Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Choloŵa Chodalirika

Choloŵa Chodalirika

Choloŵa Chodalirika

“NGATI mwalandira kalata yokuuzani kuti pali choloŵa chimene chingakhale chanu, chenjerani. N’kutheka kuti yachokera kwa tambwali amene akufuna kukuyeretsani m’maso.”

Limeneli ndi chenjezo limene bungwe loona zamtengatenga ndi mtokoma la ku United States linaika pa kompyuta yake yolumikizidwa pa Intaneti. N’chifukwa chiyani linachenjeza zimenezi? Chifukwa chakuti anthu ambirimbiri analandira kalata yakuti, ‘Mbale wanu wamwalira ndipo wakusiyirani choloŵa.’ Atamva zimenezi, anthu ambiri anam’tumizira amene anawalembera kalata ija ndalama zokwana madola 30 kapena kuposa n’cholinga chakuti awauze kumene kuli choloŵacho ndi mmene angachitengere kuti chikhale chawo. Koma anakhumudwa kwambiri. Anthu onse amene anam’tumizira ndalamawo analandira kalata zofanana zonena za choloŵacho, ndipo zoti winawake wa anthuŵa anakathadi kulandira choloŵa zinali zosatheka ngakhale pang’ono.

Anthu amatengeka ndi zinthu ngati zimenezi chifukwa mwachibadwa anthufe timafuna kulandira choloŵa. Komabe, Baibulo limayamikira anthu amene amakonzera ena choloŵa ponena kuti: “Wabwino asiyira zidzukulu zake choloŵa chabwino.” (Miyambo 13:22) Ndipotu, ndi Yesu Kristu mwiniyo amene ananena mawu otchuka ndiponso amene anthu amawakonda kwambiri a pa Ulaliki wake wa pa Phiri akuti: “Odala ali ofatsa chifukwa choloŵa chawo ndi dziko lapansi.”​—Mateyu 5:5, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

Mawu a Yesu amatikumbutsa zimene Mfumu Davide ya Israyeli wakale inauziridwa kulemba zaka mazana angapo m’mbuyomo kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—Salmo 37:11.

Mawu akuti “choloŵa chawo ndi dziko lapansi” n’ngopangitsa munthu kuyembekezera mwachidwi kwambiri. Koma kodi tingawakhulupirire mawu ameneŵa popanda kukayika kuti akungofuna kupusitsa anthu? Inde, tingawakhulupirire. Popeza kuti dziko lapansi ndi mbali ya chilengedwe chokongola cha Yehova, iye monga Wolipanga ndiponso monga Mwiniwake ali ndi ufulu wonse wolipereka kwa aliyense amene akufuna. Yehova, kudzera mwa Mfumu Davide ananena lonjezo laulosi ili kwa Mwana Wake wokondedwa, Yesu Kristu lakuti: “Undifunse, ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale choloŵa chako, ndi malekezero a dziko lapansi akhale akoako.” (Salmo 2:8) Pachifukwa chimenechi, mtumwi Paulo ananena kuti Yesu ndiye “amene [Mulungu] anamuika woloŵa nyumba wa zonse.” (Ahebri 1:2) Choncho, tingakhulupirire mosakayika m’pang’ono pomwe kuti pamene Yesu ananena kuti ofatsa “choloŵa chawo ndi dziko lapansi,” anali kunena zoona ndipo ali ndi mphamvu zokwaniritsa lonjezo lakeli.​—Mateyu 28:18.

Komano, funso lofunika n’lakuti, kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa bwanji? Kulikonse masiku ano, zikuoneka kuti anthu ankhanza ndi odzikuza ndiwo amene zinthu zikuwayendera bwino ndiponso ndi amene akudyerera kwambiri. Ndiyeno n’chiyani chidzatsale kuti chikhale choloŵa cha ofatsa? Komanso, dziko lenilenili likuwonongedwa kwadzaoneni, ndipo anthu adyera ndi osaganizira za m’tsogolo akuwononga zinthu za m’dzikoli. Kodi dziko lino lidzakhala loti n’kukhaladi choloŵa? Tikukupemphani kuŵerenga nkhani yotsatirayi kuti mupeze yankho la mafunso ameneŵa ndi la mafunso ena ofunika kwambiri.

[Chithunzi patsamba 3]

Kodi muli m’gulu la anthu odzalandira choloŵa chenicheni?