Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zozizwitsa Zimachitikadi Kapena Ayi?

Kodi Zozizwitsa Zimachitikadi Kapena Ayi?

Kodi Zozizwitsa Zimachitikadi Kapena Ayi?

MUNTHU wina anachita chidwi kwambiri atangowerenga mawu akuti “Zozizwitsa Zimachitika Ndithu, Ingofunsani Angelo.” Anawerenga mawu amenewa pa pepala lomwe analimata pa galimoto ina imene inkadutsa. Ngakhale kuti iyeyo anali wopembedza, sanadziwe zimene mawuwa anali kutanthauza. Kodi pepalali linali kusonyeza kuti woyendetsa galimotoyo amakhulupirira kuti zozizwitsa zimachitika? Kapena kodi kunali kusereula chabe kosonyeza kuti sakhulupirira zoti zozizwitsa zimachitika komanso kuti kuli angelo?

Mungachite chidwi kumva zimene ananena Manfred Barthel, wolemba mabuku wa ku Germany. Iye anati: “Owerenga amasiyana maganizo pa mawu akuti zozizwitsa moti amagawanika m’magulu awiri.” Amene amakhulupirira zozizwitsa amakhala otsimikiza kuti zimachitikadi ndiponso kuti mwina zimachitika mowirikiza. * Mwachitsanzo, lipoti lina lochokera ku Greece linati zaka zingapo zapitazi, okhulupirira zozizwitsa ananena kuti zozizwitsazo zimachitika pafupifupi mwezi uliwonse. Izi zinachititsa bishopu wa tchalitchi cha Greek Orthodox kuchenjeza kuti: “Wokhulupirira zozizwitsa amaona ngati Mulungu, Mariya, komanso oyera mtima ali ngati anthu enieni osati anthu auzimu. Okhulupirira zozizwitsa sayenera kukokomeza kwambiri zinthu.”

M’mayiko ena, si anthu ambiri amene amakhulupirira zozizwitsa. Zotsatira za kafukufuku wina amene anachitika mu mzinda wa Allensbach, ku Germany mu 2002, zinasonyeza kuti anthu 71 mwa anthu 100 alionse am’dzikomo amakhulupirira kuti zozizwitsa n’zongopeka chabe, si zochitika zenizeni. Komabe, anthu pafupifupi 30 mwa anthu 100 alionse ndi amene anali kukhulupirira zozizwitsa. Atatu mwa anthuwa ndi azimayi amene ankanena kuti analandira uthenga kuchokera kwa Namwali Mariya. Patapita miyezi yowerengeka kuchokera nthawi imene iwo ankati Mariya anawaonekera, ali pamodzi ndi angelo komanso nkhunda, nyuzipepala ya ku Germany ya Westfalenpost inati: “Tikunena pano anthu pafupifupi 50,000 achita chidwi kwambiri ndi masomphenya a azimayiwo. Ena mwa iwo ndi oti akufuna machiritso ndipo ena akungofuna kumvetsetsa nkhaniyo.” Panali chiyembekezo chakuti enanso okwana 10,000 adzafika m’tauniyo kuti adzaone Mariya ngati ataonekeranso. Ena amanena kuti Namwali Mariya anaonekeranso m’njira yomweyi ku Lourdes, m’dziko la France, m’chaka cha 1858, ndi ku Fátima, m’dziko la Portugal, mu 1917.

Kodi Zipembedzo Zomwe Si Zachikristu Zimakhulupirira Zozizwitsa?

Pafupifupi zipembedzo zonse zimakhulupirira kuti zozizwitsa zimachitikadi. Buku lakuti The Encyclopedia of Religion limati amene anayambitsa Chibuda, Chikristu, ndi Chisilamu anali ndi maganizo osiyanasiyana pankhani ya zozizwitsa. Komabe linanena kuti: “Mbiri ya zipembedzo zimenezi ikusonyeza bwino lomwe kuti zozizwitsa ndiponso nkhani za zozizwitsa zakhala mbali yofunika kwambiri yachipembedzo pa moyo wa anthu.” Bukuli limanena kuti “nthawi zina Buddha weniweniyo ankachita zozizwitsa.” Pambuyo pake, “Chibuda atachisamutsira ku China, amishonale ake ankakonda kuonetsa mphamvu zawo zochita zozizwitsa.”

