Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ozunzidwa Komabe Achimwemwe

Ozunzidwa Komabe Achimwemwe

Ozunzidwa Komabe Achimwemwe

“Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.”​—MATEYU 5:11.

1. Pankhani ya chimwemwe ndi kuzunzidwa, kodi Yesu anawatsimikizira zotani anthu omutsatira?

PA ULENDO woyamba umene Yesu anatuma atumwi ake kukalalikira za Ufumu, anawachenjeza kuti akakumana ndi anthu ena owatsutsa. Anawauza kuti: “Adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 10:5-18, 22) Komabe, m’mbuyo mwake, iye asanawachenjeze zimenezi, pa Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anatsimikizira atumwi ake limodzinso ndi anthu ena kuti kuwatsutsa kumeneku sikudzasokoneza kwenikweni chimwemwe chawo chochokera pansi pamtima. Ndipotu, Yesu anasonyeza kuti kukhala wachimwemwe kumayenderana ndi kuzunzidwa chifukwa chokhala Akristu. Kodi kuzunzidwa kukanawapatsa chimwemwe motani?

Kuzunzikira Chilungamo

2. Mogwirizana ndi zimene Yesu ndiponso mtumwi Petro ananena, kodi ndi kuvutika kotani kumene kumabweretsa chimwemwe?

2 Chifukwa chachisanu ndi chitatu chokhalira achimwemwe chimene Yesu anatchula n’chakuti: “Odala ali akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo: chifukwa uli wawo Ufumu wa Kumwamba.” (Mateyu 5:10) Kuvutikako pakokha sikosangalatsa. Mtumwi Petro analemba kuti: “[Pali] mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako zowawa mumapirira, kumeneko ndiko chisomo pa Mulungu.” Iye ananenanso kuti: “Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira; koma akamva zowawa ngati Mkristu asachite manyazi; koma alemekeze Mulungu m’dzina ili.” (1 Petro 2:20; 4:15, 16) Mogwirizana ndi mawu a Yesu, mavuto amabweretsa chimwemwe ngati munthu akuwapirira chifukwa chofuna kuchita chilungamo.

3. (a) Kodi kuzunzikira chilungamo kumatanthauzanji? (b) Kodi Akristu oyambirira anakhudzidwa motani ndi chizunzo?

3 Chilungamo chenicheni chimaonekera ngati munthu amachita zofuna za Mulungu ndiponso malamulo ake. Motero, kuvutikira chilungamo kukutanthauza kuvutika chifukwa chakuti munthu sakugonja akamakakamizidwa kuswa malamulo kapena zofuna za Mulungu. Atumwi anazunzidwa ndi atsogoleri achiyuda chifukwa chokana kusiya kulalikira m’dzina la Yesu. (Machitidwe 4:18-20; 5:27-29, 40) Kodi izi zinawalepheretsa kukhala achimwemwe kapena zinaimitsa ntchito yawo yolalikira? Ayi, sizinatero. “[Atumwiwo] anapita kuchokera ku bwalo la akulu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo. Ndipo masiku onse, m’Kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.” (Machitidwe 5:41, 42) Chizunzo ichi chinawapangitsa kukhala osangalala ndiponso chinawathandiza kulimbikira kwambiri pantchito yolalikira. Patapita nthaŵi, Akristu oyambirira anazunzidwa ndi Aroma chifukwa chokana kulambira mfumu.

4. Kodi zina mwa zifukwa zimene Akristu amazunzidwira ndi ziti?

4 Masiku ano, Mboni za Yehova zakhala zikuzunzidwa chifukwa chokana kusiya kulalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 24:14) Misonkhano yawo yachikristu ikaletsedwa, Mboni zimalolera kuvutika potsatira lamulo la m’Baibulo m’malo mosiya kusonkhana. (Ahebri 10:24, 25) Poti iwo ndi Akristu, akhala akuzunzidwa chifukwa chosaloŵerera m’zochitika za dzikoli, ndipo nthaŵi zinanso chifukwa chokana kugwiritsa ntchito magazi molakwika. (Yohane 17:14; Machitidwe 15:28, 29) Komabe, chilungamo chimene amachitachi chimawapangitsa anthu a Mulunguŵa kukhala ndi mtendere ndiponso chimwemwe chochokeradi pansi pamtima.​—1 Petro 3:14.

