Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Mungatetezere Ana Anu ndi Nzeru za Mulungu

Mmene Mungatetezere Ana Anu ndi Nzeru za Mulungu

Mmene Mungatetezere Ana Anu ndi Nzeru za Mulungu

TSIKU lililonse, matupi athu amakhala pankhondo. Amalimbana ndi majeremusi osiyanasiyana. Koma ubwino wake ndi wakuti ambiri mwa ife tinabadwa ndi mphamvu imene imatiteteza ku majeremusi amenewo ndipo imatithandiza kuti tisadwale matenda osiyanasiyana.

Mofanana ndi zimenezo, Akristu ayenera kulimbana ndi maganizo ndi mfundo zosemphana ndi Malemba ndiponso zinthu zina zimene zingawononge thanzi lathu lauzimu. (2 Akorinto 11:3) Kuti tilimbane ndi zinthu zimenezi, zimene zimafuna kuwononga maganizo ndi mitima yathu tsiku lililonse, tikufunika kupeza njira zodzitetezera mwauzimu.

Njira zimenezi n’zofunika kwambiri makamaka kwa ana athu, chifukwa sabadwa akudziwa kale mmene angadzitetezere ku mzimu wa dzikoli. (Aefeso 2:2) Ana akamakula, m’pofunika kwambiri kuti makolo awathandize kukhala ndi njira zodzitetezera mwauzimu. Kodi njira zodzitetezera zimenezo zimadalira chiyani? Baibulo limati: ‘Yehova apatsa nzeru; . . . nadikira khwalala la opatulidwa ake.’ (Miyambo 2:6, 8) Nzeru za Mulungu zingateteze achinyamata amene atati adalire nzeru zawo zokha angathe kupeza anzawo oipa, kutengera zochita za anzawowo, kapena kukhala ndi zosangalatsa zoipa. Kodi makolo angatsatire bwanji malangizo a Yehova n’kuphunzitsa ana awo nzeru za Mulungu?

Kupeza Anzawo Abwino

M’pomveka kuti achinyamata amakonda kucheza ndi achinyamata anzawo. Koma kumangokhalira kucheza ndi anthu amene alinso osadziwa zambiri m’moyo sikungawalimbikitse kugwiritsa ntchito nzeru za Mulungu. Mwambi wina umachenjeza kuti: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana.” (Miyambo 22:15) Choncho, kodi makolo ena achita chiyani kuti athandize ana awo kugwiritsa ntchito nzeru za Mulungu akamasankha anthu ocheza nawo?

Bambo wina dzina lake Don * anati: “Ana athu aamuna ankakhala nthawi yambiri ali ndi anzawo amsinkhu wawo, koma nthawi yambiri ankakhala ali m’nyumba mwathu, tikuwaona. Ana ena anali omasuka kubwera kunyumba kwathu ndipo nyumba yathu inkadzaza ndi achinyamata, amene tinkawadyetsa ndi kuwasamalira. Sitinkadandaula chifukwa cha phokoso ndi chisokonezo chimene chinkakhala m’nyumba mwathu, chifukwa tinkafuna kuti ana athu azisangalala ali pamalo otetezeka.”

Brian ndi Mary ali ndi ana atatu a khalidwe labwino, koma anavomereza kuti kuwaphunzitsa anawo sikuti nthawi zonse kunali kosavuta. Iwo anati: “Mu mpingo mwathu munali atsikana ochepa a zaka pafupifupi 20 oti akanatha kumacheza ndi mwana wathu wamkazi Jane. Koma Jane anali ndi mnzake mmodzi dzina lake Susan, amene anali mtsikana wansangala ndiponso wochezeka kwambiri. Koma makolo ake anali olekerera kwambiri kuposa ifeyo. Ankamulola Susan kubwera kunyumba usiku kwambiri kusiyana ndi nthawi imene Jane ankabwerera, kuvala masiketi aafupi, kumvetsera nyimbo zoipa, ndi kuonera mafilimu oipa. Kwanthawi yaitali, Jane ankavutika kumvetsa chifukwa chimene tinkamuletsera kuchita zinthu zina ndi zina. Kwa iyeyo, makolo a Susana ankaoneka ngati omvetsa zinthu pamene ifeyo tinkaoneka ngati ovuta kwambiri. Pamene Susan anagwa m’mavuto m’pamene Jane anadzazindikira kuti kuvuta kwathu kuja cholinga chake chinali choti timuteteze. Ndife osangalala kwambiri kuti sitinasinthe maganizo athu pa zinthu zimene tinkakhulupirira kuti zinali zabwino kwa mwana wathu.”

