuti akapitiriza kuyanjana ndi Ophunzira Baibulo, mchemwali wanga Stéphanie amusiyitsa katekizimu. Bambo anamuyankha kuti: “Musadzivutitse. Kuyambira lero, mwana wanga wamkazi ndi ana anga onse azipita nafe ku misonkhano ya Ophunzira Baibulo.” Bambo anachoka m’tchalitchimo, ndipo kumayambiriro kwa 1932, makolo anga anabatizidwa. Panthaŵi imeneyo, ku France kunali ofalitsa Ufumu pafupifupi 800 okha.

Rosa: Makolo anga anachokera ku Hungary, ndipo mofanana ndi banja la Marian, anakhazikika kumpoto kwa France, n’kumagwira ntchito m’migodi ya malasha. Ine ndinabadwa mu 1925. Mu 1937, munthu wina wa Mboni za Yehova, Auguste Beugin, kapena Papa Auguste monga momwe tinkamutchulira, anayamba kubweretsera makolo anga Nsanja ya Olonda ya m’chinenero cha ku Hungary. Iwo anasangalala nawo magaziniwo, koma onse aŵiri sanakhale Mboni za Yehova.

Ngakhale ndinali wamng’ono, mtima wanga unakhudzidwa ndi zimene ndinaŵerenga mu Nsanja ya Olonda, ndipo mkazi wa mwana wa Papa Auguste, Suzanne Beugin, anandisamalira. Makolo anga anamuloleza kuti azipita nane ku misonkhano. Kenaka nditayamba kugwira ntchito, bambo anga sanasangalale nazo zoti ndizipita ku misonkhano Lamlungu. Ngakhale kuti Bambo anali munthu wabwino, anadandaula kuti: “M’kati mwa mlungu sukhala pakhomo, ndipo Lamlungu umapita ku misonkhano yakoyo!” Koma ndinapitirizabe kupita ku misonkhanoyo. Choncho tsiku lina bambo anga anandiuza kuti: “Longedza katundu wako uchoke pakhomo pano!” Unali usiku. Ndinali ndi zaka 17 zokha, ndipo ndinalibe koloŵera. Ndinapita ku nyumba ya Suzanne, misozi ili chuchuchu. Ndinakhala ndi Suzanne mlungu umodzi kenaka Bambo anatuma mkulu wanga kuti adzanditenge. Ndinali munthu wamanyazi, koma mfundo imene ili pa 1 Yohane 4:18 inandithandiza kukhala wolimba. Lemba limenelo limati “chikondi changwiro chitaya kunja mantha.” Mu 1942, ndinabatizidwa.

Cholowa Chauzimu Chamtengo Wapatali

Marian: Ndinabatizidwa mu 1942, limodzi ndi azichemwali anga Stéphanie ndi Mélanie ndi mkulu wanga Stéphane. Kunyumba kwathu, nthaŵi zonse tinkatsatira Mawu a Mulungu. Tonse tikakhala pamipando kuzungulira thebulo, Bambo ankatiŵerengera Baibulo m’chinenero cha Chipolishi. Madzulo ambiri tinkamvetsera makolo athu akamatiuza zimene anakumana nazo mu ntchito yolalikira Ufumu. Zinthu zolimbikitsa mwauzimu zimenezi zinatiphunzitsa kukonda Yehova ndi kumudalira kwambiri. Chifukwa cha matenda bambo anasiya ntchito, koma anapitirizabe kutisamalira mwauzimu ndiponso kutipezera zosoŵa pamoyo wathu.

Popeza tsopano Bambo ankakhala ndi nthaŵi yambiri, kamodzi pa mlungu ankachititsa phunziro la Baibulo m’chinenero cha Chipolishi ndi achinyamata a mumpingomo. Pamaphunziro amenewo ndinaphunzira kuŵerenga Chipolishi. Bambo analimbikitsanso achinyamatawo m’njira zina. Nthaŵi ina pamene Mbale Gustave Zopfer, amene panthaŵiyo anali kuyang’anira ntchito ya Mboni za Yehova ku France, anadzacheza ku mpingo wathu, Bambo anakonza kwaya ndi seŵero la m’Baibulo lokhala ndi zovala zake zapadera lonena za phwando la Mfumu Belisazara ndi dzanja lolemba pakhoma. (Danieli 5:1-31) M’seŵerolo, Danieli anali Louis Piéchota, amene kenaka anadzakhala wolimba osagonjera a Nazi. * Umu ndi mmene anafe tinaleredwera mpaka kukula. Tinaona kuti makolo athu nthaŵi zonse anali kuchita khama pa zinthu zauzimu. Masiku ano ndimazindikira kuti makolo athu anatisiyira cholowa chamtengo wapatali kwambiri.

Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itayamba mu 1939, ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova inaletsedwa ku France. Panthaŵi ina, m’mudzi mwathu munabwera anthu kuti adzafufuze nyumba zathu. Asilikali achijeremani anazungulira nyumba zonse. Bambo anali atakonza pansi pa wodilopu n’kupasintha kuti kunsi kwakeko tizibisako zinthu, ndipo tinabisako mabuku osiyanasiyana ofotokoza za m’Baibulo. Komabe, timabuku tingapo ta Fascism or Freedom tinali mu dilowo ya thebulo. Bambo anatibisa msanga m’matumba a jekete imene inali pakhoma m’nyumbamo. Asilikali aŵiri ndi wapolisi wachifalansa anafufuza nyumba yathu. Tinadikira kuti amalize kufufuzako mitima ili m’malere. Msilikali mmodzi anayamba kufufuza m’zovala zimene zinali pakhoma zija, ndipo kenaka anadzalowa m’khitchini mmene tinali atanyamula timabuku tija. Anatipenyetsetsa ifeyo n’kuika timabukuto pathebulo, kenaka n’kupitiriza kufufuza kwina. Ndinanyamula timabukuto msangamsanga n’kutiika mu dilowo ina imene asilikaliwo anali ataifufuza kale. Msilikaliyo sanafunsenso za timabuku tija, ndipo zinaoneka ngati anangotiiwala basi!

Kuyamba Utumiki wa Nthaŵi Zonse

Mu 1948 ndinaganiza zoyamba kutumikira Yehova nthaŵi zonse pochita upainiya. Patatha masiku ochepa ndinalandira kalata yochokera ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku France. Kalatayo inafotokoza kuti ndaikidwa kuti ndikachite upainiya mu mpingo wa Sedan, kufupi ndi dziko la Belgium. Makolo anga anasangalala kundiona ndikutumikira Yehova m’njira yoteroyo. Komabe, Bambo anandifotokozera kuti kuchita upainiya si maseŵera. Ndi ntchito yovuta. Koma anandiuza kuti ndikhale womasuka kubwera kunyumba yawo nthaŵi iliyonse ndipo anati ngati nditakumana ndi mavuto adzandithandiza. Ngakhale kuti makolo anga analibe ndalama zambiri, anandigulira njinga yatsopano. Mpaka pano lisiti la njinga imeneyo ndikadali nalobe, ndipo ndikaliyang’ana, m’maso mwanga mumadzaza misozi. Bambo ndi Mayi anamwalira mu 1961, koma mawu anzeru a Bambo ndikuwakumbukirabe, ndipo andithandiza ndi kundilimbikitsa zaka za utumiki wanga zonsezi.

Munthu wina amene anandilimbikitsa ndi mlongo wina wa zaka 75 wa mu mpingo wa Sedan, dzina lake Elise Motte. Panthaŵi yachilimwe, ndinkapalasa njinga yanga kupita ku midzi yozungulira kukalalikira, ndipo Elise anali kundipeza kumeneko pa sitima. Koma tsiku lina okonza sitimayo anachita sitalaka ndipo Elise sakanatha kubwerera kunyumba. Nditathedwa nzeru ndinaganiza zomukweza Elise panjinga yanga n’kumutengera kunyumba kwawo, umene sunali ulendo wawofuwofu ayi. Tsiku lotsatira ndinatenga pilo wokhalira n’kukamutenga Elise kunyumba kwawo panjinga yanga. Anasiya kukwera sitimayo, ndipo anatha kumasunga ndalama zokwerera sitimazo n’kumatigulira chakumwa chotentha panthaŵi ya chakudya chamasana. Palibe anadziŵa kuti tsiku lina njinga yanga idzakhala yonyamulirapo anthu.