Kunyazitsidwa Chifukwa cha Kristu

5. Kodi chifukwa chachikulu chimene anthu a Yehova amazunzidwira masiku ano n’chiti?

5 Chifukwa chachisanu ndi chinayi chokhalira achimwemwe chimene Yesu anafotoza pa Ulaliki wake wa pa Phiri chimakhudzanso nkhani ya chizunzo. Iye anati: “Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.” (Mateyu 5:11) Chifukwa chachikulu chimene anthu a Yehova amazunzidwira n’chakuti iwo sali mbali ya dongosolo loipa la zinthu la masiku anoli. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake za lokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma Ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.” (Yohane 15:19) Mogwirizana ndi mfundoyi, mtumwi Petro anati: “Mmenemo ayesa n’chachilendo kuti simuthamanga nawo kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, nakuchitirani mwano.”​—1 Petro 4:4.

6. (a) Kodi n’chifukwa chiyani otsalira ndiponso anzawo amanyazitsidwa ndiponso kuzunzidwa? (b) Kodi kunyazitsidwa kumeneku kumatichepetsera chimwemwe chathu?

6 Taona kale kuti Akristu oyambirira anazunzidwa chifukwa chokana kusiya kulalikira m’dzina la Yesu. Yesu anauza anthu omutsatira kuti: “Mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Otsalira okhulupirika a abale odzozedwa a Kristu, mothandizidwa ndi anzawo okhulupirika a “khamu lalikulu,” akhala akugwira ntchitoyi mwakhama kwambiri. (Chivumbulutso 7:9) Motero Satana akumenya nkhondo “ndi otsala a mbewu yake [mbewu ya “mkazi,” yemwe ndi mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu], amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.” (Chivumbulutso 12:9, 17) Popeza ndife Mboni za Yehova, timachitira umboni za Yesu, yemwe tsopano ndi Mfumu yolamulira ya boma la Ufumu, limene lidzawononge maboma a anthu amene ayenera kuchotsedwa kuti pabwere dziko lapansi latsopano lachilungamo la Mulungu. (Danieli 2:44; 2 Petro 3:13) Timanyazitsidwa ndi kuzunzidwa chifukwa cha zimenezi, komabe timasangalala chifukwa chovutikira Kristu.​—1 Petro 4:14.

7, 8. Kodi anthu otsutsa anali kuwanamizira zotani Akristu oyambirira?

7 Yesu anati anthu omutsatira ayenera kukhala achimwemwe ngakhale pamene anthu ‘awanenera monama zoipa zilizonse’ chifukwa cha iye. (Mateyu 5:11) Izi n’zimene zinawachitikiradi Akristu oyambirira. Mtumwi Paulo ali m’ndende ku Roma, cha m’ma 59 mpaka 61 Kristu Atabwera, atsogoleri achiyuda kumeneko ananena zinthu zotsatirazi zokhudza Akristu: “Mpatuko uwu, tidziŵa kuti aunenera ponseponse.” (Machitidwe 28:22) Paulo ndi Sila anaimbidwa mlandu ‘wosanduliza dziko lokhalamo anthu,’ ndipo zimenezi zinali ‘zokana malamulo a Kaisara.’​—Machitidwe 17:6, 7.

8 Pofotokoza zimene zinali kuchitikira Akristu panthaŵi ya ulamuliro wa Aroma, katswiri wa mbiri yakale K. S. Latourette, analemba kuti: “Ankawanamizira zinthu zosiyanasiyana. Akristu ankanenedwa kuti sakhulupirira kuti kuli Mulungu chifukwa choti ankakana kuchita nawo miyambo yachikunja. Chifukwa choti sankachita nawo zinthu zina za kumadera amene anali kukhala, monga kupezeka pa mapwando achikunja ndiponso zisangalalo . . . , anthu ankati Akristuwo amadana ndi anthu. . . . Ankati amuna ndi akazi amakumana pamodzi usiku . . . n’kumachita zachiwerewere. . . . Popeza opezeka pa [Chikumbutso cha Imfa ya Kristu] ankakhala anthu okhawo okhulupirira, panayambika mphekesera zakuti Akristu nthaŵi zonse ankapereka khanda monga nsembe n’kudya magazi ndi thupi lake.” Kuwonjezera pamenepo, chifukwa chakuti Akristu oyambirira ankakana kulambira mfumu, anali kunenedwa kuti ndi adani a boma.

