Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ukalamba Umene Uli “Korona wa Ulemu”

Ukalamba Umene Uli “Korona wa Ulemu”

“Thandizo Langa Lidzera kwa Yehova”

Ukalamba Umene Uli “Korona wa Ulemu”

A MURIEL, omwe ali ndi zaka 101 anati: “Palibenso moyo wina wokoma kuposa umenewu.” A Theodoros, amene ali ndi zaka 70 anangoti: “Uwu ndi moyo wonyaditsa kwabasi.” A Maria, amene ali ndi zaka 73 anati, “Moyo koma umenewu.” Anthu onsewa moyo wawo wonse anali kutumikira Yehova Mulungu.

Anthu achikulire ambiri amene amalambira Yehova padziko lonse amamva chimodzimodzi. Ngakhale kuti n’ngokalamba, m’thupi simuli bwino, ndiponso ali ndi mavuto ena, iwo amatumikirabe Mulungu ndi mtima wonse. Mumpingo wachikristu, anthu amapereka ulemu kwa okalamba oterewa chifukwa chakuti n’ngodzipereka kwa Mulungu, ndipo amatsanzira chitsanzo chawo. Yehova amayamikira kwambiri utumiki wa achikulire ngakhale atamalephera kuchita zinthu zina chifukwa cha ukulamba. *​—2 Akorinto 8:12.

Zimene buku la Masalmo limanena pankhani ya moyo umene achikulire okhulupirika angayembekezere n’zomvekadi. Iwo angathe kukhala ngati mtengo waukulu mwadzaoneni umene umabalabe zipatso. Wamasalmo anaimba motere ponena za okhulupirika achikulire: “Atakalamba adzapatsanso zipatso; adzadzazidwa ndi madzi nadzakhala abiriwiri.”​—Salmo 92:14.

Ena mwina amachita mantha kuti akadzakalamba n’kutha mphamvu adzatayidwa, n’kusiyidwa okha. Davide anapempha Mulungu kuti: “Musanditaye mu ukalamba wanga; musandisiye, pakutha mphamvu yanga.” (Salmo 71:9) Kodi n’chiyani chimene chingathandize okalamba kuti zinthu ziwayendere bwino? Ndi khalidwe la Mulungu la kukhala wolungama. Wamasalmo anaimba kuti: “Wolungama adzaphuka ngati mgwalangwa.”​—Salmo 92:12.

Anthu amene amatumikira Mulungu mokhulupirika pamoyo wawo, nthawi zambiri amapitiriza kubala zipatso zabwino akakalamba. Kwenikweni, zinthu zambiri zimene akhala akuchita podzithandiza okha kapena pothandiza anthu ena zakhala zopindulitsa kwambiri, monga mmene mbewu zimakulira n’kubala zipatso zochuluka. (Agalatiya 6:7-10; Akolose 1:10) Inde, anthu amene awononga moyo wawo pochita zinthu zongokomera iwowo ndiponso zosemphana ndi njira za Mulungu, nthawi zambiri sakhala ndi zinthu zoti angaziloze akakalamba.

M’buku la m’Baibulo la Miyambo anagogomezeranso kwambiri kuti kulungama kuli ngati korona wokongoletsera munthu paukalamba. M’bukuli timawerenga mawu akuti: ‘Imvi ndiyo korona wa ulemu, ikapezedwa m’njira ya chilungamo.’ (Miyambo 16:31) Inde, khalidwe la kulungama limasonyeza kukongola kwa mumtima. Kuchita zinthu zolungama pa moyo wonse kumapatsa munthu ulemu. (Levitiko 19:32) Munthu waimvi amenenso ali ndi nzeru ndiponso makhalidwe abwino amapatsidwa ulemu.​—Yobu 12:12.

Yehova zimamusangalatsa kwambiri munthu akam’tumikira mowongoka mtima kwa moyo wake wonse. Malemba amati: “Ngakhale mpaka mudzakalamba Ine [Yehova] ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu; ndalenga, ndipo ndidzanyamula; inde, ndidzasenza, ndipo ndidzapulumutsa.” (Yesaya 46:4) N’zolimbikitsa kwambiritu kudziwa kuti Atate wathu wakumwamba yemwe ndi wachikondi amalonjeza kuthandiza anthu okalamba amene ali okhulupirika kwa iye.​—Salmo 48:14.