Maudindo Ena

Mu 1950 anandipempha kuti ndikhale woyang’anira dera lonse la kumpoto kwa France. Popeza ndinali ndi zaka 23 zokha, poyamba ndinachita mantha. Ndinaganiza kuti a ku ofesi ya nthambi alakwitsa! M’mutu mwanga munadzaza mafunso: ‘Kodi ndine woyenera kugwira ntchito imeneyi mwauzimu ndipo kodi thupi langa lingathe kugwira ntchito imeneyi? Kodi kugona malo osiyanasiyana mlungu uliwonse ndidzakuona bwanji?’ Kuwonjezera apo, kuyambira ndili ndi zaka sikisi ndakhala ndikudwala nthenda inayake ya maso. Nthenda imeneyi imachititsa kuti diso langa limodzi liziyang’ana cham’phepete. Nthaŵi zonse ndimangoona ngati anthu akundiyang’anitsitsa chifukwa cha vuto limeneli, ndipo ndimadera nkhaŵa zimene anthu achite akandiona. Koma ndikuyamikira kuti panthaŵi imeneyo Stefan Behunick, amene anamaliza maphunziro a sukulu ya amishonale ya Gileadi, anandilimbikitsa kwambiri. Mbale Behunick anali atathamangitsidwa ku Poland chifukwa cha ntchito yake yolalikira, ndipo anali atauzidwa kuti abwere ku France. Kulimba mtima kwake kunandifikadi pamtima. Ankalemekeza kwambiri Yehova ndiponso choonadi. Anthu ena ankaganiza kuti anali kundiletsa zinthu zambiri, koma ndinaphunzira zambiri kwa iye. Kulimba mtima kwake kunandithandiza kuti nanenso ndiyambe kulimba mtima.

Ntchito yoyang’anira dera inandithandiza kuti ndikumane ndi zinthu zabwino kwambiri mu utumiki wa kumunda. Mu 1953, anandipempha kuti ndikakumane ndi bambo enaake dzina lawo a Paoli, amene anali kukhala kum’mwera kwa Paris ndipo analembetsa kuti azilandira magazini ya Nsanja ya Olonda mwezi ndi mwezi. Ndinakumana nawo, ndipo anandiuza kuti kale asanapume pantchito anali msilikali ndipo anati amasangalala kwambiri kuŵerenga Nsanja ya Olonda. Anandiuza kuti ataŵerenga nkhani yonena za Chikumbutso cha imfa ya Kristu m’magazini yaposachedwa, anachita Chikumbutsocho okha ndipo nthaŵi yotsalayo madzulo amenewo anakhala akuŵerenga Masalmo. Kukambirana kwathuko kunatenga pafupifupi masana onse. Ndisanachoke, tinakambirananso mwachidule za ubatizo. Kenaka ndinawatumizira kalata yowaitana ku msonkhano wathu wadera, umene unali woti udzachitike kumayambiriro kwa 1954. Anabwera, ndipo mmodzi wa anthu 26 amene anabatizidwa pamsonkhano umenewo anali Mbale Paoli. Zochitika ngati zimenezo zimandipatsabe chimwemwe mpaka pano.

Rosa: Mu October 1948, ndinayamba kuchita upainiya. Nditatumikira m’tawuni ya Anor, kufupi ndi Belgium, ndinatumizidwa ku Paris, limodzi ndi mpainiya wina, Irène Kolanski (tsopano Leroy). Tinkakhala m’kachipinda kakang’ono ku Saint-Germain-des-Près pakati penipeni pa mzindawo. Chifukwa ndinakulira kumudzi, ndinkachita mantha ndi anthu a ku Paris. Ndinkaganiza kuti onse anali otsungula ndiponso anzeru kwambiri. Koma kenaka nditawalalikira ndinazindikira kuti anali chimodzimodzi ndi anthu ena onse. Nthaŵi zambiri alonda ankatithamangitsa, ndipo kuyambitsa maphunziro a Baibulo kunali kovuta. Ngakhale zinali choncho, anthu ena anamvetsera uthenga wathu.

Pamsonkhano wadera mu 1951, ine ndi Irène anatifunsa za utumiki wathu waupainiya. Kodi mukuganiza kuti ndi ndani amene anali kufunsa mafunsowo? Anali woyang’anira dera wachinyamata dzina lake Marian Szumiga. Tinali titakumanapo kamodzi m’mbuyomo, koma msonkhanowu utatha, tinayamba kulemberana makalata. Moyo wa Marian ndi wanga unali wofanana kwambiri, kuphatikizapo mfundo yoti tinabatizidwa chaka chimodzi ndipo tinayamba kuchita upainiya chaka chimodzi. Koma chofunika kwambiri chinali choti tonse timafuna kupitiriza utumiki wa nthaŵi zonse. Choncho titaganizira nkhaniyi n’kupemphera, tinakwatirana pa July 31, 1956. Titakwatirana choncho, ndinayamba moyo umene kwa ine unali watsopano kwambiri. Ndinafunika kuzoloŵera kukhala mkazi wapabanja komanso kupita ndi Marian mu ntchito yadera, zimene zinatanthauza kukhala m’nyumba yosiyana mlungu uliwonse. Poyamba sizinali zophweka, koma patsogolo pathu panali zinthu zosangalatsa zambiri.

