Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Maulosi a Baibulo Agona pa Kristu

Maulosi a Baibulo Agona pa Kristu

Maulosi a Baibulo Agona pa Kristu

“Umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa chinenero.”​—CHIVUMBULUTSO 19:10.

1, 2. (a) Kuyambira mu 29 C.E., kodi m’dziko la Israyeli anthu anafunika kusankha kuchita chiyani? (b) Kodi m’nkhaniyi tikambirana zotani?

ICHI ndi chaka cha 29 C.E. Nkhani yomwe ili mkamwamkamwa m’dziko la Israyeli ndi ya Mesiya wolonjezedwa. Utumiki wa Yohane Mbatizi wathandiza kuti chidwi cha anthu choyembekezera Mesiya chikule. (Luka 3:15) Yohane akukana zoti iyeyo ndiye Kristuyo. M’malo mwake, iye akufotokoza za Yesu wa ku Nazareti kuti: “Ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.” (Yohane 1:20, 34) Posapita nthawi, anthu ambiri akutsatira Yesu kuti amvetsere zophunzitsa zake ndiponso kuti achiritsidwe.

2 M’miyezi yotsatira, Yehova akupereka umboni wochuluka wodziwikitsa Mwana wake. Anthu amene anaphunzira Malemba ndiponso amene aona ntchito za Yesu ali ndi zifukwa zomveka zomukhulupirira. Komabe, ambiri mwa anthuwo, omwe anali m’pangano ndi Mulungu, sakum’khulupirira. Ndi anthu ochepa kwambiri amene akuvomereza kuti Yesu ndiye Kristu, Mwana wa Mulungu. (Yohane 6:60-69) Kodi inuyo mukanakhalapo m’nthawi imeneyo, mukanatani? Kodi mtima wanu ukanakulimbikitsani kuvomera kuti Yesu ndiye Mesiya n’kuyamba kum’tsatira mokhulupirika? Taonani umboni wonena za Yesu, womwe mwiniwakeyo anapereka pamene ankamunena kuti waswa Sabata, ndipo onaninso maumboni ena amene anapereka pambuyo pake pofuna kulimbitsa chikhulupiriro cha ophunzira ake okhulupirika.

Yesu Apereka Yekha Umboni Wake

3. Kodi ndi zinthu zotani zomwe zinachititsa Yesu kupereka umboni wosonyeza kuti iye ndani makamaka?

3 Iyi ndi nyengo ya Paskha m’chaka cha 31 C.E. Yesu ali ku Yerusalemu. Iye wangochiritsa kumene munthu wina amene wakhala akudwala kwa zaka 38. Komabe, Ayuda akuzunza Yesu chifukwa chochita izi tsiku la Sabata. Akumunenanso kuti wachitira mwano Mulungu ndipo akufuna kumupha chifukwa chonena kuti Mulungu ndi Atate wake. (Yohane 5:1-9, 16-18) Pa zimene Yesu akufotokoza podzitchinjiriza pali zifukwa zikuluzikulu zitatu zimene zingathandize Myuda aliyense woona mtima kudziwa kuti Yesu ndi ndani makamaka, popanda kukayikira chilichonse.

4, 5. Kodi cholinga cha utumiki wa Yohane chinali chiyani, ndipo anachikwaniritsa bwino motani?

4 Choyamba Yesu akufotokoza za umboni wa kalambulabwalo wake, yemwe ndi Yohane Mbatizi. Akuti: “Inu munatuma kwa Yohane, ndipo iye anachitira umboni choonadi. Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m’kuunika kwake kanthawi.”​—Yohane 5:33, 35.

