Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudikira M’njira Yoyenera?

Kodi Mukudikira M’njira Yoyenera?

Kodi Mukudikira M’njira Yoyenera?

MASIKU ano anthu ambiri amanyong’onyeka akamadikira munthu kapena chinthu chinachake. Komano Malemba amalimbikitsa anthu a Mulungu kukhala ndi mtima ‘wodikira.’ Mosiyana ndi anthu am’dera limene ankakhala, mneneri Mika ananena kuti: “Ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa.”​—Mika 7:7; Maliro 3:26.

Koma kodi kudikira Yehova n’kutani makamaka? Kodi Mkristu azidikira bwanji Mulungu? Kodi pali njira zoyenera ndi zosayenera zodikirira Mulungu? Zimene zinam’chitira mneneri Yona m’zaka za m’ma 800 Kristu Asanabwere zimatiphunzitsa kanthu kena pankhani imeneyi.

Kudikira Pachifukwa Cholakwika

Yehova Mulungu anamuuza Yona kuti akalalikire kwa anthu a mumzinda wa Nineve, womwe unali likulu la Ufumu wa Asuri. Mzinda wa Nineve unali kudziŵika kuti unali “mudzi wa mwazi” chifukwa cha nkhanza zoopsa za anthu ake, ndipo akatswiri a mbiri yakale ndiponso ofukula mabwinja atsimikizira zimenezi. (Nahumu 3:1) Poyamba Yona anayesa kupeŵa ntchito imeneyi, koma Yehova anaonetsetsa kuti mneneriyu apitebe ku Nineve.​—Yona 1:3–3:2.

“Yona anayamba kuloŵa mudziwo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anayi ndipo Nineve adzapasuka.” (Yona 3:4) Anthu anachita zodabwitsa kwambiri chifukwa cha ntchito ya Yonayi: “Anthu a Nineve anakhulupirira Mulungu, nalalikira chosala, navala chiguduli, kuyambira wamkulu kufikira wamng’ono wa iwoŵa.” (Yona 3:5) Motero, Yehova, yemwe ndi Mulungu “wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa,” sanawononge mzindawu.​—2 Petro 3:9.

Kodi Yona anatani ataona zimenezi? Nkhaniyo imati: “Koma sikudakomera Yona konse, ndipo anapsa mtima.” (Yona 4:1) N’chifukwa chiyani anatero? N’kutheka kuti Yona ankaona kuti wasanduka mneneri wonyozeka popeza kuti zimene analengeza zakuti mzindawo uwonongedwa sizinakwaniritsidwe pa tsiku limene iyeyo ankaganizira. Motero zikuoneka kuti anayamba kuganizira kwambiri za dzina lake n’kuleka kuganizira zochitira ena chifundo ndiponso zofuna kuwapulumutsa.

Inde, Yona sikuti anachita kufika polekeratu ntchito yake ya uneneri. Komabe, iye anadikira kuti ‘aone kuti chichitikire mudziwo’ n’chiyani. Inde, iye anakhala ndi kamtima koipidwa kamene kanam’chititsa kuti angopinda manja n’kumayang’ana kuti aone zimene zichitikire mzindawo. Poona kuti zinthu sizinayende mmene iyeyo anali kuganizira, Yona anamanga thandala, n’kukhala pansi pamthunzi wake ali ndwii, n’kuyamba kudikira kuti aone zimene zichitike. Yehova sanasangalale ndi kamtima kamene Yona anasonyeza, motero anam’thandiza mwachikondi mneneri wakeyu kuti asinthe maganizo ake olakwikawo.​—Yona 4:5, 9-11.

Chifukwa Chomwe Yehova Amalezera Mtima

Ngakhale kuti mzinda wa Nineve unalapa ndipo sunawonongedwe, pambuyo pake unayambiranso njira zake zoipazo. Kudzera mwa mneneri Nahumu ndi mneneri Zefaniya, Yehova analosera kuti udzawonongedwa. Ponena za “mudzi wa mwazi” umenewu, Yehova anati adzawononga Asuri n’kusandutsa Nineve bwinja. (Nahumu 3:1; Zefaniya 2:13) M’chaka cha 632 Kristu Asanabwere, mzinda wa Nineve unawonongedwa, ndipo sunadzaonekenso.

