Tinalalikira M’madera Akutali Chifukwa Chosamukasamuka
Mbiri ya Moyo Wanga
Tinalalikira M’madera Akutali Chifukwa Chosamukasamuka
YOSIMBIDWA NDI RICARDO MALICSI
Anandichotsa pantchito chifukwa chokana kulowerera ndale popeza ndine Mkristu. Zitatero ndinakhala pansi ndi banja langa n’kupemphera kwa Yehova kuti atithandize kukonza tsogolo lathu. M’pempherolo tinatchulamo kuti tikufuna kuwonjezera njira zochitira utumiki wathu. Posakhalitsa tinayamba ulendo wosamukasamuka umene unatifikitsa m’mayiko 8, a ku Africa ndi ku Asia. Motero, tinatha kuchita utumiki m’madera akutali.
INE ndinabadwira ku Phillipines mu 1933, m’banja lomwe linali m’tchalitchi cha Philippines Independent Church. Anthu tonse 14 a m’banja mwathu tinali a tchalitchi chimenechi. Ndili ndi zaka pafupifupi 12, ndinapemphera kwa Mulungu kuti andisonyeze chipembedzo choona. Mphunzitsi wanga wina anandiika m’kalasi yophunzira zachipembedzo, ndipo ndinafika pokhala m’Katolika wolimba kwambiri. Sindinkalephera kupita kokalapa Loweruka ndiponso ku Misa Lamlungu. Komabe pang’ono ndi pang’ono zimenezi ndinayamba kuzikayikira ndiponso sizinkandigwira mtima. Ndinkavutika ndi mafunso okhudza zimene zimachitika kwa anthu akafa, okhudza moto wa helo, komanso chiphunzitso cha Utatu. Mayankho amene atsogoleri achipembedzo ankandiuza anali osamveka ndiponso osagwira mtima.
Kupeza Mayankho Ogwira Mtima
Ndili ku koleji, ndinalowa m’gulu linalake limene linandichititsa kuti ndiyambe ndewu, kutchova njuga, kusuta, ndiponso makhalidwe ena olowerera. Tsiku lina madzulo ndinakumana ndi
mayi ake a mnyamata wina wa m’kalasi mwathu. Iwo anali a Mboni za Yehova. Ndinawafunsa mafunso angati amene ndinafunsa aziphunzitsi anga a zachipembedzo aja. Mayiwa anayankha funso langa lililonse ndi Baibulo, ndipo ndinakhutira kuti zimene anali kunenazo zinalidi zoona.Ndinagula Baibulo n’kuyamba kuliphunzira ndi a Mboni. Posakhalitsa ndinayamba kupita kumisonkhano yonse ya Mboni za Yehova. Potsatira mawu anzeru a m’Baibulo akuti “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma,” ndinasiyana nawo anzanga akhalidwe loipa aja. (1 Akorinto 15:33) Zimenezi zinandithandiza kuti ndiphunzire bwino Baibulo mpaka kufika podzipatulira kwa Yehova. Nditabatizidwa mu 1951, ndinachita utumiki wa nthawi zonse (upainiya) kwa nthawi yochepa. Kenaka mu December 1953, ndinakwatira Aurea Mendoza Cruz, amene anakhala mnzanga ndiponso wotumikira nane limodzi mokhulupirika kwa moyo wonse.
Yankho la Mapemphero Athu
Tinkalakalaka kwambiri titakhala apainiya. Komabe, zofuna kutumikira Yehova mmene tingathere sizinatheke panthawi yomweyo. Koma sitinalekebe kupempha Yehova kuti atitsegulire mipata ina yomutumikira. Ngakhale kuti tinkatero, moyo wathu sunali wofewa ayi. Komabe, sitinaiwale zolinga zathu zauzimu, ndipo pamene ndinali ndi zaka 25 ndinaikidwa kukhala mtumiki wa mpingo, amene ali woyang’anira wotsogolera mumpingo wa Mboni za Yehova.
