Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Mukondane ndi Chikondi Chaubale”

“Mukondane ndi Chikondi Chaubale”

“Mukondane ndi Chikondi Chaubale”

“M’chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni [“chaubale,” NW].”​—AROMA 12:10.

1, 2. Kodi mmishonale wina wanthaŵi yathu ino ndiponso mtumwi Paulo anali ndi ubale wotani ndi abale ake?

PA ZAKA zonse zokwana 43 zimene Don anakhala akuchita utumiki waumishonale ku Far East, iye anali kudziŵika kuti ndi munthu wokonda anthu amene ankawatumikira. Don atadwala matenda amene anamwalira nawo, ena mwa anthu amene anaphunzira nawo Baibulo anayenda mitunda ya itali kwambiri kukamuona ali chigonere. Cholinga chawo chinali chokamuuza kuti, “Kamsahamnida, kamsahamnida!” Mawu ameneŵa ndi a chinenero cha Chikoreya ndipo amatanthauza kuti, “Zikomo kwambiri, zikomo kwambiri!” Iwo anakhudzidwa mtima kwambiri ndi chikondi chaubale chimene Don anali nacho.

2 Pali zitsanzo zinanso zofanana ndi chitsanzo cha Don. M’zaka 100 zoyambirira, mtumwi Paulo anali kuwakonda kwambiri anthu amene ankawatumikira. Paulo anali ndi mtima wodzimana. Ngakhale kuti sankasintha chisawawa mfundo zake, anali wodekha ndiponso woganizira ena, ‘monga mmene mlezi amafukatira ana ake a iye yekha.’ Mpingo wa ku Tesalonika anaulembera kuti: “Ife poliralira inu [“chifukwa cha chikondi chaubale,” NW], tinavomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.” (1 Atesalonika 2:7, 8) Patapita nthaŵi, Paulo atauza abale ake a ku Efeso kuti sadzamuonanso, ‘onse analira kwambiri, nam’kupatira Paulo pakhosi pake, nam’psompsona.’ (Machitidwe 20:25, 37) N’zoonekeratu kuti ubale umene unalipo pakati pa Paulo ndi abale ake sikuti unangothera pa kukhala anthu a chikhulupiriro chimodzi. Koma ankakondana ndi chikondi chaubale.

Mitundu Yosiyanasiyana ya Chikondi

3. Kodi m’Baibulo muli mitundu yosiyanasiyana iti ya chikondi?

3 M’Malemba muli mitundu yosiyanasiyana ya chikondi chomwe ndi khalidwe lapamwamba kwambiri pa Chikristu. Timapezamo za chikondi chomverana chisoni, chikondi chosonyezana chifundo ndiponso za chikondi chaubale. (1 Atesalonika 2:8; 2 Petro 1:7) Makhalidwe abwino onseŵa amagwirira ntchito pamodzi ndipo amathandiza kwambiri. Amagwirizanitsa kwambiri Akristu komanso amawathandiza kukhala paubwenzi wolimba ndi Atate wawo wakumwamba. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake kuti: ‘Chikondano [chanu] chikhale chopanda chinyengo. . . . M’chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chaubale.’​—Aroma 12:9, 10.

4. Kodi mawu akuti “chikondi chaubale” amatanthauzanji?

4 Mawu a Chigiriki amene Paulo anawagwiritsira ntchito pa mawu akuti “chikondi chaubale” ali ndi mbali ziŵiri. Mbali yoyamba ya mawuwo imatanthauza ubwenzi, ndipo mbali yachiŵiriyo imatanthauza chikondi chachibadwa. Malinga ndi zimene katswiri wina wamaphunziro a Baibulo anafotokoza, izi zikutanthauza kuti Akristu “ayenera kukhala ndi chikondi chofanana ndi chimene chimakhalapo m’banja logwirizana ndiponso lothandizana.” Kodi umu ndi mmene inuyo mumawaonera abale ndi alongo anu achikristu? Mu mpingo wachikristu muyenera kukhala chikondi, ngati mmene zimakhalira pachibale. (Agalatiya 6:10) Motero, Baibulo la Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono limatembenuza lemba la Aroma 12:10 motere: “Muzikondana kwenikweni monga abale.” Ndipo Baibulo la Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero limati: “Mukondane wina ndi mnzake ndi chikondi cha ubale.” Zoonadi, Akristu amakondana osati chifukwa chakuti ndibwino kutero kapena chifukwa chakuti amalamulidwa kuchita zimenezo. Koma tiyenera ‘kukondana kwenikweni, kuchokera kumtima ndi chikondi chosanyenga.’​—1 Petro 1:22.

