Kodi “Mulungu Woona Ndi Moyo Wosatha” Ndani?
Kodi “Mulungu Woona Ndi Moyo Wosatha” Ndani?
YEHOVA, Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, ndiye Mulungu woona. Iye ndiye Mlengi, amene amapereka moyo wamuyaya kwa anthu amene amamukonda. Umu ndi mmene anthu ambiri amene amaŵerenga komanso amakhulupirira Baibulo angayankhire funso limene lili pa mutu wankhani ino. Ndipotu, Yesu mwiniyo anati: ‘Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.’—Yohane 17:3.
Komabe, mmenemu si mmene anthu ambiri amene amapita kutchalitchi amawamvera mawu ameneŵa. Mutu wa nkhani ino wachokera pa 1 Yohane 5:20, pamene mwa zina pamati: “Tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Kristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.”
Anthu amene amakhulupirira chiphunzitso cha Utatu amati mawu akuti “iye” (amene pa Chigiriki ndi houʹtos) omwe ndi mloŵam’malo woloza amanena za munthu amene watchulidwa komalizirayo, yemwe ndi Yesu Kristu. Iwo amanena kuti Yesu ndiye “Mulungu woona ndi moyo wosatha.” Komabe, zimenezi sizigwirizana ndi Malemba ena onse. Ndipo akatswiri ambiri a Baibulo odalirika savomereza maganizo a Utatu ameneŵa. Katswiri wina wamaphunziro wa pa yunivesite ya Cambridge, B. F. Westcott, analemba kuti: “N’zachidziŵikire kuti [mloŵam’malo wakuti houʹtos] sakuimira munthu amene wangotchulidwa kumeneyo koma akuimira munthu amene anali m’maganizo mwa mtumwiyo panthaŵiyo.” Chotero, mtumwi Yohane anali kuganizira za Atate wake wa Yesu. Katswiri wina wa maphunziro a zaumulungu wa ku Germany, Erich Haupt, analemba kuti: “M’pofunika kuona bwinobwino ngati [houʹtos] amene watchulidwa mbali yachiŵiriyo akunena za munthu amene wangotchulidwa kumeneyo . . . kapena ngati akunena za munthu amene watchulidwa m’mbuyomo, yemwe ndi Mulungu. . . . Malingana ndi chenjezo lakomalizira lonena za mafano, lembali likuoneka kuti likutsimikizira zakuti pali Mulungu mmodzi yekha woona osati zakuti Kristu ndiye Mulungu.”
Ngakhale buku lakuti A Grammatical Analysis of the Greek New Testament, lofalitsidwa ndi bungwe la Pontifical Biblical Institute ku Rome, limati: Mawu akuti “[houʹtos]: amene ali kumapeto kwa [mavesi] 18 mpaka 20 ndithudi akunena za Mulungu weniweni ndi woona, wosiyana ndi milungu yachikunja (vesi 21).”
Nthaŵi zambiri mawu akuti houʹtos, amene kaŵirikaŵiri anawamasulira kuti “iye” kapena “ameneyo,” sanena za munthu amene wangotchulidwa kumene m’chiganizo. Malemba ena amasonyeza zimenezi. Pa 2 Yohane 7, mtumwi yemweyo amene analemba Yohane Woyamba, analemba kuti: “Onyenga ambiri adatuluka kuloŵa m’dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Kristu anadza m’thupi. Ameneyo [houʹtosʹ] ndiye wonyenga ndi wokana Kristu.” Mloŵam’malo wakuti “ameneyo” amene anatchulidwa m’vesili sangakhale akunena za munthu amene wangotchulidwa kumeneyo, yemwe ndi Yesu. Mwachionekere, mawu akuti “ameneyo” akunena za anthu amene anakana Yesu. Onse pamodzi amatchedwa “wonyenga ndi wokana Kristu.”
