Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyadirani Kuti Ndinu Mkristu!

Nyadirani Kuti Ndinu Mkristu!

Nyadirani Kuti Ndinu Mkristu!

“Iye amene adzitamanda, adzitamande mwa Ambuye.”​—1 AKORINTO 1:31.

1. Kodi zikuoneka kuti anthu ambiri amaiona motani nkhani yopembedza?

“ALIBE nazo chidwi.” Awa ndi mawu amene mwamuna wina wothirira ndemanga pa nkhani za zipembedzo ananena posachedwapa pofotokoza mmene anthu ambiri akuonera chipembedzo chawo. Iye anafotokoza kuti: “Zimene zafala kwambiri m’zipembedzo masiku ano tingati n’kusapembedza n’komwe.” Ndiyeno anawonjezera kuti “anthu alibe nazo chidwi zopembedza ndipo salabadira n’komwe zikhulupiriro za chipembedzo chawo.” Iye anaona kuti anthu ambiri, “amakhulupirira Mulungu . . . ; koma kungoti samuikira kumtima kwenikweni.”

2. (a) N’chifukwa chiyani zili zosadabwitsa kuti anthu alibe chidwi ndi zinthu zauzimu? (b) Kodi kusowa chidwi ndi zinthu zauzimu n’koopsa motani kwa Akristu oona?

2 Kusowa chidwi kotereku sikodabwitsa kwa ophunzira Baibulo. (Luka 18:8) Ndipo m’zipembedzo zambiri, kusowa chidwi kumeneku n’kosachita kufunsa. Chipembedzo chonyenga chasocheretsa ndi kukhumudwitsa anthu kwa nthawi yaitali. (Chivumbulutso 17:15, 16) Koma kwa Akristu oona, n’zoopsa kukhala ndi mzimu umene wafalawu, wochita zinthu mokokera komanso mozengereza. Tidzalirira kuutsi tikasiya kuikirapo mtima pa chikhulupiriro chathu n’kusiya kuchita khama potumikira Mulungu ndiponso pophunzira choonadi cha m’Baibulo. Yesu anasonyeza kuti kukhala wofunda n’koopsa. Iye anachenjeza Akristu a ku Laodikaya m’zaka 100 zoyambirira kuti: “Suli wozizira kapena wotentha: mwenzi utakhala wozizira kapena wotentha. . . . Uli wofunda.”​—Chivumbulutso 3:15-18.

Kudzidziwa Kuti Ndife Ndani

3. Kodi Akristu anganyadire chifukwa chodziwika ndi zinthu ziti?

3 Kuti Akristu athane ndi kusowa chidwi ndi zinthu zauzimu, m’pofunika kuti adzidziwe bwino kuti iwowo ndi ayani, ndipo ayenera kunyadira kuti amadziwika mwa njira imeneyo. Monga atumiki a Yehova ndiponso ophunzira a Kristu, Baibulo limatiuza kuti ndife ndani makamaka. Limati, ndife “mboni” za Yehova, “antchito anzake a Mulungu,” chifukwa timauza ena ‘uthenga wabwino’ mwakhama. (Yesaya 43:10; 1 Akorinto 3:9; Mateyu 24:14) Ndife anthu ‘okondana wina ndi mnzake.’ (Yohane 13:34) Akristu oona ndi anthu amene, ‘pogwiritsa ntchito luntha lawo la kuzindikira,’ aliyense payekha ‘anaphunzitsa lunthalo kusiyanitsa chabwino ndi choipa.’ (Ahebri 5:14, NW) Ndife “mauniko m’dziko lapansi.” (Afilipi 2:15) Timayesetsa kuti “mayendedwe [athu] mwa amitundu akhale okoma.”​—1 Petro 2:12; 2 Petro 3:11, 14.

4. Kodi wolambira Yehova angadziwe bwanji zimene sizimam’khudza?

4 Olambira enieni a Yehova amadziwanso zimene sayenera kukhudzidwa nazo. Iwo “siali a dziko lapansi,” mofanana ndi Mtsogoleri wawo, Yesu Kristu amene sanali wa dziko lapansi. (Yohane 17:16) Iwo ndi olekana ndi “amitundu,” omwe ndi “odetsedwa m’nzeru zawo, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu.” (Aefeso 4:17, 18) Chifukwa cha zimenezi, otsatira Yesu ‘amakana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, ndipo amakhala ndi moyo m’dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza.’​—Tito 2:12.