‘Watiphunzitsa ndi Mulungu Kukondana’

5, 6. (a) Kodi Yehova wagwiritsira ntchito motani misonkhano yamayiko pophunzitsa anthu ake za chikondi chachikristu? (b) Kodi ubale wa pakati pa abale umalimba motani pakapita nthaŵi yaitali?

5 Ngakhale kuti m’dzikoli “chikondano cha anthu aunyinji” chikuzilala, Yehova akuphunzitsa anthu ake a masiku ano ‘kukondana wina ndi mnzake.’ (Mateyu 24:12; 1 Atesalonika 4:9) Misonkhano yamayiko ya Mboni za Yehova imatipatsa mwayi waukulu wophunzira chikondi chimenechi. Pamisonkhano imeneyi, Mboni za m’dziko lomwe mukuchitikira msonkhanowo zimakumana ndi abale a kumayiko akutali kwambiri, ndipo Mboni zambiri zimapereka malo ogona kwa alendowo. Pamsonkhano wina waposachedwapa, anthu ena anachokera kumayiko omwe anthu nthaŵi zambiri sasonyeza poyera mmene akumvera mumtima mwawo. “Alendo ameneŵa atangofika kumene, anali ndi nkhaŵa komanso manyazi kwambiri,” anatero Mkristu wina amene anali kuthandiza nawo pantchito yokonzera alendowo malo ogona. “Koma patangotha masiku asanu ndi limodzi pamene anali kutsanzikana, alendowo pamodzi ndi anthu amene anawasunga kunyumba kwawo anali kukumbatirana ndiponso kulirirana. Anasangalala kwambiri ndi chikondi chachikristu chimene sadzachiiŵala.” Kuwalandira bwino abale athu, mosaganizira za komwe akuchokera, kungapindulitse mlendoyo komanso mwininyumba.​—Aroma 12:13.

6 Zimene zimachitika pamisonkhano yotere zimakhaladi zosangalatsa kwambiri, koma chikondi cholimba chimathanso kuyambika Akristu akatumikira Yehova limodzi kwa nthaŵi yaitali. Tikawadziŵa bwino abale athu, tingathe kuyamba kuchita chidwi kwambiri ndi makhalidwe awo osangalatsa, monga kuchita zinthu moona mtima, kudalirika, kukhulupirika, kukoma mtima, kupatsa, kuganizira ena, chifundo, ndiponso kupanda dyera. (Salmo 15:3-5; Miyambo 19:22) Mark, amene anachitapo utumiki waumishonale ku East Africa, anati, “Kugwirira ntchito pamodzi ndi abale athu kumayambitsa ubale wolimba kwambiri.”

7. Kodi timafunika kuchita chiyani kuti tikondane ndi anthu a mu mpingo?

7 Kuti ubale woterewu utheke ndiponso kuti upitirizebe kukhalapo mu mpingo, anthu mumpingomo ayenera kukhala ogwirizana. Ubale umene tili nawo ndi abale ndi alongo athu umalimba tikamapezeka nthaŵi zonse pamisonkhano yachikristu. Popezeka pamisonkhano ndi kucheza ndi abale misonkhanoyo isanayambe ndiponso itatha, komanso kumachita nawo zinthu za pamisonkhanoyo, timakhala tikulimbikitsana ku “chikondano ndi ntchito zabwino.” (Ahebri 10:24, 25) Mbale wina yemwe ndi mkulu ku United States anati: “Ndimasangalala ndikamakumbukira kuti ndili mwana, banja lathu nthaŵi zonse linkakhala m’gulu la anthu omalizira kuchoka pa Nyumba ya Ufumu. Tinkakonda kucheza kwanthaŵi yaitali ndithu nkhani zabwino ndi zolimbikitsa.”

