Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kubadwa Kwake N’koyenera Kukukumbukira

Kubadwa Kwake N’koyenera Kukukumbukira

Kubadwa Kwake N’koyenera Kukukumbukira

‘Wakubadwirani inu lero, Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.’​—Luka 2:11.

ZAKA zoposa 2000 zapitazo, mkazi wina anabala mwana wamwamuna m’mudzi wotchedwa Betelehemu. Ndi anthu ochepa okha m’mudzimo amene anazindikira kuti kubadwa kwa mwanayu kunali kofunika. Koma abusa ena amene anali kugonera kubusa konko ndi ziweto zawo anaona unyinji wa angelo akuimba kuti: “Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.”​—Luka 2:8-14.

Kenako, abusawo anakapezadi Mariya ndi mwamuna wake Yosefe, m’khola monga momwe angelowo anawauzira. Mariya anamutcha mwanayo Yesu ndipo anam’goneka modyera ziweto m’kholamo. (Luka 1:31; 2:12) Tsopano, papita zaka 2000 ndipo pafupifupi munthu mmodzi pa anthu atatu alionse padziko pano amanena kuti amatsatira Yesu Kristu. Ndipo nkhani zokhudza kubadwa kwake zafotokozedwa kuposa nkhani ina iliyonse m’mbiri yonse ya anthu.

Dziko la Spain, lomwe limatsatira kwambiri miyambo ya tchalitchi cha Katolika ndiponso n’lotchuka kwambiri pochita zikondwerero za miyambo lakhala likukondwerera m’njira zosiyanasiyana zinthu zomwe zinachitika pa usiku wapadera umenewu ku Betelehemu.

Mmene Anthu a ku Spain Amakondwerera Khirisimasi

Kuyambira m’zaka za m’ma 1200 zithunzi zosonyeza nkhani ya kubadwa kwa Yesu zakhala zotchuka zedi m’zikondwerero za anthu a ku Spain. Mabanja ambiri amapanga timafanizo tawo ta chodyeramo ng’ombe m’mene Yesu anam’gonekamo. Amaumba ziboliboli za dongo zoyerekezera Anzeru a kum’mawa, Yosefe, Mariya, ndi Yesu. Ziboliboli zazikulu zofanana ndi msinkhu wa munthu kawirikawiri zimaimikidwa pafupi ndi maholo akuluakulu a m’mizinda pa nyengo ya Khirisimasi. Zikuoneka kuti Francis wa ku Assisi ndiye anayambitsa mwambowu ku Italy pofuna kuthandiza anthu kuti aziganizira zomwe zinalembedwa m’Mauthenga Abwino za kubadwa kwa Yesu. Pambuyo pake, amonke a chipani cha Franciscan ndi amene anatchukitsa mwambowu ku Spain komanso m’mayiko ena ambiri.

Anzeru a kum’mawa ndi amene amakhala mbali yaikulu ya chikondwerero cha Khirisimasi ku Spain monga mmene amachitira Santa Claus kapena kuti Tate Khirisimasi ku mayiko ena. Akuti Anzeru a kum’mawa amapatsa ana a ku Spain mphatso pa January 6, Día de Reyes (Tsiku la Mafumu), monga mmene Anzeru a kum’mawa anachitira popatsa Yesu wakhandayo mphatso malinga ndi zomwe anthu ambiri amakhulupirira. Komabe ndi anthu ochepa chabe amene amadziwa kuti Mauthenga Abwino satchula n’komwe kuti ndi Anzeru a kum’mawa angati amene anabwera kudzaona Yesu. Anzeru a kum’mawawa si mafumu ayi, koma kwenikweni ndi openda nyenyezi. * Kuwonjezera apo, pambuyo pa ulendo wa Anzeru a kum’mawawo, Herode anayesa kupha Yesu mwa njira yopha tiana tatimuna tonse mu Betelehumu “takufikira zaka ziwiri ndi tating’ono tonse.” Izi zikusonyeza kuti Anzeru a kum’mawawo anabwera kudzaona Yesu, patapita nthawi yaitali ndithu kuchokera pamene Yesuyo anabadwa.​—Mateyu 2:11, 16.

