Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Atumiki Achimwemwe a Yehova

Atumiki Achimwemwe a Yehova

Atumiki Achimwemwe a Yehova

‘Odala [“achimwemwe,” NW] ali osauka mwauzimu.’​—MATEYU 5:3.

1. Kodi chimwemwe chenicheni n’chiyani, ndipo kodi chimasonyeza chiyani?

ANTHU a Yehova amaona kuti chimwemwe chomwe ali nacho ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Wamasalmo Davide anati: “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.” (Salmo 144:15) Chimwemwe ndi chisangalalo chochokera mumtima. Kudziŵa kuti Yehova amatiyanja n’kumene kumatipatsa chimwemwe chachikulu kwambiri chochokera pansi penipeni pamtima. (Miyambo 10:22) Chimwemwe chimenechi chimasonyeza kuti timagwirizana kwambiri ndi Atate wathu wakumwambayu ndiponso kuti timadziŵa kuti tikuchita chifuniro chake. (Salmo 112:1; 119:1, 2) N’zochititsa chidwi kuti Yesu anafotokoza zifukwa zisanu ndi zinayi zimene tingakhalire achimwemwe. M’nkhani ino ndi m’nkhani yotsatirayi tiona zifukwa zokhalira achimwemwe zimenezi ndipo zitithandiza kuzindikira chimwemwe chimene tingakhale nacho tikakhala okhulupirika potumikira Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe.”​—1 Timoteo 1:11, NW.

Kuzindikira Kuti Ndife Osauka Mwauzimu

2. Kodi ndi nthaŵi iti pamene Yesu analankhula za zifukwa zokhalira achimwemwe, ndipo mawu ake oyamba anali otani?

2 M’chaka cha 31 Kristu Atabwera, Yesu anakamba nkhani imene ili m’gulu la nkhani zotchuka kwambiri m’mbiri yonse. Nkhaniyi imatchedwa kuti Ulaliki wa pa Phiri chifukwa chakuti Yesu anaikamba ali m’mphepete mwa phiri moyang’anizana ndi Nyanja ya Galileya. Uthenga Wabwino wa Mateyu umati: ‘Ndipo mmene [Yesu] anaona makamu, anakwera m’phiri; ndipo mmene iye anakhala pansi, anadza kwa iye ophunzira ake; ndipo anatsegula pakamwa, nawaphunzitsa iwo, nati: Odala ali osauka mwauzimu; chifukwa uli wawo Ufumu wa Kumwamba.’​Mateyu 5:1-3. *

3. Kodi kudzichepetsa kumatithandiza motani kuti tikhale achimwemwe?

3 Paulaliki wake wa pa Phiriwu, Yesu ananena kuti munthu amakhala wachimwemwe kwambiri akamazindikira kuti ndi wosauka mwauzimu. Akristu odzichepetsa amadziŵa kuti ndi anthu ochimwa motero amapempha Yehova kuti awakhululukire machimo awo pa maziko a nsembe ya dipo ya Kristu. (1 Yohane 1:9) Motero amapeza mtendere wa m’maganizo ndiponso chimwemwe chenicheni. “Wodala munthuyo wokhululukidwa tchimo lake; wokwiriridwa choipa chake.”​—Salmo 32:1; 119:165.

4. (a) Kodi tingasonyeze motani kuti timazindikira kuti ifeyo komanso anzathu ndi osauka mwauzimu? (b) Kodi n’chiyani chimene chimatithandiza kukhala ndi chimwemwe chochuluka tikazindikira kuti ndife osauka mwauzimu?