Kodi Mukufunikira ‘Kukulitsa’ Chikondi Chanu?

8. (a) Kodi Paulo anali kutanthauzanji pamene analimbikitsa Akorinto kuti ‘akulitsidwe’? (b) Kodi tingatani kuti tikulitse chikondi mumpingo?

8 Kuti tisonyeze kwambiri chikondi chimenechi, mwina tikufunikira ‘kukulitsa’ chikondi m’mitima mwathu. Mtumwi Paulo analembera mpingo wa ku Korinto kuti: “Mtima wathu wakulitsidwa. Simupsinjika mwa ife.” Paulo anawalimbikitsa kuti nawo ‘akulitse’ chikondi chawo. (2 Akorinto 6:11-13) Kodi nanunso mungathe ‘kukulitsa’ chikondi chanu? Musayembekezere ena kuti ayambe ndiwo kukukondani. M’kalata imene Paulo analembera Aroma, ponena za kufunika kokhala ndi chikondi chaubale anapereka malangizo aŵa: “Mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.” (Aroma 12:10) Pochitira ena ulemu, mungathe kuyamba ndi inuyo kuwapatsa moni pamisonkhano. Mwinanso mungawapemphe kuti apite nanu mu utumiki wa kumunda kapena kuti akonzekere nanu pamodzi misonkhano. Kuchita zimenezi kumathandiza kukulitsa chikondi chaubale.

9. Kodi ena achita zotani kuti ayambe kugwirizana kwambiri ndi Akristu anzawo? (Phatikizanipo chitsanzo chilichonse cha mumpingo wanu.)

9 Mabanja ndiponso Mkristu aliyense mumpingo angathe ‘kukulitsa’ chikondi mwa kuyenderana, mwinanso kudyera limodzi chakudya, ndiponso pochitira limodzi ntchito zabwino. (Luka 10:42; 14:12-14) Hakop nthaŵi zina amakonza zoti kagulu ka anthu kapite kumalo ena kukacheza pamodzi. Iye anafotokoza kuti: “Pamakhala ana, akulu ndiponso makolo opanda mwamuna kapena mkazi wawo. Aliyense amapita kunyumba ali wosangalala ndiponso amaona kuti wayamba kukondanadi ndi anzake.” Monga Akristu, tiyenera kuyesetsa kuti tisangokhala anthu achikhulupiriro chimodzi, koma tikhalenso mabwenzi enieni.​—3 Yohane 14.

10. Kodi tingatani ngati sitikukhala nawo bwino abale ndi alongo athu?

10 Komabe nthaŵi zina kumakhala kovuta kuti tigwirizane ndiponso kukondana ndi anthu ena chifukwa cha zophophonya zawo. Kodi tingachite chiyani zikatero? Choyamba, tingapemphere kuti tizikhala nawo bwino abale athu. Mulungu amafuna kuti atumiki ake azikhala nawo bwino abale awo, ndipo angayankhe mapemphero ochoka pansi pamtima okhudza zimenezi. (1 Yohane 4:20, 21; 5:14, 15) Komanso tiyenera kuchita zinthu zogwirizana ndi mapemphero athuwo. Ric, yemwe ndi mtumiki woyendayenda ku East Africa, amakumbukira za mbale wina amene anali wovuta kugwirizana naye bwino chifukwa choti anali wokonda kuyankhula mokhadzula ndiponso mosaganizira anzake. Ric anafotokoza kuti: “M’malo momupeŵa mbale ameneyu, ndinakonza zoti ndim’dziŵe bwino kwambiri. Ndinapeza kuti abambo ake a mbaleyu anali ovuta kwambiri. Nditazindikira mmene mbaleyu anavutikira kuti aiŵale za ubwana wakewu, ndiponso mmene wasintha kwambiri, ndinayamba kuchita naye chidwi, ndipo tinayamba kugwirizana kwambiri.”​—1 Petro 4:8.

