Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tavalani Zida Zonse za Mulungu”

“Tavalani Zida Zonse za Mulungu”

“Tavalani Zida Zonse za Mulungu”

“Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchirimika pokana machenjerero a Mdyerekezi.”​—AEFESO 6:11.

1, 2. Longosolani panokha zida zauzimu zimene Akristu akufunika kuvala.

MPHAMVU za mzinda wa Roma zinafika pachimake m’zaka 100 zoyambirira Kristu Atabwera. Mphamvu za asilikali a Roma zinathandiza kuti mzindawu ulamulire mbali yaikulu ya dziko lapansi limene linkadziŵika panthaŵiyo. Wolemba mbiri wina anafotokoza kuti asilikali ameneŵa anali “odziŵa bwino kumenya nkhondo kuposa magulu ena onse a asilikali amene anakhalapo.” Asilikali odziŵa ntchito yawo a Roma anali anthu osunga mwambo ndipo ankachita maphunziro ovuta kwambiri a nkhondo, koma kuti gulu lawoli lipambane zinkadaliranso zida zawo. Mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito zida za msilikali wachiroma pofuna kusonyeza zida zauzimu zimene Akristu akufunikira kukhala nazo kuti apambane pomenyana ndi Mdyerekezi.

2 Zida zauzimu zimenezi zinafotokozedwa pa Aefeso 6:14-17. Paulo analemba kuti: “Chirimikani, mutadzimangira m’chuuno mwanu ndi choonadi, mutavalanso chapachifuwa cha chilungamo; ndipo mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere; koposa zonse mutadzitengeranso chikopa [chachikulu, NW] cha chikhulupiriro, chimene mudzakhoza kuzima nacho mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Mutengenso chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la Mzimu, ndilo Mawu a Mulungu.” Malinga ndi mmene anthufe timaonera zinthu, tingati zida zimene Paulo anafotokoza zinali kum’teteza kwambiri msilikali wachiroma. Ndiyeno, msilikaliyo ankakhalanso ndi lupanga, lomwe linali lofunika kwambiri pamene akulimbana ndi mdani.

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera malangizo a Yesu Kristu ndi kutsatira chitsanzo chake?

3 Kuwonjezera pa zida ndiponso maphunziro amene asilikali achiroma ankalandira, kuti asilikaliwo apambane nkhondo ankafunika kumvera mkulu wawo wankhondo. N’chimodzimodzinso ndi Akristufe. Tiyenera kumvera Yesu Kristu, amene Baibulo limam’tchula kuti ndi “wolamulira anthu” kapena kuti mkulu wankhondo. (Yesaya 55:4) Iye alinso “mutu wa Eklesia.” (Aefeso 5:23) Yesu amatipatsa malangizo a nkhondo yathu yauzimu ndiponso amatisonyeza chitsanzo chabwino kwambiri cha mmene tingavalire zida zauzimu. (1 Petro 2:21) Popeza khalidwe longa la Kristu n’lofanana kwambiri ndi zida zathu zankhondo yauzimu, Malemba amatilangiza kuti tikhale ndi mtima wonga wa Kristu. (1 Petro 4:1) Tikatha kupenda chida chilichonse pa zida zathu zauzimu, tigwiritsira ntchito chitsanzo cha Yesu posonyeza kufunika ndi ubwino wa chidacho.

Kuteteza Chuuno, Chifuwa, ndi Mapazi

4. Kodi lamba anali kugwira ntchito yanji pa zida za msilikali, ndipo akuimira chiyani?

4 Mutadzimangira m’chuuno mwanu ndi choonadi. M’nthaŵi za m’Baibulo, asilikali ankavala lamba wamkulu wachikopa, amene m’mimba mwake mwina ankakhala wamkulu masentimita 5 kapena mpaka kufika 15. Akatswiri ena omasulira Baibulo amati vesili liyenera kumveka kuti, “mutadzimangirira zolimba m’chuuno mwanu ndi choonadi ngati lamba.” Lamba wa msilikali ankathandiza kuteteza chuuno, ndiponso anali malo abwino kukolekapo lupanga. Msilikali akamanga lamba m’chuuno, ndiye kuti wakonzekera nkhondo. Paulo anagwiritsa ntchito lamba wa msilikali posonyeza mmene miyoyo yathu iyenera kukhudzidwira ndi choonadi cha m’Malemba. Kunena mophiphiritsa tingati, tiyenera kudzimanga nacho mothinitsa kwambiri, kuti miyoyo yathu izigwirizana ndi choonadicho ndiponso kuti nthaŵi iliyonse tizitha kuyankha anthu otsutsa choonadicho. (Salmo 43:3; 1 Petro 3:15) Kuti izi zitheke, tikufunika kuphunzira Baibulo mwakhama ndi kusinkhasinkha zimene zili m’Baibulomo. Yesu anali ndi chilamulo cha Mulungu ‘m’kati mwa mtima mwake.’ (Salmo 40:8) Motero, om’tsutsa akamufunsa funso iye ankatha kuwayankha ndi Malemba amene anawaloweza pamtima.​—Mateyu 19:3-6; 22:23-32.

