Maphunziro Amene Ndikupitirizabe Mpaka Pano
Mbiri ya Moyo Wanga
Maphunziro Amene Ndikupitirizabe Mpaka Pano
YOSIMBIDWA NDI HAROLD GLUYAS
Ndimakumbukirabe zimene zinandichitikira nthaŵi ina ndili mwana, zaka zoposa 70 zapitazo. Ndinali m’khitchini ndipo ndinkayang’ana mwachidwi paketi ya masamba a tiyi yolembedwa mawu akuti “Tiyi wa ku Ceylon.” Inalinso ndi chithunzi cha azimayi akuthyola tiyi m’minda ya tiyi wobiriŵira m’dziko la Ceylon (lomwe pano amati Sri Lanka). Chithunzi chimenechi, chosonyeza chigawo chokongola chakutali kwambiri ndi dera lakwathu louma lomwe lili kum’mwera kwa Australia, sichinandichoke m’maganizo. Ndinkaganiza kuti dziko la Ceylon layenera kukhala lokongola kwambiri. Koma panthaŵiyi sindinkalotako kuti ndidzakhala zaka 45 ndikuchita ntchito yaumishonale pachilumba chokongolachi.
NDINABADWA mu April 1922, dziko lidakali mphonje. Banja lathu linkagwira ntchito pa kafamu kakumidzi ka kufupi ndi tawuni yotchedwa Kimba, yomwe ili chapakati pa dziko lalikulu la Australia ndipo ili chakum’mwera kwenikweni kwa dera lachipululu la m’dzikoli. Moyo wathu unali wovuta kwambiri chifukwa tinkalimbana ndi chilala, tizilombo towononga mbewu, ndiponso kutentha kwadzaoneni. Mayi anga ankagwira ntchito mwakhama poyang’anira bambo anga ndiponso ana asanu ndi mmodzife m’nyumba yomwe kwenikweni inali kachisakasa kamalata okhaokha.
Komabe ineyo kumeneku ndinkakhala momasuka ndiponso mosangalala kwambiri. Ndikukumbukira ndili mwana mmene ndinkachitira chidwi kuona nkhuzi zamphamvu zili pagoli zikuswa mphanje, ndiponso ndimakumbukira kulira kwa kavuluvulu amene ankachititsa kuti fumbi lingoti
koboo m’dera lonselo. Motero, ndingati maphunziro anga anayamba kale kwambiri ndisanayambe n’komwe kupita kukasukulu kokhala ndi mphunzitsi mmodzi yekha kamene kanali pamtunda wa makilomita 5 kuchoka kunyumba kwathu.Makolo anga anali opembedza, ngakhale kuti sankapita kutchalitchi makamaka chifukwa chakuti tchalitchi chinali kutawuni komwe kunali kutali kwambiri. Komabe, kumayambiriro kwa m’ma 1930, mayi anga anayamba kumvetsera nkhani za Baibulo zokambidwa ndi Judge Rutherford, zomwe ankaziulutsa mlungu uliwonse pa siteshoni ina ya wailesi ku Adelaide. Ndinkaganiza kuti Judge Rutherford ndi mmodzi wa olalikira a ku Adelaide, motero sindinachite nazo chidwi kwenikweni. Koma mlungu uliwonse mayi anga ankayembekezera mwachidwi kuti amvetsere nkhani za Rutherford ndipo ankamvetsera mwatcheru kwambiri ngakhale kuti mawu ake pena ankavuta kumva siteshoniyo ikamathaŵa pa wailesi yathu yakale yoyendera mabatire.
Tsiku lina kukutentha ndiponso kuli fumbi, galimoto yakale ya bokosibode inaima kumaso kwa nyumba yathu, ndipo munatuluka amuna aŵiri otchena bwino. Iwo anali a Mboni za Yehova. Mayi anga anamvetsera uthenga umene anabweretsa ndipo anapereka ndalama kwa anthuwo n’kutenga mabuku angapo, n’kuyamba kuwaŵerenga nthaŵi yomweyo. Mabuku ameneŵa anaŵakhudza mtima kwambiri mwakuti posapita nthaŵi anapempha bambo kuti awatenge pagalimoto pofuna kuti zimene aphunzirazo akauzeko anthu okhala moyandikana nafe.
