Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Kupeza Ngale Imodzi ya Mtengo Wapatali’

‘Kupeza Ngale Imodzi ya Mtengo Wapatali’

‘Kupeza Ngale Imodzi ya Mtengo Wapatali’

“Anthu akulimbikira kupeza mwayi wokalowa ufumu wa kumwamba, ndipo amene akulimbikira mwachamuna akuupeza.”​—MATEYU 11:12, NW.

1, 2. (a) Kodi ndi mtima wosowa wotani umene Yesu anafotokoza m’limodzi la mafanizo ake a Ufumu? (b) Kodi Yesu anati chiyani m’fanizo la ngale ya mtengo wapatali?

KODI pali chinthu chimene mumachiona kuti ndi cha mtengo wapatali kwambiri, moti mungatayirepo zonse zimene muli nazo kuti chinthucho chikhale chanu? Anthu ena amanena kuti ndi odzipereka pa cholinga chawo, monga kupeza ndalama zambiri, kutchuka, kukhala ndi mphamvu zolamulira ena, kapena udindo wapamwamba. Ngakhale zili choncho, si kawirikawiri munthu kupeza chinthu chimene angalolere kutayirapo zonse zimene ali nazo. M’limodzi la mafanizo ake ogwira mtima a Ufumu wa Mulungu, Yesu Kristu ananenapo za munthu wa mtima wosowa ndi wosiririka woterewu.

2 Fanizo limeneli ndi limene Yesu anafotokozera ophunzira ake pamene anali paokha. Kawirikawiri limatchedwa kuti fanizo la ngale ya mtengo wapatali. Yesu anati: “Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi munthu wamalonda, wakufuna ngale zabwino: ndipo mmene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita, nagulitsa zonse anali nazo, naigula imeneyo.” (Mateyu 13:36, 45, 46) Kodi Yesu anali kufuna kuti ophunzirawo aphunzirepo chiyani pa fanizolo? Ndipo ifeyo tingapindule motani ndi mawu a Yesu?

Mtengo Wapatali wa Ngale

3. N’chifukwa chiyani ngale zabwino zinali za mtengo wapatali kwambiri m’nthawi zakale?

3 Kuyambira nthawi zamakedzana, anthu akhala akuvala timiyala ta ngale monga zodzikongoletsera. Buku lina limanena kuti malinga ndi wolemba nkhani wa ku Roma, Pliny Wamkulu, ‘pa zinthu zonse za mtengo wapatali, panalibe choposa ngale.’ Mosiyana ndi golide, siliva, kapena miyala yambiri ya mtengo wapatali, ngale zimapangidwa ndi zinthu za moyo. Ambiri amadziwa kuti mitundu ina ya nkhono za m’nyanja ndi imene imapanga ngale. Chimene chimachitika n’chakuti, tinthu tina monga timiyala tikalowa m’chikamba chake, imatulutsa zinthu zamadzimadzi zimene zimakuta kamwalako. Ndiyeno kamwalako kamakhala ngale yosalala ndi yonyezimira. Kale, ngale zabwino kwambiri anali kuzipeza makamaka m’Nyanja Yofiira, m’nyanja ya Persian Gulf, ndi m’nyanja ya mchere ya Indian Ocean, kutali kwambiri ndi ku Israyeli. Mosakayikira, ndiye chifukwa chake Yesu ananena za “wamalonda [woyendayenda, NW], wakufuna ngale zabwino.” Kuti munthu apeze ngale za mtengo wapatalidi, ayenera kuyesetsa kwambiri.

4. Kodi phunziro lalikulu m’fanizo la Yesu la wamalonda n’chiyani?

4 Ngakhale kuti ngale zabwino zakhala zodula kuyambira kale, n’zoonekeratu kuti phunziro lalikulu m’fanizo la Yesu si kudula kwakeko ayi. M’fanizo limeneli, Yesu sanangoyerekezera Ufumu wa Mulungu ndi ngale ya mtengo wapatali. Mfundo yake yaikulu inali pa “munthu wamalonda, wakufuna ngale zabwino” ndiponso zimene munthuyo anachita atapeza ngaleyo. Mosiyana ndi mwinisitolo wamba, wamalonda a ngale anali kukhala katswiri wozindikira pa malondawo. Amati akaiyang’ana ngale ija, amatha kuona zina ndi zina zobisika zimene zikuchititsa ngaleyo kukhaladi yapadera. Ngale yeniyeni anali kuidziwa akangoiona, osapusitsika ndi ngale wamba kapena yachinyengo.