Insaikulopediya imeneyi itatchula zinthu zingapo zomwe akuti ndi zozizwitsa, inamaliza ndi mawu akuti: “Ena sangavomereze nkhani za zozizwitsa zoterezi, zomwe zinalembedwa ndi anthu opembedza olemba mbiri za anthu. Koma mosakayikira anazilemba ndi cholinga chabwino chofuna kupereka ulemerero kwa Buddha, amene ankatha kupatsa otsatira ake mphamvu zoterozo zochita zozizwitsa.” Ponena za Chisilamu, buku lomweli limati: “Asilamu ambiri amakhulupirirabe kuti zozizwitsa zimatha kuchitika. Mabuku otchedwa hadīth, ofotokoza za aneneri a Chisilamu, amasonyeza kuti Muhammad anachita zozizwitsa kambirimbiri ali pagulu. . . . Ena amakhulupirira kuti oyera mtima akamwalira, amapitirizabe kuchita zozizwitsa pamanda pawopo pothandiza anthu okhulupirira, ndipo anthu amapempha ndi mtima wonse kuti athandizidwe ndi oyera mtimawa.”

Kodi Zipembedzo Zachikristu Zimaona Bwanji Zozizwitsa?

Akristu ambiri amaona nkhaniyi mosiyanasiyana. Ena amavomereza kuti zozizwitsa zotchulidwa m’Baibulo za Yesu Kristu kapena za atumiki a Mulungu omwe analiko Chikristu chisanayambe zinachitikadi. Koma ambiri amagwirizana ndi mfundo za Martin Luther, Mpulotesitanti Wosintha zinthu m’chipembedzo. Ponena za iyeyu buku lakuti The Encyclopedia of Religion limati: “Luther ndi Calvin, onsewa analemba kuti nthawi ya zozizwitsa inatha ndipo anthu asayembekezere kuti zingachitikenso.” Bukuli linanenanso kuti Tchalitchi cha Katolika chimakhulupirirabe kuti zozizwitsa zimachitika “koma sichiyesa n’komwe kufotokoza mmene zimachitikira.” Komabe, “anthu ophunzira achipulotesitanti anayamba kukhulupirira kuti ntchito yaikulu ya Chikristu inali kuphunzitsa makhalidwe abwino, komanso kuti Mulungu kapena zolengedwa zauzimu sizilankhula ndi anthu kapena kusintha kwambiri moyo wawo.”

Ena amene amati ndi Akristu, kuphatikizapo atsogoleri ena azipembedzo, amakayikira ngati zozizwitsa zotchulidwa m’Baibulo zinkachitikadi. Mwachitsanzo, titenge nkhani ya chitsamba choyaka moto yomwe ikupezeka m’Baibulo pa Eksodo 3:1-5. Buku lakuti What the Bible Really Says limafotokoza kuti akatswiri ambiri azaumulungu a ku Germany saona chimenechi ngati chozizwitsa chenicheni. M’malo mwake iwo amatanthauzira zomwe zinachitikazo monga “chizindikiro chakuti Mose ankadziimba mlandu komanso anasokonezeka maganizo chifukwa cha chikumbumtima chimene chinkamuvutitsa kwambiri.” Bukuli limanenanso kuti: “N’kutheka kuti malawi a motowo anali maluwa amene anamasula mwadzidzidzi chifukwa cha kuwala kwa dzuwa kumene kunachitika panthawi imene akuti Mulungu anafika pamalowo

Mungaone kuti mfundo imeneyi n’njosagwira mtima. Nangano, n’chiyani chimene muyenera kukhulupirira? Kodi n’kwanzeru kukhulupirira kuti zozizwitsa zinkachitika? Nanga bwanji zozizwitsa zamakono? Popeza kuti angelo sitingathe kuwafunsa, tingafunse ndani?

Zimene Baibulo Limanena

Palibe angatsutse zoti Baibulo limanena kuti kalero nthawi zina Mulungu ankalowerera m’zochita za anthu mwa kuchita zinthu zina zomwe anthu sangathe kuchita. Timawerenga za iye kuti: ‘Munatulutsa anthu anu Israyeli m’dziko la Aigupto ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri.’ (Yeremiya 32:21) Tangoganizani kuti mtundu umene unali wamphamvu kwambiri m’masiku amenewo, unachititsidwa manyazi ndi milili khumi imene Mulungu anatumiza, kuphatikizapo imfa za ana awo oyamba kubadwa. Zinalidi zozizwitsa!​—Eksodo chaputala 7 mpaka 14.