5 Yohane Mbatizi anali “nyali yoyaka ndi yowala” chifukwa chakuti Herode asanam’tsekere m’ndende popanda chifukwa chomveka, iye anakwaniritsa ntchito yomwe Mulungu anam’patsa yokonzera Mesiya njira. Yohane anati: ‘Ndinadza ine kudzabatiza ndi madzi kuti [Mesiya] aonetsedwe kwa Israyeli. . . . Ndinaona Mzimu alikutsika kuchokera Kumwamba monga nkhunda; nakhalabe pa Iye. Ndipo sindinam’dziwa Iye, koma wonditumayo kudzabatiza ndi madzi, Iyeyu ananena ndi ine, Amene udzaona Mzimu atsikira, nakhala pa Iye, yemweyu ndiye wakubatiza ndi Mzimu Woyera. Ndipo ndaona ine, ndipo ndachita umboni kuti Mwana wa Mulungu ndi Yemweyu.’ * (Yohane 1:26-37) Yohane anachita kutchuliratu kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mesiya wolonjezedwa. Umboni wa Yohane unali womveka bwino moti patatha miyezi isanu ndi itatu iye atamwalira, Ayuda ambiri oona mitima anati: “Zinthu zilizonse Yohane ananena za Iye zinali zoona.”​—Yohane 10:41, 42.

6. N’chifukwa chiyani anthu anayenera kukhulupirira kuti Mulungu anali kuthandiza Yesu poona ntchito zake?

6 Kenako, Yesu akufotokoza chifukwa china chotsimikizirira kuti iye ndiyedi Mesiya. Iye akuti ntchito zabwino zimene wakhala akuchita ndi umboni woti Mulungu akum’thandiza. Iye akuti: “Ine ndili nawo umboni woposa wa Yohane; pakuti ntchito zimene Atate anandipatsa ndizitsirize, ntchito zomwezo ndizichita zindichitira umboni, kuti Atate anandituma Ine.” (Yohane 5:36) Ngakhale adani a Yesu enieniwo sakanakana umboni umenewu, umene unaphatikizapo zozizwitsa zambirimbiri. Patapita nthawi, ena a iwo anafunsa kuti: “Titani ife? Chifukwa munthu uyu achita zizindikiro zambiri.” (Yohane 11:47) Koma ena akulabadira ndi kunena kuti: “Pamene Kristu akadza kodi adzachita zizindikiro zambiri zoposa zimene adazichita ameneyo?” (Yohane 7:31) Zinali zosavuta kwa anthu amene ankamvetsera Yesu akulankhula kuzindikira makhalidwe a Atate kudzera mwa Mwanayo.​—Yohane 14:9.

7. Kodi Malemba Achihebri amapereka motani umboni wonena za Yesu?

7 Pomaliza, Yesu akutchula umboni wina woti palibe angautsutse. “Malembo, . . . akundichitira Ine umboni ndi iwo omwewo,” iye akutero ndipo akuwonjezeranso kuti: “Pakuti mukadakhulupirira Mose, mukadakhulupirira Ine; pakuti iyeyu analembera za Ine.” (Yohane 5:39, 46) Ndi zoona kuti Mose anali mmodzi chabe mwa mboni zambiri zakale, m’nthawi yomwe Chikristu chinali chisanayambe, zomwe zinalemba zinthu zokhudza Kristu. Zina mwa zinthu zomwe mbonizo zinalemba ndi maulosi ochuluka, ndiponso zinafotokoza mwatsatanetsatane mzera wa banja lomwe iye anadzabadwiramo, ndipo zonsezi zikanathandiza anthu kuzindikira Mesiya. (Luka 3:23-38; 24:44-46; Machitidwe 10:43) Nanga bwanji za Chilamulo cha Mose? “Chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu,” analemba motero mtumwi Paulo. (Agalatiya 3:24) Zoonadi, “umboni wa Yesu ndiwo Mzimu wa [kapena, mfundo ndi cholinga cha] chinenero.”​—Chivumbulutso 19:10.

