Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Masomphenya a Ufumu wa Mulungu Asanduka Zenizeni

Masomphenya a Ufumu wa Mulungu Asanduka Zenizeni

Masomphenya a Ufumu wa Mulungu Asanduka Zenizeni

‘Muchita bwino posamalira [mawu aulosi], monga nyali younikira m’malo a mdima.’​—2 PETRO 1:19.

1. Kodi m’dzikoli tikuona kusiyana kotani?

MASIKU ano m’dzikoli muli mavuto ochita kusowa popumira. Pali mavuto ambirimbiri monga kuwonongeka kwa zachilengedwe, uchigawenga wapadziko lonse, ndi enanso osiyanasiyana ndipo zikuoneka kuti anthu sangachitepo chilichonse chothetsa mavutowa. Ngakhale zipembedzo za padzikoli zalephera kuthandizapo. Ndipotu kunena zoona, zipembedzozi zimangothandizira kuti zinthu zipitirire kuwonongeka, chifukwa zimalimbikitsa makhalidwe ogawanitsa anthu monga kusalolera maganizo a ena, udani, ndiponso kusankhana mitundu. Zoonadi, mogwirizana ndi zomwe zinanenedwa kale, “mdima wa bii” waphimba “mitundu ya anthu.” (Yesaya 60:2) Komabe, ngakhale kuti zinthu zili chonchi, pali anthu ambirimbiri amene sakayika n’komwe kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino. N’chifukwa chiyani amatero? Chifukwa chakuti amatsatira mawu a Mulungu aulosi “monga nyali younikira m’malo a mdima.” Iwo alola “mawu” kapena kuti uthenga wa Mulungu, womwe tsopano uli m’Baibulo, kuwatsogolera pamoyo wawo.​—2 Petro 1:19.

2. Mogwirizana ndi ulosi wa Danieli wonena za “nthawi ya chimaliziro,” kodi ndani okha amene akuthandizidwa kuzindikira zinthu zauzimu?

2 Ponenapo za “nthawi ya chimaliziro,” mneneri Danieli analemba kuti: “Ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka. Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.” (Danieli 12:4, 10) Anthu okhawo amene moona mtima ‘akuthamanga chauko ndi chauko,’ kapena kuti kuchita khama pophunzira Mawu a Mulungu, kutsatira mfundo zake, ndi kuyesetsa kuchita zofuna zake, ndiwo akuthandizidwa kuzindikira zinthu zauzimu.​—Mateyu 13:11-15; 1 Yohane 5:20.

3. M’zaka za m’ma 1870, kodi ophunzira Baibulo oyambirira anazindikira mfundo yofunika ya choonadi iti?

3 Kale kwambiri, m’ma 1870, “masiku otsiriza” asanayambe, Yehova Mulungu anayamba kuwazindikiritsa bwino anthu za “zinsinsi za Ufumu wa Kumwamba.” (2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 13:11) Nthawi imeneyo, gulu la ophunzira Baibulo linazindikira kuti kubweranso kwa Kristu kunali kosaoneka, ndipo izi zinali zosiyana ndi zimene anthu ambiri ankaganiza. Ataikidwa pampando waufumu kumwamba, Yesu anabweranso m’njira yakuti anaika chidwi chake padziko lapansi monga Mfumu yake. Chizindikiro chooneka ndi maso chokhala ndi mbali zambirimbiri chinathandiza ophunzira ake kuzindikira kuti kukhalapo kwake mosaoneka kwayamba.​—Mateyu 24:3-14.

Chithunzithunzi Chisanduka Zenizeni

4. Kodi Yehova walimbitsa motani chikhulupiriro cha atumiki ake amakono?

4 Masomphenya a kusandulika kwa Yesu anali chithunzithunzi chabwino kwambiri cha Kristu mu ulemerero wake wa Ufumu. (Mateyu 17:1-9) Masomphenya amenewo analimbitsa chikhulupiriro cha Petro, Yakobo, ndi Yohane panthawi yomwe anthu ambiri anali atasiya kutsatira Yesu chifukwa chakuti iye sanachite zinthu zimene iwo ankamuyembekezera kuchita, ndipo zimene iwo ankafunazo zinali zosagwirizana ndi Malemba. Mofanana ndi zimenezi, m’masiku otsiriza ano, Yehova walimbitsa chikhulupiriro cha atumiki ake amakono mwa kuwathandiza kumvetsetsa kukwaniritsidwa kwa masomphenya ochititsa chidwiwo limodzinso ndi maulosi ena okhudza masomphenyawo. Tiyeni tsopano tione zina mwa zinthu zenizeni zauzimu zimenezi zomwe ndi zolimbitsa chikhulupiriro.