4 Chifukwa chozindikira kuti ndife osauka mwauzimu timaŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, timadya chakudya chauzimu ‘chapanthaŵi yake’ chochokera kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndiponso timapezeka nthaŵi zonse pamisonkhano yachikristu. (Mateyu 24:45; Salmo 1:1, 2; 119:111; Ahebri 10:25) Kukonda anansi athu kumatithandiza kuzindikira kusauka mwauzimu kwa anthu ena ndipo izi zimapangitsa kuti tizilalikira ndi kuphunzitsa uthenga wabwino wa Ufumu mwakhama. (Marko 13:10; Aroma 1:14-16) Kuuza ena choonadi cha m’Baibulo kumatipatsa chimwemwe. (Machitidwe 20:20, 35) Chimwemwe chathu chimawonjezeka tikaganizira za zinthu zosangalatsa zomwe tikuziyembekezera zokhudza Ufumu ndiponso madalitso ake a Ufumuwo. Akristu odzozedwa a “kagulu ka nkhosa” akuyembekezera kukalandira moyo wosafa kumwamba komwe akakhale mbali ya boma la Ufumu wa Kristu. (Luka 12:32; 1 Akorinto 15:50, 54) A “nkhosa zina” akuyembekezera kudzalandira moyo wosatha padziko lapansi laparadaiso lolamulidwa ndi boma la Ufumuli.​—Yohane 10:16; Salmo 37:11; Mateyu 25:34, 46.

Mmene Achisoni Angakhalire Achimwemwe

5. (a) Kodi mawu akuti “ali achisoni” amatanthauzanji? (b) Kodi anthu otere amasangalatsidwa motani?

5 Mawu otsatira a Yesu onena za chifukwa chokhalira achimwemwe amaoneka ngati otsutsana. Iye anati: “Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa.” (Mateyu 5:4) Kodi zingatheke kuti munthu akhale wachisoni komanso nthaŵi yomweyo n’kukhala wachimwemwe? Kuti timvetse tanthauzo la zimene Yesu ananenazi, tiyenera kudziŵa kuti anali kunena za chisoni chotani. Wophunzira Yakobo anafotokoza kuti tiyenera kukhala achisoni chifukwa chakuti ndife ochimwa. Analemba kuti: “Sambani m’manja, ochimwa inu; yeretsani mitima, a mitima iŵiri inu. Khalani osautsidwa, lirani, lirani misozi; kuseka kwanu kusanduke kulira, ndi chimwemwe chanu chisanduke chisoni. Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.” (Yakobo 4:8-10) Anthu amene amamvadi chisoni chifukwa chakuti ndi ochimwa amasangalala akadziŵa kuti angathe kukhululukidwa machimo awo ngati atakhulupirira nsembe ya dipo ya Kristu ndi kusonyeza kuti alapadi poyamba kuchita zimene Yehova amafuna. (Yohane 3:16; 2 Akorinto 7:9, 10) Motero angathe kukhala paubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso angayembekezere kudzakhala kwamuyaya n’kumadzam’tumikira ndi kum’tamanda. Izi zimawapatsa chimwemwe chachikulu kwambiri cha mumtima.​—Aroma 4:7, 8.

6. Kodi ena ndi achisoni m’lingaliro lotani, ndipo amasangalatsidwa motani?

6 Mawu a Yesu akuphatikizaponso anthu amene akulira chifukwa cha zinthu zoipa zimene zafala padzikoli. Yesu ananena kuti ulosi wa pa Yesaya 61:1, 2 unali kunena za iye. Ulosiwo umati: “Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mawu abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima; . . . ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro.” Akristu odzozedwa amene adakali padziko lapansi pano akuchitanso ntchito imeneyi, mothandizidwa ndi anzawo, a “nkhosa zina.” Onseŵa akugwira ntchito yosindikiza mophiphiritsira mphumi za “anthu [amene] akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake [pa Yerusalemu wampatuko, yemwe akuimira Matchalitchi Achikristu].” (Ezekieli 9:4) Anthu achisoniŵa amasangalatsidwa ndi ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Mateyu 24:14) Ali ndi chimwemwe chifukwa chodziŵa kuti posachedwapa dongosolo loipa la Satanali lichoka ndipo m’malo mwake mubwera dziko latsopano lolungama la Yehova.

Achimwemwe ndi Anthu Ofatsa

7. Kodi mawu akuti “kufatsa” satanthauza chiyani?

7 Yesu anapitiriza Ulaliki wake wa pa Phiriwu ndi mawu akuti: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Anthu nthaŵi zina amaganiza kuti kufatsa kumatanthauza kusachangamuka. Komatu, izi sizoona ayi. Pofotokoza tanthauzo la mawu omwe anamasuliridwa kuti “kufatsa,” katswiri wina wamaphunziro a Baibulo analemba kuti: “Chizindikiro chachikulu cha munthu [wofatsa] ndicho chakuti iye amakhala wodziletsa kwambiri. Kufatsa sikutanthauza kukhala munthu wogona, wochita zinthu mokomedwa kapena wopusa. Munthu amakhala munthu wochangamuka kungoti amatha kudziletsa.” Ponena za iye mwini, Yesu anati: “Ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.” (Mateyu 11:29) Komatu Yesu ankalimbikitsa mfundo zolungama molimba mtima.​—Mateyu 21:12, 13; 23:13-33.

