Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Muyenera Kulimvera Pemphero la Ambuye

Mmene Muyenera Kulimvera Pemphero la Ambuye

Mmene Muyenera Kulimvera Pemphero la Ambuye

PEMPHERO la Ambuye, limene ananena Yesu Kristu pa Ulaliki wa pa Phiri, lili m’Baibulo pa Mateyu chaputala 6, kuchokera vesi 9 mpaka 13. Asananene pempheroli, Yesu ananena kuti: “Popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwawo.”​—Mateyu 6:7.

Apatu n’zoonekeratu kuti cholinga cha Yesu sichinali chakuti anthu azilakatula pamtima Pemphero la Ambuyeli. Inde, n’zoona kuti panthaŵi ina, iye anabwereza pempheroli pophunzitsa gulu lina la anthu. (Luka 11:2-4) Komano mawu a pempheroli amene analembedwa m’buku la Uthenga Wabwino la Mateyu amasiyanako ndi amene analembedwa m’buku la Luka. Chinanso n’chakuti mapemphero amene Yesu ndiponso otsatira ake anadzapemphera patsogolo pake sankachita kutsatira ndendende mawu amene ali m’pemphero lachitsanzoli.

Nanga kodi Pemphero la Ambuye analilemberanji m’Baibulo? Pogwiritsira ntchito pempheroli Yesu anatiphunzitsa mmene tingamapempherere kuti Mulungu atimve. M’pemphero limeneli, timapezanso mayankho a mafunso ofunika kwambiri pamoyo wathu. Motero tiyeni tione mbali iliyonse ya Pemphero la Ambuye payokhapayokha.

Kodi Dzina la Mulungu Ndani?

“Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Mawu oyamba a pemphero lachitsanzoli amatithandiza kuti tikhale ndi unansi wabwino ndi Mulungu pomutchula kuti “Atate wathu.” Monga mwana, amene mwachibadwa amagwirizana ndi makolo ake amene amam’konda ndiponso kumumvetsa, ifenso tingathe kukhala omasuka kupemphera kwa Atate wathu wakumwamba, mosakayika n’komwe kuti iwo akufuna kumva pemphero lathu. Mfumu Davide anaimba kuti: “Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.”​—Salmo 65:2.

Yesu anatilangiza kuti tiyenera kupemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe. Koma kodi dzina la Mulungu ndani? Baibulo limayankha funsoli motere: “Inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, Ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” (Salmo 83:18) Kodi munayamba mwaonapo dzina lakuti Yehova m’Baibulo?

Kwenikweni, dzina la Mulungu lakuti Yehova limapezeka nthaŵi pafupifupi 7,000 m’mabuku akale a Baibulo olembedwa pamanja. Komano omasulira ena achita kufika pochotsa dzinali m’mabaibulo amene iwo amasulira. Motero m’pake kuti timapemphera kwa Mlengi wathu kuti ayeretse dzina lake. (Ezekieli 36:23) Njira imodzi yochita zinthu mogwirizana ndi pempheroli ndiyo kumatchula dzina la Yehova tikamapemphera.

Mayi wina dzina lake Patricia anakulira m’banja la Chikatolika ndipo ankalidziŵa bwino kwambiri Pemphero la Ambuye. Kodi iye anatani mayi wina wa Mboni za Yehova atamusonyeza dzina la Mulungu m’Baibulo? Iye akufotokoza kuti: “Sindinamvetse ayi! Motero ndinatenga Baibulo langa, ndipo ndinadabwa kuona kuti dzinali linalimonso. Kenaka mayi wa Mboniyo anandisonyeza Mateyu 6:9, 10 n’kulongosola kuti Pemphero la Ambuye limanenanso za dzina la Mulungu limeneli. Zimenezi zinandichititsa chidwi kwambiri ndipo ndinamuuza kuti ayambe kundiphunzitsa Baibulo.”

Zofuna za Mulungu Zikwaniritsidwe Padziko Lapansi

“Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:10) Kodi mbali imeneyi ya pemphero lachitsanzo la Yesu idzakwaniritsidwa motani? Anthu ambiri akamaganizira za kumwamba amaganiza zakuti n’kwamtendere ndiponso n’kwabata. Baibulo limati kumwamba ndi “pokhala pa [Yehova] poyera, ndi pa ulemerero.” (Yesaya 63:15) M’pake kuti timapemphera kuti kufuna kwa Mulungu kuchitike pansi pano “monga kumwamba.” Koma kodi zimenezi zidzachitikadi?