Nditayamba kudziwa bwino Baibulo ndiponso kumvetsa bwino mfundo za Yehova za makhalidwe abwino ndinazindikira kuti ntchito yanga inali yotsutsana ndi mfundo ya kusalowerera za m’dziko monga Mkristu. (Yesaya 2:2-4) Motero ndinaganiza zosiya ntchitoyo. Pamenepa chikhulupiriro chathu chinayesedwa. Kodi banja langa ndikanalisamalira bwanji? Apa tinapempheranso kwa Yehova Mulungu. (Salmo 65:2) Tinamuuza za nkhawa zathu zonse, komanso tinamuuza zakuti tikufunitsitsa kwambiri kutumikira m’madera amene mukufunikira alaliki ambiri a Ufumu. (Afilipi 4:6, 7) Panthawiyi sitinkaganizako n’komwe kuti patsogolo tidzapeza mipata yosiyanasiyana yotumikira m’njira imeneyi.
Kuyamba Ulendo Wathu
M’mwezi wa April, 1965, ndinapeza ntchito yoyang’anira ozimitsa moto wa ngozi za ndege pa bwalo la ndege la Vientiane International Airport, ku Laos, ndipo tinasamukira kumeneko. Mumzinda wa Vientiane munali Mboni 24, ndipo tinkalalikira pamodzi ndi amishonale komanso abale ochepa a komweko. Kenaka anandisamutsira ku bwalo la ndege la Udon Thani Airport, ku Thailand. M’tauni ya Udon Thani munalibe a Mboni ena aliwonse. Motero, banja lathu linkachita palokha misonkhano yonse ya mlungu ndi mlungu. Tinkalalikira kunyumba ndi nyumba, tinkachita maulendo obwereza, ndiponso tinkayambitsa maphunziro a Baibulo.
Tinakumbukira mawu a Yesu olimbikitsa ophunzira ake kuti ayenera ‘kubala chipatso chambiri.’ (Yohane 15:8) Motero tinali ofunitsitsa kutsatira chitsanzo chawo n’kupitiriza kulalikira uthenga wabwino. Posakhalitsa zinthu zinayamba kutiyendera bwino. Mtsikana wina wa ku Thailand anavomera kuphunzira choonadi ndipo anadzakhala mlongo wathu mwauzimu. Anthu awiri a ku North America anavomeranso choonadi ndipo patapita nthawi anadzakhala akulu mumpingo. Tinapitiriza kulalikira uthenga wabwino kwa zaka zopitirira teni kumpoto kwa dziko la Thailand. Ndife osangalala kwambiri kuti tsopano ku Udon Thani kuli mpingo. Zina mwa mbewu zimene tinadzala zikupitirizabe kubereka.
Komano n’zomvetsa chisoni kuti tinayenera kusamukanso, ndipo tinapemphera kuti “Mwini zotuta” atithandize kupitiriza kuchita nawo ntchito yolalikira. (Mateyu 9:38) Kenaka, kuntchito anatisamutsa n’kutipititsa mu mzinda wa Tehran, womwe ndi likulu la dziko la Iran. Apa n’kuti dzikoli likulamulidwa ndi olamulira otchedwa Shah.
Kulalikira M’magawo Ovuta
Titafika ku Tehran, tinapezana ndi abale athu auzimu nthawi yomweyo. Tinkasonkhana ndi kagulu kakang’ono ka Mboni zochokera m’mayiko 13. Tinayenera kusintha m’njira zina kuti tithe kulalikira uthenga wabwino m’dziko limeneli la Iran. Ngakhale kuti sitinkatsutsidwa mwachindunji, tinkachita zinthu mosamala.
Chifukwa chakuti anthu ena ochita chidwi ankagwira ntchito zopanikiza, nthawi zina tinkachita maphunziro a Baibulo pakati pausiku kapena mpaka mbandakucha. Komano tinali osangalala kwambiri kuona zipatso za khama limeneli. Mabanja angapo a ku Phillipines ndi ku Korea anavomereza choonadi chachikristu ndipo anadzipatulira kwa Yehova.
