Kulalikira kwa Saulo Kunamudanitsa ndi Anthu
Kulalikira kwa Saulo Kunamudanitsa ndi Anthu
AYUDA a ku Damasiko sankamvetsa kuti zinatheka bwanji kuti munthu wakhama kwambiri polimbikitsa chipembedzo chodziwika panthawiyo apanduke. Saulo anali munthu wodziwika ndi zozunza anthu amene ankakhulupirira Yesu ku Yerusalemu. Ku Damasiko anapitirako zozunza anthu zomwezo. Komano Saulo yemweyo, tsopano anali kulalikira kuti munthu yemwe ankati n’chigawenga uja, amene anapachikidwa chifukwa chochitira mwano Mulungu, ndiye Mesiya. Kodi Saulo anali atapenga?—Machitidwe 9:1, 2, 20-22.
Ayi, panali chifukwa chomveka. Anthu ena amene anali ndi Saulo paulendo wochoka ku Yerusalemu ayenera kuti anasimba zimene zinachitika pamsewu. Atayandikira Damasiko, kuwala kunaoneka mwadzidzidzi kuzungulira ponse pamene iwo anali, ndipo onse anagwa pansi. Anamvanso mawu. Aliyense anali bwinobwino, kupatulapo Saulo. Iye anali chigonere pamsewupo. Kenaka atadzuka, anzakewo anachita kumugwira padzanja kupita naye ku Damasiko, chifukwa sankatha kuona chilichonse.—Machitidwe 9:3-8; 26:13, 14.
Mdani Anasanduka Bwenzi
Kodi n’chiyani makamaka chimene chinam’chitikira Saulo pamsewu wopita ku Damasikowu? Kodi mwina anafooka kwambiri chifukwa cha kutalika kwa ulendowu kapenanso chifukwa choti masana onse dzuwa linathera pa iwo? Pofuna kupeza chifukwa china osati chokhudza zinthu zauzimu, anthu okayikira nkhaniyi masiku ano, amanena kuti mwina Sauloyu ankaona zideruderu. Kapena amati mwina chikumbumtima cha nkhanza zimene anachita chinam’sokoneza maganizo, mwinanso pamenepa mutu wake sumagwira bwinobwino, ndipo ena amati n’kutheka kuti anali ndi matenda a khunyu.
Komatu zoona zake n’zakuti Yesu Kristu anaonekera kwa Saulo pakati pa kuwala kwakukuluko, ndipo anamukhutiritsa Sauloyo kuti Iye anali Mesiya. Zojambula zina zokhudza nkhaniyi zimaonetsa Saulo akugwa pa kavalo. Ngakhale kuti n’zotheka kuti anagwa pakavalo, Baibulo limangonena kuti iye ‘anagwa pansi.’ (Machitidwe 22:6-11) Zoti Saulo anagwa bwanji kuti afike pansi zilibe ntchito kwenikweni koma nkhani yagona pa kugwa kumene anachita nako manyazi kwambiri, komwe ndi kugwa paudindo umene anali nawo. Tsopano iye anayenera kuvomereza kuti zimene otsatira Yesu ankalalikira zinali zoona. Sakanachitira mwina koma kuyamba kulalikira nawo zimenezi. Poyamba, Saulo anali munthu wodana kwambiri ndi uthenga wa Yesu, koma tsopano anakhala munthu wolalikira uthengawu mwakhama kwambiri. Atayambanso kuona, kenaka n’kubatizidwa, “Saulo anakula makamaka mumphamvu, nadodometsa Ayuda akukhala m’Damasiko, nawatsimikizira kuti ameneyo ndi Kristu.”—Machitidwe 9:22.
Chiwembu Chomupha Chinalephereka
Kodi Saulo, amene patsogolo pake anadzatchedwa kuti Paulo anapita kuti atatembenuka? M’kalata imene analembera Agalatiya iye anati: “Ndinamuka ku Arabiya, ndipo ndinabweranso ku Damasiko.” (Agalatiya 1:17) Mawu akuti “Arabiya” angatanthauze malo ena aliwonse a m’chigawo cha chisumbu cha Arabiya. Anthu ena ophunzira amanena kuti Paulo ayenera kuti anapita ku chipululu cha Suriya kapena kuchigawo china cha ku Nabataea mu ufumu wa Areta Wachinayi. N’zosakayikitsa kuti Saulo atabatizidwa ayenera kuti anapita ku malo enaake kwayekha kuti akasinkhesinkhe, monga mmene Yesu anapitira kuchipululu atabatizidwa.—Luka 4:1.
Saulo atabwerera ku Damasiko, “Ayuda anapangana kuti amuphe.” (Machitidwe 9:23) Bwanamkubwa amene ankaimira Mfumu Areta ku Damasiko anaika alonda mumzindawo kuti agwire Saulo. (2 Akorinto 11:32) Koma ngakhale kuti adani ankafuna kupha Saulo, ophunzira a Yesu anakonza zomuthawitsa.
Ena mwa anthu amene anam’thandiza Saulo kuthawa anali Hananiya ndiponso ophunzira ena amene mtumwiyu anayamba kuchezerana nawo atangotembenuka. * (Machitidwe 9:17-19) Anthu ena amene anadzakhala okhulupirira chifukwa cha kulalikira kwa Saulo ku Damasiko ayeneranso kuti anam’thandiza. Tikutero chifukwa choti lemba la Machitidwe 9:25 limati: “Ophunzira ake anam’tenga usiku, nam’pyoletsa palinga, nam’tsitsa ndi mtanga.” Mawu akuti “ophunzira ake” n’kutheka kuti akutanthauza anthu amene Saulo anawaphunzitsa. Komabe mfundo n’njakuti n’zosakayikitsa kuti anthu ena anayamba kudana naye kwambiri kuposa kale chifukwa cha kuyenda bwino kwa utumiki wake.
Zoyenera Kuphunzirapo
Tikaona zochitika zina zokhudza mmene Saulo anatembenukira ndi kubatizidwa, timaona bwinobwino kuti iye sankadandaula ndi mmene anthu ena ankamuonera; ndipo sanasiye utumiki wake chifukwa chovutitsidwa kwambiri. Kwa Saulo, chinthu chofunika kwambiri chinali ntchito yolalikira imene anapatsidwa.—Machitidwe 22:14, 15.
Kodi mwangomvetsetsa chaposachedwapa mfundo yakuti uthenga wabwino n’ngofunika kuulalikira? Ndiyetu dziwani kuti Akristu onse oona ayenera kulalikira za Ufumu. Musamadabwe mukaona kuti nthawi zina ulaliki wanu ukuchititsa kuti anthu ayambe kukuvutitsani. (Mateyu 24:9; Luka 21:12; 1 Petro 2:20) Tiyenera kutsanzira zimene Saulo anachita povutitsidwa m’njira imeneyi. Akristu amene amapirira ziyeso, osagonja adzadalitsidwa ndi Mulungu. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Anthu onse adzadana ndi inu chifukwa cha dzina langa.” Komabe, iye anawatsimikizira kuti: “Mudzakhala nawo moyo wanu m’chipiriro.”—Luka 21:17-19.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 10 N’zotheka kuti ku Damasiko Chikristu chinafikako Yesu atalalikira ku Galileya kapena pambuyo pa chikondwerero cha Pentekoste cha mu 33 C.E.—Mateyu 4:24; Machitidwe 2:5.
[Chithunzi patsamba 28]
Saulo ‘anagwa pansi’ Yesu atamuonekera
[Chithunzi patsamba 29]
Saulo anathawa chiwembu chofuna kumupha ku Damasiko