“Kukhulupirika M’nthawi ya Mayesero”
“Kukhulupirika M’nthawi ya Mayesero”
KUMAYAMBIRIRO kwa mwezi wa April m’chaka cha 1951, boma la Soviet Union lomwe linali ndi mphamvu kwambiri, linaukira gulu lina losalakwa la Akristu kumadzulo kwa dzikolo. Gululi linali la Mboni za Yehova. Mabanja ambirimbiri kuphatikizapo ana aang’ono, amayi apakati, ndiponso anthu okalamba, anawalonga m’sitima n’kuyenda nawo ulendo wowawa wa masiku 20 wopita ku Siberia. Unali ulendo wosabwerera wopita m’dera lovuta kukhalako komanso lotsalira kwambiri.
Mu April 2001, pokumbukira kuti patha zaka 50 chichitikireni zimenezi, ku Moscow anatulutsa filimu yolongosola mmene Mboni za Yehova zinazunzidwira ku Soviet Union pa zaka 50 zimenezi. M’filimuyo, akatswiri a maphunziro a mbiri yakale, ndiponso anthu amene anaona zimenezi ndi maso amasimbamo mmene Mbonizo zinapulumukira n’kumasangalala ngakhale kuti zinali kuvutitsidwa moopsa.
Dzina la filimuyi ndi, Faithful Under Trials—Jehovah’s Witnesses in the Soviet Union, [Kukhulupirika M’nthawi ya Mayesero—Mboni za Yehova ku Soviet Union] ndipo tikunena pano anthu mamiliyoni ambiri ku Russia ndi m’mayiko ena anaionera ndipo anthu ambiri aiyamikira kwambiri kuphatikizaponso akatswiri a maphunziro a mbiri yakale. Nazi zina mwa zimene ananena anthu enaake awiri ophunzira a ku Russia amene akukhala m’dera limene mabanja ambiri a Mboni anapititsidwako:
“Ndinasangalala nayo kwambiri filimuyi. Kuyambira kale ineyo ndakhala ndikuona kuti anthu a chipembedzo chanu ndi anthu abwino kwambiri, koma nditaonera filimuyi, ndaona kuti anthu inu ndinu abwino koposa mmene ndinkaganizira poyamba. Filimu imeneyi anaipanga mwaukatswiri kwambiri. Chinandisangatsa kwambiri n’chakuti munthu aliyense m’filimuyi amanena za maganizo ake a iyeyo payekha. Ndine wosangalala kwambiri ndi a Mboni ngakhale kuti ineyo chipembedzo changa ndi cha Orthodox ndipo sindikuganiza zosintha chipembedzo ayi. Ndingasangalale ngati dipatimenti yathu itakhala ndi filimu imeneyi. Ineyo ndi anzanga taganiza zoti tiwasonyeze filimuyi ophunzira athu ndiponso kuti ikhale mbali ya maphunziro awo.” Ananena zimenezi ndi pulofesa Sergei Nikolayevich Rubtsov, woyang’anira dipatimenti ya maphunziro a mbiri yakale pa yunivesite yotchedwa State Pedagogical University, ya ku Irkutsk, m’dziko la Russia.
“Ndine wosangalala kwambiri ndi filimu imene yatulukayi. Nthawi zambiri popanga filimu yonena za kupondereza anthu, zimakhala zovuta kupanga filimuyo m’njira yakuti nkhani yake ikhale yotsatirika bwinobwino. Koma inuyo munakwanitsa kutero. Ndingasangalale kwambiri ngati mutandibweretsera mafilimu ena amene munapanga.” Ananena zimenezi ndi pulofesa Sergei Ilyich Kuznetsov, woyang’anira dipatimenti ya maphunziro a mbiri yakale pa yunivesite yotchedwa Irkutsk State University, m’dziko la Russia.
Mboni za Yehova za ku Siberia zinasangalala nayonso kwambiri filimuyi. Nazi zina mwa zinthu zimene Mbonizi zinanena:
“Panthawi imene nkhani zosonyezedwa m’filimuyi zinkachitika, anthu ambiri a ku Russia anauzidwa zabodza pankhani ya ntchito za Mboni za Yehova. Koma ataonera filimuyi, iwo akutha kuona kuti gulu lathuli si kuti ndi kagulu kampatuko, monga mmene
iwo ankaganizira poyamba. Anthu ena amene akhala Mboni chaposachedwa anati: ‘Ife sitinkadziwa ngakhale pang’ono kuti nthawi yonseyi tinkakhala ndiponso kugwira ntchito limodzi ndi abale athu achikristu amene anapirira mpaka kufika pamenepa.’ Ataonera filimuyi, munthu wina wa Mboni analongosola kuti akulakalaka atayamba upainiya wa nthawi zonse.” Ananena zimenezi ndi Anna Vovchuk, amene anasamutsidwa kwawo n’kupititsidwa ku Siberia.“Ndikuonera filimuyi ndinagwidwa nthumanzi kwambiri kuona akusonyeza wapolisi wa m’gulu la apolisi achinsinsi akugogoda pa khomo la Mboni. Zinandikumbutsa kale pamene apolisiwa anagogoda pakhomo pathu, ndipo ndikukumbukira kuti mayi anga ananena kuti: ‘Mwina akudzatidziwitsa zakuti kwinakwake kwabuka moto.’ Koma filimuyi imandikumbutsanso kuti Mboni zambiri zinavutika kuposa ineyo. Zonsezi zimatilimbikitsa kwambiri ndiponso zimatipatsa mphamvu kuti tipitirize kutumikira Yehova.” Ananena zimenezi ndi Stepan Vovchuk, amene anasamutsidwa kwawo n’kupititsidwa ku Siberia.