8. N’chifukwa chiyani Ayuda ambiri sanakhulupirire Mesiya?

8 Kodi umboni wonsewu, umboni womveka bwino wa Yohane, ntchito zamphamvu za Yesu mwiniwakeyo pamodzi ndi makhalidwe ake osonyeza makhalidwe a Mulungu, ndiponso maumboni ochuluka a m’Malemba, sakukukhutiritsani kuti Yesu anali Mesiya? Aliyense amene anali kukondadi Mulungu ndiponso Mawu ake sankavutika kuzindikira zimenezi ndipo anali kukhulupirira Yesu kuti ndiye Mesiya wolonjezedwa. Komatu ambiri ku Israyeli analibe chikondi choterocho. Yesu anauza anthu om’tsutsa kuti: “Ndikudziwani inu, kuti mulibe chikondi cha Mulungu mwa inu nokha.” (Yohane 5:42) M’malo ‘mofuna ulemu wochokera kwa Mulungu yekha,’ iwo ‘ankalandira ulemu wina kwa mnzake.’ Ndiye n’zosadabwitsa kuti sankagwirizana ndi Yesu, yemwe mofanana ndi Atate wake, amadana ndi maganizo oterowo.​—Yohane 5:43, 44; Machitidwe 12:21-23.

Kulimbikitsidwa ndi Masomphenya a za M’tsogolo

9, 10. (a) N’chifukwa chiyani nthawi yomwe Yesu anakonza yoonetsa chizindikiro inali nthawi yabwino kwambiri kwa ophunzira ake? (b) Kodi Yesu analonjeza ophunzira ake zinthu zosangalatsa zotani?

9 Tsopano panali patatha chaka kuchokera pamene Yesu anapereka umboni tafotokoza uja wosonyeza kuti iye ndi Mesiya. Nyengo ya Paskha wa mu 32 C.E. yatha. Anthu ambiri amene ankam’khulupirira asiya kum’tsatira tsopano, mwina chifukwa chozunzidwa, kukonda chuma, ndiponso mavuto a m’moyo. N’kutheka kuti ena asokonezedwa maganizo kapena kukhumudwa chifukwa chakuti Yesu wakana zoti anthu amulonge ufumu. Iye wakana zimene atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda amuuza zoti awasonyeze chizindikiro chochokera kumwamba, chodzipatsa yekha ulemerero. (Mateyu 12:38, 39) N’kutheka kuti kukana kuchita zimenezi kwazunguza mitu anthu ena. Kuwonjezera apa, Yesu wayamba kuuza ophunzira ake nkhani ina yomwe sakutha kuimvetsa. Nkhaniyi ndi yakuti: “Kuyenera iye amuke ku Yerusalemu, kukazunzidwa zambiri ndi akulu, ndi ansembe aakulu, ndi alembi; ndi kukaphedwa.”​—Mateyu 16:21-23.

10 M’miyezi isanu ndi inayi kapena khumi yomwe ikubwerayi, nthawi yoti Yesu ‘achoke kutuluka m’dziko lino lapansi, kumka kwa Atate’ ikwana. (Yohane 13:1) Powadera nkhawa kwambiri ophunzira ake okhulupirikawo, Yesu akulonjeza ena mwa iwo kuti adzachita zimene anakana kuwachitira Ayuda osakhulupirira zija, zowasonyeza chizindikiro chochokera kumwamba. Yesu akuti: “Indetu ndinena kwa inu, kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa munthu atadza mu ufumu wake.” (Mateyu 16:28) N’zachidziwikire kuti Yesu sakunena kuti ena mwa ophunzira ake adzakhala ndi moyo mpaka pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mesiya mu 1914. Zimene Yesu akuganiza ndi zoonetsa atatu mwa ophunzira ake apamtimawo chithunzithunzi chochititsa chidwi cha ulemerero wake mu mphamvu za Ufumu. Masomphenya amenewa amatchedwa kuti kusandulika kwa Yesu.

