Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsatirani Chitsanzo Chimene Yesu Anatipatsa

Tsatirani Chitsanzo Chimene Yesu Anatipatsa

Tsatirani Chitsanzo Chimene Yesu Anatipatsa

“Ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.”​—YOHANE 13:15.

1. N’chifukwa chiyani Yesu ali chitsanzo choti Akristu azitsatira?

M’MBIRI yonse ya anthu, ndi munthu mmodzi yekha amene anakhala moyo wake wonse osachimwa. Munthu ameneyo ndi Yesu. Kupatulapo Yesu, “palibe munthu wosachimwa.” (1 Mafumu 8:46; Aroma 3:23) Pachifukwa chimenechi, Akristu oona amaona kuti Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri chomwe ayenera kutsatira. Ndipo pa Nisani 14, m’chaka cha 33 C.E., Yesu mwiniwakeyo atatsala pang’ono kuphedwa anauza otsatira ake kuti azimutsanzira. Iye anati: “Ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga Ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.” (Yohane 13:15) Usiku wake womaliza umenewo, Yesu anatchula njira zingapo zimene Akristu ayenera kuyesetsa kukhala ngati iyeyo. Mu nkhani ino, tikambirana zina mwa njira zimenezo.

Kufunika Kodzichepetsa

2, 3. Kodi Yesu anali chitsanzo chabwino kwambiri cha kudzichepetsa m’njira zotani?

2 Pamene Yesu analimbikitsa ophunzira ake kutsatira chitsanzo chake, iye anali kulankhula makamaka za kudzichepetsa. Nthawi zingapo, iye analangiza otsatira ake kuti ayenera kukhala odzichepetsa, ndipo pa Nisani 14 usiku, iye anasonyeza kudzichepetsa kwake posambitsa mapazi a atumwi ake. Kenaka Yesu anati: “Ngati Ine Ambuye ndi Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi wina ndi mnzake.” (Yohane 13:14) Atatero, anauza atumwi ake kuti atsatire chitsanzo chimene anawapatsacho. Ndipo chitsanzo cha kudzichepetsa chimene anawapatsacho chinali chabwino kwambiri!

3 Mtumwi Paulo anati Yesu asanabwere padziko lapansi, anali ndi “maonekedwe a Mulungu.” Komabe, anadzikhuthula n’kukhala munthu wotsika. Kuwonjezera pamenepo, “anadzichepetsa yekha, nakhala womvera kufikira imfa, ndiyo imfa ya” pamtengo wozunzirapo. (Afilipi 2:6-8) Taganizirani kaye zimenezi. Yesu, munthu wachiwiri wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse, analola kuti akhale wotsika kuposa angelo, abadwe ngati mwana yemwe satha kudzithandiza yekha, akule mogonjera makolo opanda ungwiro, ndipo pamapeto pake afe monyozeka ngati chigawenga. (Akolose 1:15, 16; Ahebri 2:6, 7) Kumenekotu n’kudzichepetsadi! Kodi n’zotheka kutsanzira “mtima” ngati umenewo ndi kukhala ndi “kudzichepetsa” koteroko? (Afilipi 2:3-5) Inde n’zotheka, koma si zophweka.

4. Kodi anthu amanyada chifukwa cha zinthu ziti, koma kodi n’chifukwa chiyani kunyada kuli koopsa?

4 Khalidwe losiyana ndi kudzichepetsa ndilo kunyada. (Miyambo 6:16-19) Kunyada n’kumene kunagwetsa Satana. (1 Timoteo 3:6) Kunyada sikuchedwa kuyamba m’mitima mwa anthu, ndipo kukayamba, kumavuta kukuthetsa. Anthu amanyada chifukwa cha dziko lawo, mtundu wawo, katundu wawo, maphunziro awo, zimene akwanitsa kuchita m’dzikoli, udindo wawo, maonekedwe awo, luso lawo pa zamasewera, ndi zinthu zina zambiri. Komabe, zinthu zonsezi si zofunika kwa Yehova. (1 Akorinto 4:7) Ndipo zinthu zimenezi zikatichititsa kukhala onyada, zimawononga ubwenzi wathu ndi Yehova. “Yehova n’ngokwezeka, apenyanso wopepukayo; koma wodzikuza am’dziwira kutali.”​—Salmo 138:6; Miyambo 8:13.

