Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kalata Yochokera kwa Alejandra

Kalata Yochokera kwa Alejandra

Olengeza Ufumu Akusimba

Kalata Yochokera kwa Alejandra

KULEMBA KALATA ndi njira yochitira ulaliki imene yakhala yothandiza kwa nthaŵi yaitali. Ngakhale kuti nthaŵi zina zotsatira zake zimakhala zosatsimikizirika, amene amachita khama kulalikira m’njira imeneyi amapindula kwambiri. Iwo amakumbukira malangizo anzeru a m’Baibulo akuti: “Mam’maŵa fesa mbewu zako, madzulonso osapumitsa dzanja lako; pakuti sudziŵa ziti zidzalola bwino ngakhale izizi, ngakhale izozo, kaya zonse ziŵiri zidzakhala bwino.”​—Mlaliki 11:6.

Alejandra, mtsikana wa Mboni amene anali atatumikira kwa zaka pafupifupi khumi pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya ku Mexico, anali kulandira chithandizo cha mankhwala a matenda a kansa. Matenda akewo anafika poipa, ndipo anafooka kwambiri moti ankalephera kugwira ntchito za masiku onse. Koma Alejandra posafuna kunyalanyaza ntchito yolalikira, anaganiza zolemba makalata. M’makalatawo analembamo za phunziro la Baibulo lapanyumba laulere komanso anaikamo nambala ya telefoni ya amayi ake. Ndiyeno anapatsira amayi ake makalatawo kuti akamachita ulaliki wa kukhomo ndi khomo aziwasiya panyumba zimene sanapeze anthu.

Panthaŵi imeneyi, Diojany, mtsikana wa ku Guatemala, anapita kukagwira ntchito zapakhomo ku Cancún, ku Mexico. Ali kumeneko, anakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo anali kusangalala kukambirana nawo nkhani za m’Baibulo. Patapita nthaŵi, mabwana ake anaganiza zosamukira ku mzinda wa Mexico ndipo anafuna kuti apite naye limodzi. Diojany sankafuna kusamuka poopa kuti sakatha kupezananso ndi a Mboni za Yehova aja.

Abwana akewo anamulimbitsa mtima kuti: “Usadandaule, a Mboni ali ponseponse. Tikakangofika kumeneko tikawafunafuna.” Diojany anavomera kupita nawo chifukwa cha mawu olimbitsa mtimaŵa. Atafika ku mzinda wa Mexico, abwana a Diojany anafunafuna a Mboni. Koma pa zifukwa zina, iwo sanawapeze, ngakhale kuti mumzindawo munali Mboni zoposa 41,000 ndiponso mipingo yoposa 730.

Posapita nthaŵi, Diojany anayamba kukhumudwa chifukwa anali asanawapeze a Mboni kuti apitirize kukambirana nawo za m’Baibulo. Tsiku lina abwana ake aakazi anamuuza kuti: “Ukudziŵa, Mulungu wako wayankha mapemphero ako.” Ndiye anam’patsa kalata, n’kunena kuti: “A Mboni akubweretsera kalata iyi.” Inali kalata yochokera kwa Alejandra.

Diojany anakumana ndi amayi ake a Alejandra komanso ndi mng’ono wake, dzina lake Blanca ndipo anavomera kuchita naye phunziro la Baibulo. Patatha milungu ingapo, anakumana ndi Alejandra ndipo anasangalala kwambiri kudziŵana naye. Alejandra anamulimbikitsa kuti apitirize kulimbikira kuphunzira Baibulo kuti apite patsogolo mwauzimu.

Patapita miyezi ingapo, mu July 2003, Alejandra anamwalira, atawasiyira okhulupirira anzake chitsanzo chabwino cha chikhulupiriro ndi kulimba mtima. Pamaliro ake, anthu ambiri anakhudzidwa mtima kuonana ndi Diojany ndiponso kumumva akunena kuti: “Alejandra ndi abale ake andipatsa chitsanzo chabwino kwambiri. Ndatsimikiza mtima kutumikira Yehova ndiponso kuti ndibatizidwe posachedwa. Ndikulakalaka kwambiri kudzaonananso ndi Alejandra m’Paradaiso akubwerayo.”

Inde, kalata ingaoneke kuti n’kanthu kakang’ono. Koma zotsatira zake zingakhale zabwino ndiponso zokhalitsa.