Mtumwi Yohane mu Uthenga wake Wabwino analemba kuti: ‘Andreya mbale wake wa Simoni Petro anali mmodzi wa aŵiriwo, anamva Yohane, nam’tsata Iye. Anayamba iye [houʹtos] kupeza mbale wake yekha Simoni.’ (Yohane 1:40, 41) N’zosachita kufunsa kuti apa mawu akuti “iye” akunena Andreya, osati munthu watchulidwa komalizirayo. Mtumwiyo anagwiritsa ntchito mloŵam’malo yemweyo m’njira yofanana ndi imeneyi pa 1 Yohane 2:22.
Luka anagwiritsanso ntchito mloŵam’maloyu mwa njira imeneyi, monga mmene tikuonera pa Machitidwe 4:10, 11, pamene pamati: ‘M’dzina la Yesu Kristu Mnazarayo, amene inu munam’pachika pamtanda, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, mwa iyeyu munthuyu aimirirapo pamaso panu, wamoyo. Iye [houʹtosʹ] ndiye mwalawo woyesedwa wopanda pake ndi inu omanga nyumba, umene unayesedwa mutu wa pangondya.’ Mloŵam’malo wakuti “iye” mwachionekere sakunena za munthu amene anaimirira atachiritsidwayo, ngakhale kuti ndi amene watchulidwa motsatana ndi mawu akuti houʹtos. Ndithudi, “iye” wopezeka mu vesi 11 akunena za Yesu Kristu yemwe anali Mnazara, yemwe ndi “mwala wa pangondya” pamene panamangidwa mpingo wachikristu.—Aefeso 2:20; 1 Petro 2:4-8.
Ndime zimenezi zikutsimikizira zimene ananena katswiri wina wamaphunziro wa ku Greece, Daniel Wallace, za aloŵam’malo oloza achigiriki. Iye anati: “Sikuti nthaŵi zonse wolemba nkhani amalemba mloŵam’malo pafupi ndi dzina limene akuliimiralo.”
“Woonayo”
Malinga ndi mmene mtumwi Yohane analembera, “Woonayo” ndi Yehova, Atate wake wa Yesu Kristu. Iye ndiye Mulungu woona yekha, Mlengi. Mtumwi Paulo anavomereza zimenezi, ndi mawu akuti: “Kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa Iye.” (1 Akorinto 8:6; Yesaya 42:8) Chifukwa china chimene Yehova alili “Woonayo” wonenedwa pa 1 Yohane 5:20, n’chakuti ndiye gwero la choonadi. Wamasalmo anati Yehova ndi “Mulungu wa choonadi” chifukwa ndi wokhulupirika m’zochita Zake zonse ndipo sanama. (Salmo 31:5; Eksodo 34:6; Tito 1:2) Mwanayo, ponena za Atate ake akumwamba, anati: “Mawu anu ndi choonadi.” Ndipo Yesu, ponena za ziphunzitso zake zomwe, anati: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha Iye amene anandituma Ine.”—Yohane 7:16; 17:17.
Yehova ndiyenso “moyo wosatha.” Iye ndi chitsime cha moyo, amene amaupereka monga mphatso yamtengo wapatali kudzera mwa Kristu. (Salmo 36:9; Aroma 6:23) N’zochititsa chidwi kuti mtumwi Paulo ananena kuti Mulungu ndi ‘wobwezera mphoto iwo akum’funa Iye.’ (Ahebri 11:6) Mulungu anapatsa mphoto Mwana wake mwa kumuukitsa kwa akufa, ndipo Atateyo adzapereka mphoto ya moyo wosatha kwa anthu amene amam’tumikira Iye ndi mtima wawo wonse.—Machitidwe 26:23; 2 Akorinto 1:9.
Choncho, kodi tingati mfundo imene tiyenera kugwira pamenepa ndi yotani? Ndi mfundo yakuti Yehova ndiye “Mulungu woona ndi moyo wosatha,” osati munthu wina aliyense. Poti iye ndiye analenga anthu, anthu onse akufunika kumulambira iye yekha basi ndi mtima wawo wonse.—Chivumbulutso 4:11.