Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunafuna ‘Ngale ya Mtengo Wapatali’ Lerolino

Kufunafuna ‘Ngale ya Mtengo Wapatali’ Lerolino

Kufunafuna ‘Ngale ya Mtengo Wapatali’ Lerolino

“Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu.”​—MATEYU 24:14.

1, 2. (a) Kodi Ayuda m’nthawi ya Yesu anali kuuona bwanji Ufumu wa Mulungu? (b) Kodi Yesu anatani kuti athandize anthu kumvetsa za Ufumuwo, ndipo panali zotsatira zotani?

PANTHAWI imene Yesu anabwera pa dziko lapansi, Ufumu wa Mulungu unali nkhani yaikulu kwambiri pakati pa Ayuda. (Mateyu 3:1, 2; 4:23-25; Yohane 1:49) Koma poyamba, ambiri mwa iwo sanali kuzindikira bwino lomwe ukulu ndi mphamvu ya Ufumuwo. Sanalinso kudziwa kuti udzakhala boma la kumwamba. (Yohane 3:1-5) Ngakhale ena amene anakhala otsatira a Yesu sanali kudziwa bwinobwino kuti Ufumu wa Mulungu n’chiyani, kapena zimene ayenera kuchita kuti alandire dalitso lokhala olamulira anzake a Kristu.​—Mateyu 20:20-22; Luka 19:11; Machitidwe 1:6.

2 M’kupita kwa nthawi, Yesu anaphunzitsa ophunzira ake zinthu zambiri moleza mtima, kuphatikizapo fanizo la ngale ya mtengo wapatali, limene takambirana m’nkhani yoyamba. Fanizolo linali lowasonyeza kufunika koyesetsa mwamphamvu pofunafuna Ufumu wa kumwambawo. (Mateyu 6:33; 13:45, 46; Luka 13:23, 24) Mfundo imeneyi iyenera kuti inawakhudza mtima kwambiri, chifukwa mosataya nthawi anayamba kulengeza uthenga wabwino wa Ufumu mosatopa ndiponso molimba mtima kumalekezero a dziko lapansi. Buku la Machitidwe lili ndi umboni wokwanira wa mfundo imeneyi.​—Machitidwe 1:8; Akolose 1:23.

3. Kunena za m’nthawi yathu ino, kodi Yesu anati chiyani za Ufumu?

3 Ndiyeno bwanji za lerolino? Anthu mamiliyoni ambiri akuuzidwa za madalitso a paradaiso wa pa dziko lapansi lolamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu. Mu ulosi wake waukuluwo wonena za “mathedwe a nthawi ya pansi pano,” Yesu ananena mosapita m’mbali kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:3, 14; Marko 13:10) Anafotokozanso kuti ntchito yaikulu imeneyi iyenerabe kuchitidwa ngakhale padzakhale zopinga ndi zovuta zazikulu, kuphatikizapo chizunzo chimene. Koma anatitsimikizira kuti: “Iye wakulimbika chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:9-13) Zonsezi n’zofuna kudzimana ndi kudzipereka kumene wamalonda wa m’fanizo la Yesu anaonetsa. Kodi lerolino alipo anthu amene amasonyeza chikhulupiriro ndi changu choterocho pofunafuna Ufumu?

