Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalidwe Labwino ‘Limakometsera Chiphunzitso cha Mulungu’

Khalidwe Labwino ‘Limakometsera Chiphunzitso cha Mulungu’

Khalidwe Labwino ‘Limakometsera Chiphunzitso cha Mulungu’

MARIA ndi mwana wa ku Kransnoyarsk, m’dziko la Russia, amene amaimba bwino zedi moti aphunzitsi ake anamulowetsa mu kwaya ya pasukulu pawo. Pasanapite nthawi yaitali, Maria anapita kwa mphunzitsi wake wina n’kukamulongosolera mwaulemu kuti pali nyimbo zinazake zimene iyeyo sakanatha kuimba nawo. N’chifukwa chiyani anatero? Chifukwa chakuti malinga ndi zimene anaphunzira m’Baibulo, kuimba nyimbo zachipembedzo zoterozo sikugwirizana ndi chikumbumtima chake. Podabwa, aphunzitsiwo anafunsa kuti, ‘Kodi cholakwika n’chiyani ndi kuimba nyimbo zotamanda Mulungu?’

Pofuna kulongosola chifukwa chimene iyeyo sakanaimbira nawo nyimbo yotamanda Mulungu wa Utatu, Maria anatsegula Baibulo lake n’kulongosola kuti Mulungu ndi Yesu Kristu si Mulungu mmodzi ayi, ndiponso analongosola kuti mzimu woyera ndi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. (Mateyu 26:39; Yohane 14:28; Machitidwe 4:31) Maria analongosola kuti: “Aphunzitsiwo ndinapitirizabe kugwirizana nawo. Aphunzitsi ambiri kusukulu kwathu ndi abwino kwambiri. Iwo amafuna kuti tizichita zinthu moona mtima.”

Pachaka chonsecho, zimene Maria anachitazi zinachititsa kuti aphunzitsi ndiponso anzake a m’kalasi mwake azimulemekeza. Maria anati: “Mfundo za m’Baibulo zimandithandiza pamoyo wanga. Potsekera telemu yomaliza, ndinalandira mphotho imene imaperekedwa kwa mwana woona mtima ndiponso wochita zinthu mwadongosolo kwambiri, ndipo makolo anga anawapatsa kalata yowathokoza pophunzitsa bwino mwana wawo.”

Maria anabatizidwa pa August 18, 2001. Iye anati: “Ndine wosangalala kuti ndikutumikira, Mulungu wabwino kwambiri, amene ndi Yehova.” Achinyamata a Mboni za Yehova padziko lonse amachita zinthu mogwirizana ndi mawu a pa Tito 2:10, pamene timawerenga kuti: ‘Kometserani chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu Mulungu m’zinthu zonse.’

[Chithunzi patsamba 32]

Kalata yothokoza ndiponso satifiketi yoyamikira khalidwe labwino

[Chithunzi patsamba 32]

Maria atangobatizidwa kumene, ali ndi makolo ake