Mneneri wa Yehova, Danieli analosera kuti: “Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [a padziko pano]. Nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Ufumu kapena kuti boma lakumwamba limeneli, posachedwapa lidzachitapo kanthu kuti libweretse mtendere padziko lonse polamulira mwachilungamo.​—2 Petro 3:13.

Timasonyeza chikhulupiriro tikamapempherera kuti Ufumu wa Mulungu udze ndi kuti kufuna kwake kuchitike padziko lapansi ndipotu chikhulupiriro chathuchi sichidzapita pachabe. Mtumwi wachikristu Yohane analemba kuti: “Ndinamva mawu akulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” Ndiyeno Yohane anapitiriza kunena kuti: “Ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu anati, . . . Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi oona.”​—Chivumbulutso 21:3-5.

Kupemphera Pofuna Zinthu Zofunikira Pamoyo Wathu

Zimene Yesu ananena m’pemphero lachitsanzoli zimasonyeza kuti Yesuyo amafuna kuti tikamapemphera tiziganizira kwambiri za dzina ndi chifuno cha Mulungu. Komabe pempheroli kenaka limayamba kutchula zinthu zotikhudza ifeyo pamoyo wathu zimene timayeneranso kumupempha Yehova.

Choyamba mwa zinthuzi n’chakuti: “Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero.” (Mateyu 6:11) Kumeneku sikuti n’kupempha chuma ayi. Yesu anatilimbikitsa kuti tizipempha “tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku.” (Luka 11:3) Mogwirizana ndi Pemphero la Ambuye, tingathe kupemphera mwachikhulupiriro kuti Mulungu atipatse zofuna zathu za tsiku ndi tsiku ngati ifeyo timam’konda ndiponso kumumvera.

Kuda nkhaŵa kwambiri ndi mavuto a zachuma kungatichititse kunyalanyaza zosoŵa zathu zauzimu motero n’kulephera kuchita zimene Mulungu amafuna kuti tizichita. Koma ngati kulambira Mulungu ndiko kuli chinthu chofunika kwambiri pamoyo wathu, tisakayike n’komwe kuti Mulungu adzamva mapemphero athu okhudza zinthu zimene timafunikira pamoyo wathu, monga chakudya ndi zovala. Yesu ananena kuti: “Muthange mwafuna Ufumu [wa Mulungu] ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:26-33) Kufuna chilungamo cha Mulungu n’kovuta, popeza kuti tonse ndife ochimwa ndipo timafunikira kukhululukidwa. (Aroma 5:12) Pemphero la Ambuye limakhudzanso nkhani imeneyi.

Kupemphera Pofuna Kukhululukidwa

“Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu.” (Mateyu 6:12) M’buku la Luka “mangawa” amene anatchulidwa m’Pemphero la Ambuyeli anawatchulanso kuti “machimo.” (Luka 11:4) Koma kodi Yehova Mulungu angatikhululukiredi machimo athu?

Mfumu Davide wa dziko lakale la Israyeli anachita machimo aakulu kwambiri, komabe analapa ndipo anapemphera mwachikhulupiriro kuti: “Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.” (Salmo 86:5) Izitu n’zolimbikitsa kwabasi! Atate wathu wakumwamba n’ngokonzeka ‘kukhululukira’ machimo anthu onse amene amaitana dzina lake mosonyeza kulapa. Yehova Mulungu angathe kutikhululukira machimo athu onse.

Komabe, Yesu ananenapo kuti choyamba ifeyo tiyenera kuchita kaye zinazake. Anati, kuti Mulungu atikhululukire, tiyenera kukhululukira kaye anthu anzathu. (Mateyu 6:14, 15) Ngakhale kuti Yobu, yemwe anali munthu wolungama anavutitsidwa ndi anzake atatu, iye anawakhululukira ndipo mpaka anawapempherera. (Yobu 42:10) Tikamakhululukira anthu amene amatichimwira, timasangalatsa Mulungu ndipo nayenso angathe kutichitira chifundo.