Kenaka, kuntchito ananditumiza ku Dhaka, m’dziko la Bangladesh. Tinafika kumeneko mu December 1977. Ili linali dziko linanso lovuta kulalikiramo. Komabe, sitinaiwale kuti tiyenera kupitiriza kulalikira. Mothandizidwa ndi mzimu wa Yehova, tinapeza mabanja ambiri a matchalitchi achikristu. Ena mwa anthuwa anali ndi ludzu la madzi abwino a choonadi opezeka m’Malemba Oyera. (Yesaya 55:1) Motero tinayambitsa maphunziro ambiri a Baibulo.
Sitinaiwale kuti cholinga cha Mulungu n’chakuti “anthu onse apulumuke.” (1 Timoteo 2:4) N’zosangalatsa kuti palibe aliyense amene anayesa kutivutitsapo. Pofuna kuti anthu asiye kutisala, tinayesetsa kukhala ansangala kwambiri muutumiki wathu. Mofanana ndi mtumwi Paulo, tinayesetsa kukhala “zonse kwa anthu onse.” (1 Akorinto 9:22) Anthu akatifunsa chimene tabwerera, tinkalongosola mwansangala, ndipo anthu ambiri ankatilandira ndi manja awiri.
Ku Dhaka tinapeza wa Mboni wina ndipo tinamulimbikitsa kuti azibwera kumisonkhano yathu ndiponso pambuyo pake kuti azichita nafe ntchito yolalikira. Kenaka mkazi wanga anayamba kuphunzira Baibulo ndi banja linalake ndipo anaitana anthu a m’banjamo kuti abwere kumisonkhano yathu. Chifukwa cha kukoma mtima kwachikondi kwa Yehova, banja lonselo linalowa m’choonadi. Pambuyo pake, ana awo aakazi awiri anathandiza nawo pantchito yomasulira mabuku ofotokoza Baibulo m’chinenero cha Bengali, ndipo abale awonso ambiri anafika podziwa Yehova. Ophunzira Baibulo ena ambiri analowanso choonadi. Ambiri mwa iwo tsopano ndi akulu kapenanso apainiya.
Mzinda wa Dhaka uli ndi anthu ochuluka kwabasi, motero tinaitana achibale athu ena kuti adzatithandize ntchito yolalikira. Angapo anavomera n’kutitsatira ku Bangladesh. Ndife osangalala ndiponso oyamikira kwambiri kuti Yehova anatipatsa mwayi wolalikira uthenga wabwino m’dziko limeneli. Poyamba, ku Bangladesh kunali munthu mmodzi yekha wa mboni, koma panopo kuli mipingo iwiri.
Mu July 1982, tinayenera kuchoka ku Bangladesh. Posiyana nawo abale tinalephera kudzigwira moti mpaka tinalira. Posakhalitsa ndinalembedwa ntchito pa Entebbe International Airport, ku Uganda, kumene tinakhalako kwa zaka zinayi ndi miyezi seveni. Kodi ndi zinthu zotani zimene tinachita polemekeza dzina lalikulu la Yehova m’dzikoli?
Kutumikira Yehova ku East Africa
Titafika pa bwalo la ndege la Entebbe International Airport, anatumiza dalaivala amene anadzanditenga ineyo pamodzi ndi mkazi wanga pagalimoto n’kutipititsa kunyumba kwathu. Tikunyamuka pa bwalo la ndegepo, ndinayamba kulalikira dalaivalayo za Ufumu wa Mulungu. Iye anandifunsa kuti: “Kodi ndinu a Mboni za Yehova?” Nditavomera, iye ananena kuti: “Mbale wanu wina amagwira ntchito m’nsanja imene mumakhala anthu olankhulana ndi amene akuyendetsa ndege.” Nthawi yomweyo, ndinamuuza kuti andipititse kumeneko. Tinakumana ndi mbaleyo amene anali wosangalala kwambiri kukumana nafe, ndipo tinagwirizana za misonkhano ndiponso utumiki wam’munda.