5. Kodi Nthanda ndani ndipo ‘anauka’ liti?

5 Pofotokoza za kusandulika kwa Yesu, mtumwi Petro analemba kuti: “Ndipo tili nawo mawu a chinenero [“mawu aulosi,” NW] okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mitima yanu.” (2 Petro 1:19) Nthanda kapena kuti “nyenyezi yonyezimira ya nthanda” yophiphiritsira imeneyo, ndi Yesu Kristu atapatsidwa ulemerero. (Chivumbulutso 22:16) ‘Anauka’ mu 1914 pamene Ufumu wa Mulungu unabadwa kumwamba, n’kukhala chizindikiro cha mbandakucha wa nyengo yatsopano. (Chivumbulutso 11:15) M’masomphenya a kusandulika kwa Yesu, pambali pa Yesu panaoneka Mose ndi Eliya, akulankhula naye. Kodi iwo anali kuimira ndani?

6, 7. Mose ndi Eliya anaimira ndani pa kusandulika kwa Yesu, ndipo kodi Malemba amasonyeza mfundo zofunika zotani zokhudza anthu omwe anaimiridwa ndi Mose ndi Eliya?

6 Popeza kuti Mose ndi Eliya nawonso anali ndi ulemerero womwe Kristu anali nawo, mboni ziwiri zokhulupirikazi zikuimira anthu amene adzalamulire ndi Yesu mu Ufumu wake. Mfundo yakuti Yesu adzakhala ndi anthu olamulira naye ikugwirizana ndi masomphenya a chithunzithunzi cha Mesiya ataikidwa pampando wa ufumu amene mneneri Danieli anaona. Danieli anaona “wina ngati mwana wa munthu” akulandira “ulamuliro wosatha” kuchokera kwa “Nkhalamba ya kale lomwe,” yomwe ndi Yehova Mulungu. Komano onani zomwe Danieli anaonetsedwa patangotha nthawi yochepa. Iye analemba kuti: ‘Ufumu, ndi ulamuliro, ndi ukulu wa maufumu, pansi pa thambo lonse, zidzapatsidwa kwa anthu opatulika a Wam’mwambamwamba.’ (Danieli 7:13, 14, 27) Zaka zoposa 500 kusandulika kwa Yesu kusanachitike, Mulungu anasonyeza kuti anthu ena “opatulika” adzalamulira nawo limodzi ndi Kristu mu ulemerero wa Ufumu.

7 Kodi opatulika amene Danieli anaona m’masomphenya ndani? Mtumwi Paulo anali kunena za anthu amenewa pamene anati: “Mzimu yekha achita umboni pamodzi ndi mzimu wathu, kuti tili ana a Mulungu; ndipo ngati ana, pomweponso olowa nyumba; inde olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Kristu; ngatitu ife timva zowawa pamodzi naye, kuti tikalandirenso ulemerero pamodzi ndi iye.” (Aroma 8:16, 17) Opatulika amenewa sangakhalenso ena ayi, koma ophunzira a Yesu odzozedwa ndi mzimu. M’masomphenya a m’Chivumbulutso, Yesu akuti: “Iye wakulakika, ndidzam’patsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinalakika, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.” ‘Olakika’ oukitsidwa amenewa, okwana 144,000, adzalamulira pamodzi ndi Yesu dziko lonse lapansi.​—Chivumbulutso 3:21; 5:9, 10; 14:1, 3, 4; 1 Akorinto 15:53.

8. Kodi ophunzira odzozedwa a Yesu agwira ntchito yotani yofanana ndi ya Mose ndi Eliya, ndipo zotsatira zake zakhala zotani?