5, 6. (a) Kodi n’chiyani chochititsa chidwi kwambiri ndi wamalonda wa m’fanizo la Yesu? (b) Kodi fanizo la chuma chobisika likusonyeza chiyani chokhudza wamalonda a ngale?

5 Pali chinanso chochititsa chidwi ndi wamalonda ameneyu. Wamalonda wamba, mwina akanayamba waona kaye mtengo umene angakagulitsire ngaleyo, n’cholinga choti adziwe kuti angaigule ndalama zingati, kuti akakaigulitsa akapezepo phindu. Akanayambanso waona ngati pali anthu amene amafuna ngale yoteroyo, kuti isakamutengere nthawi kuigulitsa. M’mawu ena, chidwi chake chikanakhala pa kupezapo phindu mofulumira, osati kukhala ndi ngaleyo. Koma wamalonda wa m’fanizo la Yesu sanali wotero. Chidwi chake sichinali pa ndalama, kapena kupeza katundu wina wake monga phindu. M’malo mwake, analolera kugulitsa “zonse anali nazo,” mwina katundu wake yense, kuti agule chimene wakhala akuchifunafuna.

6 Kwa amalonda ambiri, zimene munthu ameneyu wa m’fanizo la Yesu anachita ndiko kufa mutu. Wamalonda wosamala sangaike dala ndalama zake pangozi mwa njira imeneyi. Koma wamalonda wa m’fanizo la Yesu anali wosiyana pa zinthu zimene amaziona kukhala zofunika. Iye sanali kufuna kusangalala ndi phindu la ndalama, koma kupeza chimwemwe ndiponso kukhala wokhutira pokhala ndi chinthu china cha mtengo wapatali koposa. Yesu anamveketsa mfundo imeneyi m’fanizo linanso lofanana ndi loyambali. Iye anati: “Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m’munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m’kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.” (Mateyu 13:44) Inde, chimwemwe chodza ndi kupeza chuma, kapena kuti chinthu cha mtengo wapatali n’kukhala nacho, chinali chokwanira kuchititsa munthuyo kugulitsa zonse zimene anali nazo. Kodi alipo anthu otero lerolino? Kodi pali chinthu cha mtengo wapatali chimene munthu angafune kutayirapo zonse zimene ali nazo?

Amene Anazindikira Mtengo Wake Wapatali

7. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali kumvetsadi mtengo wapatali wa Ufumu?

7 Mmene amafotokoza fanizo lake, Yesu anali kulankhula za “Ufumu wa Kumwamba.” Iyeyo anali kumvetsadi mtengo wapatali wa Ufumuwo. Nkhani zolembedwa m’Mauthenga Abwino zili ndi umboni wamphamvu wa mfundo imeneyi. Atabatizidwa m’chaka cha 29 C.E., Yesu “anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.” Kwa zaka zitatu ndi theka, iye anaphunzitsa makamu a anthu za Ufumuwo. Anayendayenda m’dziko lonselo, “kumizinda ndi kumidzi, kulalikira ndi kuwauza Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu.”​—Mateyu 4:17; Luka 8:1.

8. Kodi Yesu anachitanji posonyeza zimene Ufumu udzachita?

8 Yesu anasonyezanso zimene Ufumu wa Mulungu udzachita mwa kuchita zozizwitsa zambiri m’dziko lonselo. Iye anachiritsa odwala, kupatsa anthu a njala chakudya, kuletsa namondwe, ngakhalenso kuukitsa akufa. (Mateyu 14:14-21; Marko 4:37-39; Luka 7:11-17) Pamapeto pake, anaonetsa umboni wakuti ndi wokhulupirika kwa Mulungu ndi Ufumu mwa kupereka moyo wake, kufera chikhulupiriro chake pa mtengo wozunzikirapo. Monga wamalonda uja anachitira, kupereka ndi mtima wonse zonse zimene anali nazo kuti agule “ngale imodzi ya mtengo wapatali,” Yesu anakhalira moyo Ufumu, ndipo anaferanso Ufumu.​—Yohane 18:37.