11. Fotokozani masomphenya a kusandulika kwa Yesu.

11 Patatha masiku asanu ndi limodzi, Yesu akutenga Petro, Yakobo, ndi Yohane, n’kupita nawo kuphiri lalitali, ndipo n’kutheka kuti linali mbali ya phiri la Hermoni. Ali kumeneko, Yesu “anasandulika pamaso pawo; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbu monga kuwala.” Pakuonekanso mneneri Mose ndi mneneri Eliya, akulankhula ndi Yesu. Mwachionekere, zinthu zochititsa chidwizi zikuchitika usiku, zomwe zikuchititsa kuti zonse zioneke bwinobwino. Ndipo zikuoneka zenizenidi moti Petro akupempha kuti amange mahema atatu, limodzi la Yesu, lina la Mose, ndi lina la Eliya. Petro akali chilankhulire, mtambo wowala kwambiri ukuwaphimba ndipo mumtambowo mukumveka mawu akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani iye.”​—Mateyu 17:1-6.

12, 13. Kodi masomphenya a kusandulika kwa Yesu anawakhudza motani ophunzira ake atatu, ndipo n’chifukwa chiyani?

12 N’zoona kuti sikale kwambiri pamene Petro anafotokoza kuti Yesu ndi “Kristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.” (Mateyu 16:16) Komano taganizirani kumva Mulungu mwiniyo akupereka umboni wake, wotsimikizira za Mwana wake wodzozedwa ndiponso ntchito yake. Petro, Yakobo, ndi Yohane ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri kuona kusandulika kwa Yesu. Popeza tsopano chikhulupiriro chawo chalimbikitsidwa, iwo tsopano ndi okonzekera kukumana ndi za m’tsogolo mwawo ndiponso akonzekera kudzagwira ntchito yofunika kwambiri mumpingo wam’tsogolo.

13 Atumwiwo sanaiwale zimene zinachitika pa kusandulika kwa Yesu. Patatha zaka zoposa 30 chichitikireni zimenezi, Petro akulemba kuti: “[Yesu] analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakum’dzera Iye mawu otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye; ndipo mawu awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m’phiri lopatulika lija.” (2 Petro 1:17, 18) Nayenso Yohane anakhudzidwa mtima chimodzimodzi ndi kusandulika kwa Yesu. Patatha zaka zoposa 60 kuchokera pamene Yesu anasandulika, iye akufotokoza zimene zinachitikazo m’mawu awa: “Tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate.” (Yohane 1:14) Komatu kusandulika kwa Yesuku sikuti kunali masomphenya omaliza omwe Yesu anaonetsa anthu om’tsatira.

Anthu Okhulupirika kwa Mulungu Athandizidwa Kuzindikira Zinthu

14, 15. Kodi mtumwi Yohane anakhala mpaka kudza kwa Yesu m’njira yotani?

14 Ataukitsidwa, Yesu akuoneka kwa ophunzira ake m’mbali mwa nyanja ya Galileya. Kunyanjako, iye akuuza Petro kuti: “Ngati ndifuna [Yohane] akhale kufikira ndidza Ine, kuli chiyani ndi iwe?” (Yohane 21:1, 20-22, 24) Kodi mawu awa akusonyeza kuti mtumwi Yohane adzakhala nthawi yaitali kuposa atumwi enawo? Zikuoneka choncho, chifukwa chakuti Yohane akutumikira Yehova mokhulupirika kwa zaka zina 70. Koma zomwe Yesu wanenazi zili ndi mfundo ina yofunika kwambiri.