Asonyezeni Mmene Mukumvera Mumtima Mwanu

11. (a) Kodi kuti chikondi chikule mumpingo pamafunika chiyani? (b) Kodi n’chifukwa chiyani kusasonyeza mmene tikumvera mumtima mwathu kuli koopsa mwauzimu?

11 Anthu ambiri masiku ano amangodzikhalira popanda kukhala paubwenzi wolimba ndi winawake. Izi ndi zomvetsa chisoni kwambiri. Umu si mmene ziyenera kukhalira mumpingo wachikristu. Chikondi chenicheni cha pa abale sikuti ndi kungolankhulana bwino ndiponso kuchitirana ulemu; kayanso kuchita zinthu zodzionetsera kuti timakonda ena. M’malo mwake tiyenera kukhala ofunitsitsa kusonyeza ena mmene tikumvera mumtima mwathu, monga mmene Paulo anachitira kwa Akorinto, ndiponso tiyenera kuwasonyeza okhulupirira anzathu kuti timawaderadi nkhaŵa. Ngakhale kuti si aliyense amene mwachibadwa amakhala wochezeka, kapena wolankhulalankhula, kusasonyeza mmene tikumvera mumtima mwathu n’koopsa. Baibulo limachenjeza kuti: “Amene amakhala payekha, angofuna kudzaza zilakolako zake. Napsa mtima pakumva malangizo abwino alionse.”​—Miyambo 18:1, Malembo Oyera.

12. N’chifukwa chiyani kulankhulana bwino kuli kofunika kwambiri kuti mumpingo mukhale ubale wolimba?

12 Kulankhulana moona mtima n’kofunika kwambiri kuti pakhale ubwenzi weniweni. (Yohane 15:15) Tonsefe timafuna anzathu amene tingawafotokozere zakukhosi kwathu. Kuwonjezera apo, tikadziŵana bwino kwambiri, kumakhala kosavuta kuchitirana zinthu. Tikamaganizira zofuna za anzathu mwanjira imeneyi, timalimbikitsa chikondi chaubale pampingo, ndipo tidzaona kuti mawu otsatiraŵa amene Yesu ananena ndi oona. Iye anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35; Afilipi 2:1-4.

13. Kodi tingachite chiyani posonyeza kuti timakonda abale athu ndi chikondi chenicheni?

13 Kuti ena apindule kwambiri ndi chikondi chathucho, tiyenera kusonyeza chikondicho. (Miyambo 27:5) Ngati tili ndi chikondi chenicheni, sizisoŵa, ndipo zingathandize anthu enanso. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Kuunika kwa maso kukondweretsa mtima.” (Miyambo 15:30) Zochita zosonyeza kuti timaganizira anthu ena zingalimbikitsenso kuti pakhale chikondi chaubale. Ngakhale kuti palibe amene angagule chikondi chenicheni, mphatso imene munthu wapereka ndi mtima wonse ingathandize kwambiri kulimbikitsa chikondi. Kulemba khadi, kalata, ndiponso “mawu oyenera a pa nthaŵi yake,” zonsezi zingasonyeze kuti tili ndi chikondi chachikulu. (Miyambo 25:11; 27:9) Tikayamba kugwirizana ndi anthu ena, tiyenera kuonetsetsa kuti mgwirizanowo usathe mwa kupitiriza kuwakonda mopanda dyera. Tiyenera kuwathandiza anzathu, makamaka panthawi ya mavuto. Baibulo limati: “Bwenzi limakonda nthaŵi zonse; ndipo mbale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.”​—Miyambo 17:17.

14. Kodi tingatani ngati zikuoneka kuti chikondi chimene tikum’sonyeza munthu wina sichikum’khudza?

14 Kunena zoona, sitingayembekezere kuti tizigwirizana ndi aliyense mumpingo. Mwachibadwa, pamakhala ena amene tingakondane nawo kwambiri kuposa ena. Motero ngati simukugwirizana kwambiri ndi munthu wina monga mmene inu mukufunira, musathamangire kuganiza kuti mwina inuyo kapena iyeyo ali ndi vuto. Ndipo musam’kakamize munthu ameneyo kuti ayambe kugwirizana nanu kwambiri. Mukamagwirizana naye moyenerana ndi mmene iyeyo akufunira, n’zotheka kuti m’tsogolo mwake mungadzagwirizane naye kwambiri.