Patapita zaka zoposa 1,500, anthu anayi amene analemba Mauthenga Abwino anafotokoza zozizwitsa 35 zimene Yesu anachita. Ndipotu mawu awo amasonyeza kuti Yesu anachita zozizwitsa zambiri kuposa zimene iwo analemba. Kodi malipoti amenewa ndi oona kapena ayi? *​—Mateyu 9:35; Luka 9:11.

Ngati Baibulo lilidi Mawu a Mulungu a choonadi, monga mmene limanenera, ndiye kuti muli ndi chifukwa chomveka chokhulupirira zozizwitsa zimene limanena. Baibulo limanena momveka bwino kuti kalero zozizwitsa zinkachitikadi. Limatchula zozizwitsa monga machiritso, kuukitsa akufa, ndi zina zotero, komabe limanenanso momveka bwino kuti zozizwitsa zoterozo sizichitika masiku ano. (Onani bokosi lakuti “Chifukwa Chake Zozizwitsa Sizichitika Monga Mwakale,” patsamba 4.) Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti ngakhale anthu amene amakhulupirira kuti Baibulo ndi loona, amaona kuti palibe chifukwa chokhulupirira zozizwitsa zamakono? Yankho la funsoli lili m’nkhani yotsatirayi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 M’nkhani ino, mawu akuti “zozizwitsa” akutanthauza zimene buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo limanena kuti: “Zochitika m’dziko lapansi zomwe sizingatheke ndi mphamvu iliyonse yaumunthu kapena yachilengedwe ndipo motero anthu amakhulupirira kuti zimachitika ndi mphamvu zauzimu.”

^ ndime 14 Onani umboni wina wosonyeza kuti n’koyenera kulikhulupirira Baibulo. Umboni umenewu ukupezeka m’buku lakuti Baibulo​—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi patsamba 4]

CHIFUKWA CHAKE ZOZIZWITSA SIZICHITIKA MONGA MWAKALE

Baibulo limatchula zozizwitsa zosiyanasiyana. (Eksodo 7:19-21; 1 Mafumu 17:1-7; 18:22-38; 2 Mafumu 5:1-14; Mateyu 8:24-27; Luka 17:11-19; Yohane 2:1-11; 9:1-7) Zambiri mwa zozizwitsa zimenezi zinkasonyeza kuti Yesu anali Mesiya, komanso kuti Mulungu anali kum’thandiza. Otsatira a Yesu oyambirira anaonetsa mphatso zawo zochita zozizwitsa, monga kulankhula malilime ndi kuzindikira mawu ouziridwa. (Machitidwe 2:5-12; 1 Akorinto 12:28-31) Mphatso zochita zozizwitsa zimenezo zinali zothandiza pamene mpingo wachikristu unali waung’ono. Kodi zinali zothandiza motani?

Chifukwa chimodzi n’chakuti mipukutu ya Malemba inali yochepa. Kawirikawiri mipukutu kapena mabuku a mtundu uliwonse ankapezeka ndi anthu olemera okha. M’mayiko achikunja, anthu sankalidziwa Baibulo kapena Mlembi wake, Yehova. Ziphunzitso zachikristu anali kungozifotokoza pakamwa. Motero, mphatso zochita zozizwitsa zinali zothandiza pofuna kusonyeza kuti Mulungu anali kugwiritsa ntchito mpingo wachikristu.

Koma Paulo anafotokoza kuti mphatso zimenezi zikadzakwanitsa cholinga chake zidzatha. Iye anati: “Koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe. Pakuti ife tizidziwa mderamdera, ndimo tinenera mderamdera. Koma pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe.”​—1 Akorinto 13:8-10.

Lerolino, anthu ali nawo mabaibulo, komanso mabuku osiyanasiyana ofotokoza nkhani za m’Baibulo. Akristu ophunzitsidwa bwino oposa 6 miliyoni akuthandiza ena kum’dziwa bwino Mulungu pogwiritsa ntchito Baibulo. Chotero, zozizwitsa sizikufunikanso kuti zipereke umboni wakuti Yesu Kristu ndi Mpulumutsi woikidwa ndi Mulungu kapena kuti zipereke umboni wakuti Yehova akuthandiza atumiki ake.