Kudzichepetsa Pakati pa Abale Athu

5. Kodi n’chifukwa chiyani akulu afunika kudzichepetsa kwambiri?

5 Sitiyenera kunyada chifukwa cha zinthu zimene tachitapo potumikira Yehova, kapena chifukwa cha maudindo amene tili nawo mu mpingo. (1 Mbiri 29:14; 1 Timoteo 6:17, 18) Ndipo ngati tili ndi maudindo aakulu, m’pamenenso timafunika kukhala odzichepetsa kwambiri. Mtumwi Petro analimbikitsa akulu kuti ‘asakhale monga ochita ufumu pa iwo a udindo wawo, koma akhale zitsanzo za gululo.’ (1 Petro 5:3) Akulu amasankhidwa kuti akhale atumiki ndi zitsanzo, osati ambuye ndi mafumu.​—Luka 22:24-26; 2 Akorinto 1:24.

6. Kodi ifeyo monga Akristu timafunika kukhala odzichepetsa m’mbali ziti za moyo wathu?

6 Si akulu okha amene amafunika kukhala odzichepetsa. Polembera amuna ocheperapo msinkhu, omwe angakhale onyada chifukwa choti amatha kuganiza mwamsanga ndiponso ali ndi matupi amphamvu poyerekezera ndi achikulire, Petro anati: “Muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.” (1 Petro 5:5) Indedi, tonsefe tikufunika kwambiri kukhala odzichepetsa monga momwe Kristu analili. Pamafunika kudzichepetsa kuti tilalikire uthenga wabwino, makamaka tikamakumana ndi anthu osafuna kumvetsera kapena omwe amadana nafe. Pamafunikanso kudzichepetsa kuti tigwiritse ntchito uphungu umene tapatsidwa kapena kuti tisinthe zinthu pamoyo wathu kuti usakhale wolira zambiri n’cholinga choti tithe kuchita zambiri mu utumiki. Kuwonjezera pamenepo, timafunika kudzichepetsa ndi kulimba mtima ndiponso chikhulupiriro kuti tipirire anthu ena akamafalitsa nkhani zabodza zotinena, akakhazikitsa malamulo odana nafe, kapena tikamazunzidwa mwankhanza.​—1 Petro 5:6.

7, 8. Kodi njira zimene zingatithandize kukhala odzichepetsa n’ziti?

7 Kodi munthu angasiye bwanji kunyada n’kuyamba kuchita zinthu ‘modzichepetsa mtima, kumaona kuti anzake ndi om’posa iyeyo’? (Afilipi 2:3) Ayenera kudziona monga momwe Yehova amamuonera. Yesu anafotokoza mtima umene tiyenera kukhala nawo pamene anati: “Inunso mmene mutachita zonse anakulamulirani, nenani, Ife ndife akapolo opanda pake, tangochita zimene tayenera kuzichita.” (Luka 17:10) Kumbukirani kuti palibe chilichonse chomwe tingachite chomwe chingapose zomwe Yesu anachita. Komabe, Yesu anali wodzichepetsa.

8 Kuwonjezera apo, tingapemphe Yehova kuti atithandize kuti tizidziona moyenera. Mofanana ndi wamasalmo, tingapemphere kuti: “Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru; pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.” (Salmo 119:66) Yehova angatithandize kuti tikhale ndi nzeru yodziona moyenera, ndipo adzatidalitsa chifukwa cha mtima wathu wodzichepetsa. (Miyambo 18:12) Yesu anati: “Aliyense akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.”​—Mateyu 23:12.

Kukhala ndi Maganizo Oyenera pa Nkhani ya Chabwino ndi Choipa

9. Kodi Yesu anali ndi maganizo otani pa chabwino ndi choipa?

9 Ngakhale kuti Yesu anakhala zaka 33 pakati pa anthu opanda ungwiro, iye anakhalabe “wopanda uchimo.” (Ahebri 4:15) Ndipo polosera za Mesiya, wamasalmo anati: “Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa.” (Salmo 45:7; Ahebri 1:9) Pankhani imeneyinso Akristu amayesetsa kutsanzira Yesu. Sikuti iwo amangodziwa kusiyanitsa chabwino ndi choipa, koma amadana nacho choipa ndi kukonda chabwino. (Amosi 5:15) Zimenezi zimawathandiza kulimbana ndi chibadwa chawo chokonda kuchimwa.​—Genesis 8:21; Aroma 7:21-25.

