Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

Kodi Mkristu angatani ngati watopa kwambiri moti sangathe kuganiza bwinobwino kapena ngati watopa mwauzimu?

Tiyenera kudziwa kaye chimene chikutitopetsa. Ndi bwino kukhala pansi n’kulemba zinthu zonse zimene timakonda kuchita ndiponso zimene tili nazo. Tikatero tichotsepo zonse zimene zimangotipatsa chintchito. Chinanso chimene chingatithandize ndi kukhala ndi zolinga zokhazo zimene tingathedi kuzikwaniritsa malingana ndi mmene zinthu zilili pamoyo wathu. Kusamalira thanzi lathu lauzimu n’kofunika kwambiri ndipo kuti titero tiyenera kupemphera ndi kusinkhasinkha nthawi zonse.​—8/15, masamba 23-6.

Kodi n’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zimaona kuti nambala ya 144,000 si yophiphiritsa?

Mtumwi Yohane atauzidwa za nambala ya 144,000, anaona ‘khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga.’ (Chivumbulutso 7:4, 9) Nambala imeneyi ikanakhala kuti n’njongophiphiritsira, ndiye kuti sizikanakhala zomveka kutchula nambalayi ndendende ndiye kenaka nambala ya khamu lalikulu n’kusaitchula ndendende. Yesu ananena kuti anthu amene adzalamulire naye adzakhala ‘kagulu ka nkhosa.’ (Luka 12:32)​—9/1, tsamba 30.

Kodi Aisrayeli ankaloledweranji kugulitsa nyama zakufa zosazinga kwa anthu akunja?

Chilamulo sichinali kukhudza munthu wakunja kapena mlendo amene sanatembenuke n’kukhala Wachiyuda. Motero Aisrayeli ankaloledwa kupereka kapena kugulitsa nyama zosazinga kwa anthu otere. (Deuteronomo 14:21) Koma anthu amene anatembenuka n’kukhala Achiyuda anali kukhudzidwa ndi Chilamulo ndipo sanali kuloledwa kudya nyama zosazingazi. (Levitiko 17:1)​—9/15, tsamba 26.

Kodi Asayansi aphunzirapo zinthu zotani pa chilengedwe ndipo kodi zimenezi zikuwakhudza bwanji Akristu?

Akatswiri asayansi amapanga zinthu zina motengera zinthu za m’chilengedwe. Mwachitsanzo, anthu awiri apachibale omwe dzina la abambo awo linali Wright anapanga ndege poonera mmene mbalame zikuluzikulu zimaulukira. Motero sayansi yotsanzira chilengedwe ingathe kulimbikitsa Mkristu kupereka ulemerero kwa Mlengi.​—10/1, tsamba 9.

Kodi ndani anatchulidwa pa 2 Akorinto 12:2-4 kuti anakwatulidwa kupita ku paradaiso?

Paulo analemba mavesi amene mukupezeka mawu amenewa atangomaliza kulemba mavesi otsutsa mfundo za anthu amene ankam’nena kuti sanali woyenerera kukhala mtumwi. Popeza kuti Baibulo silinenapo za munthu wina aliyense amene anakwatulidwapo ndiponso popeza kuti ndi Paulo mwini amene anafotokoza zimenezi, zikuoneka kuti amenewa ndi masomphenya amene Pauloyo anaona.​—10/15, tsamba 8.

Kodi Yesu ali ndi makhalidwe ena otani monga mtsogoleri woyenerera amene Mulungu anasankha?

Yesu anali wokhulupirika kwambiri pa chilichonse, ndipo ankachita zinthu moona mtima komanso molungama. Iye anadzipereka kwa Mulungu ndi mtima wonse. Yesu ankaganizira kwambiri anthu ndipo ankagwira ntchito mosanyinyirika.​—11/1, masamba 6-7.

Kodi ziwanda zidzakhala zili kuti pa Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu?

M’pomveka kunena kuti mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu, ziwanda zidzaponyedwa kuphompho pamodzi ndi Satana. (Chivumbulutso 20:1-3) Pa lemba la Genesis 3:15 pali ulosi wonena za kulalira mutu wa chinjoka, kumene kukutanthauzanso zinthu monga kuchiponya mu phompho kwa zaka 1,000 zimenezi. Ziwanda zili m’gulu la mbewu ya chinjokacho. Popeza kuti ziwanda zimaopa chiphompho chimenechi ndiye kuti zimadziwa za chilango chikubwerachi. (Luka 8:31)​—11/15, masamba 30-1.

Kodi n’chifukwa chiyani munthu ayenera kusamala ndithu ndi zakumwa zoledzeretsa, ngakhale atakhala kuti amapewa kumwa mochita kuoneka kuti waledzera?

Anthu ena saonekera kwenikweni kuti aledzera ngakhale atamwa kwambiri ndithu. Komabe, pang’ono ndi pang’ono munthu angathe kufika pokhala ndi chizolowezi chomwa mowa, motero angathe ‘kukodwa nacho chikondi cha pavinyo.’ (Tito 2:3) Yesu anati tiyenera kusamala kuti ‘tisalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera.’ (Luka 21:34, 35) Munthu amaodzera ndiponso kufooka ndi mowa asanafike poledzera nawo, ndipo izi zingasokonezenso moyo wake wauzimu.​—12/1, masamba 19-21.