Kupeza Choonadi Kumadzetsa Chimwemwe

4. Kodi choonadi cha Ufumu chikuwakhudza motani anthu lerolino?

4 Wamalonda wa m’fanizo la Yesu anasangalala kwambiri atapeza ngale imene anaizindikira kuti ndi “ya mtengo wapatali.” Chimwemwe chimenecho chinam’limbitsa mtima kuchita zonse zotheka kuti agule ngaleyo. (Ahebri 12:1) Lerolinonso, choonadi chonena za Mulungu ndi Ufumu wake chimakopa anthu ndi kuwalimbitsa mtima kuchita zonse zotheka kuti apeze Ufumuwo. Izi zikutikumbutsa mawu a Mbale A. H. Macmillan, onena za mmene anayesetsera kudziwa Mulungu ndi cholinga Chake polenga anthu. Analemba mawuwo m’buku lakuti Faith on the March. Anati: “Zimene ndapezazi, anthu ambiri chaka ndi chaka akuzipezanso. Anthu amenewa ali ngati inuyo ndi ine, chifukwa ndi osiyanasiyana, ochokera m’mitundu yonse, m’mafuko onse, ndipo ndi amisinkhu yonse. Choonadi sichiona nkhope. Chimakopa munthu aliyense, kaya akhale wa mtundu wotani.”

5. Kodi lipoti la chaka cha utumiki cha 2004 likusonyeza zinthu zotani zolimbikitsa?

5 Mawu amenewa ndi oona, chifukwa chaka ndi chaka anthu oona mtima masauzande ambiri amalimbikitsidwa ndi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kuti apereke moyo wawo kwa Yehova ndi kuchita chifuniro chake. Ndi zimene zinachitikanso m’chaka chautumiki cha 2004, chomwe chinayamba mu September 2003 mpaka mu August 2004. Pa miyezi 12 imeneyo, anthu 262,416 anaonetsa poyera kuti adzipereka kwa Yehova pobatizidwa m’madzi. Izi zinachitika m’mayiko 235. M’mayikowo, Mboni za Yehova zikuchititsa maphunziro a Baibulo a panyumba okwana 6,085,387 mlungu uliwonse. Akutero kuti athandize anthu osiyanasiyana, ochokera m’mitundu yambiri, mafuko, ndi zinenero kuphunzira choonadi cha m’Mawu a Mulungu.​—Chivumbulutso 7:9.

6. Kodi n’chiyani chachititsa kuwonjezeka pa zaka zonsezi?

6 Kodi zonsezi zinatheka bwanji? Sitingakayikire kuti Yehova ndiye amakokera anthu amenewa ofuna choonadi kwa iye. (Yohane 6:65; Machitidwe 13:48) Koma sitinganyalanyaze awo amene adzikhutula pantchito ya Ufumu mosadzikonda ndiponso mwa kuyesetsa osatopa. Pamene anali ndi zaka 79 zakubadwa, Mbale Macmillan analemba kuti: “Kuchokera pamene ndinaphunzira kwa nthawi yoyamba za malonjezo operekedwa kwa mtundu wa anthu umene ukudwala ndi kufawu, chiyembekezo changa pa zimene uthenga wa m’Baibulo umasonyeza sichinachepe. Nditangophunzira za malonjezowo, ndinatsimikiza mtima kufufuza zowonjezeka zimene Baibulo limaphunzitsa. Cholinga chinali chakuti ndikathandizenso ena ofanana ndi ine, amene akufunitsitsa kudziwa za Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova, ndi zolinga zake zabwino zokhudza mtundu wa anthu.”

7. Ndi chitsanzo chotani chimene chikusonyeza bwino lomwe chimwemwe ndi changu chimene anthu opeza choonadi cha m’Baibulo amakhala nacho?