8 Komano, n’chifukwa chiyani Akristu odzozedwa akuimiridwa ndi Mose ndi Eliya? Chifukwa chake n’chakuti Akristu amenewa, panthawi imene ali ndi matupi a anthu, amagwira ntchito yofanana ndi yomwe Mose ndi Eliya anagwira. Mwachitsanzo, iwo amakhala mboni za Yehova, ngakhale panthawi yomwe akuzunzidwa. (Yesaya 43:10; Machitidwe 8:1-8; Chivumbulutso 11:2-12) Mofanana ndi Mose ndi Eliya, iwo molimba mtima amanena poyera za chipembedzo chonyenga, kwinaku akulimbikitsa anthu oona mitima kuti ayambe kulambira Mulungu ndi mtima wosagawanika. (Eksodo 32:19, 20; Deuteronomo 4:22-24; 1 Mafumu 18:18-40) Kodi ntchito yawo yabala zipatso? Inde kwambiri! Kuwonjezera pa kuthandiza kusonkhanitsa anthu kuti chiwerengero cha odzozedwa chikwanire, iwo athandizanso anthu ambiri a “nkhosa zina” kuti azimvera Yesu Kristu ndi mtima wonse.​—Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:4.

Yesu Akumaliza Kugonjetsa

9. Kodi lemba la Chivumbulutso 6:2 limasonyeza motani mmene Yesu alili masiku ano?

9 Yesu tsopano si munthu wamba wokwera pa mwana wa bulu, koma ndi Mfumu yamphamvu. Baibulo limafotokoza kuti wakwera pa kavalo, chomwe m’Baibulo chili chizindikiro cha nkhondo. (Miyambo 21:31) “Taonani, kavalo woyera,” likutero lemba la Chivumbulutso 6:2, “ndipo wom’kwerayo anali nawo uta; ndipo anam’patsa korona; ndipo anatulukira wolakika kuti alakike.” Komanso ponena za Yesu, wamasalmo Davide analemba kuti: “Yehova adzatumiza ndodo ya mphamvu yanu kuchokera ku Ziyoni; Chitani ufumu pakati pa adani anu.”​—Salmo 110:2.

10. (a) Kodi ulendo wa Yesu wogonjetsa unayamba bwino motani? (b) Kodi kupambana koyambirira kwa Yesu kunakhudza motani dziko lapansi?

10 Oyamba kugonjetsedwa ndi Yesu anali adani ake amphamvu kwambiri, Satana ndi ziwanda. Atawathamangitsa kumwamba, anawaponyera kudziko lapansi. Pozindikira kuti nthawi yawo yatsala yochepa, mizimu yoipa imeneyi yalusira anthu, zomwe zadzetsa masoka aakulu. M’buku la Chivumbulutso, masoka amenewa akuimiridwa ndi okwera pakavalo ena atatu. (Chivumbulutso 6:3-8; 12:7-12) Mogwirizana ndi ulosi wa Yesu wofotokoza za ‘chizindikiro cha kufika kwake, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano,’ apakavalo amenewa achititsa kuti pakhale nkhondo, njala, ndiponso milili yoopsa kwambiri. (Mateyu 24:3, 7; Luka 21:7-11) Mofanana ndi ululu womwe mayi amamva pobereka, n’zosakayikitsa kuti “zowawa” zimenezi zidzapitiriza kuchuluka ndiponso kupweteka kwambiri mpaka Kristu ‘atamaliza ntchito yake yogonjetsa,’ mwa kuwononga chilichonse chokhudza gulu looneka ndi maso la Satana. *​—Mateyu 24:8.

11. Kodi mbiri ya mpingo wa wachikristu ikusonyeza motani mphamvu zimene Kristu ali nazo monga Mfumu?

11 Mphamvu zimene Yesu ali nazo monga Mfumu zikuonekanso chifukwa chakuti wasunga mpingo wachikristu kuti ugwire ntchito yomwe wapatsidwa yolalikira uthenga wabwino padziko lonse. Ngakhale kuti mpingowu ukuvutitsidwa kwambiri ndi Babulo Wamkulu, yemwe ndi ufumu wa dziko wa chipembedzo chonyenga, ndiponso ukuvutitsidwa ndi maboma ankhanza, ntchito yolalikira yapitirirabe komanso yayenda bwino kwambiri moti pamene yafika panopo m’poti siinafikeponso n’kale lonse. (Chivumbulutso 17:5, 6) Uwutu ndi umboni wamphamvu kwambiri wosonyeza kuti Kristu ndi mfumu.​—Salmo 110:3.

