Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Dikirani”

“Dikirani”

“Dikirani”

KALE kunali anthu amene ankayang’anira zipata za mizinda ndi za kachisi. Nthawi zina ankayang’anira makomo a nyumba za anthu. Usiku ntchito yawo inali kuonetsetsa kuti zipatazo ndi zotseka komanso amalondera. Imeneyi inali ntchito yofunika kwambiri chifukwa chitetezo cha mzindawo chimadalira iwo kuti azifuula kuchenjeza anthu akaona choopsa chilichonse.

Yesu Kristu ankadziwa bwino ntchito ya oyang’anira zipata amenewa, otchedwanso apakhomo. Nthawi ina iye anayerekezera ophunzira ake ndi oyang’anira zipata, ndi kuwalimbikitsa kukhala odikira poyembekezera chimaliziro cha dongosolo la zinthu lachiyuda. Anati: “Yang’anirani, dikirani, . . . pakuti simudziwa nthawi yake. Monga ngati munthu wa paulendo, adachoka kunyumba kwake, . . . nalamulira wapakhomo adikire. Chifukwa chake dikirani; pakuti simudziwa inu nthawi yake yakubwera mwini nyumba.”​—Marko 13:33-35.

Mofananamo, kwa zaka 125 tsopano, magazini ino ya Nsanja ya Olonda yakhala ikulimbikitsa anthu ndi mawu a Yesu akuti “dikirani.” Kodi imachita zimenezi motani? Monga tafotokozera pa tsamba 2 la magizini ino, “Imapitiriza kuyang’anitsitsa zochitika za dziko pamene zikukwaniritsa ulosi wa Baibulo. Imatonthoza anthu a mitundu yonse ndi uthenga wabwino wakuti Ufumu wa Mulungu posachedwapa udzawononga awo onse amene amatsendereza anthu anzawo ndi kuti udzasandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso.” Magazini oposa 26,000,000 a Nsanja ya Olonda iliyonse amagawidwa kwa anthu padziko lonse m’zinenero 150. Imeneyi ndi magazini ya mawu a Mulungu imene ikuwerengedwa ndi anthu ambiri koposa padziko lonse lapansi. Mofanana ndi oyang’anira zipata akale, Mboni za Yehova zikugwiritsa ntchito magaziniyi kulimbikitsira anthu kulikonse ‘kukhala odikira’ mwauzimu chifukwa Ambuye Yesu Kristu ali pafupi kubweranso kudzaweruza dongosolo la zinthuli.​—Marko 13:26, 37.