9. Kodi Akristu a m’zaka za 100 zoyambirira anachitanji ndi mabodza amene anthu ankawanenera, ndipo zinthu zili bwanji masiku ano?

9 Mabodza ameneŵa sanalepheretse Akristu oyambirira kugwira ntchito yomwe analamulidwa, yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. M’chaka cha 60 mpaka 61 Kristu Atabwera, Paulo anafika ponena za “uthenga wabwino” kuti “m’dziko lonse lapansi umabala zipatso, numakula,” ndiponso kuti unali ‘utalalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ (Akolose 1:5, 6, 23) Umu ndi mmenenso zikuchitikira masiku ano. Mboni za Yehova amazinamizira, monganso momwe ankawanamizira Akristu a m’zaka za 100 zoyambirira. Komabe, masiku ano ntchito yolalikira uthenga wa Ufumu ikuyenda bwino ndipo imawapatsa chimwemwe chachikulu anthu amene akuigwira.

Achimwemwe Pozunzidwa Monganso Mmene Anazunzidwira Aneneri

10, 11. (a) Kodi Yesu anamaliza motani kufotokoza chifukwa chachisanu ndi chinayi chokhalira achimwemwe? (b) Kodi n’chifukwa chiyani aneneri anazunzidwa? Perekani zitsanzo.

10 Yesu anamaliza motere kufotokoza chifukwa chachisanu ndi chinayi chokhalira achimwemwe: “Sekerani, . . . pakuti potero anazunza aneneri anakhalawo musanabadwe inu.” (Mateyu 5:12) Aneneri amene Yehova anawatuma kukachenjeza Aisrayeli osakhulupirika sanalandiridwe bwino ndipo nthaŵi zambiri anali kuzunzidwa. (Yeremiya 7:25, 26) Mtumwi Paulo anachitira umboni mfundo imeneyi, pamene analemba kuti: “Ndinene chiyaninso? pakuti idzandiperewera nthaŵi ndifotokozere za . . . aneneri; amene mwa chikhulupiriro . . . anayesedwa ndi matonzo ndi zokwapulira, ndiponso nsinga, ndi kuwatsekera m’ndende.”​—Ahebri 11:32-38.

11 Mu ulamuliro wa Mfumu Ahabu ndi mkazi wake Yezebeli, omwe anali anthu oipa, aneneri ambiri a Yehova anali kuphedwa ndi lupanga. (1 Mafumu 18:4, 13; 19:10) Mneneri Yeremiya anaikidwa m’matangadza ndipo kenako anaponyedwa m’dzenje lathope. (Yeremiya 20:1, 2; 38:6) Mneneri Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango. (Danieli 6:16, 17) Aneneri onseŵa amene anakhalako Chikristu chisanayambe anazunzidwa chifukwa choti ankalimbikitsa kulambira Yehova moona. Aneneri ambiri anazunzidwa ndi atsogoleri a chipembedzo achiyuda. Yesu anatcha alembi ndi Afarisi kuti “ana a iwo amene anapha aneneri.”​—Mateyu 23:31.

12. Kodi n’chifukwa chiyani ifeyo Mboni za Yehova timaona kuti ndi mwayi kuzunzidwa monganso mmene anazunzidwira aneneri akale?