12. N’chifukwa chiyani anthu sazindikira kukhalapo kosaoneka kwa Kristu?

12 Koma zomvetsa chisoni n’zakuti anthu ambiri, kuphatikizapo miyandamiyanda ya anthu amene amati ndi Akristu, satha kuzindikira kuti zinthu zikuluzikulu zomwe zikuchitika padziko pano zikuimira zinthu zenizeni zosaoneka. Iwowa mpaka amafika ponyoza anthu amene amalengeza za Ufumu wa Mulungu. (2 Petro 3:3, 4) Kodi n’chifukwa chiyani amatero? Chifukwa chakuti Satana wachititsa khungu maganizo awo. (2 Akorinto 4:3, 4) Ndipotu, anayamba kale kwambiri kuwaphimba m’maso anthu odzitcha Akristuwa, n’kufika mpaka powasiyitsa kuyembekezera Ufumu wofunika kwambiriwo.

Anthu Asiya Kuyembekezera Ufumu

13. Kodi mdima wauzimu umene anthu odzitcha Akristu alimo wawachititsa zotani?

13 Yesu ananeneratu kuti mofanana ndi namsongole amene wafesedwera limodzi ndi tirigu, anthu ampatuko adzalowerera mu mpingo wachikristu ndi kusokeretsa anthu ambiri. (Mateyu 13:24-30, 36-43; Machitidwe 20:29-31; Yuda 4) M’kupita kwa nthawi, anthu odzitcha Akristuwo anayamba kutengera nawo mapwando, miyambo, ndi ziphunzitso zachikunja, mpaka kufika pomanena kuti zimenezi ndi “zachikristu.” Mwachitsanzo, Khirisimasi inayambira ku miyambo yolambira milungu yachikunja yomwe mayina awo anali Mithra ndi Saturn. Koma kodi n’chiyani chinachititsa anthu odzitcha Akristu amenewa kutengera mapwando achikunjawa? Buku la The New Encyclopædia Britannica (1974) limati: “Khirisimasi, phwando lokondwerera kubadwa kwa Yesu, linakhazikitsidwa chifukwa chakuti anthu anayamba kuona kuti Kristu sabwera mwamsanga.”

14. Kodi zinthu zimene Origen ndi Augustine anaphunzitsa zinapotoza motani tanthauzo lenileni la Ufumu?

14 Komanso taonani kupotozedwa kwa tanthauzo la mawu akuti “ufumu.” Buku la The Kingdom of God in 20th-Century Interpretation limati: “Origen [yemwe anali wamaphunziro apamwamba a zaumulungu m’zaka za m’ma 200] ndiye anayambitsa zoti Akristu aziona kuti ‘ufumu’ umatanthauza ulamuliro wa Mulungu mumtima mwa anthu.” Kodi Origen anatenga kuti zimenezi? Sanazitenge m’Malemba, koma “kuchokera m’maganizo a anthu amene amati ndi anzeru ndiponso anatengera mmene dziko limaonera zinthu, ndipotu izi ndi zosiyana kwambiri ndi maganizo a Yesu ndiponso a tchalitchi choyambirira.” M’buku lake la De Civitate Dei (Mzinda wa Mulungu), Augustine wa ku Hippo (amene anabadwa mu 354 ndi kumwalira mu 430 C.E.) ananena kuti tchalitchi chenichenicho ndiye Ufumu wa Mulungu. Maganizo osachokera m’Malemba amenewa apatsa Matchalitchi Achikristu zifukwa zachipembedzo zokhalira ndi mphamvu pandale. Ndipo matchalitchiwa akhala ndi mphamvu zimenezi kwa zaka zambiri, komanso nthawi zambiri akhala akugwiritsa ntchito mphamvuzi mwankhanza zosaneneka.​—Chivumbulutso 17:5, 18.

15. Kodi lemba la Agalatiya 6:7 lakwaniritsidwa motani pa Matchalitchi ambiri Achikristu?

15 Komabe, masiku ano matchalitchiwa akututa zimene anafesa. (Agalatiya 6:7) Zikuoneka kuti matchalitchi ambiri ayamba kuchepa mphamvu ndiponso Akristu awo ayamba kuchepa. Izi zikuonekera kwambiri ku Ulaya. Malinga ndi zomwe inanena magazini ya Christianity Today, ‘matchalitchi akuluakulu ku Ulaya salinso nyumba zolambiriramo koma nyumba zosungiramo zinthu zochititsa chidwi, ndipo mumangopezeka alendo okaona malo basi.’ M’madera enanso a dziko lapansili mukuchitika zinthu zofananazi. Kodi izi zikusonyeza kuti chipembedzo chonyenga chikulowera kuti? Kodi chipembedzochi chidzangotha chifukwa chosowa thandizo la zachuma komanso kuchepa kwa Akristu ake? Ndipo kodi kulambira koona kungadzakhudzidwe motani?

