Kodi Ndani Angadyetse Anthu Padziko Pano?
Kodi Ndani Angadyetse Anthu Padziko Pano?
BUNGWE la World Food Programme, lomwe ndi nthambi imene bungwe la United Nations likugwiritsa ntchito polimbana ndi njala, linati pafupifupi anthu 800 miliyoni, omwe ambiri a iwo ndi ana, alibe chakudya chokwanira. Posachedwapa nthambiyi yanena kuti thandizo limene mayiko olemera akanapereka pothana ndi vutoli lagwiritsidwa ntchito polimbana ndi mavuto ena, monga uchigawenga. Vutoli lakulirakulira chifukwa cha kufalikira kwa matenda opatsirana. Lipoti la nthambiyi la mmene ntchito yogawa chakudya m’masukulu padziko lonse ikuyendera, linanenapo za mayiko a ku Africa kuno kumene Edzi yafalikira kwambiri. Lipotilo linati: “Makolo ambiri akumwalira ndi matenda amenewa. Ndipo akusiya ana amasiye omwe nthawi zambiri akumadzifunira okha chakudya. Ambiri a iwo ulimi saudziwa ndipo sangathe kudziimira paokha monga mmene zimakhalira akaphunzitsidwa ndi makolo awo.”
Nthambi ya World Food Programme ikulimbikitsa ntchito yomwe cholinga chake n’choyesetsa kuti ngati n’kotheka, azigawa chakudya m’masukulu tsiku lililonse. Cholinga cha ntchitoyi sindicho kungochepetsa njala, koma kuti ithandize kuti m’maphunziro awo anthawi zonse, achinyamata aziphunziranso njira zopewera kachilombo koyambitsa matenda a Edzi.
M’madera amene izi zayamba kale kuchitika, ana akumawapatsa chakudya, kuwaphunzitsa mmene angakhalire aukhondo, ndi kuwathandiza m’njira zina. Zikuonekanso kuti anthu akasintha makhalidwe awo, otenga kachilombo koyambitsa Edzi akumachepa.
Koma n’zomvetsa chisoni kuti ngakhale anthu ayesetse motani, sakwanitsa kuthetsa mavuto bwinobwino. Koma Baibulo limatipatsa lonjezo lolimbikitsa lokhudza njira yothetseratu vuto la njala. Lemba la Salmo 72:16 limati: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka.” Mu Ufumu wa Mulungu, anthu adzanena za Yehova Mulungu kuti: “Mucheza nalo dziko lapansi, mulithirira, mulilemeza kwambiri . . . Muwameretsera tirigu mmene munakonzera nthaka.”—Salmo 65:9.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
WFP/Y. Yuge