8. Kodi kufatsa n’kogwirizana ndi khalidwe liti, ndipo n’chifukwa chiyani khalidweli lili lofunika paubale wathu ndi anthu ena?

8 Motero, kufatsa n’kogwirizana kwambiri ndi kudziletsa. Ndipotu, mtumwi Paulo anaika pamodzi kufatsa ndiponso kudziletsa, pamene anali kufotokoza za “chipatso cha Mzimu.” (Agalatiya 5:22, 23) Tiyenera kuyesetsa kukhala ndi khalidwe la kufatsa mothandizidwa ndi mzimu woyera. Limeneli ndi khalidwe lachikristu limene limathandiza munthu kukhala pamtendere ndi anthu a zipembedzo zina, ndiponso anthu amene ali nawo mu mpingo. Paulo analemba kuti: “Valani . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha.”​—Akolose 3:12, 13.

9. (a) Kodi n’chifukwa chiyani kukhala wofatsa sikuti kumangotithandiza paubale wathu ndi anthu anzathu okha basi? (b) Kodi ofatsa “adzalandira dziko lapansi” motani?

9 Komabe, kufatsa sikuti kumangotithandiza paubwenzi wathu ndi anthu anzathu okha ayi. Tikamagonjera mofunitsitsa ulamuliro wa Yehova, timasonyeza kuti ndife ofatsa. Yesu Kristu ndiye chitsanzo chachikulu pankhaniyi. Pamene iye anali padziko lapansi pano anali wofatsa ndipo anali kugonjera ndi mtima wonse zofuna za Atate wake. (Yohane 5:19, 30) Choyambirira, Yesu analandira dziko lapansi ngati choloŵa, popeza kuti iye ndiye amene anasankhidwa kuti akhale Wolamulira wake. (Salmo 2:6-8; Danieli 7:13, 14) Iye amagaŵana choloŵa chimenechi ndi “oloŵa [ufumu] anzake” okwana 144,000, osankhidwa “mwa anthu” kuti ‘achite ufumu padziko.’ (Aroma 8:17; Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1, 3, 4; Danieli 7:27) Kristu limodzi ndi olamulira anzake adzalamulira amuna ndi akazi ambirimbiri onga nkhosa, ndipo ulosi wa m’Salmo udzakwaniritsidwa pa anthu ameneŵa, zomwe zidzakhale zosangalatsa kwambiri. Ulosiwo umati: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”​—Salmo 37:11; Mateyu 25:33, 34, 46.

Achimwemwe ndi Anthu Amene Akumva Njala ya Chilungamo

10. Kodi njira imodzi imene anthu ‘akumva njala ndi ludzu la chilungamo’ angakhalire okhuta ndi iti?

10 Chifukwa china chokhalira achimwemwe chimene Yesu anatchula pamene anali kulankhula m’mphepete mwa phiri ku Galileya n’chakuti: “Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo; chifukwa adzakhuta.” (Mateyu 5:6) Pankhani yochita zinthu mwachilungamo, Akristu amatengera chilungamo cha Yehova. Motero, anthu omva njala ndi ludzu la chilungamo, tinganene kuti amakhala ndi njala ndiponso ludzu la malangizo a Mulungu. Iwo amadziŵa kuti ndi ochimwa kwambiri ndiponso kuti ndi opanda ungwiro motero amayesetsa kuti akhale oyanjidwa ndi Yehova. Anthu otereŵa amasangalala kwambiri akaona m’Mawu a Mulungu kuti ngati atalapa ndi kupempha kukhululukidwa machimo pamaziko a nsembe ya dipo ya Kristu, angathe kuyanjidwa ndi Mulungu.​—Machitidwe 2:38; 10:43; 13:38, 39; Aroma 5:19.

11, 12. (a) Kodi Akristu odzozedwa amakhala motani olungama? (b) Kodi ludzu la chilungamo la anzawo a odzozedwa lidzathetsedwa motani?