Konzekerani Tsiku Lalikulu la Mulungu

16. Kodi n’chifukwa chiyani kuchuluka kwa anthu odana ndi Babulo Wamkulu kuli kofunika kukuganizira bwino?

16 Phiri lomwe linaphulikapo koma lakhala nthawi yaitali osaphulikanso, likamatuluka utsi ndi phulusa, zimasonyeza kuti sipatenga nthawi yaitali, phirilo liphulika. Mofanana ndi zimenezi anthu omwe akudana ndi chipembedzo m’madera ambiri a dziko lapansili akumka nawonjezeka ndipo ichi n’chizindikiro chakuti chipembedzo chonyenga chitha posachedwapa. Posachedwapa, Yehova achititsa kuti magulu andale padzikoli agwirizane pomuika pambalambanda Babulo Wamkulu mkazi wachigololo chauzimu ndiponso pomusakaza. (Chivumbulutso 17:15-17; 18:21) Kodi Akristu oona ayenera kuchita mantha ndi zimenezi komanso zinthu zina zokhudza ‘chisautso chachikulu’ zomwe zidzatsatirepo? (Mateyu 24:21) Ayi. Iwo adzakhala ndi zifukwa zosangalalira pamene Mulungu akulanga anthu oipa. (Chivumbulutso 18:20; 19:1, 2) Taonani chitsanzo cha Yerusalemu wa m’zaka 100 zoyambirira ndiponso cha Akristu omwe ankakhalamo.

17. Kodi n’chifukwa chiyani atumiki okhulupirika a Yehova sangakhale ndi mantha alionse pamene mapeto a dongosolo ili akufika?

17 Asilikali a Aroma atazinga Yerusalemu mu 66 C.E. Akristu atcheru mwauzimu sanadabwe kapena kuchita mantha. Popeza kuti iwo anali kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu, anadziwa “kuti chipululutso chake chayandikira.” (Luka 21:20) Iwo anadziwanso kuti Mulungu adzawatsegulira njira yothawira kupita kumalo abata. Izi zitachitika, Akristu anathawa. (Danieli 9:26; Mateyu 24:15-19; Luka 21:21) N’chimodzimodzinso masiku ano, anthu odziwa Mulungu ndiponso omvera Mwana wake sangakhale ndi mantha alionse pamene mapeto a dongosolo ili akufika. (2 Atesalonika 1:6-9) Ndipo, chisautso chachikulu chikadzayamba, iwo mosangalala ‘adzaweramuka, natukula mitu yawo; chifukwa chodziwa kuti chiwomboledwe chawo chayandikira.’​—Luka 21:28.

18. Kodi zotsatira za kuukira atumiki a Yehova komaliza kumene Gogi adzachite zidzakhala zotani?

18 Babulo Wamkulu atawonongedwa, mwa mphamvu zonse Satana, monga Gogi wa Magogi, adzaukira Mboni zokonda mtendere za Yehova. Pobwera “ngati mtambo wakuphimba dziko,” magulu a Gogi adzayembekezera kuti kugonjetsa gululi kudzakhala kosavuta. Koma adzakhumudwa kwambiri. (Ezekieli 38:14-16, 18-23) Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndinaona mutatseguka m’Mwamba; ndipo taonani, kavalo woyera, ndi Iye wakum’kwera wotchedwa Wokhulupirika ndi Woona . . . m’kamwa mwake mutuluka lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu.” “Mfumu ya Mafumu” yosagonjetsekayi idzapulumutsa olambira okhulupirika a Yehova ndi kupha adani awo onse. (Chivumbulutso 19:11-21) Apatu m’pamene kukwaniritsidwa kwa masomphenya a kusandulika kwa Yesu kudzafike pachimake penipeni.

19. Kristu akadzagonjetseratu adani ake, kodi ophunzira ake okhulupirika adzakhudzidwa motani, ndipo kodi panopo ophunzira akewo akuyenera kuyesetsa kuchita chiyani?

19 Yesu ‘adzakhala wodabwitsa mwa onse akukhulupirira m’tsiku lija.’ (2 Atesalonika 1:10) Kodi mukufuna kudzakhala mmodzi mwa anthu amene panthawiyo adzasonyeze mantha aulemu kwa Mwana wa Mulungu wopambanayu? Ndiyetu pitirizani kulimbitsa chikhulupiriro chanu ndiponso ‘khalani inunso wokonzekeratu; chifukwa munthawi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.’​—Mateyu 24:43, 44.