Ku Uganda panthawiyi kunali ofalitsa a Ufumu okwana 228 okha basi. Motero chaka chathu choyamba tinakhala tikudzala mbewu za
choonadi pamodzi ndi abale athu awiri a ku Entebbe. Popeza kuti kumeneku anthu amakonda kuwerenga, tinagawira zowerenga zambiri, kuphatikizapo magazini ambirimbiri. Tinaitana abale ochokera ku Kampala, likulu la dzikoli, kuti azitithandiza kulalikira Loweruka ndi Lamlungu m’dera la Entebbe. Pankhani yanga ya anthu onse yoyamba, panabwera anthu asanu, kuwerengera ndi ine ndemwe.Patatha zaka zitatu, tinasangalala kwambiri kuona anthu amene tinawaphunzitsa choonadi akuchita bwino n’kuyamba kulimbikira kwambiri. (3 Yohane 4) Pamsonkhano wina wadera, anthu sikisi amene tinkaphunzira nawo Baibulo anabatizidwa. Ambiri mwa anthuwa ananena kuti chimene chinawalimbikitsa kuchita utumiki wanthawi zonse chinali chifukwa chakuti ankaona ifeyo tikuchita upainiya, ngakhale kuti tinali apantchito.
Tinazindikira kuti kuntchito kwathu kungathenso kukhala gawo lobala zipatso kwambiri. Panthawi ina, ndinapita kwa mkulu wina woona za moto pa bwalo la ndege n’kumuuza za chiyembekezo cha m’Baibulo chakuti anthu adzakhala m’paradaiso padzikoli. Ndinamusonyeza m’Baibulo lake kuti anthu omvera adzakhala mwamtendere ndiponso mogwirizana, sadzavutikanso ndi umphawi, kusowa nyumba zogona, nkhondo, matenda, kapena imfa. (Salmo 46:9; Yesaya 33:24; 65:21, 22; Chivumbulutso 21:3, 4) Mkuluyu anachita chidwi kwambiri poona zimenezi m’Baibulo lake. Nthawi yomweyo ndinayamba kuphunzira naye Baibulo. Anayamba kupita kumisonkhano yonse. Posakhalitsa anadzipatulira kwa Yehova ndipo anabatizidwa. Pambuyo pake anadzayamba kuchita nafe utumiki wa nthawi zonse.
Ku Uganda kunachitika zipolowe zoopsa kawiri konse, ife tili komweko, koma zimenezi sizinaletse ntchito yathu yauzimu. Mabanja onse a anthu ogwira ntchito m’mabungwe ochokera kunja anawasamutsira mumzinda wa Nairobi, ku Kenya, kwa miyezi sikisi. Ifeyo amene tinatsala ku Uganda tinapitiriza kuchita misonkhano yathu ndiponso ntchito yathu yolalikira, ngakhale kuti tinayenera kuchita zinthu mochenjera ndiponso mosamala chifukwa choti zinthu zinafika poopsa.
Mu April, 1988, ndinamaliza ntchito yanga ndipo tinasamukanso. Mpingo wa Entebbe tinasiyana nawo tili osangalala kwambiri chifukwa chakuti zinthu zauzimu zinali kuyenda bwino kumeneko. Mu July 1997, tinali ndi mwayi wokafikanso ku Entebbe. Panthawiyi n’kuti ena mwa anthu amene tinaphunzirapo nawo Baibulo atakhala akulu mumpingo. Tinasangalala kwambiri kuona anthu 106 atafika pa Msonkhano wa Onse.
Kusamukira ku Dera Limene Linali Lisanalalikidwepo
Kodi tinatha kugwiritsira ntchito mipata ina imene inapezeka? Inde tinatero chifukwa ndinasinthanso ntchito n’kuyamba kugwira ntchito ku Mogadishu International Airport, ku Somalia. Tinali ofunitsitsa kugwiritsira ntchito bwino mwayi wapadera umenewu kutumikira m’dera limene linali lisanalalikidwepo.
Tinkalalikira makamaka anthu ogwira ntchito m’maofesi a akazembe, anthu ochokera ku Phillipines, ndiponso anthu ena akunja. Kawirikawiri tinkakumana nawo kumsika. Komanso tinkapita kunyumba kwawo kukangowaona chabe. Pogwiritsira ntchito nzeru, khama, luso, kuzindikira ndiponso kudalira Yehova ndi mtima wathu wonse, tinatha kuuzako ena choonadi cha m’Baibulo, ndipo zimenezi zinachititsa kuti tibale zipatso kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana.
