Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo “Lomasuliridwa Bwino Kwambiri”

Baibulo “Lomasuliridwa Bwino Kwambiri”

Baibulo “Lomasuliridwa Bwino Kwambiri”

MALINGA ndi zomwe anapeza pa kufufuza kwina, kuyambira m’chaka cha 1952 mpaka kudzafika mu 1990, panasindikizidwa mitundu 55 yatsopano ya mabaibulo okhala ndi Malemba Achigiriki Achikristu. Popeza kuti omasulira mabaibulowa anali ndi makonda osiyanasiyana pomasulira mawu ena ndi ena, palibe Baibulo ngakhale limodzi limene limafanana ndi linzake. Pofuna kudziwa kuti zimene anamasulirazo n’nzodalirika motani, a Jason BeDuhn, omwe ndi pulofesa wa maphunziro a zachipembedzo pa yunivesite ya Northern Arizona, ku Flagstaff, Arizona, m’dziko la United States, anawerenga mofatsa ndi kuyerekezera mabaibulo asanu ndi atatu ofala kwambiri. Iwo anatero n’cholinga choti aone Baibulo lomwe analimasulira molondola kwambiri. Pa mabaibulowo panalinso Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures, lomwe limafalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Kodi anapeza zotani?

Ngakhale kuti sanagwirizane ndi mmene mawu ena anamasuliridwira m’Baibulo la New World Translation, a BeDuhn ananena kuti Baibuloli ‘linamasuliridwa bwino kwambiri,’ “ndi labwino kwambiri” ndiponso pa mabaibulo asanu ndi atatu aja Baibuloli “lili bwino kwambiri koposa enawo m’zinthu zochuluka.” Koposa zonsezi, a BeDuhn anati, pa mabaibulo “amene alipo panopa [Baibulo la New World Translation] ndi limodzi mwa mabaibulo olondola kwambiri a Chingelezi okhala ndi Chipangano Chatsopano,” ndipo “pa mabaibulo asanu ndi atatu aja, Baibulo limeneli ndiye lolondola kwambiri.”​—Truth in Translation: Accuracy and Bias in English Translations of the New Testament.

A BeDuhn ananenanso kuti, omasulira ambiri ankakakamizika “kusintha zinthu zina kapena kufotokozera zimene Baibulo limanena pofuna kuti zigwirizane ndi zofuna za owerenga Baibulo masiku ano.” Koma Baibulo la New World Translation ndi losiyana ndi mabaibulo amenewa, chifukwa “Baibulo la NW ndiye lolondola kwambiri popeza kuti linamasuliridwa ndendende motsatira kalembedwe ka anthu omwe analemba Chipangano Chatsopano,” anatero a BeDuhn.

Mogwirizana ndi zomwe linanena bungwe lomasulira Baibulo la New World Translation m’mawu oyamba a Baibuloli, ndi “udindo waukulu kwambiri” kumasulira Malemba Opatulika, kuchokera m’zinenero zake zoyambirira kuti akhale m’zinenero zamakono. Bungwelo linapitiriza motere: “Omasulira Baibulo ili, omwe ndi oopa ndiponso okonda Mulungu yemwe ndiye Mlembi wa Malemba Opatulika, amaona kuti Iye anawapatsa udindo waukulu woti ayesetse kufotokoza molondola maganizo ndi zonena zake.”

Kuyambira mu 1961 pamene Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures linayamba kusindikizidwa, Baibuloli lamasuliridwa m’zinenero 32 komanso pali mabaibulo a mitundu iwiri a zilembo za akhungu. Baibulo la New World Translation, la Malemba Achigiriki Achikristu, kapena kuti “Chipangano Chatsopano,” lili m’zinenero zina zokwana 18 kuwonjezaponso limodzi la zilembo za akhungu. Tikukupemphani kuti muwerenge Mawu a Mulungu m’Baibulo lamakono “lomasuliridwa bwino kwambiri” limeneli, lomwe mwina liliponso m’chinenero chomwe mumadziwa.