Khalani Maso

20. (a) Kodi tingasonyeze motani kuyamikira zimene Mulungu wachita potipatsa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”? (b) Kodi ndi mafunso otani amene tiyenera kudzifunsa?

20 Nthawi ndi nthawi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amalimbikitsa anthu a Mulungu kukhala atcheru mwauzimu ndiponso kukhala maso. (Mateyu 24:45, 46; 1 Atesalonika 5:6) Kodi mumayamikira mfundo zimene timakumbutsidwa panthawi yake zimenezi? Kodi mumazigwiritsa ntchito pofuna kudziwa zinthu zimene zili zofunika kwambiri kuzichita pa moyo wanu? Bwanji osadzifunsa kuti: ‘Kodi ndimatha kuona tanthauzo lauzimu la zinthu zimene zikuchitika masiku anozi ndiponso kodi ndimatha kuona kuti Mwana wa Mulungu akulamulira kumwamba? Kodi ndimazindikira kuti panopo iye ali chire kudikira kuti apereke chiweruzo cha Mulungu pa Babulo Wamkulu komanso dongosolo la Satana lonse?’

21. Kodi n’kutheka kuti ena asiya kukhala tcheru mwauzimu chifukwa chiyani, ndipo akufunika kuchitanji mwamsanga?

21 Anthu ena omwe panopa akusonkhana ndi anthu a Yehova asiya kukhala tcheru mwauzimu. N’kuthekatu kuti atero chifukwa choti aleka kuleza mtima kapena kupirira, monganso anachitira ena mwa ophunzira oyambirira a Yesu. N’kuthekanso kuti abwerera m’mbuyo chifukwa cha mavuto a m’moyo, kukonda chuma, kapena kuzunzidwa. (Mateyu 13:3-8, 18-23; Luka 21:34-36) Ndiponso n’kutheka kuti ena aona kuti zinthu zina zimene zakhala zikufalitsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru n’zovuta kumvetsa. Ngati chimodzi mwa zinthu zimenezi chakuchitikirani, tikukulimbikitsani kuti muyambirenso kuphunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndi kupembedzera Yehova kuti mukhale nayenso paubwenzi wolimba kwambiri.​—2 Petro 3:11-15.

22. Kodi kuphunzira za masomphenya a kusandulika kwa Yesu pamodzi ndi maulosi ena okhudza kusandulikako kwakukhudzani motani?

22 Ophunzira a Yesu anaona masomphenya a kusandulika kwa Yesu panthawi yomwe iwo anafunikira kulimbikitsidwa. Lero, tili ndi chinthu choposa masomphenyawo chomwe chikutilimbikitsa, tikuona kukwaniritsidwa kwa masomphenyawo komanso kwa maulosi ena okhudzana ndi kusandulika kwa Yesuko. Pamene tikulingalira za zinthu zenizeni zaulemerero zimenezi ndiponso pamene tikulingalira za kufunika kwake m’tsogolomu, tiyeni nafenso tinene ndi mtima wonse zimene mtumwi Yohane anafotokoza. Iye anati: “Amen; idzani, Ambuye Yesu.”​—Chivumbulutso 22:20.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 M’chigiriki choyambirira, mawu omwe anawamasulira kuti “zowawa” amatanthauza “ululu wobereka.” (Mateyu 24:8) Izi zikusonyeza kuti mofanana ndi ululu wobereka, mavuto adzikoli ayamba kuchitika pafupifupi, azikhala owawa kwambiri, ndiponso azitenga nthawi yaitali kusiyana ndi m’mbuyomu, ndipo mapeto ake chidzafika chisautso chachikulu.

Kodi Mukukumbukira?

• M’ma 1870, kodi gulu laling’ono la ophunzira Baibulo linazindikiranji ponena za kubweranso kwa Kristu?

• Kodi masomphenya a kusandulika kwa Yesu akwaniritsidwa motani?

• Kodi ulendo wa Yesu wogonjetsa wakhudza motani dziko lapansi ndiponso mpingo wachikristu?

• Kodi tiyenera kuchitanji kuti tidzakhale m’gulu la opulumuka pamene Yesu akumaliza kugonjetsa kwake?

[Mafunso]

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Masomphenya asanduka zenizeni

[Zithunzi patsamba 18]

Kodi mukudziwa zimene zinachitika Kristu atayamba ntchito yake yogonjetsa?