Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Malangizo Anzeru kwa Okwatirana

Malangizo Anzeru kwa Okwatirana

Malangizo Anzeru kwa Okwatirana

“Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye. Amuna inu, kondani akazi anu.”​—Aefeso 5:22, 25.

1. Kodi ukwati tiyenera kuuona motani?

YESU ananena kuti muukwati Mulungu amaphatika mwamuna ndi mkazi kuti akhale “thupi limodzi.” (Mateyu 19:5, 6) Ukwati umabweretsa pamodzi anthu awiri aumunthu wosiyana amene amachita kuphunzira kuchita zinthu mogwirizana ndiponso mothandizana kuti akwaniritse zolinga zawo. Ukwati ndi lumbiro la moyo wonse, osati pangano la kanthawi chabe losavuta kuliswa. M’mayiko ambiri sizivuta kusudzulana, koma kwa Akristu, ukwati n’ngopatulika. Umathetsedwa pa chifukwa chachikulu chimodzi chokha basi.​—Mateyu 19:9.

2. (a) Kodi pali zinthu zotani zimene zingathandize anthu okwatirana? (b) Kodi n’chifukwa chiyani kuli kofunika kuyesetsa kuti ukwati uziyenda bwino?

2 Mlangizi wina wa nkhani za ukwati anati: “Ukwati wabwino umasintha nthawi zonse mogwirizana ndi nkhani ndiponso mavuto amene akubuka m’banjamo, ndiponso mogwirizana ndi zinthu zimene banjalo lingathandizike nazo panthawiyo.” Kwa Akristu, zinthu zoterezi ndi zinthu monga malangizo ochokera m’Baibulo, Akristu anzawo, ndiponso ubwenzi wabwino ndi Yehova womwe umalimbikitsidwa ndi pemphero. Ukwati womwe ukuyenda bwino umakhalapobe ngakhale panthawi za mavuto, ndipo okwatiranawo amasangalala pa zaka zonse zimene akhalira limodzi. Ndiponso chachikulu n’chakuti, Yehova Mulungu, yemwe ali Woyambitsa ukwati, amalemekezeka ndi ukwati wotero.​—Genesis 2:18, 21-24; 1 Akorinto 10:31; Aefeso 3:15; 1 Atesalonika 5:17.

Tsanzirani Yesu ndi Mpingo Wake

3. (a) Nenani mwachidule malangizo amene Paulo anapereka kwa anthu okwatirana. (b) Kodi Yesu anapereka chitsanzo chabwino chotani?

3 Zaka 2,000 zapitazo, mtumwi Paulo anapereka malangizo anzeru kwa Akristu okwatirana polemba kuti: “Monga Eklesia amvera Kristu, koteronso akazi amvere amuna awo m’zinthu zonse. Amuna inu, kondani akazi anu, monganso Kristu anakonda Eklesia, nadzipereka yekha m’malo mwake.” (Aefeso 5:24, 25) Chimenechitu n’chitsanzo chabwino kwambiri! Akazi achikristu amene amamvera amuna awo modzichepetsa amatsanzira mpingo chifukwa umavomereza ndiponso kumvera mfundo ya umutu. Akristu amene amakonda akazi awo pamtendere ndi pamavuto pomwe, amasonyeza kuti akuyesetsa kutsatira chitsanzo cha Kristu chokonda mpingo ndi kuusamalira.

4. Kodi amuna angatsanzire bwanji Yesu?

4 Amuna achikristu ndi mitu ya mabanja awo, koma nawonso ali ndi mutu wawo, Yesu. (1 Akorinto 11:3) Motero, poti Yesu amasamalira mpingo wake, amuna nawo ayenera kusamalira mwachikondi mabanja awo ngakhalenso kumbali ya zinthu zauzimu. Ayenerabe kutero ngakhale ngati atamachita kuvutikira. Amayenera kuganizira kwambiri za mabanja awo, osati za zolakalaka zawo ndiponso zinthu zowakomera iwowo. Yesu anati: “Zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Mfundo imeneyi n’njofunika kuiganizira kwambiri muukwati. Paulo anasonyeza zimenezi pamene ananena kuti: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. . . . Munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga.” (Aefeso 5:28, 29) Mwamuna ayenera kulera kapena kuti kupezera chakudya mkazi wake ndiponso ayenera kum’sunga bwino mofanana ndi mmene mwamunayo amachitira payekha.