Mofanana ndi Jane, achinyamata ambiri azindikira kuti n’chinthu chanzeru kulola kuti makolo awo awathandize kusankha anzawo. Mwambi wina umati: “Khutu lomvera chidzudzulo cha moyo lidzakhalabe mwa anzeru.” (Miyambo 15:31) Nzeru za Mulungu zimathandiza achinyamata kupeza anzawo abwino.

Kulimbana ndi Mtima Wofuna Kutengera Khalidwe la Anzawo

Nkhani ina yogwirizana kwambiri ndi ya anthu ocheza nawo ndi yokhudza mtima wofuna kutengera zimene achinyamata ena akuchita. Tsiku lililonse ana athu amafunika kudziteteza kuti asatengere zimene anzawo akuchita. Popeza achinyamata nthawi zambiri amafuna kufanana ndi anthu a msinkhu wawo, iwo angayambe kuchita zinthu zimene dzikoli limaona ngati zabwino.​—Miyambo 29:25.

Baibulo limatikumbutsa kuti “dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake.” (1 Yohane 2:17) Choncho makolo sayenera kulola ana awo kutengera kwambiri maganizo a dzikoli. Kodi angathandize bwanji ana awo kuganiza monga Akristu?

Richard anati: “Mwana wanga wamkazi nthawi zonse ankafuna kuvala ngati mmene atsikana ena ankavalira. Choncho tinkakambirana naye mwachifatse ubwino ndi kuipa kovala chovala chilichonse chomwe ankafuna kuvala. Ngakhale pa masitayilo amene sanali oipa, tinatsatira malangizo amene tinamva zaka zapitazo, oti, ‘Munthu wanzeru sakhala woyamba kuvala sitayilo yatsopano kapena womaliza kusiya kuvala sitayiloyo.’”

Mayi wina dzina lake Pauline anagwiritsa ntchito njira ina polimbana ndi mtima wa ana ake wofuna kufanana ndi anzawo. Iye anati: “Ndinayamba kukhala ndi chidwi ndi zinthu zimene ana anga ankakonda ndipo nthawi zambiri ndinkapita kuchipinda kwawo kukacheza nawo. Chifukwa chocheza nawo kwa nthawi yaitali, ndinatha kuwathandiza kuganiza moyenera ndi kuona zinthu mosiyana ndi mmene anali kuganizira poyamba.”

Mtima wofuna kufanana ndi anzawo sikuti umatha, choncho makolo mosakayikira afunikira nthawi zonse kuyesayesa ‘kuthetsa mitsutso’ yakudziko ndi kuthandiza ana awo ‘kumanga maganizo onse kuti akhale omvera Kristu.’ (2 Akorinto 10:5, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Koma ‘polimbikira chilimbikire m’kupemphera,’ makolo limodzi ndi ana angalimbikitsidwe kuti athe kukwanitsa ntchito yofunika imeneyi.​—Aroma 12:12; Salmo 65:2.

Chikoka cha Zosangalatsa

Chinthu chachitatu chimene makolo angavutike kulimbana nacho ndicho zosangalatsa. Mwachibadwa, ana aang’ono amakonda kusewera. Ana okulirapo msinkhu ambiri amakondanso kusangalala. (2 Timoteo 2:22) Koma ngati zosangalatsa zake zikhala zoipa, zingawawonongere moyo wawo wauzimu. Kuopsa kwake makamaka kuli pawiri.

Choyamba, zosangalatsa zambiri zimasonyeza makhalidwe onyansa a dzikoli. (Aefeso 4:17-19) Komabe, amazisonyeza mosangalatsa ndiponso mokopa. Zimenezi zingapweteke achinyamata, amene sangathe kuzindikira kuopsa kwake.

Chachiwiri, nthawi imene munthu amathera pa zosangalatsa ikhozanso kuyambitsa mavuto. Kwa ena, kufuna kusangalala kumasanduka chinthu chofunika kwambiri pamoyo wawo, ndipo kumawathera nthawi ndi mphamvu zambiri. Mwambi wina umachenjeza kuti “kudya uchi wambiri sikuli kwabwino.” (Miyambo 25:27) Mofanana ndi zimenezo, chifukwa chokhala ndi zosangalatsa zopitirira muyeso munthu angayambe kusafuna kudya zinthu zauzimu ndipo angakhale waulesi m’maganizo. (Miyambo 21:17; 24:30-34) Kusangalala ndi dziko lino mopitirira muyeso kungalepheretse achinyamata ‘kugwira moyo weniweniwo,’ moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu. (1 Timoteo 6:12, 19) Kodi makolo achita chiyani kuti athane ndi vuto limeneli?

