Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi zinatheka bwanji kuti Samsoni agwire mitembo ya anthu amene anapha koma n’kupitirizabe kukhala Mnaziri?

Kale ku Israyeli, munthu ankafuna yekha kulumbira ndi kukhala Mnaziri kwa nthawi yomwe iye angasankhe. * Chimodzi mwa zinthu zimene munthu wopanga lumbiroli ankaletsedwa chinali chakuti: “Masiku onse akudzipatulira kwa Yehova asayandikize mtembo. Asadzidetse ndi atate wake, kapena mayi wake, mbale wake, kapena mlongo wake, akafa iwowa.” Koma bwanji ngati wina ‘wafa chikomo [kapena kuti mwadzidzidzi] pali iye’? Kukhudza mtembo mwangozi ngati kumeneko kunkadetsa munthu amene anapanga lumbirolo. Motero, lamulo la lumbirolo linali lakuti: “Masiku adapitawa azikhala chabe.” Ankafunika kuchita mwambo wodziyeretsa ndi kuyambiranso nthawi yake yokhala Mnaziri.​—Numeri 6:6-12.

Koma Samsoni anali Mnaziri wamtundu wina. Iye asanabadwe, mngelo wa Yehova anauza amayi ake kuti: “Taona, udzaima, nudzabala mwana wamwamuna; pamutu pake sipadzafika lumo; pakuti mwanayo adzakhalira kwa Mulungu Mnaziri chibadwire; nadzayamba iye kupulumutsa Israyeli m’dzanja la Afilisti.” (Oweruza 13:5) Samsoni sanalumbire kukhala Mnaziri. Mulungu ndiye anam’sankha kuti akhale Mnaziri, ndipo anayenera kukhala Mnaziri moyo wake wonse. Lamulo loletsa kukhudza mtembo silikanagwira ntchito kwa iyeyo. Likanakhala logwira ntchito kwa iyeyo ndiye kuti ngati akanakhudza mtembo mwangozi, kodi zikanatheka bwanji kuti ayambirenso moyo wake wokhala Mnaziri womwe unayambira pa kubadwa kwake? Motero, zikuoneka kuti malamulo a anthu okhala Anaziri kwa moyo wawo wonse ankasiyanako ndi malamulo a Anaziri ochita kungodzipereka kwa kanthawi.

Taonani zimene Yehova analamula anthu atatu otchulidwa m’Baibulo amene anakhala Anaziri kwa moyo wawo wonse. Anthuwa ndi Samsoni, Samueli, ndi Yohane Mbatizi. Monga momwe taonera kale, Samsoni sankayenera kumeta tsitsi. Hana asanatenge n’komwe pathupi pa Samueli, analumbiriratu kuti: “Ndidzam’pereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.” (1 Samueli 1:11) Kumbali ya Yohane Mbatizi, mngelo wa Yehova anati: “Sadzamwa konse vinyo kapena kachasu.” (Luka 1:15) Komanso, “Yohane . . . anali nacho chovala chake cha ubweya wa ngamila, ndi lamba lachikopa m’chuuno mwake; ndi chakudya chake chinali dzombe ndi uchi wakuthengo.” (Mateyu 3:4) Palibe ndi mmodzi yemwe wa anthu atatuwa amene analamulidwa kuti asayandikire mtembo.

Ngakhale kuti Samsoni anali Mnaziri, anali mmodzi mwa oweruza amene Yehova anautsa kuti apulumutse Aisrayeli m’manja mwa anthu amene ankawafunkhira zinthu. (Oweruza 2:16) Ndipo pogwira ntchito yomwe anapatsidwayi, iye ankagwira mitembo. Panthawi ina, Samsoni anapha Afilisti okwana 30 ndi kuwavula zovala. Pambuyo pake, anakantha kwambiri adani ake. Anatenganso chibwano chatsopano cha bulu ndi kupha nacho amuna 1,000. (Oweruza 14:19; 15:8, 15) Zonse zimene Samsoni anachitazi zinali kum’sangalatsa Yehova ndiponso Yehovayo anali kum’thandiza. Malemba amafotokoza kuti Samsoni ndi munthu amene anali wa chitsanzo chabwino cha chikhulupiriro.​—Ahebri 11:32; 12:1.

Kodi mawu akuti Samsoni anang’amba mkango “monga akadang’amba mwana wa mbuzi” akusonyeza kuti masiku amenewo zong’amba ana a mbuzi zinali zofala?

Palibe umboni wosonyeza kuti m’nthawi za Oweruza a Israyeli, zong’amba ana a mbuzi zinali zofala. Lemba la Oweruza 14:6 limati: ‘Unam’gwera [Samsoni] kolimba mzimu wa Yehova, nang’amba [mwana wa mkango] monga akadang’amba mwana wa mbuzi, wopanda kanthu m’dzanja lake.’ N’kutheka kuti ndemangayi inaikidwa monga fanizo.

Mawu akuti ‘anaung’amba’ angathe kutanthauza zinthu ziwiri. N’kutheka kuti Samsoni anathyola zibwano za mkangowo kapena anaukhadzula ziwalo. Ngati mawu amenewa akutanthauza kuti Samsoni anauthyola zibwano mkangowo, ndiye kuti kwenikweni akunena kuti n’zotheka kuti munthu achitenso chimodzimodzi ndi mwana wa mbuzi. Ngati ndi choncho, fanizoli likusonyeza kuti kwa Samsoni, kupha mkango alibe chida chilichonse siinali nkhani chifukwa kunali ngati kupha mwana wa mbuzi. Komano bwanji ngati Samsoni anapha mkangowo mwa kuukhadzula ziwalo? Apo tinganene kuti ndemangayi ikungoyerekezera chabe zinthuzo. Mfundo ya fanizoli ingakhale yakuti mzimu wa Yehova unapatsa Samsoni mphamvu zochitira zinthu zomwe zimafunikira nyonga zapadera. Mulimonse mmene nkhaniyi ingakhalire, mfundo n’njakuti fanizo la pa Oweruza 14:6 limasonyeza kuti mothandizidwa ndi Yehova, kwa Samsoni mkango wamphamvu kwambiri sunali chinyama choopsa koma unali ngati mmene wina aliyense amaonera katonde ka mbuzi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Zinali kwa munthu amene akulumbirayo kudzisankhira kutalika kwa nthawi yomwe akufuna kukhala Mnaziri. Koma, malinga ndi nkhani zakale za Ayuda, nthawi yomwe munthu angakhale Mnaziri inkayambira pa masiku 30. Ankaganiza kuti kupanga lumbiro la masiku osakwana 30 kukanachitititsa kuti lumbiroli lingokhala ngati lumbiro wamba.