5. Fotokozani mmene malangizo a m’Malemba angatithandizire tikakumana ndi mayesero kapena tikamakopeka kuchita zoipa.

5 Tikamalola choonadi cha m’Baibulo kutitsogolera, choonadicho chingatiteteze ku maganizo olakwika ndipo chingatithandize kusankha zinthu mwanzeru. Malangizo a m’Baibulo angatilimbikitse kuti titsimikize mtima kuchita zabwino tikamakopeka kuchita zoipa kapena tikakumana ndi mayesero. Zimakhala ngati tikuona Mlangizi wathu Wamkulu, Yehova, ndi kumva mawu kumbuyo kwathu akuti: “Njira ndi iyi, yendani inu m’menemo.”​—Yesaya 30:20, 21.

6. Kodi n’chifukwa chiyani mtima wathu wophiphiritsira umafunika kuuteteza, ndipo n’chifukwa chiyani chilungamo chingauteteze bwino kwambiri?

6 Chapachifuwa cha chilungamo. Chovala chapachifuwa cha msilikali chinkateteza mtima womwe ndi chiwalo chofunika kwambiri. Mtima wathu wophiphiritsira, womwe ndi zolinga zathu ndiponso maganizo athu, umafunika kuuteteza kwambiri chifukwa chakuti n’zosavuta kuti uchite cholakwa. (Genesis 8:21) Motero, tiyenera kudziŵa ndi kukonda mfundo zolungama za Yehova. (Salmo 119:97, 105) Chifukwa choti timakonda chilungamo, timakana maganizo a anthu a m’dzikoli onyalanyaza kapena kusukulutsa malangizo omveka bwino a Yehova. Komanso, tikamakonda chabwino ndi kudana ndi choipa, timapeŵa makhalidwe amene angawononge miyoyo yathu. (Salmo 119:99-101; Amosi 5:15) Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino pankhani imeneyi, chifukwa ponena za iye, Malemba amati: “Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa.”​—Ahebri 1:9. *

7. N’chifukwa chiyani msilikali wachiroma ankafunika nsapato zabwino, ndipo izi zikuimira chiyani?

7 Mutadziveka mapazi anu ndi makonzedwe a Uthenga Wabwino wa mtendere. Asilikali achiroma ankafunika kuvala nsapato kapena nkhwayira zolimba, chifukwa chakuti pankhondo, iwo ankatha kuyenda mtunda wa makilomita 30 tsiku lililonse atavala kapena kunyamula zida ndi zinthu zina zolemera, ndipo zonse pamodzi zinkalemera makilogalamu 27. Moyenerera, Paulo anagwiritsa ntchito nsapato posonyeza kuti tizikhala okonzeka kulalikira uthenga wa Ufumu kwa aliyense amene angamvetsere. Izi ndi zofunika chifukwa chakuti anthu angam’dziŵe bwanji Yehova ngati sitili okonzeka ndiponso ofunitsitsa kulalikira?​—Aroma 10:13-15.

8. Kodi tingatsanzire motani chitsanzo cha Yesu polalikira uthenga wabwino?

8 Kodi ntchito yofunika kwambiri pamoyo wa Yesu inali yotani? Iye anauza Kazembe wa Roma, Pontiyo Pilato kuti: “Ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” Yesu ankalalikira paliponse pamene wapeza munthu wofuna kumvetsera, ndipo ankasangalala kwambiri ndi utumiki wake moti unali chinthu chofunika kuposa zofuna zake zonse. (Yohane 4:5-34; 18:37) Ngati nafe tili okonzeka kulalikira uthenga wabwino monga mmene Yesu ankachitira, tingapeze mipata yambiri yolalikirira ena. Komanso, kuchita zambiri mu utumiki wathu kumatithandiza kukhala olimba mwauzimu.​—Machitidwe 18:5.