Kutengera Zochita Zabwino za Ena Kunandithandiza
Pasanatenge nthaŵi yaitali izi zitachitika, tinasamuka chifukwa cha moyo wovuta wa m’derali ndipo tinapita mumzinda wa Adelaide, womwe unali kutali makilomita 500. Banja lathu linayamba kusonkhana ndi mpingo wa Mboni za Yehova wa Adelaide ndipo linayamba kuchita bwino pa zinthu zauzimu. Sukulu ndinalekanso panthaŵi imene tinasamukayi. Ndinali ndi zaka 13 ndipo n’kuti nditamaliza giredi seveni. Ndinali munthu wosafuna kuganizira kwambiri zinthu ndipo mtima umenewu ukanachititsa kuti ndiiwaleko mosavuta zinthu zauzimu chipanda kuti abale angapo, apainiya, kapena kuti atumiki a nthaŵi zonse anayesetsa kundithandiza.
Patatha nthaŵi ndithu, abale ameneŵa anandithandiza kuti ndiyambirenso kukonda zinthu zauzimu. Ndinkasangalala kwambiri kuchita zinthu pamodzi ndi abaleŵa ndipo ndinkakhumbira mtima wawo wolimbikira ntchito. Motero pamene anaŵerenga chilengezo cholimbikitsa anthu kuchita utumiki wa nthaŵi zonse pamsonkhano womwe unachitikira ku Adelaide mu 1940, mosayembekezera ndinalembetsa dzina langa. Panthaŵiyi n’kuti ndisanabatizidwe n’komwe ndipo sindinkadziŵa kwenikweni kulalikira. Komabe, patangotha masiku ochepa chabe ndinaitanidwa kuti ndikagwire ntchito pamodzi ndi kagulu kakang’ono ka apainiya ku Warrnambool, tawuni yomwe ili pamtunda wa makilomita mahandiredi angapo kuchokera ku Adelaide, m’boma loyandikana nalo la Victoria.
Ngakhale kuti ndinayamba choonadi mokayikakayika chonchi, posakhalitsa ndinayamba kukonda kwambiri utumiki wa kumunda, ndipo ndine wosangalala kuti chikondi chimenechi sichinazilale mpaka panopa. Kwenikweni imeneyi ndiyo nthaŵi imene ndinasintha n’kuyamba kulimbikira kwambiri zinthu zauzimu. Ndinaphunzira ubwino wokondana kwambiri ndi anthu amene amakonda
zinthu zauzimu. Ndinazindikira kuti kutengera khalidwe lawo labwino kungatithandize kuti tikhale anthu abwino ngakhale titakhala osaphunzira kwenikweni ndiponso ndinazindikira kuti zimene tingaphunzire kwa anthuŵa zingatithandize kwa moyo wathu wonse.Kulimbikitsidwa ndi Ziyeso
Nditangochita utumiki wa upainiya kwa kanthaŵi kochepa chabe ntchito ya Mboni za Yehova ku Australia inaletsedwa. Posadziŵa chochita, ndinapempha thandizo kwa abale, ndipo anandiuza kuti sanaletse kuuza anthu za Baibulo. Motero, ndinayamba kuyenda khomo ndi khomo pamodzi ndi apainiya ena, n’kumauza anthu uthenga wochokera m’Baibulo umene unali wosavuta kumva. Zimenezi zinandilimbikitsa kuti ndidzapirire mayesero amene ndinadzakumana nawo patsogolo pake.
Patangotha miyezi inayi ndinakwanitsa zaka 18 ndipo ndinaitanidwa kuti ndikalembetse usilikali. Zimenezi zinandipatsa mpata wonena za chikhulupiriro changa pamaso pa akuluakulu angapo a asilikali pamodzi ndi mkulu wina wa zamalamulo. Panthaŵiyi, abale pafupifupi 20 anali kundende ya ku Adelaide chifukwa chokana kuloŵa usilikali, ndipo ineyo anandiika limodzi ndi abaleŵa. Anatipatsa ntchito ya kalavulagaga, yoswa miyala ndi kukonza misewu. Zimenezi zinandithandiza kukhala ndi makhalidwe monga kupirira ndiponso khama. Chifukwa cha khalidwe lathu labwino ndiponso kusagonja kwathu, asilikali ambiri otilondera anayamba kutipatsa ulemu.