9. Kodi ndi mtima wosowa wotani umene ophunzira oyambirira a Yesu anaonetsa?

9 Yesu sanaike moyo wake wokha pa Ufumu, koma anasonkhanitsanso kagulu ka otsatira ake. Amenewanso anali anthu omwe anamvetsadi mtengo wapatali wa Ufumu. Mmodzi wa amenewa anali Andreya, amene poyamba anali wophunzira wa Yohane Mbatizi. Atamva Yohane Mbatizi akuchitira umboni kuti Yesu ndiye “Mwanawankhosa wa Mulungu,” Andreya limodzi ndi wophunzira winanso wa Yohane Mbatizi, mwina mwake Yohane, nthawi yomweyo anayamba kutsatira Yesu nakhala okhulupirira. Yohane ameneyu anali mmodzi mwa ana a Zebedayo. Koma sizinathere pompo. Nthawi yomweyo, Andreya anapita kwa mbale wake Simoni ndi kumuuza kuti: “Tapeza ife Mesiya.” Posapita nthawi, Simoni (yemwe kenako anadziwika ndi dzina lakuti Kefa, kapena Petro) limodzi ndi Filipo ndi bwenzi lake Natanayeli anavomerezanso kuti Yesu ndiye Mesiya. Ndipotu Natanayeli anafika pouza Yesu kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israyeli.”​—Yohane 1:35-49.

Analimbikitsidwa Kuchitapo Kanthu

10. Patapita nthawi kuchokera pamene anakumana koyamba, kodi ophunzira anatani Yesu atawapezanso n’kuwaitana?

10 Chimwemwe chimene Andreya, Petro, Yohane, ndi ena anali nacho atapeza Mesiya, n’chofanana ndi chimwemwe cha wamalonda uja atapeza ngale ya mtengo wapatali. Kodi iwo anatani kenako? Mauthenga Abwino sanena kuti anatani pambuyo pokumana ndi Yesu nthawi yoyamba imeneyi. Koma zikuonetsa kuti ambiri a iwo anabwerera ku ntchito zawo za masiku onse. Ndiyeno pambuyo pa miyezi isanu ndi umodzi, kapena pafupifupi chaka, Yesu anapezanso Andreya, Petro, Yohane, ndi Yakobo mbale wa Yohane ali pantchito yawo ya usodzi ku Nyanja ya Galileya. * Atawaona, Yesu anawauza kuti: “Tiyeni pambuyo panga, ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” Kodi iwo anatani? Nkhani yolembedwa ndi Mateyu imanena zimene Petro ndi Andreya anachita kuti: “Iwo anasiya pomwepo makokawo, nam’tsata iye.” Kunena za Yakobo ndi Yohane, timawerenga kuti: “Anasiya pomwepo ngalawayo ndi atate wawo, nam’tsata Iye.” Nkhani yolembedwa ndi Luka imawonjezapo mawu akuti iwo “anasiya zonse, nam’tsata Iye.”​—Mateyu 4:18-22; Luka 5:1-11.

11. Kodi chifukwa chake chingakhale chiyani chimene ophunzira anavomerera kuitana kwa Yesu mosazengereza?

11 Kodi ophunzira anachita zinthu mopupuluma pamene anavomera kuitana kwa Yesu? Kutalitali! Ngakhale kuti atakumana ndi Yesu kwa nthawi yoyamba iwo anabwerera ku ntchito yawo ya usodzi, n’zosakayikitsa kuti zimene anaona ndi kumva patsikulo zinawakhudza mtima kwambiri. Nthawi yokwanira pafupifupi chaka imene inadutsa, iyenera kuti inawapatsa mpata wonse wosinkhasinkha pa zimene anaona ndi kumva. Tsopano inali nthawi yoti asankhe chochita. Kodi iwo akanakhala ngati wamalonda uja amene mtima wake unasangalala kwambiri atapeza ngale ya mtengo wapatali, moti malinga ndi kunena kwa Yesu, “anapita [‘ndipo mwamsanga,’ NW]” anachita zonse zotheka kuti agule ngaleyo? Inde. Zimene anaona ndi kumva zinawakhudza mtima. Anaona kuti nthawi yafika yoti achitepo kanthu. Ndiye chifukwa chake, monga nkhaniyo ikunenera, mosazengereza anasiya zonse n’kukhala otsatira a Yesu.

12, 13. (a) Kodi ambiri amene anamva Yesu akulankhula anatani? (b) Kodi Yesu anati chiyani za ophunzira ake okhulupirika, ndipo mawu akewo amatanthauzanji?

