Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tinasankha Ulamuliro wa Mulungu Mosasunthika

Tinasankha Ulamuliro wa Mulungu Mosasunthika

Nkhani ya Moyo Wake

Tinasankha Ulamuliro wa Mulungu Mosasunthika

YOSIMBIDWA NDI MICHAL ŽOBRÁK

Atanditsekera m’ndende yandekha kwa mwezi wathunthu, ananditengera kwa munthu woti akandifunse mafunso pofufuza mlandu wanga. Nditalankhula naye kwa nthaŵi yochepa chabe anandilusira n’kunena mokalipa kuti: “Akazitape inu! Akazitape a dziko la America!” Kodi anapsa mtima n’chiyani? Anali atangondifunsa kumene za chipembedzo changa, ndipo ndinamuyankha kuti: “Ndine wa Mboni za Yehova.”

IZI zinachitika zaka zoposa 50 zapitazo. Panthaŵiyo, dziko limene ndinkakhalamo linali muulamuliro wa Chikomyunizimu. Komabe, kale kwambiri zimenezi zisanachitike, ntchito yathu yachikristu yophunzitsa anthu inkatsutsidwa kwambiri.

Tinamva Kupweteka kwa Nkhondo

Mmene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inkayamba mu 1914, ineyo n’kuti ndili ndi zaka eyiti. Panthaŵiyo, mudzi wathu wa Zálužice, unkalamulidwa ndi Ufumu wa dziko la Austria ndi Hungary. Nkhondoyi inasokoneza zinthu padziko lonse ndipo inachititsanso kuti ineyo ndizigwira ntchito zosayenerana ndi msinkhu wanga. Bambo anga, amene anali msilikali, anafa m’chaka choyamba cha nkhondoyi. Motero ineyo pamodzi ndi mayi anga komanso azilongo anga aang’ono aŵiri, tinakhala paumphaŵi wadzaoneni. Pakuti ndinali mwana wamwamuna woyamba pakhomopo, maudindo ambiri a pafamu yathu yomwe inali yaing’ono ndiponso a pakhomo anali pamutu panga. Ndinali munthu wokonda za Mulungu kungoyambira ndili wamng’ono. Moti mbusa wa tchalitchi chathu cha Reformed (Calvinist) ankandipempha kuti ndim’thandize kuphunzitsa anzanga a kusukulu, iye akachokapo.

Mu 1918 nkhondo yoyamba ya padziko lonse inatha, ndipo mitima yathu inakhala pansi. Ufumu wa Austria ndi Hungary unagonjetsedwa, ndipo tinakhala nzika za dziko la Czechoslovakia. Posakhalitsa anthu akwathu, amene anasamukira ku United States, anayamba kubwerera. M’modzi wa anthu ameneŵa anali Michal Petrík, amene anafika m’mudzi wathu mu 1922. Iye atabwera kudzachezera banja linalake la kufupi ndi kwathu, ineyo ndi mayi anga tinaitanidwa kukachezanso naye.

Tinayamba Kuona Kuti Ulamuliro wa Mulungu ndi Weniweni

Michal anali m’gulu la Ophunzira Baibulo, lomwe linali dzina la Mboni za Yehova panthaŵiyo, ndipo anafotokoza nkhani zofunika za m’Baibulo zimene ndinachita nazo chidwi kwambiri. Nkhani imene inandichititsa chidwi koposa inali ya kubwera kwa Ufumu wa Yehova. (Danieli 2:44) Anatiuza kuti Lamlungu kukakhala msonkhano wachikristu ku mudzi wa Záhor ndipo ineyo ndinali wofunitsitsa kwambiri kupitako. Ndinadzuka folo koloko m’maŵa n’kuyenda mtunda wa makilomita eyiti kuti ndikabwereke njinga kwa msuweni wanga. Ndinayamba ndamata kaye chubu chanjingayo ndipo kenako ndinayamba ulendo wa makilomita 24 wopita ku Záhor. Sindinkadziŵa kumene kukachitikire msonkhanowo, motero ndinayamba kuyenda pang’onopang’ono mukamsewu kenakake ka kumeneko. Kenako ndinamva kuimba m’nyumba ina ndipo ndinadziŵa kuti inali nyimbo yaufumu. Ndinasangalala kwambiri. Ndinaloŵa m’nyumbamo n’kulongosola chimene ndinabwerera. Eni khomolo anandiitanira chakudya chawo cham’maŵa kenaka anapita nane limodzi kumsonkhano. Ngakhale kuti pobwerera kwathu ndinayenda ulendo wa makilomita 32 pa njinga ndiponso pansi, sindinamve kutopa kulikonse ayi.​—Yesaya 40:31.