“Ndine mwana wa Mboni zimene zinasamutsidwa kwawo. Motero ndinkaganiza kuti nkhani za nthawi imeneyo ndinazimva mokwanira. Koma nditaonera filimuyi, ndinazindikira kuti palibe chimene ndimadziwa. Misozi inali ndee m’maso mwanga pomva nkhani zimene anthu anali kusimba m’filimuyi. Panopo ndinaona kuti nkhanizi ndi zenizeni osati nthano chabe ayi. Filimuyi yalimbikitsa ubwenzi wanga ndi Mulungu ndipo yandithandiza kukonzekera kudzapirira zovuta zina zilizonse za m’tsogolomu.” Ananena zimenezi ndi Vladimir Kovash, wa ku Irkutsk.
“Filimuyi ineyo ndikuona kuti n’njokhudza mtima kwambiri kuposa nkhani yochita kulembedwa. Poonerera ndiponso kumvetsera abale akusimba nkhani zimene zinawachitikira, ndinkangoona ngati kuti ndinali nawo limodzi panthawi yonse imene zinthuzo zinkawachitikira. Chitsanzo cha mbale amene ankajambula makadi n’kumatumizapo uthenga wopita kwa ana ake aakazi aang’ono pamene iyeyo anali m’ndende chimandilimbikitsa kuti ndiziyesetsa kuwafika pamtima ana anga ndikamawaphunzitsa choonadi cha m’Baibulo. Zikomo kwambiri. Filimu imeneyi yachititsa kuti Mboni za Yehova ku Russia zione kuti zilidi mbali ya gulu la Yehova la padziko lonse.” Ananena zimenezi ndi Tatyana Kalina, wa ku Irkutsk.
“Mawu akuti, ‘Kuona chinthu kamodzi kumaposa kungomva za chinthucho nthawi zambirimbiri’ akugwirizana zedi ndi filimuyi. Ndi filimu yogwira mtima, yosonyeza zinthu zenizeni, yofotokoza za moyo wathudi. Nditaionera ndinakhala nthawi ndikuiganizira. Filimuyi inandithandiza kuti ndiganizire mozama za moyo wa Mboni zimene zinathamangitsidwa kwawozo. Panopo ndikamayerekezera moyo wawo panthawiyo ndi moyo wathu panopa zimandithandiza kuti ndiziona mavuto athu masiku ano m’njira inaina.” Ananena zimenezi ndi Lidia Beda, wa ku Irkutsk.
Filimuyi pakali pano anaitulutsa m’zinenero 25 ndipo anthu akuikonda kwambiri padziko lonse. * Filimu yonseyo inasonyezedwa pa wailesi zakanema m’mizinda ya St. Petersburg, Omsk, ndiponso mizinda ina ya ku Russia. Inasonyezedwanso m’mizinda ya ku Ukraine ya Vynnytsya, Kerch, Melitopol ndiponso m’chigawo cha Lviv. Filimuyi yapatsidwaponso mphoto ndi mabungwe a padziko lonse oona za mafilimu abwino koposa.
Chikoka cha uthenga wa m’filimu imeneyi chagona pa zitsanzo za anthu wamba ambirimbiri amene anaonetsa chamuna chogometsa ndiponso kulimba kwauzimu pa zaka zambiri zimene anali kuzunzidwa. Mboni za Yehova ku Soviet Union zinasonyezadi mosakayikira kuti zinali zokhulupirika m’nthawi ya mayesero. Mboni za Yehova zingasangalale kukupezerani filimuyi ngati mutafuna kuionera. Yesetsani kupezana ndi wa Mboni aliyense m’dera lanulo pa nkhani imeneyi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 13 Filimuyi ili m’zinenero izi: Chibugariya, Chikantonizi, Chitcheki, Chidanishi, Chidatchi, Chingelezi, Chifinishi, Chifalansa, Chijeremani, Chigiriki, Chihangare, Chiindonesiya, Chiitaliyana, Chijapanizi, Chikoreyani, Chilituyeniyani, Chimandarini, Chinowejani, Chipolishi, Chiromeniyani, Chirashani, Chisilovaki, Chisiloveniyani, Chisipanya, ndi Chiswidishi.
[Mawu a Chithunzi patsamba 8]
Stalin: U.S. Army photo
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Stalin: U.S. Army photo