12 Masiku ano, ifeyo Mboni za Yehova timazunzidwa kaŵirikaŵiri chifukwa choti timalimbikira ntchito yathu yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Adani athu amatinena kuti “timatembenuza anthu mowaumiriza,” koma timadziŵa kuti nawonso olambira okhulupirika a Yehova amene anakhalako m’mbuyomo ananamiziridwanso chimodzimodzi. (Yeremiya 11:21; 20:8, 11) Timaona kuti ndi mwayi waukulu kuvutika pa chifukwa chimodzimodzicho chimene aneneri okhulupirika akale anavutikira. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, [cha] aneneri amene analankhula m’dzina la Ambuye. Taonani tiwayesera odala opirirawo.”​—Yakobo 5:10, 11.

Zifukwa Zogwira Mtima Zokhalira Achimwemwe

13. (a) N’chifukwa chiyani sititaya mtima tikakumana ndi chizunzo? (b) Kodi n’chiyani chimatithandiza kukhala olimba, ndipo zimenezi zimapereka umboni wa chiyani?

13 M’malo mokhumudwa chifukwa chozunzidwa, timalimbikitsidwa poona kuti tikutsatira mapazi a aneneri, Akristu oyambirira, ndiponso Kristu Yesu mwiniyo. (1 Petro 2:21) Timasangalala kwambiri ndi Malemba, monga mawu otsatiraŵa a mtumwi Petro, akuti: “Okondedwa, musazizwe ndi mayesedwe amoto adakugwerani inu akhale chakukuyesani, ngati chinthu chachilendo chachitika nanu: Mukatonzedwa pa dzina la Kristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.” (1 Petro 4:12, 14) Malingana ndi zimene takhala tikukumana nazo m’moyo wathu tikudziŵa kuti chimene chimatilimbitsa panthaŵi ya chizunzo makamaka ndi mzimu wa Yehova. Thandizo limene timalandira la mzimu woyera ndi umboni wakuti Yehova akutidalitsa, ndipo izi zimatipatsa chimwemwe chachikulu.​—Salmo 5:12; Afilipi 1:27-29.

14. Kodi tili ndi zifukwa zotani zokhalira achimwemwe tikamazunzidwa chifukwa cha chilungamo?

14 Chifukwa china chimene timakhalira achimwemwe potsutsidwa ndiponso kuzunzidwa chifukwa cha chilungamo n’chakuti zimatsimikizira kuti tikukhaladi moyo wa Akristu oona omwe uli moyo opembedza kapena kuti odzipereka kwa Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.” (2 Timoteo 3:12) Timakhala achimwemwe kwambiri tikamaganizira kuti tikakhalabe okhulupirika pachiyeso timathandiza nawo kutsutsa Satana pamfundo yakuti anthu ndi angelo amatumikira Yehova chifukwa cha dyera. (Yobu 1:9-11; 2:3, 4) Ngakhale patakhala pang’ono pokha, timasangalala kuti tikuthandizira nawo kutsimikizira kuti ulamuliro wolungama wa Yehova ndiwo woyenera.​—Miyambo 27:11.

Sangalalani Chifukwa cha Mphoto

15, 16. (a) Kodi Yesu anapereka chifukwa chotani choti ‘tisekere ndi kusangalala’? (b) Kodi Akristu odzozedwa awasungira mphoto yotani m’Mwamba, nanga anzawo a “nkhosa zina” nawonso adzapatsidwa mphoto yotani?

15 Yesu anapereka chifukwa chinanso chokhalira osangalala tikamanamiziridwa ndi kuzunzidwa monga mmene anachitira aneneri akale. Chakumapeto kwa chifukwa chachinayi chokhalira achimwemwe, iye anati: “Sekerani, sangalalani: chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu m’Mwamba.” (Mateyu 5:12) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mphoto yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Inde, ‘mphoto yaikulu’ imene anatchulayi ndi moyo, ndipotu moyo umenewu sikuti uli ngati malipiro ogwirizana ndi ntchito imene tagwira. Imeneyi ndi mphatso yaulere. Chifukwa chakuti ndi yochokera kwa Yehova, Yesu ananena kuti mphotoyi ili “m’Mwamba.”