Ndinachita chidwi kwambiri kumva mmene Mboni za Yehova zimalongosolera zinthu momveka bwino ndiponso mogwirizana ndi Baibulo. Ndinakhudzidwa mtima kwambiri kudziŵa kuti n’zotheka kudzakhala ndi moyo wosangalatsa muulamuliro wa Mulungu. (Salmo 104:28) Ine ndi mayi anga tinaganiza zolembera kalata tchalitchi chathu, kufotokoza kuti tasiya tchalitchicho. Nkhani imeneyi inavuta kwambiri m’mudzi mwathu. Moti panali anthu ena amene anasiya kulankhula nafe kwa kanthaŵi ndithu, komabe tinkacheza ndi Mboni za Yehova zambiri za m’dera lathu. (Mateyu 5:11, 12) Posakhalitsa ndinabatizidwa mumtsinje wa Uh.

Kulalikira Kunangosanduka Moyo Wathu

Tinkayesetsa kulalikira za Ufumu wa Yehova tikapeza mwayi wina uliwonse. (Mateyu 24:14) Tinkakonda makamaka kulalikira m’magulu olinganizidwa bwino pa Lamlungu. Masiku amenewo anthu ankalaŵirira kudzuka, motero tinkayamba m’maŵa kwambiri kulalikira. Masana, tinkakhala ndi msonkhano wa anthu onse. Nthaŵi zambiri abale amene ankaphunzitsa za m’Baibulo ankakamba nkhani zawo mosaonera pa pepala. Ankaganizira makamaka za kuchuluka kwa anthu achidwi amene asonkhana, zipembedzo zawo, ndiponso nkhani zimene zinali kuwasoŵetsa mtendere.

Choonadi cha m’Baibulo chimene tinkalalikira chinatsegula maso a anthu ambiri oona mtima. Patangotha nthaŵi yochepa chabe nditabatizidwa, ndinayamba kulalikira m’mudzi wa Trhovište. Panyumba ina, ndinalankhula ndi mayi enaake amtima wabwino kwambiri ndiponso ansangala. Dzina lawo linali a Zuzana Moskal. Mayiŵa ndi banja lawo anali achipembedzo cha Calvinist, monga mmene inenso ndinalili. Ngakhale kuti Baibulo silinali buku lachilendo kwa mayiŵa, iwo anali ndi mafunso ambiri okhudza Baibulo. Tinakambirana kwa ola lathunthu ndipo ndinawapatsa buku lakuti Zeze wa Mulungu. *

Banja la a Moskal linayamba nthaŵi yomweyo kuŵerenga buku la Zeze poŵerenga Baibulo monga linkachitira nthaŵi zonse. Mabanja ambiri m’mudziwo anachita chidwi ndi uthenga wathu n’kuyamba kusonkhana nafe. Mbusa wa tchalitchi chawo cha Calvinist anachenjeza anthuwo kuti asamale nafe ndiponso ndi mabuku athu. Kenaka ena mwa anthu achidwiwo anauza mbusayo kuti adzabwere kumsonkhano wathu kuti adzatsutsane nafe poyera pa nkhani ya ziphunzitso zathu.

