Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ataukitsidwa anachita kuuza Tomasi kuti amukhudze pamene poyamba analetsa Mariya wa Magadala kutero?

Mabaibulo ena akale amasonyeza ngati kuti Yesu anauza Mariya wa Magadala kuti asam’khudze. Mwachitsanzo, Baibulo lakuti Buku Lopatulika Ndilo Mawu a Mulungu limati Yesu analankhula motere: “Usandikhudze, pakuti sindinatha kukwera kwa Atate.” (Yohane 20:17) Koma mawu oyambirira a Chigiriki amene nthawi zambiri amamasuliridwa kuti “khudza,” amatanthauza kuti “kukakamira, kugwira mosataya, kugwiritsitsa.” M’pomveka kunena kuti Yesu sankaletsa Mariya wa Magadala kuti angom’khudza chabe, popeza kuti Yesu analola azimayi ena amene anali pamanda ‘kum’gwira iye mapazi ake.’​—Mateyu 28:9.

Mabaibulo ambiri omasuliridwa malinga ndi chinenero chamakono, monga mabaibulo a New World Translation of the Holy Scriptures, The New Jerusalem Bible, ndi The New English Bible, amatithandiza kumvetsa tanthauzo lenileni la mawu a Yesu mwa kunena kuti iye anati: “Usandikakamire.” N’chifukwa chiyani Yesu ananena izi kwa Mariya wa Magadala, amene anali kuchita naye zinthu zambiri limodzi?​—Luka 8:1-3.

Mwachionekere, Mariya wa Magadala ankaopa kuti Yesu watsala pang’ono kuchoka ndi kukwera kupita kumwamba. Chifukwa chofunitsitsa kukhala ndi Ambuye wake, iye anakakamira Yesu, osasiyana naye. Pofuna kum’tsimikizira kuti sanali kuchoka panthawi imeneyo, Yesu analangiza Mariya kuti asam’kakamire, m’malo mwake akauze ophunzira ake nkhani ya kuukitsidwa kwake.​—Yohane 20:17.

Nkhani imene Yesu anakambirana ndi Tomasi inali yosiyana ndi imeneyi. Pamene Yesu anaoneka kwa ophunzira ake ena, Tomasi panalibe. Kenako, Tomasi anasonyeza kukaikira za kuuka kwa Yesu, ponena kuti sangakhulupirire nkhaniyi pokhapokha ataona mabala a Yesu a misomali ndi kuika dzanja lake m’nthiti mwa Yesu momwe anabayidwa ndi mkondo. Patatha masiku asanu ndi atatu, Yesu anaonekanso kwa ophunzirawo. Paulendo uwu, Tomasi analipo, ndipo Yesu anamuuza kuti agwire mabalawo.​—Yohane 20:24-27.

Motero, Mariya wa Magadala, Yesu anali kum’thandiza kukonza maganizo olakwika ofuna kum’lepheretsa kuchoka; pamene Tomasi, Yesu anali kum’thandiza kuti asiye kukayikira. Pazochitika zonsezi, Yesu anali ndi zifukwa zomveka zochitira zinthu zimene anachitazi.