Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Malangizo Anzeru a Solomo Okhudza Zoyenerera Kuwerenga

Malangizo Anzeru a Solomo Okhudza Zoyenerera Kuwerenga

Malangizo Anzeru a Solomo Okhudza Zoyenerera Kuwerenga

“SALEKA kulemba mabuku ambiri; ndipo kuwaphunzira kwambiri kutopetsa thupi.’ (Mlaliki 12:12) Polemba mawu amenewa zaka pafupifupi 3,000 zapitazo, sikuti Solomo, yemwe anali Mfumu yanzeru ya Israyeli, ankaletsa kuwerenga. M’malo mwake, iye anali kufotokoza za kufunika kosankha zinthu zowerenga. Malangizo amenewa n’ngofunika kwambiri masiku ano, chifukwa chaka ndi chaka padziko lonse pamasindikizidwa zinthu zankhaninkhani zoti anthu awerenge.

N’zoonekeratu kuti “mabuku ambiri” omwe Solomo ankanena, ndi mabuku omwe sanali olimbikitsa kapena otsitsimutsa munthu. Motero, iye anati kuphunzira kwambiri mabuku amenewa ‘kumam’topetsa thupi’ munthu, m’malo moti apindule nawo.

Komano, kodi Solomo anali kunena kuti palibe mabuku a malangizo abwino ndi odalirika amene munthu angapindule nawo? Ayi, chifukwa chakuti iye analembanso kuti: “Mawu a anzeru akunga zinsonga, omwe akundika mawu amene mbusa mmodzi awapatsa mawu awo akunga misomali yokhomedwa zolimba.” (Mlaliki 12:11) Zoonadi, pali mawu amene analembedwa omwe mofanana ndi “zinsonga,” kapena kuti zikwapu zolishira ziweto, angatithandize kwambiri. Angalimbikitse munthu kuchita zinthu zabwino. Komanso, ‘monga misomali yokhomedwa zolimba,’ mawu amenewo angalimbikitse munthu kukhala wotsimikiza pochita zinthu ndiponso wosasunthika.

Kodi mawu anzeru oterowo tingawapeze kuti? Mogwirizana ndi zomwe Solomo ananena, mawu anzeru kwambiri ndi amene amachokera kwa Mbusa mmodzi, yemwe ndi Yehova. (Salmo 23:1) Motero, munthu angachite bwino kwambiri kuwerenga buku limene Mulungu anauzira, lomwe ndi Baibulo. Kuwerenga nthawi zonse mawu ouziridwa amenewa kungam’thandize munthu kukhala “woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.”​—2 Timoteo 3:16, 17.