Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pindulani Polimbikira Kuchita Zinthu Zauzimu

Pindulani Polimbikira Kuchita Zinthu Zauzimu

Pindulani Polimbikira Kuchita Zinthu Zauzimu

“Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu.”​Mlaliki 5:10.

KUGWIRA ntchito mopambanitsa kungayambitse kuvutika maganizo, ndipo kuvutika maganizo kungayambitse matenda, nthaŵi zina ngakhale kudzetsa imfa imene. M’mayiko ambiri mabanja akupasuka chifukwa chosudzulana. Nthaŵi zambiri, kukondetsa chuma n’kumene kumachititsa mavuto ameneŵa. M’malo mokhutira ndi zimene ali nazo, munthu amene amafunitsitsa chuma amangokhalira kusakasaka chuma, mosaganizira za moyo wake. Buku lina la malangizo limati: “Anthu m’dziko lathu lino amafuna kukhala ndi zinthu zofanana ndi zimene mnzawo ali nazo ngakhale mnzawoyo atakhala munthu wogwira ntchito mosapumira amene angathe kudwala matenda a mtima mwina ali ndi zaka 43 zokha.”

Nthaŵi zina, munthu angasakesake chuma mosakhutitsidwa nacho, ndipo zimenezi zingachititse kuti akhale wosasangalala. Chifukwa cha kufooka kwathu pankhaniyi, anthufe nthaŵi zambiri timatengeka ndi mawu achikoka a otsatsa malonda. Malonda a pa TV ndi pa wailesi nthaŵi zonse amalimbikitsa kwambiri kugula zinthu zimene mwina zili zosafunikira ndiponso zimene simungazikwanitse n’komwe kugula. Zonsezi zingakuikeni m’mavuto aakulu.

Kukonda chuma mosadziletsa kungatiike m’mavuto aakulu kwambiri okhudza thanzi ndiponso khalidwe lathu, ngakhale kuti vutolo silingaonekere kwenikweni. Mwachitsanzo, Mfumu yanzeru Solomo inati: “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi.” (Miyambo 14:30) Mosiyana ndi zimenezi, kugwira ntchito mopambanitsa, kuda nkhaŵa, ndiponso mavuto amene amabwera chifukwa chosakasaka chuma zingawononge thanzi lathu ndipo zingatilande chimwemwe chathu. Kukonda chuma kwambiri kungawonongenso ubwenzi wathu ndi anthu ena. Ndipo banja la munthu ndiponso ubwenzi wake ndi anthu ena zikasokonezeka, moyo wake umasokonezekanso kwambiri.

Kupambana kwa Zinthu Zauzimu

Zaka zambirimbiri zapitazo, mtumwi Paulo anati: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano.” (Aroma 12:2) Dzikoli limakonda anthu amene amachita zofuna zake. (Yohane 15:19) Limayesa kutikopa potionetsa zinthu zoti tizilakalaka kuziona, kuzigwira, kuzinunkhiza, ndi kuzimva, ndiponso kuti titengere moyo wake wokonda chuma. Limalimbikitsa kwambiri “chilakolako cha maso” kuti inuyo ndiponso anthu ena muzisakasaka chuma.​—1 Yohane 2:15-17.

Komatu pali zinthu zina zofunika kwambiri kuposa ndalama, kutchuka, ndi chuma. Zaka zambirimbiri zapitazo, Mfumu Solomo inali ndi chuma chamtundu uliwonse. Inamanga nyumba ndipo inali ndi minda ya mbewu zosiyanasiyana ndiponso zipatso, inali ndi antchito, ziŵeto, anthu oimba aamuna ndi aakazi, komanso golide ndi siliva wambiri. Solomo anali ndi chuma kuposa anthu onse a m’mbuyo mwake. Iye anali wolemera kwambiri, osati maseŵera ayi. Tingati, Solomo anali ndi zinthu zonse zimene ankafuna. Koma, ataona zimene anachita, anati: “Zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima.”​—Mlaliki 2:1-11.

Mwanzeru zapadera zimene Yehova anamupatsa, Solomo anadziŵa kuti chimwemwe chenicheni chimabwera polimbikira kuchita zinthu zauzimu. Iye analemba kuti: “Mawu atha, zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”​—Mlaliki 12:13.