12 Anthu okhulupirika amenewa anali osiyana kwambiri ndi ena amene anatchulidwa pambuyo pake m’nkhani za m’Mauthenga Abwino. Panali ambiri amene Yesu anawachiritsa kapena kuwapatsa chakudya koma amene anangopitiriza zochita zawo za masiku onse. (Luka 17:17, 18; Yohane 6:26) Ena anachita kukana ndithu, Yesu atawaitana kuti akhale otsatira ake. (Luka 9:59-62) Mosiyana kwambiri ndi amenewa, Yesu anadzanena za okhulupirika kuti: “Koma kuyambira m’masiku a Yohane Mbatizi mpaka tsopano anthu akulimbikira kupeza mwayi wokalowa ufumu wa kumwamba, ndipo amene akulimbikira mwachamuna akuupeza.”​—Mateyu 11:12, NW.

13 ‘Kulimbikira.’ Kodi mawu amenewa akutanthauzanji? Pofotokoza mawu achigiriki amene m’Baibulo la Chichewa anawatembenuza kuti ‘kulimbikira,’ buku la Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words limati: “Mawuwa amatanthauza kuyesetsa mwamphamvu.” Ndiponso, pothirira ndemanga vesili, katswiri wa Baibulo Heinrich Meyer anati: “Mawuwa akufotokoza kuyesetsa mwamphamvu pofuna kupeza ufumu wa Mesiya umene ukubwera . . . Munthuyo ali ndi chidwi chachikulu kwambiri ndiponso champhamvu zedi, moti sakungokhalanso phee n’kumauyembekeza.” Mofanana ndi wamalonda a ngale uja, anthu ochepa amenewa anazindikira mofulumira chinthu cha mtengo wapatali, ndipo ndi mtima wonse anasiya zonse zimene anali nazo kuti achite ntchito ya Ufumu.​—Mateyu 19:27, 28; Afilipi 3:8.

Enanso Anayamba Kufunafuna Ufumuwo

14. Kodi Yesu anawakonzekeretsa motani atumwi kuchita ntchito yolalikira za Ufumu, ndipo panali zotsatira zotani?

14 Popitiriza utumiki wake, Yesu anaphunzitsa ndi kuthandiza anthu ena kuti akalamire Ufumu. Anayamba ndi kusankha anthu 12 mwa ophunzira ake n’kuwatcha atumwi, kapena kuti otumizidwa ndi iye. Amenewa, Yesu anawapatsa malangizo atsatanetsatane onena mmene adzachitire utumiki wawo komanso machenjezo a zopinga ndi zovuta zimene adzakumane nazo. (Mateyu 10:1-42; Luka 6:12-16) Pazaka ngati ziwiri zotsatira, iwo anatsagana ndi Yesu pa maulendo ake olalikira m’dziko lonselo, ndipo anali paubwenzi wolimba ndi iye. Iwo anamva zonena zake, anaona ntchito zake zamphamvu ndi chitsanzo chake. (Mateyu 13:16, 17) Mosakayikira, zonsezi zinawakhudza mtima kwambiri, moti mofanana ndi wamalonda uja, iwo anali achangu pantchito ya Ufumu, ndipo anachita ntchitoyo ndi mtima wonse.

15. Kodi Yesu anati chifukwa chenicheni cha kusangalala kwa otsatira ake chinali chiyani?

15 Kuwonjezera pa atumwi 12, Yesu “anaika ena makumi asanu ndi awiri, nawatuma iwo awiriawiri pamaso pake kumudzi uliwonse, ndi malo alionse kumene ati afikeko mwini.” Amenewanso anawauza za ziyeso ndi zovuta zimene adzakumane nazo. Anawalangizanso kuuza anthu kuti: “Ufumu wa Mulungu wayandikira kwa inu.” (Luka 10:1-12) Anthu 70 amenewa anabwerako akusangalala kwambiri, nauza Yesu kuti: “Ambuye, zingakhale ziwanda zinatigonjera ife m’dzina lanu.” Koma Yesu anawauza kuti m’tsogolo, iwo adzasangalala kuposa pamenepo chifukwa cha changu chawo pantchito ya Ufumu. Ayenera kuti anadabwa kumva zimenezo. Powauza, Yesu anati: “Musakondwera nako kuti mizimu idakugonjerani, koma kondwerani kuti mayina anu alembedwa m’Mwamba.”​—Luka 10:17, 20.