Chikopa, Chisoti, ndi Lupanga

9. Kodi chikopa chachikulu chinkamuteteza bwanji msilikali wachiroma?

9 Chikopa chachikulu cha chikhulupiriro. Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “chikopa chachikulu” amanena za chishango chimene chinkakhala chachikulu chotha kubisa mbali yaikulu ya thupi. Chida ichi chinali kuteteza munthu ku ‘mivi yoyaka moto’ yotchulidwa pa Aefeso 6:16. M’nthaŵi za m’Baibulo, asilikali anali kugwiritsira ntchito mivi yopangidwa ndi bango. Miviyi inkakhala ndi kachitsulo kamene ankathiramo mafuta otchedwa nafuta amene amayaka. Katswiri wina wamaphunziro ananena kuti mivi imeneyi inali “m’gulu la zida zoopsa kwambiri pankhondo zakale.” Ngati msilikali alibe chikopa chachikulu chomuteteza ku mivi yotereyi, ankatha kuvulazidwa kwambiri kapena mwinanso kuphedwa kumene.

10, 11. (a) Kodi ndi ‘mivi yoyaka moto’ iti ya Satana imene ingafoole chikhulupiriro chathu? (b) Kodi chitsanzo cha Yesu chikusonyeza motani kufunika kwa chikhulupiriro panthaŵi ya mayesero?

10 Kodi ndi ‘mivi yoyaka moto’ yotani imene Satana amagwiritsira ntchito pofuna kufoola chikhulupiriro chathu? Iye angathe kuyambitsa chizunzo kapena kupangitsa kuti a m’banja, kuntchito, kapena kusukulu kwathu azititsutsa. Komanso kukhala ndi maganizo ofuna kupeza chuma chambiri ndiponso msampha wachiwerewere zawawononga mwauzimu Akristu ena. Kuti tidziteteze ku ngozi zotere, ‘koposa zonse tiyenera kudzitengeranso chikopa chachikulu cha chikhulupiriro.’ Timakhala ndi chikhulupiriro chifukwa chophunzira za Yehova, kuyankhula naye kaŵirikaŵiri m’pemphero, ndi kudziŵa mmene iye amatitetezera ndi kutidalitsira.​—Yoswa 23:14; Luka 17:5; Aroma 10:17.

11 Yesu ali padziko lapansi pano anasonyeza kufunika kokhala ndi chikhulupiriro cholimba panthaŵi za mavuto aakulu. Iye anadalira ndi mtima wake wonse maganizo a Atate wake ndipo anali kusangalala kuchita chifuniro cha Mulungu. (Mateyu 26:42, 53, 54; Yohane 6:38) Yesu pamene anathedwa nzeru kwambiri m’munda wa Getsemane, anauza Atate wake kuti: “Si monga ndifuna Ine, koma Inu.” (Mateyu 26:39) Yesu sanaiŵale n’kamodzi komwe kufunika kokhala wokhulupirika ndi kukondweretsa Atate wake. (Miyambo 27:11) Ngati timadalira Yehova monga momwe Yesu anachitiramu, ndiye kuti sitidzalola kuti chikhulupiriro chathu chifooke chifukwa chonenedwa kapena kutsutsidwa. M’malo mwake, chikhulupiriro chathu chidzalimba ngati tidalira Mulungu, kumukonda, ndi kusunga malamulo ake. (Salmo 19:7-11; 1 Yohane 5:3) Palibe mphoto ina iliyonse kapena chisangalalo chilichonse cha nthaŵi yochepa chabe chimene chingafanane ndi madalitso amene Yehova wasungira anthu amene amam’konda.​—Miyambo 10:22.

12. Kodi chisoti chathu chophiphiritsira chimateteza chiwalo chofunika kwambiri chiti, ndipo n’chifukwa chiyani chitetezo chimenecho chili chofunika?

12 Chisoti cha chipulumutso. Chisoti chinali kuteteza bongo wa msilikali, kumene kumachoka nzeru. Chiyembekezo chathu chachikristu chikuyerekezeredwa ndi chisoti chifukwa chakuti chimateteza maganizo athu. (1 Atesalonika 5:8) Ngakhale kuti tinasankha zochita pamoyo motsatira zinthu zoona za m’Mawu a Mulungu, tidakali anthu ofooka, opanda ungwiro. N’zosavuta kuti maganizo athu asokonezeke. Zolinga zimene dzikoli limalimbikitsa zingathe kudodometsa ngakhalenso kutiiwalitsa zimene tikuyembekezera kuti Mulungu adzatichitira. (Aroma 7:18; 12:2) Mdyerekezi anayesetsa kupatutsa Yesu mwa kumulonjeza kuti am’patsa “mayiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo,” koma sanakwanitse. (Mateyu 4:8) Yesu anakaniratu lonjezo limenelo, ndipo Paulo ananena za iye kuti: “Chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake [Yesu], anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala pa dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.”​—Ahebri 12:2.