10. Ngati tipitiriza kuchita zinthu “zoipa” mosalapa, kodi timasonyeza mtima wotani?

10 Yesu anauza Mfarisi wina dzina lake Nikodemo kuti: “Yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake. Koma wochita choonadi adza kukuunika, kuti ntchito zake zionekere kuti zinachitidwa mwa Mulungu.” (Yohane 3:20, 21) Taganizirani mfundo iyi: Yohane anati Yesu ndiye “kuunika kwenikweni, kumene kuunikira anthu onse.” (Yohane 1:9, 10) Koma Yesu anati ngati tichita “zoipa,” zinthu zomwe sizikondweretsa Mulungu, ndiye kuti timadana ndi kuunika. Kodi munthu angafune kudana ndi Yesu ndi mfundo zimene Iye amayendera? Koma zimenezo n’zimene anthu amene amachimwa mosalapa amachita. Mwina iwo saganiza kuti akudana ndi Yesu ndi mfundo zake, koma mmenemo ndi mmene Yesu amawaonera.

Kukhala ndi Maganizo a Yesu pa Nkhani ya Chabwino ndi Choipa

11. Kodi n’chiyani chomwe chili chofunika kwambiri kuti tikhale ndi maganizo a Yesu pa nkhani ya chabwino ndi choipa?

11 Tikufunika kudziwa kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choipa mogwirizana ndi momwe Yehova amaonera zinthu. Palibenso njira ina yodziwira zimenezo kupatulapo kuphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo, basi. Tikamaphunzira Mawu a Mulunguwo, tiyenera kupemphera monga momwe wamasalmo anapempherera, kuti: “Mundidziwitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu.” (Salmo 25:4) Komabe, kumbukirani kuti Satana ndi wonyenga. (2 Akorinto 11:14) Akhoza kuchititsa chinthu choipa kuoneka ngati chabwino kwa Mkristu amene sali tcheru. Choncho timafunika kusinkhasinkha mozama zinthu zimene timawerenga ndi kutsatira mosamala malangizo a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Kuphunzira, kupemphera, ndi kusinkhasinkha zimene timaphunzira kungatithandize kukhwima maganizo ndi kukhala mmodzi wa anthu “amene mwa kuchita nazo anazoloweretsa zizindikiritso zawo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Ahebri 5:14) Tikatero ndiye kuti sitingavutike kudana nacho choipa ndi kukonda chabwino.

12. Kodi ndi malangizo ati a m’Baibulo amene amatithandiza kuti tisamachite zinthu zoipa?

12 Ngati timadana nacho choipa, tiyenera kutchinjiriza mitima yathu kuti isayambe kulakalaka zinthu zoipa. Patapita zaka zambiri Yesu atamwalira, mtumwi Yohane analemba kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichili mwa iye. Pakuti chilichonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi.”​—1 Yohane 2:15, 16.

13, 14. (a) Kodi n’chifukwa chiyani kukonda zinthu za m’dzikoli kuli koopsa kwa Akristu? (b) Kodi tingatani kuti tisayambe kukonda zinthu za m’dzikoli?

13 Ena angaganize kuti si zinthu zonse za m’dzikoli zomwe zili zoipa. Ngakhale zili choncho, dzikoli ndi zokonda zake zingatidodometse kuti tisatumikire bwino Yehova. Ndipo palibe chilichonse cha m’dzikoli chimene cholinga chake n’kutilimbikitsa kuyandikana ndi Mulungu. Choncho tikayamba kukonda zinthu za m’dzikoli, ngakhale zinthu zimene pazokha si zoipa, ndiye kuti tili pangozi. (1 Timoteo 6:9, 10) Ndiponso, zinthu zambiri m’dzikoli n’zoipadi ndipo zingawononge maganizo athu. Ngati tionera mafilimu kapena mapulogalamu a pa TV omwe amasonyeza chiwawa, kukonda chuma, kapena chiwerewere, tingayambe kuona zinthu zimenezo ngati zabwino n’kuyamba kukopeka nazo. Ngati timacheza ndi anthu amene cholinga chawo chachikulu m’moyo ndicho kukhala opeza bwino kapena kupeza mwayi wabwino wa mabizinezi, zinthu zimenezo zikhozanso kusanduka zofunika kwambiri pamoyo wathu.​—Mateyu 6:24; 1 Akorinto 15:33.