5. Kodi mawu otilimbikitsa kuti ‘tidzitamande mwa Ambuye’ tanthauzo lake n’chiyani?

5 Kudzidziwa bwino kuti ndife ndani ndi kuona mmene ubwenzi wathu ulili ndi Wolamulira Wamkulu m’chilengedwe chonse, kumatilimbikitsa ‘kudzitamanda mwa Ambuye.’ (1 Akorinto 1:31) Kodi kumeneku n’kudzitamanda kotani? Pakuti ndife Akristu oona, timanyadira kuti Yehova ndiye Mulungu wathu. Timatsatira mawu olimbikitsa akuti: “Koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m’dziko lapansi.” (Yeremiya 9:24) ‘Timadzitamanda’ chifukwa tili ndi mwayi wodziwa Mulungu, komanso akutigwiritsa ntchito kuti tithandize ena.

Sizophweka

6. N’chifukwa chiyani ena zimawavuta kukumbukira nthawi zonse kuti ndi Akristu?

6 Kunena zoona, sizophweka kukumbukira nthawi zonse kuti ndife Akristu. Mnyamata wina amene anakulira m’banja lachikristu amakumbukira kuti kwa nthawi yaitali anafooka mwauzimu. Iye anati: “Nthawi zina, ndinkaona kuti sindikudziwa chifukwa chake ndinali wa Mboni za Yehova. Ndaphunzitsidwa choonadi kuyambira ubwana wanga. Nthawi zina ndinkaganiza kuti ichi n’chipembedzo changati zipembedzo zina zonse zotchukazi.” Mwina ena asintha mmene amadziwikira potengera zochitika m’malo achisangalalo, m’zofalitsira nkhani, ndiponso chifukwa choona moyo mosiyana ndi mmene Mulungu amauonera, zomwe n’zofala masiku ano. (Aefeso 2:2, 3) Nthawi zina Akristu ena angamadzikayikire ndiponso kuunika mofatsa makhalidwe awo komanso zolinga zawo.

7. (a) Kodi kudziunika koyenera atumiki a Mulungu ndi kuti? (b) Nanga n’kudziunika kotani komwe kuli koopsa?

7 Kodi n’kulakwa nthawi zina kuunika mofatsa za moyo wanu? Ayi. Kumbukirani kuti mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu kupitiriza kudziunika bwinobwino. Iye anati: “Dziyeseni nokha, ngati muli m’chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha.” (2 Akorinto 13:5) Palembali Paulo anali kulimbikitsa Akristu kudziunika moona mtima ndi kuona ngati ayamba kufooka mwauzimu, ndi cholinga choti achitepo kanthu pofuna kuthetsa vutolo. Mkristu amene akudziyesa yekha ngati ali m’chikhulupiriro, ayenera kuona ngati mawu ake ndi zochita zake zimagwirizana ndi zomwe iye amati ndi zimene amakhulupirira. Koma kudziunika ndi zolinga zolakwika n’kosathandiza komanso n’kowononga mwauzimu, chifukwa kungatipatse mtima wofuna kudzitchukitsa, kapena wofuna kudziwa zinthu zomwe zingatiwonongetse ubwenzi wathu ndi Yehova kapena mpingo wachikristu. * Sitingafune kuti ‘chikhulupiriro chathu chitayike’!​—1 Timoteo 1:19.

Nafenso Timakumana ndi Mavuto

8, 9. (a) Kodi Mose anasonyeza motani kudzikayikira kwake? (b) Kodi Yehova anachitanji ataona kuti Mose akudzikayikira? (c) Kodi mawu olimbikitsa a Yehova akukukhudzani motani?