16 Odzozedwa amalandira “korona wa moyo,” kutanthauza kukakhala ndi moyo wosafa ali limodzi ndi Kristu kumwamba. (Yakobo 1:12, 17) Anthu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi pano, a “nkhosa zina,” akuyembekezera kudzalandira moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. (Yohane 10:16; Chivumbulutso 21:3-5) Kwa magulu onseŵa, “mphoto” yawoyi sikuti ili ngati malipiro amene munthu amalandira mogwirizana ndi ntchito imene wagwira. Onse, odzozedwa ndiponso a “nkhosa zina” amalandira mphoto yawo chifukwa cha “chisomo choposa” cha Yehova, zimene zinachititsa mtumwi Paulo kunena kuti: “Ayamikike Mulungu chifukwa cha mphatso yakeyake yosatheka kuneneka.”​—2 Akorinto 9:14, 15.

17. N’chifukwa chiyani tingakhale achimwemwe pamene tikuzunzidwa ndiponso kukhala osangalala kwambiri?

17 Kwa Akristu, omwe ena mwa iwo anali atatsala pang’ono kuzunzidwa mwankhanza ndi Mfumu Nero, mtumwi Paulo analemba kuti: “Tikondwera m’zisautso; podziŵa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizoloŵezi; ndi chizoloŵezi chichita chiyembekezo: ndipo chiyembekezo sichichititsa manyazi.” Iye ananenanso kuti: “Kondwerani m’chiyembekezo, pirirani m’masautso.” (Aroma 5:3-5; 12:12) Kaya tikuyembekezera kukakhala kumwamba kapena kudzakhala padziko lapansi pano, mphoto imene tidzalandire chifukwa chokhala okhulupirika panthaŵi ya mayesero ndi yaikulu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse chomwe tiyenera kukhala nacho. Timasangalala kwambiri tikamaganizira zoti tidzakhala kwamuyaya n’kumatumikira ndiponso kutamanda Atate wathu wakumwamba, Yehova, tikulamulidwa ndi Mfumu Yesu Kristu.

18. Kodi tingayembekezere kuti amitundu achita zotani pamene mapeto akuyandikira, nanga Yehova adzachita zotani?

18 M’mayiko ena, Mboni za Yehova zakhala zikuzunzidwa m’mbuyomu ndipo zikuzunzidwabe mpaka pano. Mu ulosi wake wonena za mapeto a dongosolo lino la zinthu, Yesu anachenjeza Akristu oona kuti: ‘Anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.’ (Mateyu 24:9) Pamene tikuyandikira mapeto, Satana adzachititsa mitundu kusonyezadi mmene imadera anthu a Yehova. (Ezekieli 38:10-12, 14-16) Ichi chidzakhala chizindikiro chakuti Yehova achitepo kanthu. “Ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziŵika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziŵa kuti Ine ndine Yehova.” (Ezekieli 38:23) Pochita izi, Yehova adzayeretsa dzina lake lalikulu ndi kupulumutsa anthu ake ku chizunzo. Motero, “wodala munthu wakupirira poyesedwa.”​—Yakobo 1:12.

19. Kodi tiyenera kuchita chiyani pamene tikuyembekezera ‘tsiku lalikulu la Ambuye’?

19 ‘Tsiku lalikulu la Ambuye’ likumka liyandikira, motero tiyeni tisangalale chifukwa chakuti ‘timayesedwa oyenera kunyozedwa’ chifukwa cha dzina la Yesu. (2 Petro 3:10-13; Machitidwe 5:41) Mofanana ndi Akristu oyambirira, tiyeni ‘tisaleke kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu’ ndi boma lake la Ufumu pamene tikuyembekezera mphoto yathu m’dziko latsopano lolungama la Yehova.​—Machitidwe 5:42; Yakobo 5:11.

Kubwereza

• Kodi kuvutikira chilungamo kumatanthauzanji?

• Kodi Akristu oyambirira anakhudzidwa motani ndi chizunzo?

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mboni za Yehova zikuzunzidwa mofanana ndi mmene anazunzidwira aneneri akale?

• N’chifukwa chiyani ‘timasekerera ndi kusangalala’ pamene tikuzunzidwa?

[Mafunso]

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

“Odala muli inu mmene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu”

[Mawu a Chithunzi]

Group in prison: Chicago Herald-American