15 Mawu akuti “kufikira ndidza Ine” akutikumbutsa zimene Yesu ananena zokhudza ‘kudza kwa Mwana wa munthu mu ufumu wake.’ (Mateyu 16:28) Yohane akukhalabe mpaka kudza kwa Yesu m’njira yakuti pambuyo pake Yohaneyo akuonetsedwa masomphenya aulosi a kubwera kwa Yesu m’mphamvu za Ufumu. Chakumapeto kwa moyo wake, ali pachisumbu cha Patmo, Yohane akuona Vumbulutso lokhala ndi zizindikiro zaulosi zochititsa chidwi kwambiri za zinthu zimene zidzachitike ‘m’tsiku la Ambuye.’ Yohane wakhudzidwa mtima kwambiri ndi masomphenya ochititsa chidwiwa moti pamene Yesu akuti: “Indetu; ndidza msanga,” iye akufuula kuti: “Amen; idzani, Ambuye Yesu.”​—Chivumbulutso 1:1, 10; 22:20.

16. Kodi n’chifukwa chiyani tikufunika kupitiriza kulimbitsa chikhulupiriro chathu?

16 Anthu oona mitima a m’zaka 100 zoyambirira akuvomereza kuti Yesu ndiye Mesiya ndipo akum’khulupirira. Popeza anthuwo anali kukhala limodzi ndi anthu ambiri osakhulupirira, ndiponso poganizira za ntchito yomwe anali kufunika kuigwira, komanso mayesero omwe anali kutsogolo kwawo, anthu omwe akukhulupirira Yesu akufunika kulimbikitsidwa. Pofuna kulimbikitsa om’tsatira ake okhulupirika, Yesu wapereka umboni wochuluka wotsimikizira kuti iye ndiye Mesiya ndipo wapereka masomphenya aulosi othandiza otsatira ake kumvetsetsa zinthu. Lero, tili m’katikati mwa “tsiku la Ambuye.” Posachedwapa, Kristu adzawononga dongosolo lonse loipali la Satana ndi kupulumutsa anthu a Mulungu. Nafenso tikufunika kulimbitsa chikhulupiriro chathu mwa kugwiritsa ntchito zinthu zonse zimene Yehova watipatsa kuti tikhale athanzi mwauzimu.

Anawasunga Panthawi ya Mdima ndi Masautso

17, 18. Kodi m’zaka 100 zoyambirira panali kusiyana kwakukulu kotani pakati pa anthu otsatira Yesu ndi anthu omwe ankatsutsana ndi cholinga cha Mulungu, ndipo gulu lililonse linaona zotani?

17 Yesu atafa, ophunzira ake akumvera molimba mtima lamulo lake lokhala mboni zake “m’Yerusalemu, ndi m’Yudeya lonse, ndi m’Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.” (Machitidwe 1:8) Ngakhale kuti mpingo wachikristuwo ukuzunzidwa nthawi zina, Yehova akudalitsa mpingo wongokhazikitsidwa kumenewo pouthandiza kuzindikira zinthu zauzimu ndiponso poupatsa ophunzira ambiri atsopano.​—Machitidwe 2:47; 4:1-31; 8:1-8.

18 Komabe, chiyembekezo cha anthu amene amatsutsa uthenga wabwino chikumka chichepa. Lemba la Miyambo 4:19 limati: “Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwapunthwitsa.” ‘Mdimawu’ ukukula kwambiri m’chaka cha 66 C.E. pamene asilikali a Aroma akuzinga Yerusalemu. Atabwerera kwawo kwakanthawi kochepa pachifukwa chosadziwika bwinobwino, Aromawo akubweranso mu 70 C.E., ndipo ulendo uno akuphwasula mzindawo. Malinga ndi zomwe ananena wolemba mbiri wachiyuda, dzina lake Josephus, Ayuda oposa wani miliyoni anafa. Koma Akristu okhulupirika akupulumuka. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti, asilikali a Aroma atabwerera kwawo kwakanthawi kochepa, Akristuwo akumvera lamulo la Yesu loti athawe.​—Luka 21:20-22.

19, 20. (a) N’chifukwa chiyani anthu a Mulungu alibe chifukwa chochitira mantha pamene dongosolo lilipoli likuyandikira mapeto ake? (b) Chisanafike chaka cha 1914, kodi Yehova anathandiza anthu ake kudziwa zinthu zofunika kwambiri ziti?