8 Kodi Akristu amene nthawi zina amadzikayikira ayenera kuona ngati alephereratu? Ayi, sayenera kutero! Ndithudi, angalimbe mtima kudziwa kuti kudziona ngati wolephera sikunayambe lero. Mboni zokhulupirika za Mulungu kalero zinkamvanso chimodzimodzi. Mwachitsanzo, talingalirani za Mose, amene anasonyeza chikhulupiriro, kukhulupirika, ndi kudzipereka, mochititsa chidwi kwambiri. Koma atam’patsa ntchito yooneka ngati yoopsa, Mose anafunsa mwamantha kuti: “Ndine yani ine?” (Eksodo 3:11) Zikuoneka kuti iye ankaganiza kuti, ‘Ndine wopanda pake!’ kapena ‘Sindingakwanitse zimenezo!’ N’kutheka kuti zochitika zosiyanasiyana m’moyo wa Mose n’zomwe zinam’chititsa kudziona ngati woperewera. Mwachitsanzo mtundu wake unali mu ukapolo. Aisrayeli anamukana. Komanso sankatha kulankhula bwinobwino. (Eksodo 1:13, 14; 2:11-14; 4:10) Kuwonjezera apo, ankagwira ntchito yodyetsa ziweto, ntchito yomwe kwa Aigupto inali yonyansa. (Genesis 46:34) M’pake kuti ankadziona ngati wosayenera kumasula anthu a Mulungu mu ukapolo!

9 Yehova anam’tsimikizira Mose kuti adzakwanitsa ntchitoyi, mwa kum’patsa malonjezo olimbikitsa kwambiri awiri awa: “Ine ndidzakhala ndi iwe; ndipo ichi ndi chizindikiro cha iwe, chakuti ndakutuma ndine; utatulutsa anthuwo m’Aigupto, mudzatumikira Mulungu paphiri pano.” (Eksodo 3:12) Mulungu anali kuuza mtumiki wake wamanthayo kuti Iye adzakhala naye nthawi zonse. Komanso Yehova anali kutsimikizira kuti adzapulumutsa anthu akewo zivute zitani. Kwa zaka zambiri, Mulungu wakhala akulonjeza kuti adzathandiza anthu ake. Mwachitsanzo, kudzera mwa Mose, anauza mtundu wa Israyeli uli pafupi kulowa m’Dziko Lolonjezedwa kuti: “Khalani amphamvu, limbikani mitima, . . . Yehova Mulungu wanu ndiye amene amuka nanu; iye sadzakusowani, kapena kukusiyani.” (Deuteronomo 31:6) Yehova anatsimikiziranso Yoswa kuti: “Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; . . . ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.” (Yoswa 1:5) Ndipo Akristu nawonso anawalonjeza kuti: “Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.” (Ahebri 13:5) Popeza tili ndi thandizo lamphamvu chotere, tiyeneratu kunyadira kuti ndife Akristu!

10, 11. Kodi Asafu, yemwe anali Mlevi, anathandizidwa bwanji kuti aziganiza moyenera za phindu la utumiki wake kwa Yehova?

10 Patapita zaka pafupifupi 500 Mose atafa, Mlevi wina wokhulupirika dzina lake Asafu analemba moona mtima kuti anali kukayikira phindu lochita zinthu zolungama. Iye anali kuyesetsa kutumikira Mulungu kwinaku akulimbana ndi ziyeso ndiponso zokopa, koma Asafu anaona kuti anthu ena amene anali kunyoza Mulungu anali amphamvu kwambiri ndipo zinthu zinali kuwayendera bwino. Kodi zimenezi zinam’khudza bwanji Asafu? Ananena yekha kuti: “Koma ine, ndikadagwa; mapazi anga akadaterereka. Pakuti ndinachitira nsanje odzitamandira, pakuona mtendere wa oipa.” Anayamba kukayikira ngati kukhala wolambira Yehova kunalidi kwa phindu. M’maganizo mwake ankati: “Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe, ndipo ndinasamba m’manja mosalakwa; popeza andisautsa tsiku lonse.”​—Salmo 73:2, 3, 13, 14.

11 Kodi Asafu anathana nawo bwanji maganizo osowetsa mtenderewa? Kodi anangowanyalanyaza? Ayi. Anamuuza Mulungu zimenezi m’pemphero monga momwe tikuonera mu Salmo 73. Asafu anasintha kwambiri maganizo ake pamene anapita kukachisi. Ali kumeneko, anazindikira kuti palibe chinthu chinanso chopindulitsa kuposa kutumikira Mulungu modzipereka. Atayamba kuonanso bwino zinthu zauzimu, Asafu anazindikira kuti Yehova amadana ndi zinthu zoipa komanso kuti ochita zoipa adzalangidwa. (Salmo 73:17-19) Ndi maganizo ake atsopanowa, Asafu anali wofunitsitsa kuti azidziwika ndi ulemu umene anali nawo pokhala mtumiki wa Yehova. Iye anauza Mulungu kuti: “Ndikhala ndi Inu chikhalire: Mwandigwira dzanja langa lamanja. Mudzanditsogolera ndi uphungu wanu, ndipo mutatero, mudzandilandira m’ulemerero.” (Salmo 73:23, 24) Asafu anayambanso kunyadira naye Mulungu wake.​—Salmo 34:2.