5. Kodi akazi angatsanzire bwanji mpingo wachikristu

5 Akazi olambira Mulungu amatengera chitsanzo cha mpingo wachikristu. Yesu ali padziko lapansi, ophunzira ake anali osangalala kusiya ntchito zawo zakale n’kuyamba kumutsatira. Yesu atafa, iwo anapitirizabe kumumvera. Tsopano patha zaka pafupifupi 2,000, ndipo mpingo woona wachikristu ukupitirizabe kumvera Yesu ndi kutsatira utsogoleri wake m’zinthu zonse. Akazi achikristu nawonso sanyoza amuna awo kapena kuyesa kuchepetsa umutu wa m’banja umene Malemba amatchula. M’malo mwake, iwo amathandiza amuna awo komanso amawamvera ndiponso kugwirizana nawo maganizo, motero amunawo amalimbikitsidwa. Mwamuna ndi mkazi akamachita zinthu mwachikondi chotere, ukwati wawo umayendadi bwino ndipo onse awiri amakhala osangalala muukwatiwo.

Pitirizani Kukhala Nawo

6. Kodi Petro anapereka malangizo otani kwa amuna, ndipo kodi malangizo amenewa n’ngofunika chifukwa chiyani?

6 Mtumwi Petro anaperekanso malangizo kwa anthu okwatirana, ndipo amuna anawauza mawu osapita m’mbali akuti: “Khalani nawo [akazi anu] monga mwa chidziwitso, ndi kuchitira mkazi ulemu, monga chotengera chochepa mphamvu, monganso wolowa nyumba pamodzi wa chisomo cha moyo, kuti mapemphero anu angaletsedwe.” (1 Petro 3:7) Mawu otsiriza a vesi limeneli akutithandiza kuona kuti malangizo amene Petro anaperekawa n’ngofunika kuwatenga mosamala. Ngati mwamuna sakulemekeza mkazi wake, ubwenzi wake ndi Yehova umasokonezeka. Mapemphero ake samvedwa.

7. Kodi mwamuna azilemekeza bwanji mkazi wake?

7 Koma kodi amuna angachitire bwanji ulemu akazi awo? Kuchitira ulemu mkazi ndiko kukhala naye mwachikondi ndiponso momulemekeza. Kwa anthu ambiri kalelo zinali zachilendo kwambiri kukhala ndi mkazi m’njira yokoma mtima chonchi. Munthu wina wophunzira kwambiri wa ku Greece analemba kuti: “M’malamulo a Aroma, akazi sankapatsidwa ufulu uliwonse. Kwa moyo wawo wonse, ufulu wawo unali wofanana ndi wa mwana basi. . . . Nthawi zonse anayenera kumvera zofuna za amuna awo, ndipo mwamunayo ankawachita chilichonse chimene angafune.” Izitu zinali zosiyana kwambiri ndi chiphunzitso cha Chikristu. Mwamuna aliyense wachikristu ankalemekeza mkazi wake. Mwamunayo ankamuchitira mkazi wake zinthu zogwirizana ndi mfundo zachikristu, osati zilizonse zimene zangom’bwerera m’mutu mwake. Kuphatikizanso apo, ankamuganizira “monga mwa chidziwitso,” podziwa kuti n’ngopanda mphamvu.

Kodi Akazi Ndi “Chotengera Chochepa Mphamvu” M’njira Yotani?

8, 9. Kodi akazi n’ngofanana ndi amuna m’njira zotani?

8 Ponena kuti akazi ndi “chotengera chochepa mphamvu,” Petro samatanthauza kuti akazi n’ngoperewera pa nzeru kapena pa moyo wauzimu powayerekezera ndi amuna. N’zoona kuti amuna ambiri achikristu ali ndi maudindo mumpingo amene akazi sayembekezera kukhala nawo, komanso m’banja akazi amayenera kumvera amuna awo. (1 Akorinto 14:35; 1 Timoteo 2:12) Komabe amuna ndiponso akazi, onse amafunika kukhala ndi chikhulupiriro, kukhala opirira ndiponso amakhalidwe abwino. Ndipo monga mmene Petro ananenera mkazi ndi mwamuna wake, onse ndi ‘olowa nyumba . . . a chisomo cha moyo.’ Pankhani ya chipulumutso, Yehova Mulungu sasiyanitsa pakati pa amuna ndi akazi. (Agalatiya 3:28) Petro ankalembera kalata yakeyi Akristu odzozedwa a m’zaka 100 zoyambirira. Motero mawu ake anakumbutsa amuna achikristu kuti pakuti iwowo pamodzi ndi akazi awo ndi “olowa anzake a Kristu” onse anali ndi chiyembekezo chomwecho chokakhala kumwamba. (Aroma 8:17) Tsiku lina, onse pamodzi adzakhala ansembe ndi mafumu mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu.​—Chivumbulutso 5:10.