Zimene zimapezeka m’Mawu a Mulungu, Baibulo, n’zofunika kwambiri kuposa golide kapena siliva. (Miyambo 16:16) Monga miyala yamtengo wapatali, pali mfundo zofunika kwambiri za choonadi zoti inu muzidziŵe. Kodi mudzazifunafuna ndi kuzifufuza? (Miyambo 2:1-6) Mlengi wathu, yemwe amapereka zinthu zimene zili zofunikadi, akukulimbikitsani kuchita zimenezo, ndipo adzakuthandizani. Kodi adzakuthandizani bwanji?

Yehova amapereka mfundo za choonadi zamtengo wapatali kudzera m’Mawu ake, mzimu wake, ndi gulu lake. (Salmo 1:1-3; Yesaya 48:17, 18; Mateyu 24:45-47; 1 Akorinto 2:10) Kuŵerenga mfundo zamtengo wapatali zimenezi, zomwe n’zofunika kwambiri, kumakuthandizani kuti muthe kusankha mwanzeru njira yopindulitsa kwambiri pamoyo. Ndipo kusankha zimenezi sikovuta chifukwa Yehova, Mlengi wathu, amadziŵa zimene timafunikira kuti tikhaledi osangalala.

Baibulo Limalimbikitsa Kuchita Zinthu Zopindulitsa Kwambiri

Malangizo a m’Baibulo ndi othandiza kwambiri ndiponso n’ngoposa ena onse. Limalimbikitsa mfundo za makhalidwe abwino zapamwamba koposa zina zonse. Malangizo ake amapindulitsa nthaŵi zonse. Akhala oona ndi othandiza kwa nthaŵi yaitali. Zitsanzo za malangizo abwino a m’Baibulo ndi monga kulimbikira ntchito, kukhala woona mtima, kusamala ndalama, ndiponso kusakhala munthu waulesi.​—Miyambo 6:6-8; 20:23; 31:16.

Mogwirizana ndi zimenezi, Yesu anati: “Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziwononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: koma mudzikundikire nokha chuma m’Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba.”​—Mateyu 6:19, 20.

Malangizo a panthaŵi yake ameneŵa ndi othandiza masiku ano monga momwe analili zaka 2,000 zapitazo. M’malo motanganidwa ndi kusakasaka chuma, zinthu zingatiyendere bwino panopo polimbikira kuchita zinthu zofunika kuposa chuma. Chinsinsi chake chagona pokundika chuma chauzimu, chimene chimapangitsa munthu kukhala ndi moyo wachimwemwe ndi wosangalaladi. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingatero poŵerenga Mawu a Mulungu, Baibulo, ndi kutsatira zimene limaphunzitsa.

Zinthu Zauzimu Zimapindulitsa

Zinthu zauzimu tikazitsatira bwino, zimatipindulitsa pa moyo wathu watsiku ndi tsiku, pa maganizo athu, ndiponso pa moyo wathu wauzimu. Monga momwe mpweya winawake wa mlengalenga umatitetezera ku mphamvu ya dzuŵa yowononga, mfundo za makhalidwe abwino zimatiteteza potidziŵitsa kuopsa kokonda chuma. Mtumwi wachikristu Paulo analemba kuti: “Iwo akufuna kukhala achuma amagwa m’chiyesero ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zotere zonga zimiza anthu m’chiwonongeko ndi chitayiko. Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pandalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.”​—1 Timoteo 6:9, 10.

Kukonda chuma kumalimbikitsa anthu kufunafuna chuma chambiri, udindo wapamwamba, ndiponso mphamvu zochuluka. Nthaŵi zambiri, munthu amachita chinyengo kuti zimenezi zitheke. Kulimbikira kusaka chuma kumawonongetsa nthaŵi, mphamvu, ndiponso luso la munthu. Kukhozanso kum’soŵetsa tulo munthu. (Mlaliki 5:12) Ndithudi, kusakasaka chuma kumalepheretsa anthu kulimbikira zinthu zauzimu. Yesu Kristu, yemwe ndi munthu woposa onse amene anakhalako, ananena mosabisa njira yabwino kuitsatira. Iye anati: “Odala ali osauka mumzimu,” kapena kuti ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu. (Mateyu 5:3) Iye anadziŵa kuti chuma chauzimu chimapangitsa munthu kupindula kwamuyaya ndiponso n’chimene chili chofunika kwambiri kuposa katundu, chifukwa katundu sakhala kosatha.​—Luka 12:13-31.

Kodi N’kopindulitsadi?