16, 17. (a) Kodi Yesu anawauzanji atumwi ake okhulupirika pamene anali nawo usiku womaliza? (b) Kodi mawu a Yesu anapatsa atumwi chimwemwe ndi chitsimikizo chotani?

16 Pomalizira, pa Nisani 14, 33 C.E., usiku womaliza ndi atumwi, Yesu anayambitsa mwambo umene pambuyo pake unatchedwa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Analamula atumwiwo kuti azichita mwambo umenewo. Usiku umenewo, Yesu anauza atumwi 11 otsalawo kuti: “Inu ndinu amene munakhala ndi Ine chikhalire m’mayesero anga; ndipo Ine ndikuikirani ufumu, monganso Atate wanga anandiikira Ine, kuti mukadye ndi kumwa kugome kwanga mu Ufumu wanga; ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu ndi kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israyeli.”​—Luka 22:19, 20, 28-30.

17 Atumwi atamva mawu amenewa kwa Yesu, ayenera kuti anadzazidwa ndi chimwemwe chachikulu m’mitima yawo. Iwo anali kupatsidwa chiyembekezo chodzakhala ndi ulemerero ndiponso mwayi wapamwamba kuposa wina uliwonse umene munthu angakhale nawo. (Mateyu 7:13, 14; 1 Petro 2:9) Mofanana ndi wamalonda uja, iwo anali atasiya zambiri kuti atsatire Yesu pantchito ya Ufumu. Tsopano anawatsimikizira kuti kudzipereka kwawo kumene anali atachita sikunapite pachabe.

18. Kupatulapo atumwi 11, enanso ndani amene anali kudzapindula ndi Ufumu?

18 Amene anali kudzapindula ndi Ufumuwo si atumwi okhawo amene anali ndi Yesu usiku umenewo. Chifuniro cha Yehova chinali kulowetsa anthu okwanira 144,000 m’pangano la Ufumu, kuti akakhale olamulira anzake a Yesu Kristu mu Ufumu wa ulemerero wa kumwamba. Kuwonjezera apo, mtumwi Yohane anaona m’masomphenya “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, . . . akuimirira ku mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, . . . nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” Amenewa ndi nzika za Ufumu za pa dziko lapansi. *​—Chivumbulutso 7:9, 10; 14:1, 4.

19, 20. (a) Kodi anthu a mitundu yonse ali ndi mwayi wotani? (b) Tiyankha funso loti bwanji m’nkhani yotsatira?

19 Yesu atatsala pang’ono kukwera kumwamba, analamula otsatira ake okhulupirika kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza iwo m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera: ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.” (Mateyu 28:19, 20) Chotero, anthu a mitundu yonse anali kudzakhala ophunzira a Yesu Kristu. Amenewanso anali oti adzaika mtima wawo pa Ufumu, monga anachitira wamalonda uja atapeza ngale yabwino. Cholinga chawo ndicho kulandira mphoto ya kumwamba kapena ya pa dziko lapansi.

20 Mawu a Yesu anasonyeza kuti ntchito yopanga ophunzira idzapitirizabe mpaka “chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.” Chotero, kodi m’masiku athu ano, alipobe anthu ofanana ndi wamalonda a ngale uja, omwe ndi okonzeka kupereka zonse ali nazo kuti apeze Ufumu wa Mulungu? Funso limeneli tiliyankha m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Yohane, mwana wa Zebedayo, ayenera kuti analondola Yesu atakumana koyamba, ndipo anaona zina zimene Yesu anachita. Mwina ndi zimene zinachititsa Yohane kulemba zinthuzo mogwira mtima kwambiri mu Uthenga wake Wabwino. (Yohane, machaputala 2-5) Koma anadzabwererabe ku ntchito yake ya usodzi kwa nthawi ndithu Yesu asanamuitanenso.

^ ndime 18 Kuti mudziwe zambiri pa mfundoyi, onani mutu 10 m’buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi phunziro lalikulu m’fanizo la Yesu la wamalonda a ngale ndi lotani?

• Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali kumvetsadi mtengo wapatali wa Ufumu?

• N’chiyani chinachititsa Andreya, Petro, Yohane, ndi enanso kuvomera nthawi yomweyo Yesu atawaitana?

• Ndi mwayi waukulu uti umene anthu a mitundu yonse ali nawo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

‘Iwo anasiya zonse, natsata Yesu’

[Chithunzi patsamba 12]

Asanakwere kumwamba, Yesu analamula otsatira ake kupanga ophunzira