“Mwa Iwe Ndikondwera”

15. Kodi zimawakhudza bwanji ena tikamawayamikira kapena tikapanda kuwayamikira?

15 Yesu ayenera kuti anasangalala kwambiri paubatizo wake, pamene anamva mawu ochokera kumwamba akuti: “Mwa Iwe ndikondwera.” (Marko 1:11) Chikhulupiriro chimene Yesu anali nacho chakuti Atate wake amam’konda chiyenera kuti chinakula kwambiri atamva mawu ameneŵa osonyeza kuti Atate wakewo amakondwera naye. (Yohane 5:20) N’zomvetsa chisoni kuti ambiri samva mawu owayamikira ngati ameneŵa kuchokera kwa anthu amene iwoŵa amawalemekeza ndi kuwakonda. Ann anati: “Achinyamata ambiri angati ineyo alibe achibale mumpingo wachikristu.” Anapitiriza kuti, “Kunyumba amangokhalira kutikalipira. Izi zimatimvetsa chisoni kwambiri.” Koma, achinyamata ameneŵa akakhazikika mumpingo amaona kuti banja lothandizana ndiponso losamalirana lauzimu, lomwe lili atate, amayi, achimwene ndi achemwali achikhulupiriro chimodzi, limawakonda.​—Marko 10:29, 30; Agalatiya 6:10.

16. Kodi n’chifukwa chiyani mtima wokonda kudzudzula ena si wabwino?

16 M’zikhalidwe zina, makolo, anthu akuluakulu, ndiponso aphunzitsi kaŵirikaŵiri sayamikira ana mochokera pansi pamtima, ati poganiza kuti akatero angathe kuwapangitsa anawo kusalimbikira kapena kudzikuza. N’zotheka kuti mabanja achikristu ndiponso mpingo utengere maganizo ameneŵa. Pofotokoza za nkhani imene mwana wakamba kapena chinthu china chimene iye wachita, anthu akuluakuluwo anganene kuti: “Wachita bwino ndithu, koma ungathe kuchita bwino kwambiri kuposa pamene paja.” Kapenanso angasonyeze m’njira ina kuti sakusangalala ndi zochita za mwanayo. Anthu ambiri amaganiza kuti akamachita zimenezi amakhala akulimbikitsa ana kuti azichita bwino kwambiri. Koma nthaŵi zambiri zinthu zimene zimachitika zimakhala zosemphana ndi zimenezi, popeza kuti anawo mwina angathe kungogwa ulesi kapena kuona kuti sangathe kuchita bwino.

17. N’chifukwa chiyani tiyenera kufufuza mipata yoyamikirira ena?

17 Komabe, sikuti kuyamikira kuzingokhala mawu oyamba popatsa munthu uphungu. Kuyamikira kochokera pansi pamtima kumalimbikitsa kuti m’banja ndiponso mumpingo mukhale chikondi chaubale, zomwe zimalimbikitsa ana kupita kukafunsira malangizo kwa abale ndi alongo odziŵa zambiri. Motero, m’malo mongotsatira chikhalidwe chathu pamene tikuchita zinthu ndi anthu ena, tiyeni ‘tivale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.’ Tiyeni tiziyamikira ena monga mmene Yehova amachitira.​—Aefeso 4:24.

18. (a) Ananu, kodi malangizo ochokera kwa anthu akuluakulu muyenera kuwaona motani? (b) N’chifukwa chiyani anthu akuluakulu amakhala osamala popereka malangizo?