11 Yesu anati anthu ameneŵa adzakhala achimwemwe, chifukwa chakuti “adzakhuta.” (Mateyu 5:6) Akristu odzozedwa amene anaitanidwa ‘kukachita ufumu’ ndi Kristu kumwamba amayesedwa a “chilungamo cha moyo.” (Aroma 5:1, 9, 16-18) Yehova amawatenga n’kukhala ana ake auzimu. Iwo amakhala oloŵa ufumu anzake a Kristu, oitanidwa kuti akakhale mafumu ndi ansembe m’boma lake la Ufumu la kumwamba.​—Yohane 3:3; 1 Petro 2:9.

12 Panopa, anzawo a odzozedwa sanayambe kuyesedwa olungama. Komabe Yehova amawaona kuti ndi olungama ndithu chifukwa choti iwo amakhulupirira mwazi wokhetsedwa wa Kristu. (Yakobo 2:22-25; Chivumbulutso 7:9, 10) Iwo amaonedwa kuti ndi olungama popeza kuti ndi mabwenzi a Yehova oyenerera kudzapulumutsidwa pa “chisautso chachikulu.” (Chivumbulutso 7:14) Ludzu lawo la chilungamo lidzathanso akamadzalamulidwa ndi miyamba yatsopano ndi kukhala mbali ya dziko lapansi latsopano limene ‘mudzakhalitsa chilungamo.’​—2 Petro 3:13; Salmo 37:29.

Achimwemwe ndi Achifundo

13, 14. Kodi tiyenera kuchita zotani posonyeza kuti ndife achifundo, ndipo kodi tingapindule motani?

13 Popitiriza ndi Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anati: “Odala ali akuchitira chifundo; chifukwa adzalandira chifundo.” (Mateyu 5:7) M’nkhani za malamulo, anthu amaona kuti woweruza milandu akachotserako chilango chimene munthu wolakwa amayenera kulandira ndiye kuti wachita chifundo. Koma, m’Baibulo, mawu a chinenero choyambirira amene anamasulidwa kuti “chifundo” kaŵirikaŵiri amanena za kuchita chinachake chosonyeza kukoma mtima kapena chisoni pothandiza anthu ovutika. Motero, anthu achifundo amachita zinthu zosonyeza kukoma mtima. Fanizo la Yesu la Msamariya wachifundo ndi chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu ‘wochitira chifundo’ munthu wovutika.​—Luka 10:29-37.

14 Kuti tipeze chimwemwe chomwe chimadza chifukwa chokhala wachifundo, tiyenera kuchita zinthu zosonyeza kukoma mtima pothandiza anthu ovutika. (Agalatiya 6:10) Yesu ankachitira chifundo anthu amene anali kuwaona. ‘Anagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.’ (Marko 6:34) Yesu ankadziŵa kuti chinthu chimene anthu amafunikira kwambiri ndicho zinthu zauzimu. Nafenso tingasonyeze kuti ndife okoma mtima ndi achifundo mwa kugaŵirako ena chosoŵa chawo chachikulu chomwe ndi ‘uthenga wabwino wa Ufumu.’ (Mateyu 24:14) Tingathenso kuthandiza Akristu anzathu okalamba, akazi ndiponso ana amasiye, ndi ‘kulimbikitsa amantha mtima,’ kapena kuti achisoni. (1 Atesalonika 5:14; Miyambo 12:25; Yakobo 1:27) Tikamatero timakhala achimwemwe komanso Yehova amatichitira chifundo.​—Machitidwe 20:35; Yakobo 2:13.

Kuyera Mtima Ndiponso Kukonda Mtendere

15. Kodi tingakhale motani oyera mtima ndiponso odzetsa mtendere?

15 Yesu anafotokoza motere chifukwa chachisanu ndi chimodzi ndiponso chachisanu ndi chiŵiri chokhalira achimwemwe: “Odala ali oyera mtima; chifukwa adzaona Mulungu. Odala ali akuchita mtendere; chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.” (Mateyu 5:8, 9) Mtima woyera ndi mtima umene uli wamakhalidwe abwino komanso wosadetsedwa mwauzimu ndiponso wodzipereka kwathunthu kwa Yehova. (1 Mbiri 28:9; Salmo 86:11) Anthu ochita kapena kuti odzetsa mtendere amakhala mwamtendere ndi abale awo achikristu ndiponso amayesetsa kukhala mwamtendere ndi anansi awo. (Aroma 12:17-21) ‘Amafunafuna mtendere ndi kuulondola.’​—1 Petro 3:11.

