Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumatha Kupanga Chithunzithunzi cha Zimene Mukuŵerenga?

Kodi Mumatha Kupanga Chithunzithunzi cha Zimene Mukuŵerenga?

Kodi Mumatha Kupanga Chithunzithunzi cha Zimene Mukuŵerenga?

KUTI poŵerenga mupange chithunzithunzi cha zochitika zinazake m’maganizo mwanu, ndi bwino kudziŵa bwino za dera limene zinthuzo zinachitikira. Mwachitsanzo, taganizirani maulendo aumishonale a mtumwi Paulo, amene anafotokozedwa m’buku la Machitidwe. Paulendo wake woyamba waumishonale, Paulo ananyamukira ku Antiokeya, komwe otsatira a Yesu anayambira kutchedwa kuti Akristu. Atachoka kumeneko anapita ku madera ena monga Salami, Antiokeya wa ku Pisidiya, Ikoniyo, Lustra, ndi Derbe. Kodi mungapange chithunzithunzi m’maganizo mwanu cha kumene madera ameneŵa anali?

Mwina simungatero, pokhapokha mutakhala ndi mapu. M’kabuku katsopano kamasamba 36 kotchedwa ‘Onani Dziko Lokoma,’ muli mapu otereŵa. Munthu wina wa ku Montana, ku United States, amene anagwiritsirapo ntchito kabukuka anayamikira motere: “Ndimatha kuona bwinobwino maulendo a Paulo ndipo ndimayesetsa kuganizira za kayendedwe ka maulendo akeŵa ndiponso za ntchito imene iye ndi Akristu ena oyambirira anachita pofalitsa uthenga wabwino. Zikomo kwambiri popanga kabuku kameneka komwe n’kothandiza kwambiri kuti munthu akhale ndi chithunzithunzi cha zimene akuŵerenga.”

M’kabukumu muli mapu enanso ambirimbiri kuphatikizapo mapu a maulendo a Pauloŵa ndipo mapuŵa n’ngothandiza kuti munthu akhale ndi chithunzithunzi cha zimene akuŵerenga m’Baibulo. Mungathe kuitanitsa kabuku kanu ka ‘Onani Dziko Lokoma’ polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika n’kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 2 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma.’

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

[Mawu a Chithunzi patsamba 32]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.