7 Kufunitsitsa komweko tikukuonanso pakati pa atumiki a Yehova lerolino. Chitsanzo ndi Daniela wochokera ku Vienna, m’dziko la Austria. Iye anati: “Kuyambira ndili mwana, Mulungu anali bwenzi langa la pamtima. N’chifukwa chake ndinali kufunitsitsa kudziwa dzina lake, chifukwa kwa ineyo, kungom’tchula kuti ‘Mulungu’ zinali kumveka ngati ndi wakutali kwambiri woti sangakhale bwenzi langa. Koma sindinalidziwe mpaka pamene ndinali ndi zaka 17 zakubadwa, pamene a Mboni za Yehova anabwera kunyumba kwathu. Iwo anandifotokozera zonse zokhudza Mulungu zimene ndinali kufuna kudziwa. Ndinasangalala kwambiri kupeza choonadi pamapeto pake, moti ndinayamba kulalikira kwa wina aliyense.” Posakhalitsa, chifukwa cha changu chake, anzake ku sukulu anayamba kum’seka. Koma Daniela anati: “Kwa ine zinali ngati kuona ulosi wa m’Baibulo ukukwaniritsidwa, chifukwa ndinali nditaphunzira kuti Yesu ananena kuti otsatira ake adzadedwa ndi kuzunzidwa chifukwa cha dzina lake. Ndinakondwera kwambiri ndipo ndinadabwa kuona zikuchitikadi.” Posapita nthawi, Daniela anapereka moyo wake kwa Yehova, ndipo anabatizidwa. Kenako, anayamba kuchita zinthu zom’thandiza kuti afike pa cholinga chake chokhala mmishonale. Atakwatiwa, Daniela, limodzi ndi mwamuna wake, Helmut, anayamba kulalikira kwa anthu ochokera ku Africa, ku China, ku Philippines, ndi ku India omwe anali mu mzinda wa Vienna. Daniela ndi Helmut tsopano ndi amishonale kum’mwera koma chakumadzulo kwa Africa.

Saleka

8. Kodi ochuluka asonyeza chikondi chawo pa Mulungu ndi kukhulupirika ku Ufumu wake m’njira yokhutiritsa yotani?

8 Ndithudi, umishonale ndi imodzi mwa njira zimene anthu a Yehova lerolino amasonyezera chikondi chawo kwa Mulungu ndiponso kukhulupirika ku Ufumu wake. Mofanana ndi wamalonda woyendayenda wa m’fanizo la Yesu, amene amalowa utumiki umenewu amakhala ofunitsitsa kupita kutali kwambiri chifukwa cha Ufumu wa Mulungu. Koma amishonale amenewa sayenda ulendowo kuti akapeze uthenga wabwino wa Ufumu ayi. Iwo amapititsa uthengawo kwa anthu okhala kumadera akutali kwambiri, kuwaphunzitsa ndi kuwathandiza kukhala ophunzira a Yesu Kristu. (Mateyu 28:19, 20) M’mayiko ambiri, iwo amapirira mavuto adzaoneni. Koma amapeza mphoto yaikulu pa kupirira kwawo.

9, 10. Kodi amishonale akuona zosangalatsa zotani m’mayiko ngati Central African Republic?

9 Chitsanzo chimodzi ndi dziko la Central African Republic. Chaka chatha, anthu 16,184 anasonkhana pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu, pamene m’dzikolo muli ofalitsa Ufumu 2,426 okha. Popeza kuti madera ambiri m’dziko limenelo kulibe magetsi, anthu pochita ntchito zawo za pakhomo zatsiku ndi tsiku amakhala panja, pansi pa mtengo. Ndiye amishonale nawonso amachita ntchito yawo m’njira yomweyo, kuchititsa maphunziro a Baibulo atakhala pa mthunzi, pansi pa mtengo wogudira bwino. Panjapo pamakhala powala bwino ndipo pamakhala kamphepo kayaziyazi. Koma si zokhazo. Anthu m’dzikolo amakonda kwambiri Baibulo, ndipo amatha kucheza nkhani zokhudza Mulungu paliponse, mmene anthu amachezera za mpira ndi zanyengo. Chotero, odutsa chapafupi amaona phunziro la Baibulo limene likuchitika ndipo amangopatuka n’kukhala nawo pa phunzirolo.

10 N’zimene zinachitika mmishonale wina akuchititsa phunziro la Baibulo panja pa nyumba ina. Mnyamata amene anali kukhala tsidya lina la msewu anafika pomwe panali mmishonale uja, n’kumuuza kuti mmishonaleyo afikenso ku nyumba kwa mnyamatayo kudzaphunzira naye Baibulo, chifukwa palibe anam’fikira. Mmishonaleyo analola, ndipo mnyamatayo akupita patsogolo kwambiri. M’dziko limenelo, apolisi kawirikawiri amaimitsa a Mboni pa msewu, osati kuti awapatse chisamani kapena kuti awalipiritse pa mlandu winawake, koma kuti awapemphe magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, kapena kuti awathokoze chifukwa cha nkhani ina ya m’magazini amenewa imene inawasangalatsa kwambiri.

