Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nthawi Yachakudya si Nthawi Yongodya Basi!

Nthawi Yachakudya si Nthawi Yongodya Basi!

Nthawi Yachakudya si Nthawi Yongodya Basi!

ALIYENSE amakonda chakudya chabwino. Ndipo pa nthawi yachakudyayo pakakhala kuti palinso anthu amene timakonda ndipo tikucheza nawo bwino, timasangalala kwambiri ndipo timapindula m’njira zambiri, osati kungothetsa njala yathu yokha. Mabanja ambiri ali ndi chizolowezi chodyera pamodzi kamodzi kapena kangapo patsiku. Nthawi yachakudya imapereka mpata kwa anthu a m’banjamo woti akambirane zimene zachitika kapena zimene akufuna kuchita tsiku limenelo. Makolo amene amamvetsera zonena za ana awo amadziwa mmene anawo akuganizira ndi kumvera. M’kupita kwa nthawi, chifukwa cha macheza abwino amene banjalo limakhala nawo panthawi yachakudya anthu a m’banjamo amamva kuti ndi otetezeka, okhulupirirana, ndiponso okondana. Mapeto ake banjalo limalimba.

Masiku ano, chifukwa choti anthu ambiri m’mabanja amakhala otanganidwa nthawi zonse, zimawavuta kuti adyere limodzi chakudya. Ku madera ena padziko lapansi kuli miyambo imene amati n’kulakwa kuti mabanja azidyera limodzi kapena azilankhulana akamadya. Mabanja ena ali n’chizolowezi choonerera TV akamadya, zimene zimawalepheretsa kugwiritsa ntchito nthawi imeneyi kuti alankhulane bwino.

Koma makolo achikristu nthawi zonse amafunafuna mpata woti alimbikitsire banja lawo. (Miyambo 24:27) Kalekale, makolo anauzidwa kuti mpata umodzi wabwino kwambiri wophunzitsira ana awo mawu a Mulungu unali ‘akakhala pansi m’nyumba zawo.’ (Deuteronomo 6:7) Kukhala pansi limodzi nthawi zonse panthawi yachakudya kumapatsa makolo mpata wabwino kwambiri wophunzitsira ana awo kukonda kwambiri Yehova ndi mfundo zake zabwino. Mukathandiza anthu a m’banja lanu kuti azikhala omasuka akakhala panyumbapo, nthawi yachakudya izikhalanso yosangalatsa ndi yolimbikitsa kwa banja lanu. Indedi, chitani zotheka kuti nthawi yachakudya isamakhale nthawi yongodya basi!