Ndinamasulidwa patatha miyezi ingapo, ndipo ndinasangalala kuyambiranso kudya chakudya cholongosoka ndiponso kuchita upainiya. Koma popeza kuti anthu ochita nawo upainiya anali kusoŵa, anandipempha kuti ndikatumikire ndekha ku dera lina lakutali lamafamu chakum’mwera kwa Australia. Ndinavomera ndipo ndinanyamuka pa sitima yapamadzi kupita ku chisumbu cha Yorke, nditangotenga zinthu zofunikira paulaliki wanga komanso ndi njinga basi. Nditafika kumeneku, banja lina lochita chidwi ndi choonadi linandilondolera ku kanyumba kogonako alendo komwe mzimayi wachifundo kwambiri anandisamalira ngati ndine mwana wake amene. Masana, ndinkayenda panjinga m’misewu yafumbi, n’kumalalikira m’matawuni ang’onoang’ono amene anali momwazikanamwazikana pachilumbachi. Kuti ndikafike m’madera akutali, nthaŵi zina ndinkagona m’timahotela kapena m’nyumba zogona alendo. Motero, ndinafika kutali kwambiri ndipo ndinakumana ndi zinthu zambiri zosangalatsa. Kulalikira ndekha sindinkadandaula nako kwambiri ndipo popeza Yehova ankandisamalira ndinayamba kukondana naye kwambiri.
Kuthana ndi Maganizo Odziderera
M’chaka cha 1946, ndinalandira kalata yondiitana kuti ndikayambe ntchito ya mtumiki wa kwa abale (yemwe masiku ano amatchedwa woyang’anira dera). Ntchito imeneyi inali yofunika kuti ndiziyendera mipingo yosiyanasiyana m’dera lililonse limene ndapatsidwa. Kunena zoona ntchitoyi ndinkaiona kuvuta kwambiri. Tsiku lina ndinamva mbale wina akuuza mnzake kuti, “Harold si munthu wodziŵa kwambiri kukamba nkhani, koma amaudziŵa bwino kwambiri utumiki wa kumunda.” Zimene ananenazi zinandilimbikitsa kwambiri. Ndinkadziŵa kuti ndinalibe kwenikweni luso lolankhula kapena kulinganiza zinthu, koma ndinkazindikira kuti ntchito yolalikira ndi imene makamaka ili ntchito yaikulu ya Akristu.
M’chaka cha 1947 anthu anali kuyembekezera mwachidwi kubwera kwa Mbale Nathan Knorr ndi Mbale Milton Henschel amene anachokera ku likulu la Mboni za Yehova ku Brooklyn. Umenewu unali ulendo wawo woyamba chibwerereni Mbale Rutherford mu 1938 ndipo paulendowu anachita msonkhano waukulu ku Sydney. Monga anachitira
achinyamata ambiri amene anali apainiya, inenso ndinachita chidwi ndi maphunziro aumishonale amene ankachitikira ku Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo imene inali itangotsegulidwa kumene ku South Lansing, mumzinda wa New York, ku United States. Ambiri amene tinali pamsonkhanowu tinkaganiza kuti mwina munthu ayenera kukhala wophunzira kwambiri kuti akaloŵe m’sukuluyi. Koma Mbale Knorr analongosola kuti ngati tingathe kuŵerenga nkhani m’magazini ya Nsanja ya Olonda n’kutha kukumbukira mfundo zikuluzikulu za m’nkhaniyo, n’kutheka kuti tingathe kukachita bwino kusukuluyi.Ineyo ndinkaganiza kuti sanditenga kusukuluyi popeza sindinali wophunzira kwambiri. Koma ndinadabwa kuona kuti patatha miyezi yochepa chabe anandiuza kuti ndilembe kalata yofunsira malo kusukuluyi. Kenaka, anandivomera kukayamba sukuluyi ndipo ndinali nawo m’kalasi ya nambala 16 yomwe inachitika m’chaka cha 1950. Sukuluyi inandithandiza kwambiri ndipo inandichititsa kuti ndiyambe kuchita zinthu mosadziderera. Inandithandiza kuzindikira kuti kupita patali ndi maphunziro sikofunika kwambiri kuti zinthu zikuyendere bwino. M’malo mwake chofunika kwambiri ndicho khama ndi kumvera. Aphunzitsi athu ankatilimbikitsa kuti tiziyesetsa kuchita zinthu ndi mtima wonse. Pomvera malangizo awo, ndinaona kuti ndikuchita bwino ndipo ndikuwatsata bwino maphunziro onsewo.
