Anauzako Anthu Am’kalasi Mwake Zimene Iye Amakhulupirira
Anauzako Anthu Am’kalasi Mwake Zimene Iye Amakhulupirira
KODI mukufuna kuthandiza anthu am’kalasi mwanu kudziŵa bwino zikhulupiriro zanu za m’Baibulo? Magdalena, mtsikana wapasukulu ina ya sekondale ku Poland wazaka 18, nthaŵi zambiri amauza anthu am’kalasi mwake zikhulupiriro zake popeza ndi wa Mboni za Yehova. Chifukwa cha zimenezi, nthaŵi zambiri anthu am’kalasi mwake amam’funsa mafunso angati akuti, ‘Kodi munthu kuti akhale wa Mboni za Yehova amafunika kutani?’ ndiponso kuti ‘Kodi mumakhulupirira Yesu Kristu?’ Kodi akanawathandiza bwanji anzakewo? Magdalena anapemphera kuti Yehova amutsogolere ndipo anachita zinthu mogwirizana ndi pemphero lakelo.—Yakobo 1:5.
Tsiku lina, Magdalena anapempha aphunzitsi ake amene satsutsa zikhulupiriro zake, kuti iye adzaonetse anthu am’kalasimo vidiyo yonena za Mboni za Yehova yakuti Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name. * Mphunzitsiyo anavomera. Ndiyeno Magdalena anawauza anthu am’kalasimo kuti: “Ndikukonza zoti mnzanga adzaphunzitse kalasi ino kwa mphindi 90. Pamaphunziropo adzationetsanso vidiyo ndiponso tidzakambirana za Mboni za Yehova. Kodi mungakonde kudzakhalapo?” Aliyense anavomera. Magdalena ndi Wojciech, yemwe ndi mlaliki wa nthaŵi zonse waluso, anayamba kukonzekera zimenezi.
Anakonza zoti adzayambe ndi nkhani ya mphindi 20 yochokera m’kabuku kakuti Mboni za Yehova—Kodi iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani? * ndipo akadzatha zimenezi ophunzirawo adzapatsidwe mpata wofunsa mafunso. Kenako adzaonetse vidiyo ija mu laibulale ya pasukulupo. Wophunzira aliyense wam’kalasimo adzalandire mphatso, emvulopu yaikulu ataikamo timabuku tingapo, buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, * komanso mathirakiti ndi magazini.
Patsiku la zimenezi, panali anthu am’kalasi mwake 14, aphunzitsi, ndi ophunzira ena anayi amene anali mu laibulalemo panthaŵiyo. Wojciech anayamba wafotokoza kuti anthu angapo olemba ndakatulo ndi nkhani a ku Poland anatchulapo dzina la Mulungu, Yehova, m’zolemba zawo. Iye anatchulanso akatekisimu ena achikatolika akale amene ali ndi dzina la Mulungu. Pofotokoza ntchito ya Mboni za Yehova ya masiku ano, anaonetsa timabuku tosiyanasiyana ta maofesi a nthambi ndiponso zithunzi zingapo za Nyumba za Misonkhano.
Ndiyeno onse anayamba kukambirana. Magdalena ndi Wojciech anagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunsowo. Zimenezi zinachititsa chidwi omverawo ndipo zinawatsimikizira kuti Mboni za Yehova sizimalalikira zinthu za m’mutu mwawo. Kodi ena mwa mafunso amene anafunsidwa anali otani, nanga anawayankha bwanji?
Funso: M’Baibulo muli mawu ndi mafanizo osamvetsetseka ambirimbiri, amene angamasuliridwe mosiyanasiyana. Kodi zingatheke bwanji kutsatira zimene Baibulo limanena?
Yankho: Anthu ena amanena kuti munthu angathe kugwirizanitsa Baibulo ndi mfundo iliyonse imene angafune. Koma taganizani izi: Ngati mukufuna kumvetsa bwino zimene wolemba mabuku wina walemba, kodi njira yabwino si ndiyo kungom’funsa? Mosiyana ndi anthu olemba mabuku amene anamwalira, Wolemba Baibulo, Aroma 1:20; 1 Akorinto 8:5, 6) Nkhani imene mukupezeka lembalo ingasonyeze tanthauzo loyenera la lembalo. Komanso, Baibulo nthaŵi zambiri limanena nkhani yofananayo m’malo angapo, choncho kuyerekezera malembawo kungathandize kumvetsa bwino nkhaniyo. Motero, Mulungu angatsogolere maganizo athu, ngati kuti iyeyo akutifotokozera yekha lembalo. Mwa kuchita zimenezo, tingazindikire zimene amafuna ndi kuchita zofuna zakezo pamoyo wathu monga momwe zalembedwera m’Baibulo, kodi si choncho?