Munthu wina dzina lake Greg anati: “Makolo anga anayesetsa umu ndi umu kundipangitsa kuona zinthu zauzimu ngati zopanda phindu. Komabe ndapeza mtendere wambiri wa m’maganizo chifukwa cholimbikira kuchita zinthu zauzimu popeza sindivutika maganizo chifukwa cholimbirana chuma ndi anthu ena.”

Zinthu zauzimu zimathandizanso munthu kukhala ndi anzake abwino. Anzanu enieni amakukondani chifukwa cha makhalidwe anu, osati chifukwa cha zinthu zimene muli nazo. Baibulo limalimbikitsa kuti: ‘Yenda ndi anzeru ndipo udzakhala wanzeru.’ (Miyambo 13:20) Ndiponso, banja limayenda bwino chifukwa cha nzeru ndi chikondi, osati chifukwa cha katundu.​—Aefeso 5:22–6:4.

Sitibadwa tikudziŵa kale zinthu zofunika kwambiri pamoyo. Tiyenera kuphunzira kwa anthu anzathu kapena kwa Mulungu. N’chifukwa chake kuphunzira Baibulo kungasinthe kwambiri mmene timaonera chuma. Don, yemwe kale anali wothandiza anthu kusungitsa ndalama ku banki, ananena kuti: “Ndinathandizidwa kusintha mmene ndimaonera zinthu pa moyo wanga, ndipo ndinaphunzira kukhala moyo wosalira zambiri.”

Limbikirani Kupeza Chuma Chauzimu Chomwe N’chosatha

Munthu akamaona zinthu mwauzimu amaganizira kwambiri mmene angadzapindulire patsogolo, osati panthaŵi yokhayo chabe. Paulo analemba kuti: “Zinthu zooneka [chuma], zili za nthaŵi, koma zinthu zosaoneka [zauzimu] zili zosatha.” (2 Akorinto 4:18) N’zoona kuti kusakasaka chuma kungam’khutiritse munthu kwa nthaŵi yochepa, koma dyera lotereli silingathandize munthu kukhala ndi tsogolo labwino. Zinthu zauzimu n’zopindulitsa kwamuyaya.​—Miyambo 11:4; 1 Akorinto 6:9, 10.

Baibulo limaletsa kukondetsa chuma komwe n’kofala kwambiri masiku ano. Limatiphunzitsa kuti tingathetse kulakalaka zinthu mwadyera pokhala ndi diso lakumodzi, longokhala pa zinthu zofunika kwambiri, zinthu zauzimu. (Afilipi 1:10) Limanena kuti kwenikweni kukhala ndi mtima wadyera n’kudzilambira. Tikamatsatira zimene timaphunzira m’Mawu a Mulungu, timakhala achimwemwe kwambiri. Timasiya mtima womangofuna kulandira zinthu ndipo m’malo mwake timayamba kukhala ndi mtima wopatsa. Zimenezi n’zothandiza kwambiri kuti tisiye kukonda chuma n’kuyamba kukonda zinthu zauzimu.

Inde, ndalama zimathandiza. (Mlaliki 7:12) Koma Baibulo limanena zoona, kuti: “Chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.” (Miyambo 23:5) Anthu awononga zinthu zofunika kwambiri monga thanzi, mabanja, ngakhalenso chikumbumtima chabwino, chifukwa chofuna chuma, ndipo zimenezi zawaika m’mavuto aakulu. Komano, kukonda zinthu zauzimu kumatithandiza kupeza zinthu zimene timafunikira kwambiri pamoyo wathu, monga kukondedwa, kukhala ndi cholinga, ndiponso kulambira Mulungu wachikondi, Yehova. Kumathandizanso kudziŵa njira yopezera moyo wosatha, pa nthaŵi imene anthu adzakhale angwiro m’dziko lapansi la paradaiso. Izi n’zimene timayembekeza kuti Mulungu adzatichitira.

Posachedwapa, m’dziko latsopano la Mulungu, anthu adzakhala ndi moyo wabwino umene amaulakalaka. (Salmo 145:16) Panthaŵiyo dziko lonse lapansi “lidzadzala ndi odziŵa Yehova.” (Yesaya 11:9) Munthu aliyense azidzakonda kuchita zinthu zauzimu. Mtima wokonda chuma ndiponso mavuto amene umabweretsa zidzatheratu. (2 Petro 3:13) Ndiyeno zinthu zimene zingapangitse moyo wathu kukhala wosangalatsa kwambiri monga thanzi langwiro, ntchito yabwino, zinthu zabwino zochita panthaŵi yongosangalala, kugwirizana pabanja, ndiponso ubwenzi wosatha ndi Mulungu, zidzapangitsa anthu kukhala ndi chimwemwe chenicheni kwamuyaya.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 6]

Muzisamala Ndalama!