Mbusayo anabweradi, koma analephera kutchula ngakhale mfundo imodzi yochokera m’Baibulo yotsimikizirira ziphunzitso zake. Mfundo yake inali yongoti: “Sitingakhulupirire zonse zimene zili m’Baibulo. Linalembedwa ndi anthu, komanso dziŵani kuti mafunso okhudza nkhani zachipembedzo angayankhidwe mosiyanasiyana.” Pamenepa m’pamene anthu ambiri anasinthira. Ena anamuuza kuti ngati iye sakhulupirira Baibulo, iwo sadzapitanso kukamvetsera ulaliki wake. Motero anthuwo anachoka m’tchalitchi cha Calvinist, ndipo anthu pafupifupi 30 ochokera m’mudziwu anagwira choonadi cha Baibulo ndi mtima wawo wonse.

Kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu kunangosanduka moyo wathu, motero ineyo ndinkafuna mkazi wochokera m’banja lolimba mwauzimu. Mnzanga wina amene ndinkachita naye ntchito ya utumiki anali Ján Petruška, ndipo iyeyu anaphunzira choonadi ali ku United States. Mwana wake wamkazi Mária anandigometsa kwambiri chifukwa cha changu chake polalikira kwa munthu wina aliyense, monga mmenenso ankachitira bambo akeŵa. Tinakwatirana mu 1936, ndipo Mária anakhala nane mokhulupirika kwa zaka 50, mpaka pamene anamwalira mu 1986. Mu 1938 mwana wathu Eduard, anabadwa ndipo uyu ndi mwana yekhayu amene tinakhala naye. Koma panthaŵiyo, ku Ulaya kunkaoneka kuti kuyambika nkhondo ina. Kodi nkhondo imeneyi inadzakhudza bwanji ntchito yathu?

Tinayesedwa Chifukwa Chosaloŵerera Nkhondo Poti Ndife Akristu

Pamene nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse inkayamba, dziko la Slovakia, lomwe linasanduka dziko palokha, linali muulamuliro wa boma la chipani cha Nazi. Koma palibe chilichonse chimene aboma anachita choletsa ntchito ya Mboni za Yehova monga gulu. Inde, tinayenera kuchita ntchito yathu mwachinsinsi, ndipo aboma ankaunika mabuku athu kuti aone zinthu zimene zalembedwamo. Komabe, ife tinapitiriza kuchita ntchito yathu mosamala.​—Mateyu 10:16.

Nkhondo itakula, ndinalamulidwa kuti ndikalembetse usilikali, ngakhale kuti zaka zanga zinali zitapitirira 35. Ndinakana kuchita nawo nkhondoyo chifukwa sindikanaloŵerera nkhani zotere pakuti ndine Mkristu. (Yesaya 2:2-4) Mwayi wake, aboma asanaganize zochita nane, anamasula anthu tonse a msinkhu wanga.

Tinaona kuti abale athu a m’tauni zinkawavuta kwambiri kupeza zofunika pa moyo wawo kusiyana ndi akumidzife. Tinkafuna kuti tiziwagaŵira zinthu zathu. (2 Akorinto 8:14) Motero, tinkatenga zakudya zambiri monga mmene tikanakwanitsira kunyamula n’kupita nazo ku Bratislava, womwe unali ulendo wa makilomita oposa 500. Chikondi ndiponso ubwenzi wachikristu umene tinakhala nawo panthaŵi yankhondoyi zinatithandiza m’mavuto amene tinadzakumana nawo m’zaka zotsatira.

Kupeza Chilimbikitso Chomwe Tinkafunikira

Nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse itatha, dziko la Slovakia linakhalanso mbali ya dziko la Czechoslovakia. Kuchokera mu 1946 mpaka mu 1948, misonkhano ya Mboni za Yehova yokhudza dziko lathu lonselo inkachitikira ku Brno kapena ku Prague. Ifeyo ochokera ku dera la kum’maŵa kwa Slovakia tinkayenda pa sitima zapadera zongonyamula nthumwi za kumsonkhano. Mungati izi zinali sitima zanyimbo, chifukwa chakuti tinkaimba nyimbo ulendo wonsewo.​—Machitidwe 16:25.

