Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
Kodi mmene Yesu anauza otsatira ake kuti “kongoletsani osayembekeza kanthu konse” anali kutanthauza kuti asamafune kubwezeredwa ngakhale ndalama imene anakongoletsayo?
Mawu amene Yesu ananena pa Luka 6:35 tingawamvetse bwino tikaganizira zimene Chilamulo cha Mose chinanena. M’chilamulo chimenechi Mulungu analamula Aisrayeli kuti Aisrayeli anzawo amene asauka ndipo akufuna chithandizo aziwakongoza popanda kufuna chiwongoladzanja. (Eksodo 22:25; Levitiko 25:35-37; Mateyu 5:42) Zimenezi sizinali ngongole zopezerapo kangachepe. Komano cholinga chake chinali chomuthandiza munthu amene ali paumphaŵi kapena pamavutoyo. Chifukwatu akanati anthu ena azipindulira pa umphaŵi wa anzawo zikanasonyeza kusoŵa chikondi kwenikweni. Komabe, munthu amene akukongoza ndalamayo ankayenera kubwezeredwa ndalama imene anakongoletsa yokhayo, ndipo nthaŵi zina ankatenga chikole (kapena kuti chinthu chotsimikizira kuti adzabwezadi ngongoleyo).
Ponena kuti munthu amene akuthandiza mnzake sayenera ‘kuyembekezera kanthu kalikonse,’ Yesu anasonyeza mbali zinanso zimene Chilamulo chimagwira ntchito, ndipo sikuti anali kuchichepetsa mphamvu ayi. Monga Aisrayeli, Akristu nthaŵi zina amakumana ndi mavuto a zachuma kapena mavuto ena amene angawaike paumphaŵi, mwinanso kuchita kuwasoŵetsa pogwira. Ngati mbale wachikristu amene ali mu vuto lotereli akufuna chithandizo cha zachuma, kodi sitingamuthandize chifukwa chomuchitira chifundo? Inde, chikondi chenicheni chingachititse Mkristu kuthandiza mbale mnzake amene wakumana ndi mavuto a zachuma mosachita kuwaputa dala. (Miyambo 3:27) Mbale amene vuto lotere lamugwera mungathe kungom’patsa thandizolo ngati mphatso, ngakhale kuti mwina lingakhale locheperapo kusiyana ndi mmene mungam’patsire ngati mutafuna kuti ikhale ngongole.—Salmo 37:21.
M’zaka za m’ma 100 Kristu Atabwera, mtumwi Paulo ndi Barnaba anatumidwa kuti akatenge zopereka zochokera kwa Akristu a ku Asiyamina kupita nazo kwa abale awo ku Yudeya chifukwa cha chilala. (Machitidwe 11:28-30) Moteronso masiku ano kukabuka mavuto ngati ameneŵa, Akristu nthaŵi zambiri amatumiza mphatso kwa abale awo amene ali pamavuto. Potero, iwo amapereka umboni wabwino kwa anthu ena. (Mateyu 5:16) N’zoona kuti ndi bwinonso kuganizira kaye za mtima wa munthu amene akufuna thandizoyo ndiponso vuto lake. Kodi n’chifukwa chiyani wakumana ndi vutolo? Mawu a Paulo akuti, “ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso,” n’ngothandiza pa nkhaniyi.—2 Atesalonika 3:10.
Ngati mbale amene akufuna ngongoleyo mwina akungofuna chithandizo cha nthaŵi yochepa chabe pa vuto laling’ono la zachuma, mungaone kuti m’poyeneradi kum’patsa ngongole popanda kufuna chiwongoladzanja. Ngati zinthu zili choncho, kum’patsa munthuyo ngongole yoti adzabweze ndalama zonse zimene wakongolazo sikosemphana ndi mawu a Yesu a pa Luka 6:35. Muyenera kulemba zimene mwagwirizana pankhani ya kabwezedwe ka ngongoleyo, ndipo munthu wokongolayo ayenera kuyesetsa kubweza ngongoleyo malingana ndi panganolo. Inde, chikondi chachikristu chiyenera kum’pangitsa munthu wokongolayo kubweza ngongoleyo monga mmene chinapangitsira wokongozayo kupereka ngongoleyo.
Munthu amene akuganizira zokongoza mnzake ndalama (kapena zongom’patsa ndalamayo ngati mphatso) ayenera kuganizira za mmene nayenso zinthu zilili m’banja mwake. Mwachitsanzo, kodi kukongoza munthu wina ndalama kungam’chititse kuti avutike kusamalira anthu a m’banja mwake, amene Malemba amati ndiwo ali oyenera kuwaganizira poyamba? (2 Akorinto 8:12; 1 Timoteo 5:8) Komabe mfundo yaikulu ndi yakuti Akristu amayesetsa kuona mmene angasonyezerane chikondi, pothandizana m’njira zimene zili zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.—Yakobo 1:27; 1 Yohane 3:18; 4:7-11.