Mari Carmen, mayi wa ana aakazi atatu anati: “Tinkafuna kuti ana athu azikhala ndi zosangalatsa zabwino. Choncho nthawi zambiri tinkapita limodzi koyenda ngati banja ndiponso ankacheza ndi anzawo a mumpingo. Koma sitinali kupyola muyeso. Tinkaziyerekezera ndi chakudya chotsitsira mkhuto. Chimakhala chotsekemera koma chapang’ono. Ana athu anaphunzira kugwira ntchito mwakhama kunyumba, kusukulu, ndi mumpingo.”

Don ndi Ruth nawonso anachitapo kanthu pa nkhani ya zosangalatsa. Iwo anafotokoza kuti: “Tinakhazikitsa Loweruka kukhala tsiku loti banja lathu lizichitira zinthu limodzi. Tinkapita mu utumiki wa kumunda m’mawa, kupita kokasambira masana, n’kudya chakudya chapadera madzulo.”

Zimene makolo amenewa ananenazi zikusonyeza kufunika kosamala popezera ana anu zosangalatsa zabwino, ndiponso kuzipezera nthawi yake yoyenera pamoyo wanu monga Akristu.​—Mlaliki 3:4; Afilipi 4:5.

Khulupirirani Yehova

Zimatenga zaka zambiri kuti munthu aphunzire kudziteteza mwauzimu. Palibe njira yachidule yophunzitsira munthu nzeru za Mulungu imene ingachititse ana kukhulupirira Atate wawo wakumwamba. M’malo mwake makolo ayenera ‘kulera [ana awo] m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.’ (Aefeso 6:4) ‘Chilangizo cha Ambuye’ chimenechi, chimene chiyenera kuperekedwa nthawi zonse, chimathandiza ana kuona zinthu monga momwe Mulungu amazionera. Kodi makolo angachite bwanji zimenezo?

Kukhala ndi phunziro la Baibulo la banja nthawi zonse ndiye chinsinsi choti zinthu zikuyendereni bwino. Phunzirolo ‘limatsegula maso a ana kuti apenye zodabwitsa za m’chilamulo cha Mulungu.’ (Salmo 119:18) Diego ankaona kuti phunziro la banja linali lofunika kwambiri ndipo anathandiza ana ake kuyandikana ndi Yehova. Iye anati: “Ndinkakonzekera bwino kwambiri phunzirolo. Pochita kafukufuku m’mabuku ofotokoza za m’Malemba, ndinatha kuphunzitsa ana anga m’njira yowathandiza kuona kuti anthu a m’Baibulo ndi enienidi. Ndinalimbikitsa anawo kuti aziona kufanana kwa moyo wawo ndi wa anthu okhulupirika. Zimenezi zinawakumbutsa bwino kwambiri ana anga zinthu zimene zimasangalatsa Yehova.”

Ana amaphunziranso mwanjira zina. Mose analimbikitsa makolo kuuza ana awo malamulo a Yehova ‘pokhala pansi m’nyumba zawo, ndi poyenda iwo panjira, ndi pogona iwo pansi, ndi pouka iwo.’ (Deuteronomo 6:7) Bambo wina anafotokoza kuti: “Mwana wanga wamwamuna amafunika nthawi kuti aulule zakukhosi kwake. Tikapitira limodzi kokawongola miyendo kapena kugwirira limodzi ntchito inayake, pamapeto pake amayamba kulankhula momasuka. Panthawi zimenezi, timalankhulana bwino kwambiri ndipo zimenezi zimatithandiza awiri tonsefe.”

Mapemphero amene makolo amanena amakhudzanso kwambiri ana awo. Ana akamva makolo awo akulankhula ndi Mulungu modzichepetsa n’kumupempha kuti awathandize ndiponso awakhululukire, zimawathandiza “kukhulupirira kuti alipo.” (Ahebri 11:6) Makolo ambiri amene zinthu zinawayendera bwino amagogomezera kufunika kwa mapemphero abanja, amene amaphatikizaponso mapemphero okhudza zinthu zakusukulu ndi zinthu zina zimene zikudetsa nkhawa anawo. Bambo wina anati mkazi wake nthawi zonse amapemphera ndi ana awo asanapite kusukulu.​—Salmo 62:8; 112:7.