Ankadzidziwa Bwino Lomwe Kuti Anali Ndani

12, 13. Tchulani zitsanzo za m’Baibulo za anthu amene ankanyadira pokhala paubwenzi ndi Mulungu.

12 Njira imodzi yothandiza kuti tizikumbukira kuti ndife Akristu ndiyo kudziunika mofatsa ndiponso kutsatira chikhulupiriro cha olambira okhulupirika. Iwowa anali kunyadira kwambiri kukhala paubwenzi ndi Mulungu ngakhale kuti anali kukumana ndi mavuto. Talingalirani za Yosefe, mwana wa Yakobo. Ali wamng’ono, anam’gulitsa mouma mtima monga kapolo ndipo anam’tengera ku Igupto, kutali kwambiri ndi bambo ake oopa Mulungu komanso achibale amene anali kum’konda ndi kum’thandiza. Ku Igupto, Yosefe analibe munthu woti n’kumupatsa malangizo auzimu, ndipo anakumana ndi zovuta zimene zinayesa makhalidwe ake abwino ndi kudalira kwake Mulungu. Komabe, iye anayesetsa ndi mtima wonse kuti asasinthe mawanga, koma kuti azidziwikabe monga mtumiki wa Mulungu, ndipo anakhalabe wokhulupirika pa zimene anali kudziwa kuti ndi zolondola. Ankanyadira kukhala wolambira Yehova ngakhale kuti zinthu zinali zovuta, ndipo sanachite mantha kufotokoza maganizo ake.​—Genesis 39:7-10.

13 Patatha zaka pafupifupi 800, mtsikana wina wachiisrayeli amene anali kapolo wa Namani, mkulu wa asilikali a Asuri, sanaiwale kuti anali wolambira Yehova. Mtsikanayu atapeza mpata, analimba mtima n’kuchitira umboni Yehova, mwa kufotokoza kuti Elisa ndi mneneri wa Mulungu woona. (2 Mafumu 5:1-19) Patapita zaka, Mfumu yachinyamata Yosiya inasintha kwambiri zinthu zokhudzana ndi chipembedzo, ngakhale kuti zinthu sizinali bwino m’nthawi yake. Inakonzanso kachisi wa Mulungu, ndi kuthandiza mtundu wake kuyambiranso kulambira Yehova. Mfumuyi inkanyadira chikhulupiriro ndi chipembedzo chake. (2 Mbiri, machaputala 34, 35) Ali ku Babulo, Danieli ndi anzake atatu achihebri aja, sanaiwale kuti anali atumiki a Yehova, ndipo pamene anali kupanikizidwa ndi kuyesedwa, iwo anakhalabe okhulupirika. N’zoonekeratu kuti iwowa ankanyadira kuti ndi atumiki a Yehova.​—Danieli 1:8-20.

Nyadirani Kuti Ndinu Akristu

14, 15. Kodi tingadzitamande bwanji chifukwa chokhala Akristu?

14 Atumiki a Mulungu amenewa zinthu zinawayendera bwino chifukwa chakuti ankanyadira nthawi zonse kuti ali paubwenzi ndi Mulungu. Nanga bwanji ifeyo masiku ano? Tingadzitamande bwanji chifukwa chokhala Akristu?

15 Kwenikweni, tingatero poona kuti ndi mwayi waukulu kwambiri kuti tili m’gulu la anthu odziwika ndi dzina la Yehova, odalitsika amenenso Mulungu amakondwera nawo. Mulungu sakayikira n’komwe kuti ndani ali kumbali yake. Panthawi ya mtumwi Paulo zinthu zinali zosokonezeka kwambiri pankhani ya chipembedzo ndipo iye analemba kuti: “Ambuye azindikira iwo amene ali ake.” (2 Timoteo 2:19; Numeri 16:5) Yehova amanyadira ndi anthu “amene ali ake.” Yehovayo amati: ‘Iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m’diso langa.’ (Zekariya 2:8) N’zoonekeratu apa kuti, Yehova amatikonda. Nafenso tiyenera kukhala naye paubwenzi chifukwa chakuti tikum’konda kwambiri. Paulo anati: “Ngati wina akonda Mulungu, yemweyu adziwika ndi Iye.”​—1 Akorinto 8:3.