Sindiiwala msonkhano wa mu 1947 wa ku Brno, umene panabwera oyang’anira atatu achikristu ochokera ku likulu lathu la padziko lonse, kuphatikizapo Mbale Nathan H. Knorr. Pofuna kulengeza za nkhani ya anthu onse, ambirife tinkayenda mumzindawu titanyamula zikwangwani zotchula mutu wa nkhaniyo. Mwana wathu Eduard, amene panthaŵiyi anali ndi zaka naini zokha, anadandaula kwambiri chifukwa chakuti analibe chikwangwani chake. Motero abale anapanga zikwangwani zing’onozing’ono zakuti iyeyo komanso ana ena ambiri azinyamula. Kagulu ka ana kameneka kanathandiza kwambiri pantchito yolengeza za nkhaniyi.

Mu February, 1948 boma la Chikomyunizimu linakhazikitsidwa. Tinadziŵa kuti posakhalitsa bomali liletsa utumiki wathu. M’mwezi wa September 1948, tinachita msonkhano ku Prague ndipo tinali osangalala komanso ankhaŵa poganizira zakuti n’kutheka kuti misonkhano yathu yapoyera iletsedwanso, patangotha zaka zitatu chabe zaufulu wosonkhana. Pamsonkhanopo, tinavomereza chosankha chimene mbali yake ina inali yakuti: “Ifeyo, Mboni za Yehova, amene tasonkhana pano . . . tatsimikiza mtima kupitirizabe kuchita utumiki wosangalatsa umenewu, ndipo mwachisomo cha Ambuye, tatsimikiza kupitirizabe kuchita utumikiwu panthaŵi zabwino ndi zamayesero zomwe, ndiponso kufalitsa mwakhama kwambiri uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.”

“Adani a Boma”

Patangotha miyezi iŵiri yokha msonkhano wa ku Prague uja utachitika, apolisi ogwira ntchito yawo mwachinsinsi anapita ku nyumba ya Beteli kufupi ndi ku Prague. Analanda nyumbayo, mabuku onse amene anawapeza, n’kumanga atumiki onse a pa Beteli pamodzinso ndi abale ena. Koma zovutazi sizinathere pomwepa ayi.

Tsiku lina usiku, pa February 3, 1952, asilikali a zachitetezo anayenda m’dziko lathu lonselo n’kumanga Mboni zopitirira 100. Ineyo ndinali m’gulumo. Cha m’ma fili koloko m’maŵa, apolisi anabwera n’kudzadzutsa banja langa lonse. Anangondiuza kuti akunditenga, koma sanandiuze chifukwa chake. Anandimanga unyolo n’kundimanganso m’maso ndipo anandiponya kumbuyo kwa galimoto pamodzinso ndi abale ena angapo. Mapeto ake ananditsekera m’ndende yandekha.

Ndinatha mwezi wathunthu popanda kulankhula ndi wina aliyense. Munthu yekhayo amene ndinkaonana naye anali msilikali wondilondera amene ankandipatsa chakudya chochepa chabe kudzera pa malo oboola a pachitseko. Kenaka anandiuza kuti ndikaonane ndi munthu amene ankandifunsa mafunso amene ndatchula kumayambiriro kwa nkhaniyi. Munthuyo anandinena kuti ndine kazitape ndipo kenaka anapitiriza kunena kuti: “Kupembedza ndi umbuli weniweni. Mulungu kulibe! Sitingalole kuti uzipusitsa anthu m’dziko muno. Ukanyongedwa apo ayi uwolera m’ndende. Ndipo Mulungu wakoyo akangoyerekeza kubwera kunoko, nayenso tim’nyonga!”