“Tisaleme Pakuchita Zabwino”

Makolo onse amalakwitsa zinthu nthawi zina ndipo angakhumudwe ndi mmene anachitira zinthu zinazake. Komabe, Baibulo limatilimbikitsa kuti tipitirizebe kuyesetsa, ndipo “tisaleme pakuchita zabwino.”​—Agalatiya 6:9.

Koma nthawi zina makolo angafune kungosiya osayeseranso makamaka pamene akulephera kuwamvetsa bwino ana awo. N’zosavuta kuganiza kuti ana a masiku ano ndi osiyana ndi mbadwo wakale ndiponso ndi ovuta. Komabe, zoona zake n’zakuti ana masiku ano ali ndi zofooka zofanana ndi za mibadwo yam’mbuyomu, ndipo amakumana ndi mayeso ofanana, ngakhale kuti panopa zinthu zowakopa kuti achite zinthu zoipa zawonjezereka. Choncho bambo wina atadzudzula mwana wake, anafewetsako mawu ake powonjezera kuti: “Mtima wako ukungofuna kuchita zimene mtima wanga unkafuna kuchita pamene ndinali msinkhu wakowu.” Mwina makolo sangadziwe zambiri zokhudza makompyuta, koma amadziwa bwino zofooka za thupi lopanda ungwiro.​—Mateyu 26:41; 2 Akorinto 2:11.

Ana ena mwina amanyinyirika kuti amvere malangizo a makolo awo ndipo nthawi zina satsatira n’komwe malangizo amene apatsidwa. Koma pamenepanso kupirira n’kofunika. Ngakhale kuti ana ambiri poyamba amanyinyirika ndipo nthawi zina samvera malangizo a makolo awo, pomalizira pake amamvera. (Miyambo 22:6; 23:22-25) Matthew, mnyamata wachikristu amene panopa akutumikira pa ofesi inayake ya nthambi ya Mboni za Yehova, anati: “Pamene ndinali wachinyamata, ndinkaona kuti makolo anga ankanyanyira pondiletsa kuchita zinthu zambiri. Ndinkaganiza kuti ngati makolo a anzanga ankawalola kuchita zinthu zinazake, ndiye kuti makolo anganso anayenera kundilola. Ndipo ndinkakwiya kwambiri nthawi zina makolo anga akandilanga pondiletsa kuti ndisapite kukapalasa bwato, chinthu chimene ndinkakonda kwambiri. Koma tsopano ndikamaganizira za m’mbuyo, ndimaona kuti malangizo amene makolo anga anandipatsa anali abwino ndiponso ofunika. Ndikuyamikira kwambiri kuti ananditsogolera bwino panthawi imene ndinkafunika kuti anditsogolere.”

N’zosachita kufunsa kuti ngakhale kuti ana athu nthawi zina amafunika kukhala pamalo amene salimbikitsa munthu kuchita zinthu zauzimu, akhozabe kukula bwino n’kukhala Akristu olimba. Monga momwe Baibulo limalonjezera, nzeru za Mulungu zingawateteze mwauzimu. “Nzeru idzalowa m’mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziwa, kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza; kukupulumutsa ku njira yoipa.”​—Miyambo 2:10-12.

Kunyamula mwana m’mimba kwa miyezi naini si chinthu chophweka. Ndipo zaka 20 zotsatira zingabweretse mavuto ndiponso chimwemwe. Koma chifukwa choti makolo achikristu amakonda ana awo, amayesetsa ndi mphamvu zawo zonse kuteteza anawo ndi nzeru za Mulungu. Amamva mofanana ndi mmene Yohane, mtumwi wokalamba, anamvera poganizira ana ake auzimu. Mtumwiyo anati: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’choonadi.”​—3 Yohane 4.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Mayina ena mu nkhani ino asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 24]

“Ana ena anali omasuka kubwera kunyumba kwathu ndipo nyumba yathu inkadzaza ndi achinyamata”

[Chithunzi patsamba 25]

Muzikhala ndi chidwi ndi zinthu zimene ana anu amakonda

[Zithunzi patsamba 26]

“Ndinkakonzekera bwino kwambiri phunzirolo”