9 Akazi odzozedwa achikristu sanali apansi m’njira iliyonse powayerekezera ndi amuna awo odzozedwa. Ndipo mfundo yomweyi imagwiranso ntchito kwa amuna ndi akazi a chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi pano. Amuna pamodzinso ndi akazi a “khamu lalikulu” amatsuka zovala zawo n’kuziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa. Amuna pamodzinso ndi akazi amatama Yehova padziko lonse “usana ndi usiku.” (Chivumbulutso 7:9, 10, 14, 15) Amuna pamodzinso ndi akazi amayembekezera kudzakhala ndi “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu,” ndipo panthawiyi adzakhala ndi “moyo weniweniwo.” (Aroma 8:21; 1 Timoteo 6:19) Kaya ndi odzozedwa, kapena ndi a nkhosa zina, Akristu onse amatumikira Yehova pamodzi monga “gulu limodzi” lokhala ndi “mbusa mmodzi.” (Yohane 10:16) Ichitu n’chifukwa chomveka kwambiri choti amuna ndi akazi achikristu azilemekezana.

10. Kodi akazi ndi ‘zotengera zochepa mphamvu’ m’njira yotani?

10 Komano kodi akazi ndi ‘zotengera zopanda mphamvu’ m’njira yotani? Zikuoneka kuti Petro anali kunena za mfundo yoti nthawi zambiri, akazi amakhala ndi matupi aang’onopo kuyerezera ndi amuna ndiponso akazi n’ngocheperapo mphamvu. Kuphatizanso apo, pakuti ndife anthu opanda ungwiro, mphatso yapadera yobereka imafooketsa thupi la akazi. Akazi akafika msinkhu wobereka amavutika m’thupi nthawi ndi nthawi. Motero amafunika kuwasamalira mwapadera ndiponso kuwaganizira akamakumana ndi zoterezi kapenanso akafooka m’thupi chifukwa cha uchembere. Mwamuna amene amalemekeza mkazi wake, amenenso amazindikira kuti amafunika kumulimbikitsa, angathandize kwambiri kuti banja lake liziyenda bwino.

M’banja Limene Mwamuna ndi Mkazi N’ngosiyana Zipembedzo

11. Kodi ngakhale mwamuna ndi mkazi atakhala osiyana zipembedzo ukwati wawo ungayende bwino m’njira yotani?

11 Kodi zinthu zingayende bwanji ngati mwamuna ndi mkazi amakhulupirira zinthu zosiyana pankhani ya chipembedzo chifukwa chakuti mwina winayo anavomereza choonadi chachikristu patatha nthawi atalowa m’banja pamene mnzakeyo sanatero? Kodi ukwati woterewu ungathe kuyenda bwino? Pali maukwati ambiri otere amene akhala akuyenda bwino. Mwamuna ndi mkazi osiyana maganizo pankhani ya chipembezo angathebe kukhala ndi ukwati woyenda bwino m’njira yakuti ukwatiwo ungathe kukhala wokhalitsa ndiponso wochititsa kuti onse akhale osangalala. Komanso ukwatiwu Yehova amauona kuti ndi ukwati weniweni, ndiponso kuti iwowo ndi “thupi limodzi.” Motero amuna kapena akazi achikristu amalangizidwa kuti ayenera kukhala nayebe mnzawo wosakhulupirira ngati iyeyo akufuna. Ngati pali ana, anawo amatha kupindula chifukwa cha kukhulupirika kwa kholo la Chikristulo.​—1 Akorinto 7:12-14.

12, 13. Potsatira malangizo a Petro, kodi akazi achikristu angathandize bwanji amuna osakhulupirira?