Popeza kuti abomawo ankadziŵa kuti panalibe lamulo lenileni loletsa ntchito yathu yachikristu, ankafuna kuti ntchito yathu aipezere mlandu wogwirizana ndi malamulo a panthaŵiyo, motero anati ndife “adani a boma” ndiponso kuti ndife akazitape a mayiko akunja. Kuti atero ankafuna kuti atilefule kaye maganizo kuti tingovomereza mlandu wongotisemerawu. Atandifunsa mondiopseza chonchi usikuwo, sanandilole kuti ndigone. Patangotha maola ochepa chabe, anayambanso kundifunsa chimodzimodzi. Panthaŵiyi wondifunsayo ankafuna kuti ndisaine chikalata chonena mawu akuti: “Ineyo ndine mdani wa dziko la Czechoslovakia ndipo ndinakana kugwira nawo ntchito yolima minda ya boma chifukwa chakuti ndimatumikira dziko la America.” Nditakana kusaina zabodzazi, anandipititsa m’selo yolangira anthu.

Anandiletsa kugona tulo, kukhala chogona, ngakhalenso kukhala pansi kumene. Anandiuza kuti ndizingokhala choimirira kapena ndizingoyendayenda basi. Nditatheratu n’kutopa, ndinagona pasimenti. Kenaka asilikali ondilonderawo ananditenga n’kundipititsanso ku ofesi ya wofunsa mafunso uja. Ndiye anandifunsa kuti: “Tsopano usayina eti?” Nditakananso anandimenya kunkhope, ine n’kuyamba kutuluka magazi. Moipidwa, anauza asilikali ondilondera aja kuti: “Chikufuna kudzipha chimenechi. Muzichiyang’anira kuti chilephere kudziphako.” Kenaka ananditsekeranso m’kachipinda kokhalamo ndekha kaja. Anandichita zimenezi kambirimbiri kwa miyezi isanu ndi umodzi. Ndinakhalabe wokhulupirika kwa Yehova ngakhale kuti anayesa umu ndi umu kuti andisokoneze maganizo kapena kundichititsa kuti ndivomere bodza lakuti ndine mdani wa dzikolo.

Patatsala mwezi umodzi kuti ndikazengedwe mlandu, kunabwera munthu wodzazenga mlandu wathuwo wochokera ku Prague ndipo abale tonse 12 anatifunsa mafunso patokhapatokha. Ineyo anandifunsa kuti: “Kodi ungatani ngati mayiko olimbana ndi dziko lathuli ataloŵa m’dziko mwathu muno mwankhondo?” Ndiye ndinayankha kuti: “Ndingachite zomwezo zimene ndinachita pamene dziko lino pamodzi ndi Hitler linachita nkhondo ndi USSR. Panthaŵiyo, sindinamenye nawo nkhondo, ndipo ndingachitenso chimodzimodzi panopa chifukwa chakuti ndine Mkristu motero sindiloŵerera nawo nkhondo.” Nditamuuza zimenezi iye anati: “M’dziko lino Mboni za Yehova sitizifuna ayi. Tikufunikira asilikali oteteza dzikoli ngati mayiko olimbana nafe ataloŵamo ndi nkhondo, ndipo tikufunikira asilikali oti akamasule anthu athu amene ali m’mayiko olimbana nafe.”

Pa July 24 1953, anatiloŵetsa m’khoti kuti tiŵeruzidwe. Tinalipo anthu 12 ndipo ankatiitana mmodzimmodzi, kukaonana ndi gulu la oŵeruza. Pamenepa, tinatengerapo mwayi wowauza za chikhulupiriro chathu. Tinatsutsa mabodza onse amene anatinamizira ndipo loya wina wa m’khotilo anaimirira n’kunena kuti: “Ineyo m’khoti lino ndabweramo kambirimbiri. Anthu ambiri oimbidwa mlandu muno, amaulula, kulapa, ngakhale kuyamba kulira kumene. Koma anthu awawa akamatuluka muno amakhala thima lili zii kusiyana ndi mmene analili poloŵa.” Pambuyo pake, anthu 12 tonsefe anatipeza ndi mlandu wokonza chiwembu choukira boma. Ine anandiŵeruza kuti ndikhale m’ndende zaka zitatu komanso kuti boma litenge katundu wanga yense.