Popeza kuti Mulungu amafunitsitsa kumva mapemphero athu nafenso tiyenera kufunitsitsa kuchita zinthu zoti azitiyanja. Ndipotu tingatero ngakhale kuti sindife angwiro. (Mateyu 26:41) Apanso, Yehova angatithandize, monga mmene Yesu anasonyezera pomaliza pemphero lachitsanzo lija mwa kupempha chinthu chofunika kwambiri.

Kupemphera Pofuna Kupitiriza Kuchita Zinthu Molungama

“Musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.” (Mateyu 6:13) Yehova samatisiya pamene tikuyesedwa ndipo samatichititsa kuti tichimwe. Mawu ake amati: “Mulungu sakhoza kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu.” (Yakobo 1:13) Mulungu amalola kuti tiyesedwe, koma angathe kutichotsa m’manja mwa Woyesa Wamkulu “woipayo” Satana Mdyerekezi.

Mtumwi Petro analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu Mdyerekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akam’likwire.” (1 Petro 5:8) Pajatu Satana anayesa Yesu Kristu, ngakhale kuti anali wangwiro. Kodi cholinga cha Satana chinali chotani? Ankafuna kuti amusiyitse Yesu kulambira Yehova Mulungu moona. (Mateyu 4:1-11) Cholinga cha Satana n’chakuti inunso akuchiteni zomwezi, ngati mukufuna kutumikira Mulungu!

Mdyerekezi amatha kugwiritsira ntchito dzikoli, lomwe lili m’manja mwake, potiyesa kuti tichite zinthu zotsutsana ndi Mulungu. (1 Yohane 5:19) Motero m’pofunika kwambiri kuti nthaŵi zonse tizipempha thandizo kwa Mulungu, makamaka tikakhala ndi chiyeso chimene chikupitirirabe. Ndipo tikamalambira Yehova mogwirizana ndi Baibulo, lomwe lili Mawu ake ouziridwa, iye angatipulumutse potithandiza kulimbana naye bwinobwino Mdyerekeziyo. Baibulo limatiuza kuti: “Mulungu ali wokhulupirika,” ndiye limatinso, “sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza.”​—1 Akorinto 10:13.

M’pofunika Kukhulupirira Mulungu

N’zolimbikitsa kwambiri kudziŵa kuti Atate wathu wakumwamba amatiganizira aliyense payekhayekha. Iye anafika pomuuza Mwana wake Yesu Kristu kuti atiphunzitse kupemphera. Mosakayikira zimenezi zimatilimbikitsa kusangalatsa Yehova Mulungu. Koma kodi tingamusangalatse bwanji?

Baibulo limanena kuti: “Wopanda chikhulupiriro sikutheka kum’kondweretsa [Mulungu]; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.” (Ahebri 11:6) Kodi chikhulupiriro chotere munthu angachipeze bwanji? Baibulo limati: “Chikhulupiriro chidza ndi mbiri.” (Aroma 10:17) Mboni za Yehova zimasangalala zikamauza Mawu a Mulungu anthu amene ali ofunitsitsa kutumikira Mulungu ndi chikhulupiriro chenicheni.

Tikukhulupirira kuti nkhani yolongosola Pemphero la Ambuye ino yakuthandizani kumvetsetsa pempheroli. Mungathe kuyamba kukhulupirira kwambiri Yehova popitiriza kuphunzira za Iye ndiponso za mphoto zimene adzapereke kwa “iwo akum’funa Iye.” Pitirizani kuphunzira za Atate wanu wakumwambayu ndiponso za zolinga zake kuti muzikondana naye kwambiri mpaka kalekale.​—Yohane 17:3.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

“Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu. Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.”​—Mateyu 6:9-13

[Chithunzi patsamba 7]

Yehova amapereka zinthu zofunikira pamoyo kwa anthu onse amene amam’konda

[Chithunzi patsamba 7]

Mulungu amatithandizanso kulimbana ndi Mdyerekezi

[Chithunzi patsamba 7]

Ifeyo, ngati Yobu, tikamakhululukira anthu amene akutilakwira, Mulungu angatichitire chifundo