Kuchoka M’dziko Louma Kupita ku Chilumba Chokongola
Nditamaliza sukuluyi, ineyo ndi abale ena aŵiri a ku Australia anatitumiza ku Ceylon (komwe masiku ano amati ku Sri Lanka). Tinafika ku mzinda wa Colombo, womwe ndi likulu la dzikoli mu September 1951. Kunali kotentha ndipo zimene tinali kuona, kumva ngakhalenso kununkhiza zinali zachilendo. Tikutsika sitima, m’mishonale wina amene anali kutumikira m’dzikolo anangofikira kundipatsa kapepala koitanira anthu kuti akamvere nkhani Lamlungu lotsatira pa malo a panja mumzindawo. Ndinadabwa kuona kuti pakapepalapo panalembedwa kuti akakambe nkhaniyo ndi ineyo. Ingoganizirani nkhaŵa imene ndinali nayo. Koma pa zaka zimene ndinali kuchita upainiya ku Australia ndinaphunzira kuvomera ntchito iliyonse imene ndapatsidwa. Motero, mothandizidwa ndi Yehova, ndinakwanitsa kukamba nkhaniyo bwinobwino. Pamodzi ndi abale anayi amene tinawapeza ku nyumba ya amishonale ku Colombo, atatufe tinayamba chintchito chovuta chophunzira chinenero cha Sinhala ndiponso kuchita nawo ntchito ya utumiki wa kumunda. Nthaŵi zambiri tinkagwira ntchitoyi patokha, ndipo tinasangalala kuona kuti anthu a kumeneku anali aulemu ndiponso okonda kuchereza alendo. Pasanatenge nthaŵi yaitali anthu obwera kumisonkhano anayamba kuchuluka.
Patatha nthaŵi, ndinayamba kuganizira za mlongo wina wokongola, dzina lake Sybil, amene anali kuchita upainiya. Mlongoyu ndinakumana naye m’sitima pamene ndinali kupita ku Sukulu ya Gileadi. Iyeyu anali kupita ku msonkhano wa mayiko womwe unali kukachitikira ku New York. Pambuyo pake anapita ku Sukulu ya Gileadi, m’kalasi ya nambala 21 ndipo anamutumiza ku Hong Kong mu 1953. Ndinaganiza zomalemberana naye makalata, ndipo tinapitiriza kulemberana mpaka mu 1955 pamene iyeyu ananditsatira ku Ceylon, komwe tinakwatirana.
Gawo limene tinapatsidwa titakwatirana linali ku mzinda wa Jaffna, womwe uli chakumpoto kwenikweni kwa dziko la Sri Lanka. Cham’katikati mwa m’ma 1950 anthu a mafuko a Sinhala ndi Tamil anayamba kusiyana maganizo pankhani zandale, ndipo patatha zaka makumi angapo zimenezi zinayambitsa nkhondo. Zinali zolimbikitsa kwambiri kuona Mboni za mafuko a Sinhala ndi Tamil zikubisana kwa miyezi ingapo panthaŵi yovutayi. Ziyeso
zimenezi zinalimbikitsa kwambiri chikhulupiriro cha abaleŵa.Kulalikira ndi Kuphunzitsa ku Sri Lanka
Tinafunika kuleza mtima ndiponso kupirira kuti tizoloŵerane ndi anthu a Chihindu ndi Chisilamu. Komabe anthu azikhalidwe ziŵiri zonsezi tinayamba kuwamvetsa ndiponso kuona mbali zawo zina zabwino. Popeza kuti zinali zodabwitsa kuona anthu akunja atakwera basi wamba, nthaŵi zambiri tikakwera basi anthu ankatiyang’ana modabwa. Sybil anangofika poganiza kuti anthu akamamuyang’ana iyeyo azingomwetulira kwambiri. Zinali zosangalatsa kuona anthuwo akumwetuliranso akaona kuti iyeyo akuwamwetulira.