12 Petro analangiza mwachifundo akazi achikristu amene amuna awo sali Akristu. Mawu akewo angathenso kugwira ntchito kwa amuna achikristu amene ukwati wawo uli wotero. Petro analemba kuti: “Akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, akakodwe opanda mawu mwa mayendedwe a akazi; pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu.”​—1 Petro 3:1, 2.

13 Ngati mkazi angathe kumuuza mochenjera mwamuna wake za zimene amakhulupirira, ndi bwino kutero. Komano angatani ngati mwamunayo sakufuna kumvera? Sangam’kakamize chifukwa uko n’kufuna kwake. Komabe sikuti zikatero ndiye kuti palibenso njira ina iliyonse, chifukwatu khalidwe lachikristu palokha limapereka umboni wamphamvu kwabasi. Amuna ambiri amene poyamba sankachita chidwi ndi chikhulupiriro cha akazi awo, mwinanso ankatsutsa kumene, pambuyo pake anasanduka anthu “ofuna moyo wosatha” ataona khalidwe labwino la akazi awo. (Machitidwe 13:48, NW) Ngakhale mwamuna atakhala kuti savomereza choonadi chachikristu, angasangalale nawo makhalidwe abwino a mkazi wake, motero banjalo lingamayende bwino. Mwamuna wina amene mkazi wake ndi wa Mboni za Yehova anavomereza kuti iyeyo sangawakwanitse makhalidwe abwino kwambiri a Mboni za Yehova. Komabe ananena kuti ndi “wosangalala kukhala ndi mkazi wabwino chonchi” ndipo anam’tama mkazi wakeyo moona mtima komanso anatama anzake a Mboni, m’kalata imene analembera ku nyuzipepala inayake.

14. Kodi amuna angathandize bwanji akazi awo osakhulupirira?

14 Amuna achikristu amene atsatira mfundo za m’mawu a Petro nawonso athandiza akazi awo kusintha chifukwa cha khalidwe lawo labwino. Akazi osakhulupirira aona kuti amuna awo ayamba kuchita zinthu mosungadi banja, asiya kuwononga ndalama posuta fodya, pomwa mowa, ndi potchova juga, ndiponso asiya kutukwana. Ena mwa amuna ndi akazi osakhulupirirawa akumanapo ndi anthu ena a mumpingo wachikristu. Iwo anagoma kwambiri kuona chikondi cha ubale wachikristu, ndipo zimene anaona pakati pa abalewo zinawachititsa kuti ayambe kukonda Yehova.​—Yohane 13:34, 35.

“Munthu Wobisika Wamtima”

15, 16. Kodi ndi khalidwe lotani limene mkazi wachikristu angaonetse kuti asinthe mwamuna wake wosakhulupirira?

15 Kodi ndi khalidwe lotani limene lingasinthe mwamuna? Ndi khalidwe limene akazi achikristu amakhala nalo mongadi Akristu. Petro anati: “Kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kuvala za golidi, kapena kuvala chovala; koma kukhale munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu. Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna awo a iwo okha; monga Sara anamvera Abrahamu, namutcha iye mbuye; ameneyo mukhala ana ake ngati muchita bwino, osaopa choopsa chili chonse.”​—1 Petro 3:3-6.

16 Petro analangiza akazi achikristu kuti asamadalire maonekedwe awo akunja. M’malo mwake azikhala ndi khalidwe lochititsa mwamuna wawo kuona kuti zimene Baibulo limaphunzitsa zikukhudza mtima wawo. Mwamunayo aziona mmene mkazi wake akusinthira n’kuvala umunthu watsopano. Mwina angathe kusiyanitsa umunthu umenewu ndi umunthu wakale umene mkaziyo anali nawo poyamba. (Aefeso 4:22-24) N’zosakayikitsa kuti mwamunayo angasangalale kwambiri poona “mzimu wofatsa ndi wachete” umene mkazi wakeyo akuonetsa. Khalidwe kapena kuti mzimu umenewu umasangalatsa mwamunayo komanso ndi “wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.”​—Akolose 3:12.