Popeza kuti Yehova amasangalala naye munthu amene wagwiritsira ntchito moyo wake wonse pomutumikira, anthu ena ayeneranso kumulemekeza munthu wotero. Motero, potsanzira Mulungu, ifenso timaona kuti okhulupirira anzathu amene ali okalamba n’ngofunika kwambiri. (1 Timoteo 5:1, 2) Choncho, tiyeni tiziyesetsa kupeza njira zothandizira anthuwa posonyeza chikondi chathu chachikristu.

Kuyamba Kuyenda M’njira ya Chilungamo Mutakalamba

Solomo akutitsimikizira kuti: “M’khwalala la chilungamo muli moyo.” (Miyambo 12:28) Munthu sangalephere kuyamba kuyenda m’khwalala kapena kuti m’njira imeneyi chifukwa cha ukalamba. Mwachitsanzo ku Moldova kuli agogo a zaka 99 amene paunyamata wawo wonse ankangochita za ndale zachikomyunizimu. Panthawi imeneyo ankaona kuti n’zonyaditsa kuti analankhulapo ndi anthu otchuka pa ndale zachikomyunizimu, anthu monga V. L. Lenin. Komano Chikomyunizimu chitatha, bambo okalambawa anayamba kuona kuti moyo wawo sakupindula nawo. Koma Mboni za Yehova zitawasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo njira yokhayo yothetsera mavuto a anthu, iwo anavomera kuphunzira choonadi cha Baibulo ndipo anayamba kuphunzira Malemba mozama. Akanapanda kumwalira akanakhala mtumiki wobatizidwa wa Yehova.

Akuphunzira za makhalidwe abwino amene Mulungu amafuna, gogo wina wa zaka 81 wa ku Hungary anazindikira kuti ukwati wawo ndi mwamuna amene anakhala naye kwa zaka zambiri ndithu ayenera kukaulembetsa kuboma. Gogoyu analimba mtima n’kufotokozera mwamuna wakeyo zimene Baibulo limanena pankhaniyi. Iye anadabwa ndiponso anasangalala kwambiri mwamuna uja atavomera kukalembetsa ukwatiwo. Atadula mtchato, gogoyu analimbikira kwambiri pa zinthu zauzimu. Patangotha miyezi isanu ndi itatu yokha kuchokera panthawi imene anayamba kuphunzira Baibulo, gogoyu anakhala wofalitsa wosabatizidwa, ndipo patangotha nthawi yochepa chabe anabatizidwa. Koma ndiyetu n’zoona kuti kulungama kungathe kuwakongoletsa zedi anthu okalamba.

Inde, Akristu okhulupirika achikulire asamakayike n’komwe kuti Mulungu amawaganizira. Yehova sangasiye anthu amene akhala okhulupirika kwa iye. M’malo mwake, iye amalonjeza kuti adzawatsogolera, ndi kuwathandiza mpaka paukalamba wawo. Ndipo iwowa amasonyeza kuti mawu a wamasalmo otsatirawa n’ngoonadi. Mawu ake ndi oti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova.”​—Salmo 121:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani Kalendala ya Mboni za Yehova ya 2005, pa mwezi wa January ndi February.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

‘Imvi ndiyo korona wa ulemu, ikapezedwa m’njira ya chilungamo.’​—MIYAMBO 16:31

[Bokosi patsamba 8]

YEHOVA AMASAMALIRA ATUMIKI AKE OKALAMBA

“Pali aimvi uziwagwadira, nuchitire ulemu munthu wokalamba.”​—Levitiko 19:32.

“Ngakhale mpaka mudzakalamba Ine ndine, ndipo ngakhale mpaka tsitsi laimvi, Ine ndidzakusenzani inu.”​—Yesaya 46:4.