19 Zinthu zilinso chimodzimodzi kwa ife. Chisautso chachikulu chomwe chikubwera chidzakhala chizindikiro cha mapeto a dongosolo lonse loipa la Satana. Koma anthu a Mulungu sakuyenera kuchita mantha, chifukwa Yesu analonjeza kuti: “Onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 28:20) Pofuna kulimbitsa chikhulupiriro cha ophunzira ake oyambirira ndiponso powakonzekeretsa za m’tsogolo mwawo, Yesu anawapatsa chithunzithunzi cha ulemelero wake wakumwamba monga Mfumu ya Umesiya. Nanga bwanji masiku ano? Chithunzithunzi chimenechi chinasanduka zenizeni mu 1914. Ndipo izi zalimbitsa kwambiri chikhulupiriro cha anthu a Mulungu. Zimenezi ndi lonjezo la m’tsogolo mosangalatsa kwambiri, ndipotu atumiki a Yehova athandizidwa kuumvetsa bwino Ufumu wa Mesiyawu. M’katikati mwa dziko lamdimali, “mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, [komwe] kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.”​—Miyambo 4:18.

20 Ngakhale 1914 isanakwane, gulu laling’ono la Akristu odzozedwa linayamba kumvetsa mfundo zofunika kwambiri zokhudza kubweranso kwa Ambuye. Mwachitsanzo, iwo anazindikira kuti kubweranso kumeneku kudzakhala kosaoneka, monga momwe anasonyezera angelo awiri amene anaonekera kwa ophunzira a Yesu mu 33 C.E. pamene Yesu anali kukwera kupita kumwamba. Yesu ataphimbika kwa Ophunzira ake ndi mtambo, angelowo anati: ‘Yesu amene walandiridwa kumka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.’​—Machitidwe 1:9-11.

21. Kodi m’nkhani yotsatirayi muli zotani?

21 Anthu okhulupirika omwe ankam’tsatira ndi okhawo omwe anaona Yesu pamene anali kupita. Mofanana ndi zomwe zinachitika pa kusandulika kwa Yesu, panalibe anthu ena, ndipo dziko lonse silinadziwe n’komwe zomwe zinachitika. Izi ndi zomwenso zinachitika pamene Kristu anabwerera m’mphamvu zake za Ufumu. (Yohane 14:19) Ophunzira odzozedwa okhulupirika ndi okhawo omwe anazindikira kukhalapo kwake monga Mfumu. M’nkhani yotsatirayi tiona mmene kuzindikira zimenezi kunawakhudzira, n’kufika pakuti kuyambe kusonkhanitsidwa anthu ambirimbiri omwe adzakhale padziko lapansi pano pamene Yesu akulamulira.​—Chivumbulutso 7:9, 14.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Zikuoneka kuti paubatizo wa Yesu, ndi Yohane yekha amene anamva mawu a Mulungu. Ayuda amene Yesu akuwalankhula ‘sanamve konse mawu [a Mulungu], kapena maonekedwe ake sanamuone.’​—Yohane 5:37.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Yesu anapereka umboni wotani wosonyeza kuti anali Mesiya panthawi imene anthu ankamunena kuti waswa Sabata ndiponso kuti akuchitira mwano Mulungu?

• Kodi ophunzira oyambirira a Yesu anapindula motani ndi kusandulika kwa Yesu?

• Kodi Yesu ankatanthauzanji pamene ananena kuti Yohane adzakhala mpaka kudza kwake?

• Kodi ndi chithunzithunzi chotani chomwe chinasanduka zenizeni mu 1914?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 10]

Yesu anapereka umboni wosonyeza kuti iye anali Mesiya

[Chithunzi patsamba 12]

Masomphenya a kusandulika kwa Yesu anali olimbitsa chikhulupiriro

[Chithunzi patsamba 13]

Yohane anakhala mpaka ‘kudza’ kwa Yesu