Moyo Watanthauzo

Marian: M’zaka zapitazi, takhala ndi mwayi wothandiza nawo kukonzekera misonkhano yachigawo ingapo. Ndimakumbukira makamaka msonkhano umene unachitika mu 1966, ku Bordeaux. Panthaŵi imeneyo, ntchito ya Mboni za Yehova ku Portugal inali yoletsedwa. Choncho pulogalamu ya msonkhanoyo inakonzedwanso m’Chipwitikizi kuti Mboni zimene zikanatha kubwera ku France zidzapindule. Abale ndi alongo athu ambiri a ku Portugal anabwera, koma vuto linali kuwapezera malo okhala. Popeza Mboni za ku Bordeaux zinalibe malo ambiri m’nyumba zawo, tinachita lendi holo yoonetseramo maseŵero kuti ikhale ngati chipinda chogona. Tinachotsa mipando yonse, ndipo tinatenga katani ya kutsogolo kwa holoyo n’kugawa holoyo paŵiri, kuti mbali imodzi ikhale ya abale ndipo mbali ina ikhale ya alongo. Tinaikamonso zipinda zosambira ndi masinki, tinaika udzu wouma pansi, ndipo pamwamba pake tinaikapo malona. Aliyense anasangalala ndi zimene tinakonzazi.

Misonkhano ikatha, tinali kuchezera abale ndi alongo athu ku malo ogonawo. Kunali macheza abwino kwambiri. Tinalimbikitsidwa kwambiri ndi zimene anakumana nazo ngakhale kuti anapirira chizunzo kwa zaka zambiri. Pamene amachoka msonkhanowo utatha, tonsefe tinali ndi misozi m’maso mwathu.

Mwayi wina unabwera zaka ziŵiri izi zisanachitike, mu 1964, pamene anandipempha kuti ndikhale woyang’anira chigawo. Kachiŵirinso, ndinakayikira ngati ndikanatha kukwanitsa ntchito imeneyi. Koma ndinaganiza kuti ngati anthu a maudindo anandipempha kuti ndichite ntchito imeneyi, ndiye kuti amaona kuti ndingathe kuikwanitsa. Zinali zolimbikitsa kwambiri kutumikira mogwirizana ndi oyang’anira oyendayenda ena. Ndinaphunzira zambiri kwa iwo. Ambiri a iwo ndi zitsanzo zabwino za anthu oleza mtima ndi opirira, makhalidwe amene ali ofunika kwambiri m’maso mwa Yehova. Ndazindikira kuti ngati tiphunzira kudikira, Yehova amadziŵa kumene angatipeze.

Mu 1982 ofesi ya nthambi inatipempha kusamalira kagulu ka ofalitsa 12 a Chipolishi ku Boulogne-Billancourt, kumalekezero kwa Paris. Zimenezo zinandidabwitsa kwambiri. Ndinkadziŵa mawu okhudza ziphunzitso zathu m’Chipolishi, koma ndinkavutika kupanga ziganizo. Koma kukoma mtima ndi kufunitsitsa kuchita zinthu mogwirizana kwa abale amenewo kunandithandiza kwambiri. Masiku ano, mu mpingo umenewo muli ofalitsa pafupifupi 170, kuphatikizapo apainiya pafupifupi 60. Kenaka, ine ndi Rosa tinayendera magulu ndi mipingo ya Chipolishi ku Austria, Denmark, ndi Germany.

Kusintha kwa Zinthu

Moyo wathu unali woyendera mipingo yosiyanasiyana koma chifukwa cha kufooka kwa thanzi langa, ndinasiya utumiki woyendayenda mu 2001. Tinapeza nyumba m’tawuni ya Pithiviers, kumene mchemwali wanga Ruth akukhala. A ku ofesi ya nthambi mwachifundo anatiika kukhala apainiya apadera n’kutilola kuti tizilalikira maola ogwirizana ndi thanzi lathu.