14 Koma tikamakonda kwambiri Mawu a Yehova, “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, [ndi] matamandidwe a moyo” sizidzakhalanso zinthu zokopa kwa ife. Kuwonjezera apo, tikamacheza ndi anthu amene amaona kuti zinthu za Ufumu wa Mulungu n’zofunika kwambiri pamoyo wawo, tingayambe kufanana nawo, ndipo tingayambe kukonda zinthu zimene iwowo amakonda ndi kupewa zimene amapewa.​—Salmo 15:4; Miyambo 13:20.

15. Mofanana ndi Yesu, kodi kukonda chilungamo ndi kudana ndi zoipa kungatilimbikitse bwanji?

15 Kudana ndi zoipa ndi kukonda chilungamo kunathandiza Yesu kuika maganizo ake onse pa “chimwemwe choikidwacho pamaso pake.” (Ahebri 12:2) Ifenso tingachite chimodzimodzi. Tikudziwa kuti “dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake.” Chisangalalo chilichonse chimene dzikoli lingapereke n’chakanthawi chabe. Komabe, “iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthawi yonse.” (1 Yohane 2:17) Chifukwa choti Yesu anachita chifuniro cha Mulungu, zinakhala zotheka kuti anthu apeze moyo wosatha. (1 Yohane 5:13) Tiyeni tonsefe timutsanzire ndi kupindula ndi kukhulupirika kwake.

Kupirira Chizunzo

16. N’chifukwa chiyani Yesu analimbikitsa otsatira ake kukondana?

16 Yesu anasonyeza njira ina imene ophunzira ake angamutsanzirire, ndipo anati: “Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake, monga ndakonda inu.” (Yohane 15:12, 13, 17) Pali zifukwa zambiri zimene Akristu amakondera abale awo. Panthawi imeneyi Yesu anali kuganizira makamaka chidani chimene ophunzira akewo anali kudzakumana nacho m’dziko. Iye anati: “Ngati dziko lapansi lida inu, mudziwa kuti lidada Ine lisanayambe kuda inu. . . . Kapolo sali wamkulu ndi mbuye wake. Ngati anandilondalonda Ine, adzakulondalondani inunso.” (Yohane 15:18, 20) Inde, ngakhale akamazunzidwa, Akristu amafanana ndi Yesu. Amafunika kukondana kwambiri kuti athandizane kupirira chidani chimenecho.

17. Kodi n’chifukwa chiyani dzikoli limadana ndi Akristu oona?

17 N’chifukwa chiyani Yesu anati dziko lidzada Akristu? Chifukwa choti, mofanana ndi Yesu, Akristu “siali a dziko lapansi.” (Yohane 17:14, 16) Satenga nawo mbali pankhondo kapena pandale, ndipo amatsatira mfundo za m’Baibulo. Amaona kuti moyo ndi wopatulika ndiponso amatsatira mfundo zapamwamba za makhalidwe abwino pamoyo wawo. (Machitidwe 15:28, 29; 1 Akorinto 6:9-11) Zolinga zawo zazikulu pamoyo zimakhala zauzimu, osati zokhudza chuma. Amakhala m’dzikoli, koma monga momwe Paulo analembera, ‘sachita nalo’ kwambiri. (1 Akorinto 7:31) N’zoona kuti anthu ena anenapo kuti amasirira mfundo zapamwamba zimene Mboni za Yehova zimayendera. Koma Mboni za Yehova sizisintha mfundo zawo kuti anthu awasirire kapena asangalale nawo. Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri m’dzikoli sawamvetsa, ndipo ambiri amawada.

18, 19. Potsatira chitsanzo cha Yesu, kodi Akristu amatani akamatsutsidwa ndi kuzunzidwa?

18 Atumwi a Yesu anaona chidani chachikulu cha dzikoli pamene Yesu anagwidwa ndi kuphedwa, ndipo anaonanso zimene Yesu anachita pamene anali kudedwa choncho. M’munda wa Getsemane, adani a Yesu achipembedzo anabwera kudzamugwira. Petro anayesera kumuteteza ndi lupanga, koma Yesu anauza Petro kuti: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Mateyu 26:52; Luka 22:50, 51) Mu nthawi za m’mbuyomo, Aisrayeli ankagwiritsa ntchito lupanga pomenyana ndi adani awo. Koma tsopano zinthu zinali zitasintha. Ufumu wa Mulungu sunali “wa dziko lino lapansi” ndipo unalibe dziko lapadera lililonse loti uteteze. (Yohane 18:36) Panali patangotsala nthawi yochepa kuti Petro akhale mbali ya mtundu wauzimu, umene anthu ake kwawo kudzakhale kumwamba. (Agalatiya 6:16; Afilipi 3:20, 21) Kuyambira nthawi imeneyi, otsatira a Yesu anayenera kuthana ndi chidani ndi chizunzo monga momwe Yesu anachitira, mopanda mantha koma mwamtendere. Anayenera kusiya zonse m’manja mwa Yehova pokhulupirira kuti adzatsogolera zonse bwinobwino, n’kumudalira kuti awapatsa mphamvu zoti ziwathandize kupirira.​—Luka 22:42.