Dziŵani zimene mumafunikadi. Yesu anatiphunzitsa kupemphera kuti: ‘Tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku.’ (Luka 11:3) Musamafune kukhala ndi zinthu zonse zimene mumalakalaka. Kumbukirani kuti moyo wanu sudalira katundu amene muli naye.​—Luka 12:16-21.

Konzani mmene mugwiritsire ntchito ndalama. Musamangogula zinthu chisawawa. Baibulo limati: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphaŵi.” (Miyambo 21:5) Yesu analangiza omvera ake kuti asanachite chinthu cholira ndalama aziyamba aganizira bwinobwino za mtengo wake.​—Luka 14:28-30.

Peŵani ngongole zosafunika kwenikweni. Ngati zingatheke, muzisunga ndalama kuti zikwanire chinthu chimene mukufuna kugula osati kungochigula pangongole. Mwambi wina umanena izi: “Wokongola ndiye kapolo wa wom’kongoletsa.” (Miyambo 22:7) Mungathe kukonza bwinobwino zodzagula zinthu zikuluzikulu m’tsogolo ngati muli wodziletsa ndiponso ngati mumagwiritsira ntchito ndalama zimene mumapezazo basi.

Peŵani kuwononga. Muzisamala zinthu zimene muli nazo kuti zikhalitse, poopa kuwononga. Yesu anasonyeza maganizo abwino pankhani yosunga zinthu zimene anagwiritsa ntchito.​—Yohane 6:10-13.

Tsogozani zinthu zofunika kwambiri. Munthu wanzeru ‘amachita machawi’ kapena kuti amapatula nthaŵi yochitira zinthu zofunika kwambiri.​—Aefeso 5:15, 16.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 7]

Pali Njira Yabwino Yophunzirira Zinthu Kuposa Yoyamba Mwakumana Nazo Kaye

Zinthu zabwino ndiponso zoipa zimene timakumana nazo zingatiphunzitse zinthu zofunika kwambiri. Koma kodi n’zoona kuti njira yabwino yophunzirira zinthu ndi yoyamba takumana nazo kaye? Ayi, pali njira yabwino kwambiri imene tingapezere nzeru zotidziŵitsa zinthu zoyenera kuchita. Wamasalmo anasonyeza njira imeneyi pamene ananena m’pemphero kuti: ‘Mawu anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.’​—Salmo 119:105.

Kodi n’chifukwa chiyani kuphunzira pogwiritsa ntchito malangizo a Mulungu kuli bwino kwambiri kuposa kuphunzira pa zimene timakumana nazo? Chifukwa chimodzi n’chakuti, kuphunzira pa zimene timakumana nazo basi, mwa kungoyesera, kungawonongetse zinthu ndiponso kungatipweteketse, komanso n’kosafunikira. Mulungu anauza Aisrayeli akale kuti: “Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”​—Yesaya 48:18.

Chifukwa chimodzi chimene chimapangitsa Mawu a Mulungu kukhala njira yabwino kwambiri yopezera nzeru zabwino n’chakuti ali ndi nkhani zakalekale ndiponso zolondola zimene zinachitikira anthu. Mosakayikira inuyo mumadziŵa kuti ndi bwino kuphunzira zinthu poona zimene anthu ena anachita bwino ndi zimene analakwitsa kusiyana n’kuphunzira pochita zinthu zokupweteketsani zimene anzanuwo analakwitsapo kale. (1 Akorinto 10:6-11) Chofunika koposa n’chakuti, m’Baibulo, Mulungu amatipatsa malamulo abwino kwambiri ndi mfundo zodalirika kwambiri zimene tingatsatire. ‘Malamulo a Yehova ali angwiro . . . Mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa [kapena kuti osadziŵa] nzeru.’ (Salmo 19:7) Ndithudi, kuphunzira pogwiritsa ntchito nzeru za Mlengi wathu wachikondi ndi njira yophunzirira zinthu yabwino koposa.

[Zithunzi patsamba 4]

Dziko limafuna kuti inuyo mutengere mtima wake wokonda chuma

[Chithunzi patsamba 5]

Zimene zimapezeka m’Baibulo, n’zofunika kwambiri kuposa golide kapena siliva