Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Si Maseŵera Chabe

Si Maseŵera Chabe

Si Maseŵera Chabe

ANA amakonda kuseŵera. Koma “sikuti zimene amachitazo n’zinthu zopanda ntchito kwenikweni kapena zosapindulitsa,” linatero buku lina lofotokoza za ana lakuti The Developing Child. “Zikuoneka kuti maseŵeraŵa amayala maziko a mmene mwanayo amadzaonera zinthu akadzakula.” Poseŵera, ana amaphunzira kugwiritsira ntchito ziwalo monga mphuno, makutu, ndi lilime, amayamba kumvetsa zochitika m’malo amene akukhala, ndiponso kuphunzira kukhala ndi ena.

Ana akakwanitsa zaka zinayi kapena zisanu, amayamba kuchita maseŵera ena oyesezera ntchito za akuluakulu. Nthaŵi ina Yesu analankhulapo zokhudza ana akuseŵera. Ena ankafuna kuti achite maseŵera oyesezera “mwambo wa ukwati,” pamene ena ankafuna kuyesezera “mwambo wa maliro” ndipo, monga momwe ana amachitira nthaŵi zonse, anali kutsutsana chifukwa chakuti ena sankafuna kuchita nawo maseŵerawo. (Mateyu 11:16, 17) Kuchita maseŵera amtundu umenewu kungathandize anawo kuphunzira ntchito zofunika kwambiri.

Ana amene mukuwaona m’zithunzi zili panozi akuchita maseŵera oyesezera zimene wophunzira Baibulo ndi mphunzitsi wake amachita. Apa sikuti akuchitadi phunziro la Baibulo, koma n’zoonekeratu kuti akuganizira za ntchito yodziŵitsa ena uthenga wa m’Baibulo. Ndipo ili ndi phunziro lofunika kwambiri, chifukwa chakuti Yesu analamula anthu onse omutsatira kuti apange ophunzira ndi kuphunzitsa anthu kusunga zinthu zonse zimene iye anali atawaphunzitsa.​—Mateyu 28:19, 20.

Makolo amene ana awo amakonda kuyesezera akuchititsa maphunziro a Baibulo, kukamba nkhani, kapena kulalikira kunyumba ndi nyumba, amanyadira ndipotu mpake kuti amatero. Mwachibadwa, ana amatengera zinthu zimene amaona kwa anthu akuluakulu amene amakhala nawo. Maseŵera a zinthu zokhudza Baibulo amene ana amachita amasonyeza kuti anawo akuleredwa “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”​—Aefeso 6:4.

Yehova amafuna kuti ana azithandizira nawo pa kulambira koona. Anauza Mose kuti aziitanitsanso “ana aang’ono” pamene Chilamulo chikuŵerengedwa. (Deuteronomo 31:12) Ana akamaona kuti nawonso amaŵerengeredwa pa kulambira koona, maseŵera awo amasonyeza zimenezi. Ndipo mwana amene amachita maseŵera oyesezera kukhala mtumiki wa Mulungu amakhala akuchita chiyambi chomuthandiza kuti adzagwire ntchito imeneyo.