19 Patapita zaka zingapo, Petro anadzalemba kuti: “Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake; . . . amene pochitidwa chipongwe sanabwezera chipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama.” (1 Petro 2:21-23) Monga momwe Yesu anachenjezera, Akristu akumana ndi chizunzo chankhanza kwa zaka zambiri. M’zaka 100 zoyambirira ndiponso mu nthawi yathu ino, iwo atsatira chitsanzo cha Yesu ndipo akhala ndi mbiri yabwino chifukwa chopirira ndiponso chifukwa chokhalabe ndi chikhulupiriro, ndipo achita zimenezi mwamtendere. (Chivumbulutso 2:9, 10) Tiyeni tonsefe aliyense payekha tizichitanso chimodzimodzi pamene tikufunika kutero.​—2 Timoteo 3:12.

‘Valani Ambuye Yesu Kristu’

20-22. Kodi Akristu ‘amavala Ambuye Yesu Kristu’ motani?

20 Paulo analembera mpingo wa ku Roma kuti: “Valani inu Ambuye Yesu Kristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.” (Aroma 13:14) Akristu amavala Yesu, kunena kwake titero, ngati kuti Yesuyo ndi chovala. Amayesetsa kutsanzira makhalidwe ake ndi zochita zake kwambiri moti amakhala ngati iwowo ndi chithunzi cha Ambuye wawo Yesu, ngakhale kuti ndi opanda ungwiro.​—1 Atesalonika 1:6.

21 Tingathe ‘kuvala Ambuye Yesu Kristu’ bwinobwino ngati tiudziwa bwino moyo wa Yesu n’kuyesetsa kukhala monga momwe iyeyo ankakhalira. Timatsanzira Yesu pa nkhani ya kudzichepetsa, kukonda chilungamo, kudana ndi zoipa, kukonda abale ake, kusakhala mbali ya dziko, ndi kupirira mavuto moleza mtima. ‘Sitiganizira za thupi kuti tichite zofuna zake,’ kutanthauza kuti, cholinga chathu chachikulu m’moyo sichikhala chofuna kupeza zinazake m’dzikoli kapena kukhutiritsa zilakolako za thupi. M’malo mwake, tikamafuna kuchita chinachake kapena tikamalimbana ndi vuto linalake, timadzifunsa kuti: ‘Kodi Yesu akanatani pamenepa? Kodi angafune kuti ineyo nditani?’

22 Pomaliza, timatsanzira Yesu pogwira mwakhama ntchito ‘yolalikira uthenga wabwino.’ (Mateyu 4:23; 1 Akorinto 15:58) Pochita zimenezonso Akristu amatsatira chitsanzo chimene Yesu anawapatsa, ndipo nkhani yotsatirayi ifotokoza momwe amachitira zimenezo.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi n’chifukwa chiyani Mkristu amafunika kwambiri kukhala wodzichepetsa?

• Kodi tingatani kuti tikhale ndi maganizo oyenera pa nkhani ya chabwino ndi choipa?

• Kodi Akristu amatsanzira bwanji Yesu ena akamawatsutsa ndi kuwazunza?

• Kodi zimatheka bwanji ‘kuvala Ambuye Yesu Kristu’?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 7]

Yesu anatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri cha kudzichepetsa

[Chithunzi patsamba 8]

Mbali iliyonse ya moyo wa Mkristu, kuphatikizapo kulalikira, imafuna kudzichepetsa

[Chithunzi patsamba 9]

Satana angachititse Mkristu kuti aziona zosangalatsa zoipa ngati zabwino

[Chithunzi patsamba 10]

Chikondi cha abale athu chingatilimbikitse ena akamatitsutsa