Ukalamba Sunandibwezere M’mbuyo

Nditabwerera kunyumba, apolisi ogwira ntchito yawo mwachinsinsi ankandiwendawenda kuti aziona zimene ndikuchita. Koma ndinapitirizabe ntchito zauzimu ndipo ndinapatsidwa udindo woyang’anira mpingo wathu. Ngakhale kuti anatilola kumakhala m’nyumba imene anatilanda ija, sanatibwezere nyumbayi mwalamulo kuti ikhale yathuyathu mpaka panthaŵi imene Chikomyunizimu chinatha ndipo apa n’kuti patatha zaka 40.

Siine munthu womaliza kumangidwa m’banja lathu. Nditangotha zaka zitatu ndili panyumba, Eduard anamuitana kuti akalembetse usilikali. Chifukwa cha chikumbumtima chake chogwirizana ndi zimene anaphunzira m’Baibulo anakana ndipo anam’manga. Patatha zaka zambiri, ngakhale mdzukulu wanga, dzina lake Peter, anamangidwaponso, ngakhale kuti anali sanali ndi thanzi labwino.

Mu 1989 ku Czechoslovakia boma la Chikomyunizimu linatha. Ndinali wosangalala kwambiri kuyambanso kulalikira mwaufulu kunyumba ndi nyumba patatha zaka 40 ntchito yathu ili yoletsedwa. (Machitidwe 20:20) Nthaŵi iliyonse imene ndikumva bwino m’thupi ndinkachita ntchito imeneyi. Panopo ndili ndi zaka 98 ndipo thupi langa linafooka, koma ndikusangalala kuti ndimathabe kulalikira anthu za zinthu zosaneneka zimene Yehova walonjeza kuti achita m’tsogolo muno.

Ndikukumbukira atsogoleri okwana 12 ochokera m’mayiko asanu amene alamulirapo dera la kwathu. Ena mwa iwo anali olamula ankhanza, mapulezidenti, ndiponso mfumu imodzi. Palibe aliyense wa anthu ameneŵa amene anabweretsapo njira yothetseratu mavuto onse amene ankasautsa anthu ake. (Salmo 146:3, 4) Ndikuthokoza Yehova polola kuti ndimudziŵe ndidakali wamng’ono. Zimenezi zinandithandiza kuzindikira kuti Ufumu wake wa Umesiya ndiwo udzathetsedi mavuto athu motero ndinapeŵa mavuto a moyo wosaopa Mulungu. Ndakhala ndikulalikira mwakhama uthenga wabwino kwambiri zaka zopitirira 75, ndipo uthengawu wandithandiza kuchita zakupsa, kukhala wosangalala, ndiponso kukhala ndi chiyembekezo chosangalatsa cha moyo wosatha padziko lapansi. Ndithudi, palibe uthenga wina umene ukanandithandiza koposa umenewu? *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 14 Linkafalitsidwa ndi Mboni za Yehova koma tsopano anasiya kulisindikiza.

^ ndime 38 N’zomvetsa chisoni kuti Mbale Michal Žobrák anatisiya. Anamwalira nkhani ino ikukonzedwa kuti ifalitsidwe ndipo anali wokhulupirika komanso anali ndi chiyembekezo cholimba chakuti adzaukitsidwa.

[Chithunzi patsamba 26]

Titangokwatirana chakumene

[Chithunzi patsamba 26]

Ndili ndi Eduard kumayambiriro kwa m’ma 1940

[Chithunzi patsamba 27]

Kulengeza msonkhano ku Brno, mu 1947