Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata Amene Amatamanda Yehova Amakhala ndi Moyo Wabwino

Achinyamata Amene Amatamanda Yehova Amakhala ndi Moyo Wabwino

“Thandizo Langa Lidzera kwa Yehova”

Achinyamata Amene Amatamanda Yehova Amakhala ndi Moyo Wabwino

“NDIKUFUNA zinthu zabwino koposa m’moyo wanga.” Umu ndi mmene mnyamata wina wosakwanitsa zaka 20 anafotokozera zokhumba zake. Koma kodi wachinyamata angapindule nawo bwanji moyo? Baibulo limapereka yankho losapita m’mbali kuti: ‘Uzikumbukira Mlengi wako masiku a unyamata wako.’​—Mlaliki 12:1.

Sikuti kutamanda Yehova ndi kum’tumikira n’kwa akuluakulu okha ayi. Samueli, mwana wa Elikana ndi Hana, anayamba kutumikira Yehova pa chihema ali wamng’ono kwambiri. (1 Samueli 1:19, 20, 24; 2:11) Mtsikana wamng’ono wachihebri anasonyeza chikhulupiriro champhamvu mwa Yehova mwa kunena kuti Namani, yemwe anali mkulu wa gulu lankhondo la Aramu, apite kwa mneneri Elisa kuti akachiritsidwe khate lake. (2 Mafumu 5:2, 3) Pa Salmo 148:7, 12, anyamata ndi atsikana omwe, akulimbikitsidwa kutamanda Yehova. * Yesu ali ndi zaka 12 zokha, anali wofunitsitsa kutumikira Atate wake. (Luka 2:41-49) Anyamata ena ophunzitsidwa Malemba, ataona Yesu pakachisi anafuula kuti: “Hosana kwa Mwana wa Davide.”​—Mateyu 21:15, 16.

Kutamanda Yehova Masiku Ano

Masiku ano, achinyamata ambiri a Mboni za Yehova amanyadira zikhulupiriro zawo, ndipo molimba mtima amauza ena zikhulupiriro zawozo kusukulu ndi kwina kulikonse. Onani zitsanzo ziwiri zotsatirazi.

M’kalasi la Stephanie wa zaka 18 wa ku Britain, ana asukulu anzake anali kukambirana nkhani yochotsa mimba ndi nkhani zina zokhudza makhalidwe. Mphunzitsi wawo ananena kuti masiku ano ambiri amavomereza kuti palibe cholakwika chilichonse ndi kuchotsa mimba ndipo palibe chifukwa chilichonse chomwe mtsikana angakanire kuchotsa mimba. Ophunzira onse m’kalasimo atavomereza maganizo amenewa, Stephanie anali wofunitsitsa kuteteza chikhulupiriro chake cha m’Baibulo pankhaniyi. Mwayi wochita zimenezi unafika pamene mphunzitsiyo anapempha Stephanie kuti anenepo maganizo ake. Ngakhale kuti poyamba anali ndi mantha, Stephanie anagwiritsa ntchito mpata umenewu kufotokoza zimene Malemba amanena. M’mawu akeake, anagwira lemba la Eksodo 21:22-24, kenako anafotokoza kuti ngati kuvulaza mwana wosabadwa kunali kulakwa, n’zodziwikiratu kuti kuchotsa mimba n’kosemphana ndi chifuno cha Mulungu.

Mphunzitsiyo, yemwenso ndi mmodzi wa atsogoleri achipembedzo, anali asanawerengepo mavesi amenewa. Chifukwa cha kuchitira umboni molimba mtima, Stephanie anali ndi mwayi wokambirana nkhani zosiyanasiyana ndi anzake a m’kalasiwo. Mtsikana wina wa m’kalasi momwemo tsopano amalandira magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! nthawi zonse. Anzake ena awiri anafika pa msonkhano wa chigawo wa Mboni za Yehova kudzaonerera Stephanie akubatizidwa posonyeza kudzipereka kwake kwa Mulungu.

Vareta wa zaka zisanu ndi chimodzi wa ku Suriname, ku South America, atazindikira kuti mphunzitsi wake akufunika chilimbikitso cha m’Malemba, anagwiritsa ntchito mwayi umenewu kutamanda Mulungu. Mphunzitsi ameneyu sanapite kuntchito kwa masiku atatu, ndipo atapita anafunsa ana asukuluwo ngati akudziwa chifukwa chake sanali kubwera kuntchito. Anawo anayankha kuti, “Mwina mumadwala.” Mphunzitsiyo anati: “Ayi, mchemwali wanga anamwalira, ndipo ndili ndi chisoni. Choncho musachite phokoso.”

Tsiku lomwelo masana Vareta anatanganidwa kusakatula magazini akale ndi kumawerenga mitu yake. Apa n’kuti amayi ake akugona. Kenako anapeza Nsanja ya Olonda ya July 15, 2001 ya mutu wakuti “Kodi Munthu Akamwalira Amakhala ndi Moyo Kwinakwake?” Mosangalala, anadzutsa amayi akewo ndi kunena kuti, “Amayi, Amayi, onani! Aphunzitsi anga ndawapezera magazini iyi yonena za akufa.” Vareta anatumiza magaziniyo kwa aphunzitsi akewo limodzi ndi kalata imene anawalembera. M’kalatayo iye anati: “Ndikufuna kuti muwerenge magaziniyi. Mchemwali wanuyo mudzaonana nayenso m’Paradaiso chifukwa Yehova sanama. Iye analonjeza kuti adzadzetsa Paradaiso padziko lapansi pompano, osati kumwamba.” Mphunzitsiyo anayamikira kwambiri chilimbikitso cha m’Baibulo chomwe anapeza m’magazini imeneyo.

Kukonza Tsogolo

Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe,” ndipo amafuna kuti achinyamata azikhala achimwemwe. (1 Timoteo 1:11, NW) Mawu ake enieniwo amati: “Kondwera ndi unyamata wako, . . . nukasangalale masiku a unyamata wako.” (Mlaliki 11:9) Yehova amaona patali ndipo amadziwa zotsatira zam’tsogolo za khalidwe labwino ndi loipa lomwe. N’chifukwa chake m’Mawu ake iye akulangiza achinyamata kuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo.”​—Mlaliki 12:1.

Inde, Yehova akufuna kuti achinyamata apindule mokwanira ndi mphatso yamtengo wapatali ya moyo. Achinyamata angakhale moyo wokhutiritsa ndi wopindulitsa mwa kukumbukira ndi kutamanda Mulungu. Atakumana ndi mavuto, anganene mwachidaliro kuti: “Thandizo langa lidzera kwa Yehova.”​—Salmo 121:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Onani Kalendala ya 2005 ya Mboni za Yehova, pa mwezi wa March ndi wa April.

[Mawu Otsindika patsamba 9]

“Lemekezani Yehova kuchokera ku dziko lapansi, . . . anyamata ndiponso anamwali.”​—SALMO 148:7, 12.

[Bokosi patsamba 8]

YEHOVA AMATHANDIZA ACHINYAMATA

“Inu ndinu chiyembekezo changa, Ambuye Yehova; mwandikhalira wokhulupirika kuyambira ubwana wanga.”​—Salmo 71:5.

“[Mulungu] akhutitsa m’kamwa mwako ndi zabwino; nabweza ubwana wako unge mphungu.”​—Salmo 103:5.