Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tsogolo Lanu Linakonzedweratu?

Kodi Tsogolo Lanu Linakonzedweratu?

Kodi Tsogolo Lanu Linakonzedweratu?

“ANTHU ali ngati zinyama, alibe mphamvu iliyonse yokonza zodzachitika m’tsogolo mwawo,” anatero John Gray, wasayansi wina wokhulupirira zoti anthu anachokera ku zinyama. Shmuley Boteach ananena maganizo osiyana kwambiri ndi amenewa m’buku lake lakuti An Intelligent Person’s Guide to Judaism. Iye anati: “Anthu si zinyama ayi, motero nthawi zonse iwo amakhala ndi mphamvu yokonza zodzachitika m’tsogolo mwawo.”

Anthu ambiri amagwirizana ndi maganizo a Gray ndipo amakhulupirira zoti tsogolo la anthu onse linakonzedwa kale mwachilengedwe. Komano anthu ena amaona kuti anthu anachita kulengedwa ndi Mulungu ndiponso kuti anapatsidwa mphamvu zotha kukonza tsogolo lawo mmene eniakewo akufunira.

Anthu ena amaona kuti tsogolo lawo lili m’manja mwa atsogoleri akuluakulu. Wolemba mabuku wina, dzina lake Roy Weatherford anati: “N’zachidziwikire kuti chifukwa choponderezedwa ndiponso kudyeredwa masuku pamutu, anthu ambiri padziko pano alibe . . . mphamvu zilizonse pa moyo wawo ndipo akazi ambiri, kuyambira kale, ndiwo achita kunyanyira kusowa mphamvu zotere.” (Zachokera m’buku la The Implications of Determinism) Kulimbana pakati zipani zandale ndiponso mayiko kwalepheretsa anthu ambiri kukhala ndi tsogolo labwino limene ankaliganizira.

Kuyambira kale anthu ena akhala akusowa pogwira chifukwa choganiza kuti tsogolo lawo lili m’manja mwa mizimu. Boteach uja anati: “Kwa Agiriki akale, kukhala n’chiyembekezo chinachake ankakuona ngati kutaya nthawi chabe chifukwa iwo ankaona kuti zochitika za pamoyo wa anthu zinakonzedwa kale.” Iwowo ankaona kuti zochitika zonse za pamoyo wa munthu zimakonzedwa ndi milungu inayake yaikazi yomwe ili yosapanganika. Iwo ankakhulupirira kuti milungu imeneyi inakonzeratu nthawi imene munthu aliyense adzafe komanso mavuto ndiponso ululu wonse umene munthuyo adzamve pamoyo wake.

Masiku ano chikhulupiriro chakuti zochitika zonse za pamoyo wa anthu zili m’manja mwa munthu winawake wauzimu n’chofala. Mwachitsanzo anthu ambiri amakhulupirira kuti Mulungu anakonzeratu zotsatira za chilichonse chimene anthu amachita ndiponso nthawi imene munthu aliyense adzafe. Ena amakhulupirira chiphunzitso choti zinthu zonse zimachitika mwa chikonzero cha Mulungu ndipo chiphunzitsochi chimalimbikitsa mfundo yakuti “chipulumutso kapenanso chiwonongeko cha munthu aliyense chinakonzedwa kale” ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Anthu ambiri omwe amadziona kuti ndi Akristu amakhulupirira chiphunzitso chimenechi.

Kodi inuyo mumaiona bwanji nkhaniyi? Kodi tsogolo lanu linakonzedwa kale moti mulibe mphamvu iliyonse yochitapo kanthu pa tsogolo lanulo? Kapena kodi zimene ananena Mngelezi wina wolemba zisudzo dzina lake William Shakespeare n’zoona ndithu? Iye anati: “Nthawi zina zinthu zimene zimawachitikira anthu pamoyo wawo zimawachitikira chifukwa cha zochita zawo.” Taonani zimene Baibulo limanena pankhaniyi.