Mofanana ndi mzindawu dziko la masiku anoli nalonso lapha anthu ambirimbiri mwachisawawa ndipo laposeratu zimene mzinda wakale wa Nineve unachita. Pachifukwa chimenechi ndiponso pa zifukwa zina, Yehova anagamula kuti dziko loipa lilipo masiku anoli lidzatha panthaŵi ya ‘chisautso chachikulu’ imene padzachitike zinthu zimene sizinaonekepo n’kale lonse.​—Mateyu 24:21, 22.

Komabe, Yehova waimitsa kaye zimene analonjeza zakuti adzawononga dzikoli kuti anthu oona mtima masiku ano alape, n’kupulumuka monga anachitira anthu a ku Nineve. Mtumwi Petro ananena motere za kuleza mtima kwa Mulungu: “Ambuye sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.”​—2 Petro 3:9, 10, 13.

Kudikira M’njira Yoyenera

Petro anapitiriza kunena kuti: “Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga m’mayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” (2 Petro 3:11,12) Onani kuti pamene tikudikira tsiku la Yehova, tiyenera kuchita zinthu zosonyeza ‘mayendedwe opatulika ndi chipembedzo,’ kutanthauza kuti m’pofunika kumachita zinazake osati kungokhala ayi.

Inde, munthu amene akudikira m’njira yoyenera amasonyeza kuti sakukayika ngakhale pang’ono kuti malingana ndi nthaŵi imene Yehova anakonza, tsiku la Yehova silidzachedwa ngakhale mphindi imodzi. Chikhulupiriro choterechi chimachititsa munthu kugwira ntchito zopatulika ndiponso zaumulungu ndipo ntchito yaikulu kwambiri pa ntchito zoterezi ndiyo yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Yesu anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kulalikira, ndipo analangiza otsatira ake odzozedwa kuti: “Khalani odzimangira m’chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka; ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wawo, pamene ati abwera kuchokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akam’tsegulire pomwepo. Odala akapolowo amene mbuye wawo, pakudza iye, adzawapeza odikira.”​—Luka 12:35-37.

Akapolo a m’zaka za m’ma 100 Kristu Atabwera ‘ankadzimangira m’chuuno’ pogwira pamodzi nsalu ya m’munsi mwa mikanjo yawo, kumaso ndi kumbuyo komwe, n’kuikokera m’chuuno poidutsitsa m’mphechepeche kenaka n’kumanga ndi lamba wansalu. Ankatero pofuna kuti ayambe kugwira ntchito yolimba. Motero, Mkristu ayenera kuchita ntchito zabwino mwamphamvu ndiponso mwakhama. Ayenera kuthetsa kamtima kalikonse kosonyeza ‘ulesi’ mwauzimu, ndipo asamathere mphamvu zake pa zinthu zosangalatsa kapena pofunafuna chuma. M’malo mwake ayenera “kuchuluka mu ntchito ya Ambuye” kwinaku akudikira tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova.​—Aroma 12:11; 1 Akorinto 15:58.

Tizidikira Kwinaku Tikugwira Ntchito

A Mboni za Yehova akhala akugwira ntchito kwinaku akudikira tsiku la Yehova. Mwachitsanzo, m’chaka chautumiki cha 2003, tsiku lililonse ankalalikira mawu a Yehova maola 3,383,000. Kuti munthu mmodzi akwanitse kulalikira maola a tsiku limodzi okhaŵa ndiye kuti ayenera kulalikira kwa zaka 386 mosalekeza.

Komabe, ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo pandekha ndimadikira m’njira yoyenera?’ Yesu anapereka fanizo limene limalongosola mtima wokonda ntchito umene Akristu odzozedwa okhulupirika ayenera kukhala nawo. Iye anatchulapo za akapolo atatu: “Mmodzi [mbuye wake] anam’patsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziŵiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zawo; namuka iye. Pomwepo uyo amene analandira ndalama zisanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo ndalama zina zisanu. Chimodzimodzinso uyo wa ziŵirizo, anapindulapo zina ziŵiri. Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa ndalama ya mbuye wake. Ndipo itapita nthaŵi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, naŵerengera nawo pamodzi.”​—Mateyu 25:15-19.