11. Mosasamala za mayesero, kodi amishonale amene atumikira kwa nthawi yaitali amamva bwanji za utumiki wawo?

11 Ochuluka amene anayamba umishonale zaka 40 kapena 50 zapitazo akutumikirabe mokhulupirika. Alitu chitsanzo chabwino zedi kwa tonsefe cha chikhulupiriro ndi kulimbikira. Pa zaka 42 zapitazi, mbale wina ndi mkazi wake achita umishonale m’mayiko atatu. Mbaleyo anati: “Takumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, tinalimbana ndi malungo zaka 35. Koma sitinalingalirepo kuti tinalakwitsa kukhala amishonale.” Mkazi wake anawonjezapo kuti: “Nthawi zonse pamakhala zinthu zambiri zimene timaziyamikira. Utumiki wa kumunda umadzetsa chimwemwe chachikulu, ndipo kuyambitsa maphunziro a Baibulo n’kosavuta. Ukamaona ophunzira akufika pamisonkhano, n’kumadziwana nawo bwino, nthawi zonse misonkhano imakhala ngati macheza a pabanja.”

Amaona Zonse Kukhala Zosapindulitsa

12. Kodi munthu amaonetsa motani kuti amayamikiradi mtengo wapatali wa Ufumu?

12 Wa malonda uja atapeza ngale ya mtengo wapatali, “anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.” (Mateyu 13:46) Mtima umenewu wololera kusiya zimene zimaonedwa kukhala za mtengo wapatali, ndiwo uli ndi anthu amene amayamikiradi mtengo wapatali wa Ufumu. Monga mmodzi mwa amene adzalandira ulemerero wa Ufumu pamodzi ndi Kristu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Ndiyesa zonse zikhale chitayiko chifukwa cha mapambanidwe a chizindikiritso cha Kristu Yesu Ambuye wanga, chifukwa cha Iyeyu ndinatayikitsa zinthu zonse, ndipo ndiziyesa zapadzala, kuti ndikadziwonjezere Kristu.”​—Afilipi 3:8.

13. Kodi munthu wina ku Czech Republic anaonetsa motani chikondi chake pa Ufumu?

13 Mofananamo, ambiri lerolino ndi ofunitsitsa kusintha zinthu zikuluzikulu m’moyo wawo kuti apeze madalitso a Ufumu. Mwachitsanzo, mu October 2003, ku dziko la Czech Republic, mwamuna wina wa zaka 60 zakubadwa, yemwe ndi mphunzitsi wamkulu pa sukulu, anapeza buku lothandiza kuphunzira Baibulo lotchedwa Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Ataliwerenga, nthawi yomweyo anapempha a Mboni za Yehova a kuderalo kuti azikam’phunzitsa Baibulo. Anapita patsogolo mwauzimu, ndipo posapita nthawi, anayamba kupezeka pa misonkhano yonse. Nangano bwanji za maganizo ake ofuna kudzapikisana nawo pa chisankho cha meya, kenako cha aphungu? Anasankha kulowa mpikisano wina, mpikisano wothamangira moyo wosatha, monga wolengeza Ufumu. Iye anati: “Ndinagawira mabuku ophunzitsa Baibulo ochuluka kwa ana a sukulu pa sukulu yathu.” Anaonetsa kuti wadzipereka kwa Yehova pobatizidwa m’madzi pa msonkhano wachigawo mu July 2004.

14. (a) Kodi uthenga wabwino wa Ufumu walimbitsa mtima anthu ambirimbiri kuchita chiyani? (b) Kodi aliyense wa ife angadzifunse mafunso otani ofuna kuganizapo kwambiri?