Yehova Mulungu, ndi wamoyo. (Funso: Kodi Akristu amasiyana bwanji ndi Mboni za Yehova?
Yankho: Ifeyo ndi Akristu. Koma m’malo mongonena pakamwa kuti ndi Akristu, a Mboni za Yehova amayesetsa kutsatira zimene amakhulupirira ndi zimene Mulungu amawaphunzitsa n’cholinga chakuti apindule. (Yesaya 48:17, 18) Popeza kuti ziphunzitso zawo zonse ndi za m’Baibulo, amadziŵa kuti amakhulupirira zoona.—Mateyu 7:13, 14, 21-23.
Funso: N’chifukwa chiyani mumalankhula ndi anthu amene simuwadziŵa n’komwe komanso kukakamira kulankhula nawo? Kodi kumeneku si kukakamiza anthu kuti azikhulupirira zimene inu mumakhulupirira?
Yankho: Kodi munthu atakulankhulani mwaulemu pamsewu ndi kukufunsani zimene mukuganiza pankhani inayake, mungati walakwa? (Yeremiya 5:1; Zefaniya 2:2, 3) (Ndiyeno Wojciech ndi Magdalena anachita chitsanzo cha mmene ankafunsira anthu mumsewu ngati Mulungu amaganizira anthu amene anali kuvutika chifukwa cha kusefukira kwa madzi kumene kunachitika chaposachedwapa ku Poland komweko.) Tikamva maganizo a munthuyo timamuŵerengera Baibulo. Ngati munthu sakufuna kulankhula nafe, timatsanzikana naye bwinobwino, ife n’kumapitiriza ntchito yathu. (Mateyu 10:11-14) Kodi kumeneku n’kukakamiza ena kulankhula nafe? Ngati mungati n’kukakamiza ena ndiye kutitu mukunena kuti anthu asiye kulankhalana.
Funso: N’chifukwa chiyani simuchita nawo maholide?
Yankho: Timachita mwambo umodzi wokha umene Baibulo linatilamula kuchita, ndipo mwambo wake ndi Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu. (1 Akorinto 11:23-26) Mukanena za maholide, mukhoza kukaŵerenga mabuku osiyanasiyana odalirika kuti mukaone kuti anayamba bwanji. Mukatero, simudzavutika kuona chifukwa chake sitichita nawo zinthu zimenezo.—2 Akorinto 6:14-18.
Ophunzirawo anafunsa mafunso ambiri ndipo iwo anayankha mafunsowo. Kukambiranako kunatenga nthaŵi yaitali moti anasintha kuti vidiyo adzaonera nthaŵi ina.
Kodi ophunzirawo anatani? Tiyeni timulole Magdalena atiuze: “Ndinadabwa kuona kuti ophunzira ena amene nthaŵi zambiri amachita zopusa ndiponso amakonda kunyoza anzawo anafunsa mafunso aphindu. Ngakhale kuti ankati sakhulupirira kuti kuli Mulungu, pokambiranapo anasonyeza kuti amakhulupirira Mulungu.” Onse amene analipo panthaŵiyi analandira mosangalala mphatso zija. Anawapatsa mabuku okwanira 35, timabuku 65, ndi magazini 34.
Iyitu ndi nkhani yosangalatsa yochitika chifukwa cha ntchito ya kusukulu. Ntchito imeneyi inathandiza anthu am’kalasi mwa Magdalena kudziŵa ndi kuwamvetsa bwino a Mboni za Yehova komanso inalimbikitsa achinyamata ambiri kuganizira za cholinga cha moyo. Bwanji inuyo osayesetsa kuthandiza anthu am’kalasi mwanu kuphunzira zambiri zokhudza zimene mumakhulupirira?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Amafalitsa ndi a Mboni za Yehova.
^ ndime 4 Amafalitsa ndi a Mboni za Yehova.
^ ndime 4 Amafalitsa ndi a Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 31]
Magdalena ndi Wojciech akukonzekera zokakamba