Akapolo atatu onsewo anadikira kuti mbuye wawo abwere. Aŵiriwo, amene ankadikira kwinaku akugwira ntchito, mbuyeyo atabwera anawauza kuti: “Chabwino, [kapena kuti wachita bwino] kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika.” Koma kapolo amene ankangodikirira osachitapo kanthu kalikonse sanam’thokoze ayi. Mmalo mwake mbuyeyo anati: “Ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja.”​—Mateyu 25:20-30.

Ngakhale kuti fanizoli limanena za Akristu odzozedwa, tonsefe tingaphunzirepo kanthu ngakhale titakhala osadzozedwa. Mbuye wathu, Yesu Kristu, amafuna kuti tonsefe tizigwira ntchito yake mwakhama kwinaku tikudikira kubwera kwake pa tsiku lalikulu la Yehova. Iye amayamikira ntchito imene aliyense amachita payekhapayekha ‘monga mwa nzeru zake,’ kapena kuti monga mmene angathere, ndiponso mmene zinthu zilili pa moyo wake. Pamapeto pa kudikiraku, zidzakhala zosangalatsa kwambiri kumva Mbuye akutiuza kuti ‘mwachita bwino.’

Kuleza Mtima kwa Ambuye Kumatipatsa Mwayi Wodzapulumuka

Kodi tingatani ngati tikuona kuti nthaŵi imene tinkaganizira kapena kufuna kuti dziko lino lidzathe yapitirira? Sikuti zimenezi zangochitika popanda chifukwa ayi. Mtumwi Petro analemba kuti: “Yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso.” (2 Petro 3:15) Kudziŵa bwino cholinga cha Mulungu ndiponso kudzichepetsa pozindikira kuti siife ofunika kuposa china chilichonse kungatithandize kukhala oleza mtima kwa nthaŵi yonse imene Yehova akuona kuti ayenera kuleza mtima posawononga dziko lino.

Pofuna kulimbikitsa Akristu kuti azikhala oleza mtima, wolemba Baibulo Yakobo, anatchulapo chitsanzo. Iye analemba kuti: “Taonani, wolima munda alindira chipatso chofunikatu cha dziko, ndi kuleza mtima nacho kufikira chikalandira mvula ya myundo ndi masika. Lezani mtima inunso, limbitsani mitima yanu; pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira.”​—Yakobo 5:7, 8.

Yehova Mulungu safuna kuti titope kapena kugonja pamene tikudikira. Iye ali ndi ntchito imene akufuna kuti tichite ndipo amasangalala ngati tikudikira kwinaku tikugwira ntchito imeneyi mwakhama. Iye akufuna kuti tikhale m’gulu la anthu amene mtumwi Paulo anawalongosola m’kalata yake yopita kwa Ahebri, momwe anati: “Tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga ku chiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro; kuti musakhale aulesi, koma akuwatsanza iwo amene alikuloŵa malonjezano mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima.”​—Ahebri 6:11, 12.

Choncho tisaleme. M’malo mwake ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu, chikhulupiriro chathu mu nsembe ya dipo ya Yesu, ndiponso chiyembekezo chathu chosangalatsa cha dongosolo latsopano la zinthu zizitipatsa mphamvu pamoyo wathu. Monga kapolo “wabwino ndi wokhulupirika” amene Yesu anam’tchula m’fanizo lake, nafenso tisonyeze kuti ndife woyenerera kuyamikiridwa ndiponso kupatsidwa mphoto popitirizabe kuchita ntchito yotamanda Mulungu wathu, monga mmene anachitira wamasalmo amene ananena kuti: “Ine ndidzayembekeza kosaleka, ndipo ndidzawonjeza kukulemekezani.”​—Salmo 71:14.

[Chithunzi patsamba 21]

Pokhumudwa, Yona anadikira kuti aone kuti chichitikire mzinda wa Nineve n’chiyani

[Zithunzi pamasamba 22, 23]

Tiyeni tisonyeze kudzipereka pochita ntchito ya Mulungu kwinaku tikudikira tsiku la Yehova