13. Kodi tingatani kuti tipitirize kudalira malonjezo a m’tsogolo?

13 Chidaliro chimene Yesu anali nacho sikuti chinangobwera chokha. Tikadzadza maganizo athu ndi zolinga za dongosolo lino la zinthu m’malo moika mtima wathu pa zinthu zimene tikuyembekezera m’tsogolo, chikhulupiriro chathu pa malonjezo a Mulungu chingayambe kufooka. M’kupita kwa nthaŵi, tingathenso kufika pokhala opanda chikhulupiriro. Koma ngati timasinkhasinkha malonjezo a Mulungu nthaŵi zonse, tidzapitiriza kusangalala ndi chiyembekezo chomwe tapatsidwa.​—Aroma 12:12.

14, 15. (a) Kodi lupanga lathu lophiphiritsira n’chiyani, ndipo kodi tingaligwiritse ntchito motani? (b) Fotokozani mmene lupanga la mzimu lingatithandizire kugonjetsa chiyeso.

14 Lupanga la mzimu. Mawu a Mulungu, kapena kuti uthenga wake, amene ali m’Baibulo ali ngati lupanga lakuthwa konsekonse lamphamvu kwambiri limene lingathe kudula mabodza a zipembedzo ndi kuthandiza anthu a mitima yabwino kupeza ufulu wauzimu. (Yohane 8:32; Ahebri 4:12) Lupanga lauzimu limeneli lingatithandizenso pamene takumana ndi zokopa kapena ampatuko amene akufuna kuwononga chikhulupiriro chathu. (2 Akorinto 10:4, 5) Ndife oyamikira kwambiri kuti ‘lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo limatikonzekeretsa kuchita ntchito iliyonse yabwino.’​—2 Timoteo 3:16, 17.

15 Yesu poyesedwa ndi Satana m’chipululu anagwiritsira ntchito bwino lupanga la mzimu pokana malingaliro olakwika ndiponso ziyeso. Pa chiyeso chilichonse cha Satana, iye ankayankha kuti: ‘Kwalembedwa.’ (Mateyu 4:1-11) David, yemwe ndi wa Mboni za Yehova ndipo amakhala ku Spain, nayenso anaona kuti Malemba anam’thandiza kugonjetsa chiyeso. Pamene anali ndi zaka 19, mtsikana wina wokongola kwambiri amene anali kugwira naye ntchito pakampani ina yoyeretsa zinthu, anamuuza mawu osonyeza kuti akufuna kugona naye. David anakana zimene mtsikanayo anali kuchita pofuna kum’kopa ndipo anapempha bwana wake kuti am’sinthe malo antchito n’cholinga choti zinthu izi zisadzachitikenso. David anati: “Ndinakumbukira chitsanzo cha Yosefe. Anakana kuchita zachiwerewere ndipo mwamsangamsanga anachoka pamalowo. Inenso ndinachita zomwezo.”​—Genesis 39:10-12.

16. Fotokozani chifukwa chake timafunika kuphunzira kuti ‘tilunjike nawo bwino mawu a choonadi.’

16 Yesu anagwiritsiranso ntchito lupanga la mzimu pothandiza ena kuchoka m’manja mwa Satana. Yesu anati: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.” (Yohane 7:16) Kuti titengere kaphunzitsidwe kaluso ka Yesu, tikufunika kuphunzira mmene tingachitire zimenezo. Pofotokoza za asilikali achiroma, Josephus amene anali katswiri wa mbiri yakale wachiyuda, analemba kuti: “Msilikali aliyense amachititsidwa maseŵera olimbitsa thupi tsiku ndi tsiku, ndipo amachita khama kwambiri ngati kuti ndi nthaŵi ya nkhondo ndipo n’chifukwa chake siziwavuta kupirira zowawa za kunkhondo.” Pankhondo yathu yauzimu, timafunika kugwiritsira ntchito Baibulo. Komanso, tiyenera ‘kuchita changu kudzionetsera kwa Mulungu ovomerezeka, antchito opanda chifukwa cha kuchita manyazi, olunjika nawo bwino mawu a choonadi.’ (2 Timoteo 2:15) Ndipo timasangalala kwambiri tikayankha ndi Malemba mafunso oona mtima a anthu achidwi!