Rosa: Chaka choyamba titasiya ntchito yadera ndinavutika kwambiri. Kusinthako kunali kwakukulu kwambiri moti ndinaona ngati ndatha ntchito. Kenaka ndinadzikumbutsa kuti ndingathebe kugwiritsa ntchito nthaŵi ndi mphamvu zimene ndili nazo mwa kutumikira monga mpainiya. Masiku ano ndimasangalala kutumikira limodzi ndi apainiya ena mu mpingo mwathu.

Yehova Wakhala Akutisamalira Nthaŵi Zonse

Marian: Ndikuyamikira kwambiri kwa Yehova kuti Rosa wakhala mnzanga kwa zaka 48 zapitazi. Nthaŵi yonse yomwe tinali mu ntchito yoyendayenda, wakhala akundichirikiza kwambiri. Sindinamumvepo ngakhale n’kamodzi komwe akunena kuti, ‘Zikanakhala bwino tikanakhazikika n’kukhala ndi nyumba yathu.’

Rosa: Nthaŵi zina anthu ankandiuza kuti, “Moyo umene mukukhalawu si moyo weniweni. M’mangokhala ndi anthu ena nthaŵi zonse.” Koma kodi “moyo weniweni” ndiye uti? Nthaŵi zambiri timadziunjikira zinthu zambirimbiri zimene zingatilepheretse kuchita zinthu zauzimu. Zimene timafunikira kwenikweni ndi bedi labwino, thebulo, ndi zinthu zina zochepa zofunika pamoyo. Pokhala apainiya, tinali ndi katundu wochepa kwambiri, koma tinali ndi zonse zofunika kuti tichite chifuniro cha Yehova. Nthaŵi zina anthu ankandifunsa kuti, “Kodi mudzachita chiyani mukadzakalamba mulibe nyumba yanuyanu ndi penshoni?” Ndiyeno ndinkawauza mawu amene ali pa Salmo 34:10 oti: “Koma iwo akufuna Yehova sadzasoŵa kanthu kabwino.” Yehova wakhala akutisamalira nthaŵi zonse.

Marian: Zoonadi! Ndipo Yehova watipatsa zambiri kuposa zimene timafunikira. Mwachitsanzo, mu 1958 anandisankha kuti ndikaimire dera lathu pamsonkhano wa mayiko ku New York. Koma tinalibe ndalama zogulira tikiti ya ndege ya Rosa. Madzulo enaake mbale wina anatipatsa envulopu yolembedwa “New York” pamwamba pake. Mphatso imene inali m’kati mwake inathandiza kuti Rosa athe kupita nane!

Ine ndi Rosa sitidandaula m’pang’ono pomwe za zaka zimene tathera mu utumiki wa Yehova. Sitinataye chilichonse koma tinapeza zambiri​—moyo watanthauzo ndi wosangalala mu utumiki wa nthaŵi zonse. Yehova ndi Mulungu wodabwitsadi. Taphunzira kumukhulupirira ndi mtima wonse, ndipo chikondi chathu pa iye chakula. Abale athu ena achikristu ataya miyoyo yawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Koma ndikukhulupirira kuti m’kupita kwa zaka, munthu angapereke moyo wake nsembe pang’onopang’ono. Zimenezo n’zimene ine ndi Rosa tayesetsa kuchita mpaka pano, ndipo n’zimene tikufuna kuchitabe m’tsogolo muno.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Nkhani ya moyo wa Louis Piéchota yoti, “I Survived the ‘Death March,’” inafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda yachingelezi ya August 15, 1980.

[Chithunzi patsamba 20]

François ndi Anna Szumiga ndi ana awo, Stéphanie, Stéphane, Mélanie, ndi Marian cha m’ma 1930. Marian ndi amene waimirira pa kathebuloyo

[Chithunzi patsamba 22]

Pamwambapa: Kufalitsa mabuku ofotokoza za m’Baibulo pamsika ku Armentières, kumpoto kwa France, mu 1950

[Chithunzi patsamba 22]

Kumanzere: Stefan Behunick ndi Marian mu 1950

[Chithunzi patsamba 23]

Rosa (kumanzere) ndi mnzake wochita naye upainiya Irène (wachinayi kuchokera kumanzere) akuitanira anthu ku msonkhano mu 1951

[Chithunzi patsamba 23]

Marian ndi Rosa tsiku loti achita ukwati wawo mawa

[Chithunzi patsamba 23]

Pokayendera mipingo nthaŵi zambiri tinkakwera njinga