Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kodi Chinsinsi Chanu Chagona Pati?”

“Kodi Chinsinsi Chanu Chagona Pati?”

“Kodi Chinsinsi Chanu Chagona Pati?”

MURIEL, yemwe ndi mayi wa ana atatu, anadabwa atafunsidwa funso limeneli ndi bambo winawake wachikulire pa lesitilanti inayake. Muriel anali atachedwa chifukwa anapita kuchipatala ndi ana ake motero sakanatha kubwerera kunyumba n’kukadya chakudya chamadzulo asanapite kumisonkhano yawo yachikristu. Motero anatenga ana ake kuti akangodya pa lesitilanti inayake ya pafupi.

Akumaliza chakudyacho, bambo wina anafika kwa Muriel n’kunena kuti: “Ndakhala ndikukuyang’anani chifikireni pano. Ndipo ndaona kuti ana anu n’ngosiyana kwambiri ndi ana amene ndimawaona nthawi zonse. Ana ena amachita zofuntha kwambiri ndi matebulo ndiponso mipando. Amapondaponda patebulo. Mipandoyi amangoibalalitsa. Koma ana anuwa onse ndi aphee ndiponso akhalidwe labwino. Kodi chinsinsi chanu chagona pati”

Muriel anayankha kuti: “Ineyo ndi amuna anga timaphunzira Baibulo nthawi zonse ndi ana athu, ndipo timayesetsa kutsatira zimene timaphunzirazo. Ifeyo ndife Mboni za Yehova.” Atamva zimenezi, bamboyo ananena kuti: “Ineyo ndine Wachiyuda ndipo ndinapulumuka panthawi imene chipani cha Nazi chinapulula Ayuda ambirimbiri. Ndimakumbukira mmene a Mboni za Yehova anazunzidwira ku Germany. Komabe iwo ankasiyana kwambiri ndi anthu ena. Khalidwe la ana anuwa landichititsa chidwi kwambiri. Ndiyesetsa kufufuza bwinobwino za chipembedzo chanuchi.”

Baibulo ndi buku labwino kwambiri lokuthandizani kulera ana anu kuti akule bwino. Mboni za Yehova zimafunitsitsa kuthandiza anthu kuti apindule ndi malangizo amene Malemba limapereka. Tikufunitsitsa kuti mutsatire zimene mawu ali m’munsiwa akukupemphani kuchita.