Patatha zaka ziwiri, tinachoka ku Mogadishu, kutangotsala pang’ono kubuka nkhondo.Kenaka bungwe la International Civil Aviation Organization linanditumiza ku Yangon, m’dziko la Myanmar. Ukunso tinapeza mipata yabwino kwambiri yothandiza anthu oona mtima kuphunzira za cholinga cha Mulungu. Titachoka ku Myanmar, anatitumiza ku Dar es Salaam, ku Tanzania. Popeza kuti ku Dar es Salaam kunali anthu olankhula Chingelezi, kulalikira uthenga wabwino khomo ndi khomo kunali kosavuta.
M’mayiko onse amene tinachitako ntchito, sitinapeze mavuto ambiri pochita utumiki wathu, ngakhale kuti m’mayiko ambiri, ntchito ya Mboni za Yehova inali yosaloledwa. Chifukwa cha ntchito imene ineyo ndinkagwira, imene nthawi zambiri inali yogwirizana ndi boma ndiponso mabungwe a padziko lonse, anthu sankakayikira zochita zathu.
Ntchito yanga yolembedwa inachititsa kuti ineyo ndi mkazi wanga tizikhala moyo wongosamukasamuka kwa zaka 30. Komabe, ntchitoyi tinkaiona ngati ntchito yotithandiza kukwaniritsa cholinga chathu chachikulu chomwe ndi kuthandiza kuti Ufumu wa Mulungu upite patsogolo. Tikuthokoza Yehova potithandiza kugwiritsira ntchito bwino mipata imene tinapeza chifukwa chosamukasamuka ndi kukhala ndi mwayi wofalitsa uthenga wabwino m’madera akutali.
Tinabwerera Komwe Tinachokera
Nditakwanitsa zaka 58, ndinaganiza zopuma pantchito nthawi yanga isanakwane n’kubwerera kwathu ku Philippines. Titabwerera kwathu, tinapemphera kuti Yehova atsogolere mapazi athu. Tinayamba kutumikira mumpingo winawake wa mumzinda wa Trece Martires m’chigawo cha Cavite. Titangofika, kunali anthu 19 okha ofalitsa uthenga wa Ufumu wa Mulungu. Ntchito yolalikira tsiku ndi tsiku inakonzedwa, ndipo maphunziro a Baibulo ambirimbiri anayambitsidwa. Mpingowo unayamba kukula. Panthawi ina, mkazi wanga anali ndi maphunziro a panyumba a Baibulo okwana 19, ndipo ineyo ndinali ndi maphunziro 14.
Posakhalitsa Nyumba ya Ufumu inayamba kuchepa. Tinapempha Yehova kuti atithandize. Mbale wina wauzimu ndi mkazi wake anaganiza zopereka malo awo, ndipo ofesi ya nthambi inavomereza kutibwereka ndalama zomangira Nyumba ya Ufumu. Nyumba yatsopanoyi yathandiza kwambiri pa ntchito yolalikira, ndipo mlungu uliwonse anthu obwera kumisonkhano amawonjezeka. Pakali pano timayenda mtunda wa ola lathunthu kuti tikathandize ku mpingo wina wa ofalitsa 17.
Ineyo ndi mkazi wanga timaona kuti ndi mwayi wapadera kwambiri kuti tatumikira m’mayiko osiyanasiyana chonchi. Tikamaganizira za moyo wathu wosamukasamuka, timasangalala kwambiri podziwa kuti tinaugwiritsira ntchito m’njira yabwino kwambiri, pothandiza ena kuphunzira za Yehova.
[Mapu pamasamba 24, 25]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
TANZANIA
UGANDA
SOMALIA
IRAN
BANGLADESH
MYANMAR
LAOS
THAILAND
PHILIPPINES
[Chithunzi patsamba 23]
Ineyo ndi mkazi wanga, Aurea