Kodi Kumenyana ndi Mawu N’kopweteka Chifukwa Chiyani?
Kodi Kumenyana ndi Mawu N’kopweteka Chifukwa Chiyani?
“Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu?”—YAKOBO 4:1.
POLEMBA funsoli, wolemba Baibulo Yakobo sikuti anali kufunsa asilikali achiroma, amene panthawiyo anali kumenya nkhondo zolanda mayiko. Komanso sikuti anali kufuna kufukula zolinga za Ayuda a m’zaka 100 zoyambirira a m’kagulu kenakake kamene kanaukira ulamuliro wa Aroma. Komano Yakobo anali kunena za mikangano ya pakati pa anthu ochepa, mwina ngakhale anthu awiri okha basi. N’chifukwa chiyani ananena zimenezi? Chifukwa chakuti mikangano imawononga zinthu ngati mmene nkhondo imachitira. Taganizirani zitsanzo za m’Baibulo izi.
Ana a kholo lakale Yakobo, ankadana kwambiri ndi mbale wawo Yosefe moti mpaka anamugulitsa kuukapolo. (Genesis 37:4-28) Patsogolo pake, Sauli, yemwe anali Mfumu ya Israyeli, anayesa kupha Davide. N’chifukwa chiyani anatero? Chifukwa cha nsanje. (1 Samueli 18:7-11; 23:14, 15) M’zaka 100 zoyambirira, akazi awiri achikristu, Euodiya ndi Suntuke, anasokoneza mtendere mu mpingo wonse chifukwa chokangana.—Afilipi 4:2.
Panthawi ina, osati kale kwambiri, anthu awiri akasiyana maganizo ankathetsa mkangano wawowo pomenyana ndi malupanga kapena mfuti. Nthawi zambiri winayo ankaphedwa kapena kulumala kwa moyo wake wonse. Mikangano ya masiku ano, nthawi zambiri zida zake zimangokhala mawu owawa ndiponso okhadzula basi. Ngakhale kuti pa mikanganoyi sipakhala magazi chuchuchu, mawu okhadzulawo amapweteka kwambiri ndiponso amaipitsa mbiri yamunthu. Nthawi zambiri ena amangofera za eni pa nkhondo zamawuzi.
Taganizirani zimene zinachitika zaka zambiri zapitazo wansembe wina wa tchalitchi cha Angilikani atanena kuti wansembe mnzake akuwononga ndalama za tchalitchicho. Mkangano wawo unafika podziwika, ndipo mpingo umene ankachitamo ntchito yawo yaunsembe unagawanikana. Anthu ena mumpingowo ankakana kulowa m’tchalitchi panthawi imene wansembe yemwe iwowo sankagwirizana naye akuchititsa mwambo wamapemphero. Ansembewo ankazondana kwambiri moti anafika
posiya kulankhulana akakumana nthawi ya mapemphero kutchalitchiko. Mkanganowu unachita kufika ponyanyira pamene wansembe amene ananena mnzake uja anadzapezeka ndi nkhani yokhudza zachiwerewere.Bishopu Wamkulu wa ku Canterbury anayesa kuwalangiza ansembe awiriwo, ndipo anati mkangano wawowo unali ngati matenda osachiritsika a “khansa” ndiponso kuti “ukuyalutsa dzina la Ambuye Wathu.” M’chaka cha 1997 mmodzi wa ansembewo anavomera kupuma pa ntchito yake yaunsembe. Winayo anapitirizabe ntchitoyo mpakana kufika pamsinkhu umene wansembe aliyense amayenera kupuma pantchito. Koma iyeyu sanapumebe pantchitoyo mpaka kufika pa tsiku lake lenileni lopumira pantchitoyi, moti anapuma patsiku limene anakwanitsa zaka 70, pa August 7, 2001. Nyuzipepala ya The Church of England Newspaper inati tsiku limene iyeyu anapuma paunsembe linalinso tsiku la chikondwerero cha munthu amene amati ndi Woyera, dzina lake Victricius. Kodi Victricius anali ndani? Iyeyu anali bishopu wa m’zaka za m’ma 300 amene akuti anapatsidwa chilango chokwapulidwa chifukwa chokana kumenya nkhondo m’gulu la asilikali. Poyerekezera mtima wa bishopuyu ndi mtima wa wansembe uja, nyuzipepalayo inati: “[Wansembe amene wapumayu] sanasonyeze mtima wodana ndi nkhondo ya mumpingo.”
Ansembe amenewo akanatha kupewa kuvulazana ndiponso kuvulaza anthu ena akanangotsatira malangizo amene ali pa lemba la Aroma 12:17, 18, lomwe limati: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu zaulemu pamaso pa anthu onse. Ngati n’kutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.”
Nanga inuyo bwanji? Kodi munthu akakukhumudwitsani mumakwiya kwambiri mpaka kufika pomenyana naye ndi mawu? Kapena kodi mumayesetsa kudzigwira kuti musalankhule pambali, n’kukhala wokonzeka kugwirizananso ndi munthuyo? Nanga kodi inuyo mukalakwira munthu winawake, mumangomuzemba basi n’kumayembekezera kuti nkhaniyo idzaiwalika yokha pakapita nthawi? Kapena kodi mumapepesa mwamsanga? Dziwani kuti kuyesetsa kukhalanso mwamtendere ndi anzanu powapempha kuti akukhululukireni kapenanso powakhululukira, kungakuthandizeni kuti mukhale moyo wabwino. Malangizo a m’Baibulo angatithandize kuthetsa mikangano iliyonse, ngakhale itazika mizu motani. Izi n’zimene nkhani yotsatirayi ilongosole.