14 Enanso ambirimbiri achita zofananazo atamva uthenga wabwino wa Ufumu. Iwo atuluka m’dziko loipali, avula umunthu wawo wakale, asiyana ndi mabwenzi awo akale, ndi kusiyanso zotanganitsa za dziko. (Yohane 15:19; Aefeso 4:22-24; Yakobo 4:4; 1 Yohane 2:15-17) N’chifukwa chiyani amatero? Amatero chifukwa amaona madalitso a Ufumu wa Mulungu kukhala apamwamba kuposa china chilichonse chimene angapeze m’dongosolo lino la zinthu. Kodi inunso mumaona uthenga wabwino wa Ufumu mofananamo? Kodi wakulimbitsani mtima kusintha zina ndi zina kuti moyo wanu, zolinga zanu, ndi zinthu zimene mumaona kukhala zofunika zikhale zogwirizana ndi zimene Yehova amafuna? Mukatero, mudzalandira madalitso ochuluka, lerolino ndi m’tsogolo momwe.

Ntchito Yotuta Yafika Pachimake

15. Kodi ulosi unati anthu a Mulungu adzachita zotani m’masiku otsiriza?

15 Wamasalmo analemba kuti: “Anthu anu adzadzipereka eni ake tsiku la chamuna chanu.” Odziperekawo akuphatikizapo “mame a ubwana,” kapena kuti anyamata ochuluka ngati mame. Palinso “khamu lalikuku” la ‘akazi olalikira uthengawo.’ (Salmo 68:11; 110:3) Kodi pakhala zotsatira zotani masiku otsiriza ano chifukwa cha khama ndi kudzipereka kwa anthu a Yehova, amuna ndi akazi, ana ndi achikulire?

16. Perekani chitsanzo cha mmene atumiki a Mulungu akuyesetsera kuthandiza ena kuphunzira za Ufumu.

16 Mpainiya wina, kapena kuti wolengeza Ufumu nthawi zonse, ku India anali ndi nkhawa poganiza mmene anthu ogontha oposa mamiliyoni awiri m’dzikolo angathandizidwire kudziwa za Ufumu. (Yesaya 35:5) Anaganiza zochita kosi ya chinenero cha manja mu mzinda wa Bangalore. Ali ku kosiko, mlongoyu anauza ogontha ambiri za chiyembekezo cha Ufumu, ndipo anayambitsa magulu ophunzira Baibulo. Pambuyo pa milungu yochepa chabe, anthu oposa 12 anayamba kufika pamisonkhano ku Nyumba ya Ufumu. Kenako, ali pa phwando la ukwati, mpainiyayu anakumana ndi mnyamata wina wogontha wochokera ku mzinda wa Calcutta. Ameneyu anali ndi mafunso ambiri ndipo anasonyeza chidwi chofuna kudziwa zambiri za Yehova. Koma panali vuto. Mnyamatayo anafunikira kubwerera ku Calcutta, ulendo wa makilomita 1,600, kuti akayambe maphunziro a ku koleji. Koma kumeneko kunalibe Mboni zodziwa chinenero cha manja. Atalimbikira kukambirana ndi bambo ake, anamulola kuimba sukulu yakeyo mu mzinda wa Bangalore m’malo mwake, n’cholinga choti apitirize kuphunzira Baibulo. Iye anapita patsogolo mwauzimu, ndipo patatha pafupifupi chaka chimodzi, anapereka moyo wake kwa Yehova. Kenako, iyeyo anaphunzitsa Baibulo anthu ogontha angapo, kuphatikizapo mnyamata amene anali bwenzi lake la paubwana. Ofesi ya nthambi ku India tsopano ikukonza zoti apainiya aphunzire chinenero cha manja kuti azithandiza anthu ogontha.

17. Fotokozani chimene mwaona kukhala cholimbikitsa kwambiri pa lipoti la chaka chautumiki cha 2004, pa masamba 19 mpaka 22.

