Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Ndine Wosangalala ndi Zimene Ndaphunzira’

‘Ndine Wosangalala ndi Zimene Ndaphunzira’

‘Ndine Wosangalala ndi Zimene Ndaphunzira’

MTSIKANA wina dzina lake Kazuna anachita kakasi aphunzitsi ake atamuuza kuti achite nawo mpikisano wokamba nkhani m’Chingelezi. Umenewu ndi mpikisano wa sukulu zonse zasekondale za pachisumbu chachikulu kwambiri cha kumpoto kwa Japan chotchedwa Hokkaido. Komano, aka kanali koyamba kuti sukulu ya mtsikanayu ikhale ndi mwana wasukulu wochita nawo mpikisanowo. Patsiku la mpikisanowo, Kazuna anali ndi mantha kwambiri chifukwa chakuti anayenera kupikisana ndi anzake okwana 50. Anachitanso mantha makamaka poona kuti panali Angelezi enieni awiri oona ana asukulu amene achita bwino pampikisanowo.

Itafika nthawi yolengeza opambana pampikisanopo, anayamba kaye kulengeza wophunzira amene anapatsidwa mphoto yomaliza. Kazuna anachita kakasi kumva dzina lake likulengezedwa komalizira. Modabwa, iye anayang’anana ndi aphunzitsi ake, omwe anakhala nawo pamodzi. Anapita kukalandira mphoto yake yoyamba, koma sankamvetsetsabe.

Chimwemwe chili tsaya, Kazuna analongosola kuti: “Zimenezi zatheka chifukwa cha zimene gulu la Yehova limandiphunzitsa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Ndine wosangalala kwambiri ndi zimene ndimaphunzirazi.” Kazuna wakhala akuphunzira mu sukulu imeneyi kuyambira ali wamng’ono, ndipo sukuluyi kwenikweni ili m’gulu la misonkhano ya Mboni za Yehova. Pokonzekera mpikisanowo, Kazuna anaonetsetsa kuti akudziwa bwino zinthu monga kugwiritsira ntchito maikolofoni, kulankhula mosonyeza ubwenzi ndiponso mwaumoyo, kuti manja komanso nkhope yake ikusonyeza kuti n’ngomasuka, kuti akuyang’ana omvetsera, ndiponso akuchita zinthu zina zimene anthu amaphunzira mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.

Tikukupemphani kuti muyesetse kukaona mmene sukuluyi imakhalira. Imachitika mlungu uliwonse ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova m’dera limene inuyo mumakhala. Pitani kuti mukadzionere nokha mmene ana ndi akulu omwe akupindulira ndi sukuluyi. Pamsonkhano umenewu amalola wina aliyense kukhalapo. Kuti mudziwe zambiri zokhudza sukulu yotere yomwe imachitikira kufupi ndi kwanu, funsani Mboni za Yehova m’dera lanulo.