18 Komanso, ananu, musamaganize kuti anthu akuluakulu akamakulangizani, ndiye kuti amadana nanu. (Mlaliki 7:9) Sichoncho ayi. N’zachidziŵikire kuti amatero chifukwa chokuganizirani ndiponso kukukondani kwambiri. Akanakhala kuti sakukondani sibwenzi akudzivutitsa kukupatsani malangizowo. Popeza amadziŵa mmene mawu amakhudzira anthu ena, anthu akuluakulu, makamaka akulu mumpingo, nthaŵi zambiri amayesetsa kuganizira mofatsa ndi kupemphera asanayambe kum’patsa munthu malangizo, chifukwa amafuna kum’thandiza.​—1 Petro 5:5.

“Ambuye Ali Wodzala Chikondi” Chaubale

19. Kodi n’chifukwa chiyani anthu amene anagwiritsidwapo fuŵa lamoto m’mbuyomu angayembekezere Yehova kuwathandiza?

19 Chifukwa chakuti m’mbuyomo anakhumudwitsidwapo atasonyeza chikondi chaubale, ena angaganize kuti kusonyeza chikondichi kungathe kuwagwiritsanso fuŵa lamoto. Kuti anthu oterowo ayambirenso kukondana kwambiri ndi ena, amafunika kulimba mtima ndiponso kukhala ndi chikhulupiriro cholimba. Koma sayenera kuiŵala kuti Yehova “sakhala patali ndi yense wa ife.” Iye akutipempha kuti timuyandikire. (Machitidwe 17:27; Yakobo 4:8) Iye amamvetsanso maganizo amene tili nawo owopa kukhumudwitsidwa, ndipo akulonjeza kuti adzakhala nafe ndi kutithandiza. Wamasalmo Davide akutsimikizira kuti: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.”​—Salmo 34:18.

20, 21. (a) Kodi tikudziŵa bwanji kuti n’zotheka kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova? (b) Kodi kuti munthu ayanjane ndi Yehova pamafunika chiyani?

20 Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiye ubale wofunika kwambiri womwe tingakhale nawo. Koma kodi n’zothekadi kukhala paubwenzi woterowo? Inde, n’zotheka. Baibulo limafotokoza za amuna ndi akazi olungama amene anaona kuti anali paubwenzi wolimba ndi Atate wathu wakumwamba. Zimene iwo ananena mosangalala zinasungidwa kuti zitipatse chikhulupiriro chakuti nafenso tingathe kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova.​—Salmo 23, 34, 139; Yohane 16:27; Aroma 15:4.

21 Zimene Yehova amafuna kwa anthu ‘oyanjana’ naye ndi zoti aliyense angathe kuchita. “Yehova, ndani adzagonera m’chihema mwanu?” anafunsa motero Davide. “Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake.” (Salmo 15:1, 2; 25:14, Malembo Oyera [Salmo 25:14, mu Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu]) Tikayamba kuona kuti kutumikira Mulungu n’kopindulitsa ndiponso kumapangitsa kuti iye azititsogolera ndi kutiteteza, tidzafika podziŵa kuti “Ambuye ali wodzala chikondi” chaubale.​—Yakobo 5:11.

22. Kodi Yehova amafuna kuti anthu ake akhale ndi chikondi chotani?

22 Ndife odala kwambiri kuti Yehova amafunitsitsa kukhala paubwenzi wolimba ngati umenewu ndi anthu opanda ungwirofe. Motero, kodi sitiyenera kukondana ndi chikondi chaubale? Mothandizidwa ndi Yehova, aliyense wa ife angasonyeze ndiponso angasonyezedwe chikondi chaubale chomwe chimadziŵikitsa ubale wathu wachikristu. Mu Ufumu wa Mulungu, aliyense padziko lapansi adzakondedwa motere.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi zinthu ziyenera kukhala bwanji mumpingo wachikristu?

• Kodi aliyense wa ife angatani polimbikitsa chikondi chaubale mumpingo?

• Kodi kuyamikira ena mochokera pansi pamtima kumathandiza motani kukulitsa chikondi chachikristu?

• Kodi chikondi chaubale cha Yehova chimatithandiza motani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Akristu sikuti amangokondana chifukwa chakuti ndi udindo wawo kutero

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Kodi ‘mungakulitse’ chikondi chanu?

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi mumakonda kudzudzula kapena mumakonda kulimbikitsa?