17. Kodi Sara ndi chitsanzo chabwino motani kwa akazi achikristu?

17 Sara anatchulidwa monga chitsanzo, ndipotu iyeyu ndi chitsanzodi chabwino kwa akazi okwatiwa, ngakhale amuna awo atakhala osakhulupirira. N’zosakayikitsa kuti Sara ankaona Abrahamu ngati mutu wake. Ngakhale mumtima mwake, iye ankamutcha Abrahamu kuti ‘Ambuye.’ (Genesis 18:12) Komatu zimenezi sizinamunyozetse Sarayo ayi. N’zoonekeratu kuti iye anali mkazi wolimba mwauzimu ndipo payekha, anali ndi chikhulupiriro champhamvu mwa Yehova. Inde, iyeyu ali m’gulu la ‘mtambo waukulu wa mboni’ zimene chitsanzo chawo cha chikhulupiriro chiyenera kutilimbikitsa kuti “tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira.” (Ahebri 11:11; 12:1) Mkazi wachikristu akakhala ngati Sara sindiye kuti akunyozeka ayi.

18. Kodi maukwati okhala ndi mwamuna kapena mkazi wosakhulupirira ayenera kutsatira mfundo ziti?

18 M’banja limene mwamuna ndi mkazi sali achipembedzo chimodzi, mutu wa banjalo ndi mwamunayobe basi. Ngati mwamunayo ali wokhulupirira ayenera kusanyoza zimene mkazi wakeyo amakhulupirira komano azisamala kuti potero asachite zinthu zotsutsana ndi chikhulupiriro cha iye mwini. Ngati mkazi ndiye wokhulupirira, nayenso sayenera kuchita zinthu zotsutsana ndi chikhulupiriro chake. (Machitidwe 5:29) Komabe, sayenera kunyoza umutu wa mwamuna wake. Ayenera kulemekeza udindo wa mwamuna wake n’kupitiriza kukhala “ku lamulo la mwamunayo.”​—Aroma 7:2.

Malangizo Anzeru a M’Baibulo

19. Kodi zina mwa zinthu zimene zingabweretse mavuto muukwati ndi ziti, koma kodi n’kuthana nazo bwanji zinthuzi?

19 Masiku ano pali zinthu zambiri zimene zingabweretse vuto muukwati. Pali amuna ena amene amalephera kukwanitsa maudindo awo. Akazi ena safuna kumvera umutu wa amuna awo. M’mabanja ena mkazi kapena mwamuna amazunzidwa ndi mnzakeyo. Komanso Mkristu angavutike kukhala wokhulupirika chifukwa cha mavuto a zachuma, kupanda ungwiro, ndiponso mzimu wa dzikoli womwe umalimbikitsa zinthu monga chiwerewere ndiponso makhalidwe oipa. Komabe, amuna ndi akazi achikristu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo, ngakhale pa mavuto, amadalitsidwa ndi Yehova. Zinthu zimayendako bwino ndithu ngakhale zitakhala kuti mwamuna kapena mkazi yekha ndiye amatsatira mfundo za m’Baibulo. Komanso, Yehova amakonda ndiponso kuchirikiza atumiki ake amene saswa pangano laukwati ngakhale atakumana ndi zovuta. Iye saiwala kukhulupirika kwawo.​—Salmo 18:25; Ahebri 6:10; 1 Petro 3:12.

20. Kodi Petro anapereka malangizo otani kwa Akristu onse?

20 Atamaliza kupereka malangizo kwa amuna ndi akazi apabanja, mtumwi Petro anamaliza ndi mawu olimbikitsa akuti: “Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa; osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.” (1 Petro 3:8, 9) Awatu ndi malangizo anzeru kwambiri kwa aliyense, koma makamaka kwa okwatirana.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi amuna achikristu amatsanzira bwanji Yesu?

• Kodi akazi achikristu amatsanzira bwanji mpingo?

• Kodi amuna angachitire bwanji ulemu akazi awo?

• Kodi ndi njira yotani imene ili yabwino kwambiri kuitsatira kwa mkazi wachikristu amene mwamuna wake ali wosakhulupirira?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Mwamuna wachikristu amakonda mkazi wake ndi kumusamalira

Mkazi wachikristu amalemekeza mwamuna wake ndi kum’patsa ulemu

[Chithunzi patsamba 17]

Mosiyana ndi lamulo lachiroma, chiphunzitso cha Chikristu chinkalamula mwamuna kuchitira ulemu mkazi wake

[Chithunzi patsamba 18]

Amuna pamodzinso ndi akazi a “khamu lalikulu” amayembekezera moyo wosatha m’Paradaiso

[Chithunzi patsamba 20]

Sara ankaona kuti Abrahamu anali mbuye wake