16, 17. N’chifukwa chiyani Akristu, achinyamata ndi achikulire omwe, ayenera kunyadira cholowa chawo chauzimu?

16 Achinyamata amene akulira m’banja la Mboni za Yehova, ayenera kudziunika bwinobwino kuti aone ngati akudziwikadi monga Akristu, chifukwa chakuti ali paubwenzi wolimba ndi Mulungu. Sayenera kungodalira chikhulupiriro cha makolo awo chokha basi. Ponena za mtumiki aliyense wa Mulungu, Paulo analemba kuti: “Iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwiniyekha.” Ndiyeno Paulo anapitiriza kunena kuti: “Munthu aliyense wa ife adzadziwerengera mlandu wake kwa Mulungu.” (Aroma 14:4, 12) N’zosachita kufunsa kuti kulambira Yehova mosayikirapo mtima kwenikweni chifukwa chakuti tikungotsatira makolo athu, sikungatithandize kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova kwa nthawi yaitali.

17 Mboni za Yehova zakhalapo kuyambira kalekale. Zinayambira pa munthu wokhulupirika uja Abele, yemwe anakhalako zaka pafupifupi 6000 zapitazo, kudzafika pa “khamu lalikulu” la Mboni zamakono, ndiponso namtindi wa olambira Yehova amene adzasangalale ndi moyo wopanda malire. (Chivumbulutso 7:9; Ahebri 11:4) Ifeyo tili m’gulu lamakono la olambira okhulupirikawa. Tilitu ndi cholowa chauzimu chamtengo wapatali zedi!

18. Kodi mfundo zimene timayendera ndi miyezo yathu zimatisiyanitsa bwanji ndi dzikoli?

18 Timadziwikanso monga Akristu chifukwa cha mfundo zimene timayendera, makhalidwe anthu abwino komanso chifukwa chotsatira miyezo yachikristu. Imeneyi ndiyo “Njirayo,” ndipo ndi njira yokhayi yopindulitsa m’moyo komanso yosangalatsira Mulungu. (Machitidwe 9:2; Aefeso 4:22-24) Akristu ‘amatsimikizira zinthu zonse’ ndi ‘kugwira zolimba chimene chili chabwino’! (1 Atesalonika 5:21, NW) Tikudziwa bwino lomwe kusiyana kwakukulu kumene kulipo pakati pa Chikristu ndi dziko lotalikirana ndi Mulunguli. Yehova amasiyanitsa moonekeratu kulambira koona ndi kulambira konyenga. Kudzera mwa mneneri wake Malaki, iye anati: “Mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.”​—Malaki 3:18.

19. Kodi n’chiyani chimene Akristu oona sangalole ngakhale pang’ono?

19 Popeza kuti kudzitamanda mwa Yehova n’kofunika kwambiri m’dziko losokonekerali, kodi n’chiyani chingatithandize kunyadira naye Mulungu wathu nthawi zonse ndi kumakumbukira kuti ndife Akristu? Njira zothandiza zikupezeka m’nkhani yotsatirayi. Pamene mukuona njira zimenezi dziwani kuti ndithu, Akristu oona sangalole ngakhale pang’ono kuti chidwi chawo pa chipembedzo chawo chizilale.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Pano tikungonena za kudzidziwa mmene tilili mwauzimu basi. Ena amene ali ndi vuto la m’maganizo, angachite bwino kupita kuchipatala.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Akristu ‘angadzitamande bwanji mwa Ambuye’?

• Kodi mwaphunzira chiyani pa zitsanzo za Mose ndi Asafu?

• Ndi anthu ati otchulidwa m’Baibulo amene anali kunyadira potumikira Mulungu?

• Kodi tingadzitamande bwanji chifukwa chokhala Akristu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 14]

Kwa kanthawi, Mose anali kudzikayikira

[Zithunzi patsamba 15]

Ambiri mwa atumiki akale a Yehova ankanyadira kuti anali atumiki a Yehova