Panthaŵi ina, apolisi osecha magalimoto pamsewu anatiimitsa. Wapolisi amene anali pamenepo anatifunsa kuti tikuchokera kuti ndipo tikupita kuti, kenaka anayamba kutifunsa mafunso ngati kuti tikudziŵana bwino kwambiri.
“Mkazi uli nayeyu ndani?”
Ndinayankha kuti: “Ameneyu ndi mkazi wanga.”
“Mwakhala m’banja zaka zingati?”
“Zaka eyiti.”
“Muli ndi ana?”
“Ayi.”
“Pepani, pepani! Koma, kuchipatala munapita?”
Mafunso otereŵa poyamba ankatidabwitsa, koma patapita nthaŵi tinayamba kuona kuti anthuŵa ankasonyeza mtima woganizira ena umene anali nawo. Kwenikweni, khalidwe limeneli linali limodzi mwa makhalidwe awo abwino kwambiri. Munthu ukangokhala malo odutsa anthu kwa kanthaŵi kochepa chabe winawake ankabwera n’kukufunsa ngati angakuthandize m’njira inayake.
Kusintha kwa Zinthu Ndiponso Kuyang’ana M’mbuyo
Pa zaka zonsezi, takhala tikupatsidwa ntchito zosiyanasiyana kuphatikiza pa ntchito yathu yaumishonale ku Sri Lanka. Ndinapatsidwako ntchito yoyang’anira dera ndiponso yoyang’anira chigawo komanso yokhala m’Komiti ya Nthambi. Pofika chaka cha 1996, ndinali m’zaka za m’ma 75. Ndinali wosangalala kuyang’ana m’mbuyo n’kumaganizira za utumiki waumishonale umene ndinachita kwa zaka 45 ku Sri Lanka. Pamsonkhano woyamba umene ndinachita ku Colombo, panali anthu pafupifupi 20. Tsopano nambala imeneyi yapitirira 3,500! Ineyo ndi Sybil tinkawaona ambiri mwa okondedwa athuŵa ngati ana ndi zidzukulu zathu zauzimu. Komabe, panali ntchito yambiri yoyenera kuchitika m’dziko lonselo, ntchito yofunika mphamvu ndiponso luso la anthu achinyamata kuposa ifeyo. Poganizira zimenezi, Bungwe Lolamulira litatipempha kuti tibwerere ku Australia tinavomera. Zimenezi zatheketsa mabanja achinyamata amene ali woyenerera ntchito yaumishonale kuti apite ku Sri Lanka kukaloŵa m’malo mwathu.
Tsopano ndili ndi zaka 82, ndipo ineyo ndi Sybil timasangalala kuti tidakali athanzi mwakuti tikupitirizabe utumiki wathu wa upainiya wapadera kumudzi kwathu ku Adelaide. Utumiki wathu umatithandiza kuti tikhalebe ndi nzeru zakuthwa ndiponso kuti tithe kuzoloŵera mosavuta zinthu zikamasintha. Utumikiwu watithandizanso kuti tithe kuzoloŵera moyo wa m’dziko la Australia lino womwe wasintha kwambiri.
Yehova wapitirizabe kutipatsa zinthu zonse zofunikira pamoyo wathu watsiku ndi tsiku, ndipo abale ndi alongo a mumpingo wathu amatikonda ndi kutisamalira kwambiri. Posachedwapa ndinapatsidwa ntchito yatsopano. Ndinapatsidwa ntchito yoti ndikhale mlembi mumpingo wathu. Motero, ndaona kuti pamene ndikuyesetsa kutumikira Yehova mokhulupirika, maphunziro anga akupitirirabe. Ndikayang’ana m’mbuyo, nthaŵi zonse ndimadabwa ndikamaganiza kuti zinatheka bwanji kuti kamnyamata kakumudzi ngati ineyo, ndiphunzire maphunziro apamwamba otereŵa, amene ndikupitirizabe mpaka panopa.
[Chithunzi patsamba 26]
Patsiku la ukwati wathu, mu 1955
[Chithunzi patsamba 27]
Mu 1957 ndikuchita utumiki wa kumunda ndi mbale wa ku Sri Lanka konko, dzina lake Rajan Kadirgamar
[Chithunzi patsamba 28]
Ineyo ndi Sybil panopo