17 Pa masamba 19 mpaka 22 a magazini ino, pali lipoti losonyeza ntchito imene Mboni za Yehova zagwira m’munda, m’chaka chautumiki cha 2004 padziko lonse lapansi. Liwerengeni mofatsa kuti mudzionere nokha umboni wakuti anthu a Yehova padziko lonse lapansi aikadi maganizo awo onse pa ‘ngale ya mtengo wapatali’ lerolino.

Pitirizani ‘Kufunafuna Ufumu Choyamba’

18. N’chiyani chimene Yesu sananene m’fanizo lake la wamalonda a ngale, ndipo sananenerenji?

18 Tiyeni tibwererenso ku fanizo la Yesu la wamalonda uja. Tikuona kuti Yesu sananene kalikonse kokhudza mmene wamalondayo anali kupezera zofunika pa moyo, atagulitsa zonse zimene anali nazo. Pachifukwa chimenechi, ena angafunse kuti: ‘Tsono wamalondayu akanapeza bwanji chakudya, zovala, ndi pogona, alibe kena kalikonse? Ngale ya mtengo wapatali imeneyo inalinso ndi phindu lanji?’ Amenewo angaoneke ngati mafunso anzeru malinga ndi kaganizidwe ka munthu. Koma kodi Yesu sanalimbikitse ophunzira ake kuti: “Muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu”? (Mateyu 6:31-33) Mfundo yaikulu ya fanizo limeneli ndiyo kufunika kosonyeza kudzipereka ndi mtima wonse kwa Mulungu, ndi kuchita changu pantchito ya Ufumu. Kodi pali phunziro kwa ife?

19. Kodi tingaphunzire mfundo yanji yaikulu pa fanizo la Yesu la ngale ya mtengo wapatali?

19 Kaya tangophunzira kumene za uthenga wabwino kapena takhala tikugwira ntchito ya Ufumu ndi kuuza ena za madalitso ake kwa nthawi yaitali, tiyenera kupitirizabe kuika chidwi chathu chonse pa Ufumuwo. Tili m’nthawi zovuta, koma tili ndi zifukwa zabwino zokhulupirira kuti chimene tikuchigwirira ntchito ndi chinthu chenicheni ndipo sitingachiyerekeze ndi china chilichonse. Chili ngati ngale imene wamalonda uja anapeza. Zimene zikuchitika m’dziko ndiponso maulosi a m’Baibulo amene akwaniritsidwa ndizo umboni wotsimikizika wakuti tikukhala ‘m’mathedwe a nthawi ya pansi pano.’ (Mateyu 24:3) Mofanana ndi wamalonda uja, tiyeni tisonyeze changu chochokera pansi pa mtima, pogwira ntchito ya Ufumu wa Mulungu. Ndiponso, tisangalale ndi mwayi umenewu wolengeza uthenga wabwino.​—Salmo 9:1, 2.

Kodi Mukukumbukira?

• Pa zaka zonsezi, n’chiyani chathandiza kuti olambira oona awonjezeke?

• Kodi amishonale amaonetsa mtima wotani?

• Kodi anthu ena asintha zinthu zotani chifukwa cha uthenga wabwino wa Ufumu?

• Kodi pa fanizo la Yesu la ngale ya mtengo wapatali, tingaphunzire mfundo yanji yofunika kwambiri?

[Mafunso]

[Tchati pamasamba 19-22]

LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 2004 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

[Chithunzi patsamba 14]

“Choonadi . . . chimakopa munthu aliyense, kaya akhale wa mtundu wotani.”​—A. H. Macmillan

[Chithunzi patsamba 15]

Daniela ndi Helmut analalikira kwa anthu a zinenero zakunja ku Vienna

[Zithunzi patsamba 16, 17]

Mofanana ndi wamalonda a ngale, amishonale lerolino amadalitsidwa kwambiri

[Chithunzi patsamba 17]

“Anthu anu adzadzipereka eni ake”