Kuyambira m’zaka za m’ma 1100, m’matauni ena a ku Spain mwakhala mukuchitika zisudzo za nkhani ya kubadwa kwa Yesu, kuphatikizapo kubwera kwa abusa ku Betelehemu ndiponso kwa Anzeru a kum’mawa omwe anabwera pambuyo pawo. Masiku ano, m’mizinda ya ku Spain mumachitika mwambo womwe pamakhala chigulu cha anthu choyenda m’misewu pa January 5 paliponse, ndipo apa Anzeru a kum’mawa ongoyerekezera kapena kuti “mafumu atatu” amakhala atakwera galimoto za mpandadenga podutsa m’katikati mwa mizindayo, kwinaku akugawa masiwiti kwa anthu odzaonerera. Pofuna kuti Khirisimasi ikhale yosangalatsa, panyengoyi pamakhala zokongoletsakongoletsa ndiponso nyimbo za chipembedzo.

Mabanja ambiri ku Spain amakonda kudya chakudya chosowa madzulo oti Khirisimasi ili mawa lake. Nthawi zonse zakudya zake zimakhala masiwiti opangidwa kuchokera ku zipatso za mchiwu ndiponso uchi komanso mabisiketi opangidwa kuchokera ku phala la mchiwu, shuga, ndi mazira; amadyanso zipatso zofutsa, nyama ya nkhosa yowotcha ndi nsomba. Achibale ngakhale amene amakhalirana kutali, amayesetsa kuchita chilichonse chotheka kuti adzadyere limodzi phwandoli. Pa chakudya chinanso cha panyengoyi, pa January 6, banja limadya keke yoboola pakati ya Anzeru a kum’mawa aja omwe amawatchanso kuti Mafumu, yokhala ndi kachidole kobisika m’kati mwake. Mwambo wangati umenewu, umene unkachitika m’nthawi yakale ku Roma umachititsa kuti kapolo amene keke yake mwapezeka kachidole akhale ngati mfumu kwa tsiku limodzi.

“Nthawi Yosangalatsa Komanso Yotangwanitsa Koposa pa Chaka”

Pa miyambo yonse imene imachitika kwina kulikonse, Khirisimasi tsopano ndiyo yatenga malo monga chikondwerero chachikulu koposa padziko lonse. Buku la The World Book Encyclopedia limafotokoza kuti Khirisimasi ndi “nthawi yosangalatsa kwambiri komanso yotangwanitsa koposa pa chaka kwa Akristu mamiliyoni ambiri komanso kwa ena osakhala Akristu padziko lonse.” Kodi chikondwererochi n’chabwinodi?

Mwachionekere, kubadwa kwa Kristu ndi chinthu chofunika kwabasi m’mbiri ya anthu. Tikaganizira kuti angelo enieniwo analengeza kuti kubadwa kwake kukusonyeza kuti kudzabwera ‘mtendere mwa anthu amene akondwera nawo,’ timaona kuti kunalidi kofunika kwambiri.

Komabe, mtolankhani wina wa ku Spain, Juan Arias anati, “m’masiku oyambirira a Chikristu, anthu sankakondwerera kubadwa kwa Yesu.” Ngati izi n’zoona, nanga kodi Khirisimasi inachokera kuti? Kodi ndi njira iti imene ili yabwino koposa yokumbukirira kubadwa komanso moyo wa Yesu? M’nkhani yotsatira, mupezamo mayankho a mafunso amenewa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Buku lotchedwa La Sagrada Escritura y comentario por profesores de la Compañía de Jesús (Malemba Opatulika, Nkhani ndi Ndemanga Zolembedwa ndi Gulu la Aphunzitsi a Chipani cha Yesu) limafotokoza kuti “pakati pa Aperisi, Amedi ndi Akasidi, Anzeru a kum’mawa ndiwo anali gulu la ansembe amene ankalimbikitsa maphunziro a zamatsenga, kupenda nyenyezi komanso mankhwala.” Komabe, pofika m’zaka za m’ma 500 mpaka 1500 C.E, gulu la Anzeru a kum’mawa amene anabwera kudzaona Yesu ali mwana, anayamba kutchedwa kuti oyera ndipo anapatsidwa mayina akuti: Melchior, Gaspar, ndi Balthasar. Ndipo mafupa awo akuti amasungidwa mu tchalitchi chachikulu cha mu mzinda wa Cologne, ku Germany.