Pempherani Nthaŵi Yonse

17, 18. (a) Kodi pemphero limathandiza motani polimbana ndi Satana? (b) Perekani chitsanzo posonyeza phindu la pemphero.

17 Paulo atatha kufotokoza za zida zonse zauzimu anaperekanso malangizo ena ofunika kwambiri. Potsutsa Satana, Akristu ayenera kupereka “pemphero lonse ndi pembedzero.” Kodi azichita izi kangati? Paulo analemba kuti: “Mupemphere nthaŵi yonse mwa Mzimu.” (Aefeso 6:18) Pemphero lingatilimbitse kwambiri pamene takumana ndi zokopa, ziyeso, kapena zinthu zolefula. (Mateyu 26:41) Yesu “anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kum’pulumutsa Iye mu imfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu.”​—Ahebri 5:7.

18 Milagros, amene wakhala akudwazika mwamuna wake yemwe wakhala akudwala matenda aakulu kwa zaka zoposa 15, anati: “Ndikalefulidwa, ndimapemphera kwa Yehova. Palibe amene angandithandize kuposa mmene Iye angandithandizire. N’zoona kuti ndimafika pena poona kuti sindingathenso kupirira. Koma nthaŵi zonse ndikatha kupemphera kwa Yehova, ndimaona kuti ndapezanso mphamvu ndiponso ndimamva bwino kwambiri.”

19, 20. Kodi timafunikira chiyani kuti tipambane pomenyana ndi Satana?

19 Mdyerekezi akudziŵa kuti watsala ndi nthaŵi yochepa, ndipo wagundika pantchito yake yofuna kutigonjetsa. (Chivumbulutso 12:12, 17) Tiyenera kutsutsa mdani wamphamvu ameneyu ndi ‘kulimba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro.’ (1 Timoteo 6:12) Izi zimafuna kuti tikhale ndi mphamvu zoposa zachibadwa. (2 Akorinto 4:7) Timafunikiranso thandizo la mzimu woyera wa Mulungu ndipo pachifukwa chimenechi tiyenera kuupempherera. Yesu anati: “Ngati inu, okhala oipa, mudziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akum’pempha Iye?”​—Luka 11:13.

20 N’zoonekeratu kuti kuvala zida zonse zimene Yehova amapereka n’kofunika kwambiri. Kuvala zida zauzimu zimenezi kumafuna kuti tikhale ndi makhalidwe a Mulungu, monga chikhulupiriro ndi chilungamo. Pamafunika kuti tizikonda kwambiri choonadi ngati kuti tachita kudzimanga nacho, tikhale okonzeka kufalitsa uthenga wabwino nthaŵi iliyonse, ndiponso tiziganizira kwambiri zimene tikuyembekezera. Tiyenera kuphunzira kugwiritsira ntchito mwaluso lupanga la mzimu. Tikavala zida zonse za Mulungu, tingathe kupambana polimbana ndi mizimu yoipa ndipo tingachititse kuti dzina loyera la Yehova lilemekezeke.​—Aroma 8:37-39.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mu ulosi wa Yesaya, Yehova mwiniyo akufotokozedwa kuti wavala “chilungamo monga chida cha pachifuwa.” Motero, iye amafuna kuti oyang’anira m’mipingo azichita zinthu mwachilungamo.​—Yesaya 59:14, 15, 17.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi ndani amene amasonyeza chitsanzo chabwino chovala zida zauzimu, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira bwinobwino chitsanzo chake?

• Kodi tingateteze motani maganizo ndi mtima wathu wophiphiritsira?

• Kodi tingatani kuti tigwiritsire ntchito mwaluso lupanga la mzimu?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera nthaŵi zonse?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 17]

Kuphunzira Baibulo mwakhama kungatilimbikitse kuti tizilengeza uthenga wabwino nthaŵi iliyonse

[Chithunzi patsamba 18]

Chiyembekezo chathu chotsimikizika chimatithandiza polimbana ndi ziyeso

[Chithunzi patsamba 19]

Kodi mumagwiritsira ntchito “lupanga la mzimu” mu utumiki?