16, 17. (a) Kodi n’chifukwa chiyani odzozedwa amatchedwa “ana a Mulungu,” ndipo ‘amaona Mulungu’ motani? (b) Kodi a “nkhosa zina” ‘amaona Mulungu’ motani? (c) Kodi a “nkhosa zina” adzakhaladi “ana a Mulungu” motani ndipo ndi liti pamene zimenezi zidzachitike?

16 Anthu odzetsa mtendere amene ali oyera mtima, akulonjezedwa kuti “adzatchedwa ana a Mulungu” ndiponso “adzaona Mulungu.” Akristu odzozedwa ndi obadwa mumzimu ndipo amatengedwa kukhala “ana” a Yehova adakali padziko lapansi pom’pano. (Aroma 8:14-17) Akamaukitsidwa kuti akakhale ndi Kristu kumwamba, amakatumikira pamaso pa Yehova ndipo amamuonadi zenizeni.​—1 Yohane 3:1, 2; Chivumbulutso 4:9-11.

17 “Nkhosa zina” zomwe zimadzetsa mtendere zimatumikira Yehova motsogoleredwa ndi Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, ndipo iyeyu amakhala ‘Atate wawo Wosatha.’ (Yohane 10:14, 16; Yesaya 9:6) Anthu amene adzachite bwino pamayeso omaliza Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu ukadzatha, adzatengedwa kukhala ana a Yehova apadziko lapansi ndipo ‘adzaloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.’ (Aroma 8:21; Chivumbulutso 20:7, 9) Poyembekezera zimenezi, iwo amatcha Yehova Atate wawo, popeza amapatulira moyo wawo kwa iye, poona kuti iye ndiye anawapatsa moyo. (Yesaya 64:8) Mofanana ndi Yobu ndiponso Mose, iwo ‘amaona Mulungu’ ndi maso achikhulupiriro. (Yobu 42:5; Ahebri 11:27) Pogwiritsa ntchito ‘maso a mitima yawo’ ndiponso zinthu zolondola zokhudza Mulungu zimene akuzidziŵa, iwo amazindikira makhalidwe abwino a Yehova ndipo amayesetsa kumutsanzira mwa kuchita zofuna zake.​—Aefeso 1:18; Aroma 1:19, 20; 3 Yohane 11.

18. Malinga ndi zifukwa zisanu ndi ziŵiri zimene Yesu anafotokoza koyambirira zokhalira achimwemwe, kodi ndani amene amapeza chimwemwe chenicheni masiku ano?

18 Taona kuti anthu osauka mwauzimu, achisoni, ofatsa, anjala ndi ludzu la chilungamo, achifundo, oyera mtima, ndiponso odzetsa mtendere amapeza chimwemwe chenicheni potumikira Yehova. Komatu anthu ameneŵa nthaŵi zonse akhala akutsutsidwa, ngakhalenso kuzunzidwa kumene. Kodi zimenezi zimawalepheretsa kukhala achimwemwe? Nkhani yotsatirayi ikuyankha funso limeneli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 M’malo mwa mawu akuti “odala,” mabaibulo ena, monga The Jerusalem Bible ndi Today’s English Version, amati “achimwemwe.” Motero, m’nkhani ino ndi m’nkhani yotsatirayi tigwiritsa ntchito mawu akuti “achimwemwe,” pofotokozera malemba amene akutchula mawu akuti “odala.”

Kubwereza

• Kodi anthu osauka mwauzimu amapeza chimwemwe chotani?

• Kodi olira amasangalatsidwa m’njira zotani?

• Kodi timasonyeza motani kuti ndife ofatsa?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala achifundo, oyera mtima, ndiponso odzetsa mtendere?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

“Odala ali osauka mwauzimu”

[Zithunzi patsamba 10]

“Odala ali akuchitira chifundo”

[Chithunzi patsamba 10]

“Odala ali akumva njala ndi ludzu la chilungamo”