Chochitika Chosaiwalika
Chochitika Chosaiwalika
KODI chochitika chimenechi n’chiyani? Ndi imfa ya munthu winawake amene anafa zaka pafupifupi 2,000 zapitazo. Munthu ameneyu anati: “Nditaya Ine moyo wanga, kuti ndikautengenso. Palibe wina andichotsera uwu, koma ndiutaya Ine ndekha.” (Yohane 10:17, 18) Munthu ameneyu ndi Yesu Kristu.
Yesu analangiza otsatira ake kuti azichita mwambo wa Chikumbutso cha imfa yake ya nsembe. Mwambo umenewu umatchedwa kuti “mgonero wa Ambuye.” (1 Akorinto 11:20) Mboni za Yehova limodzi ndi mabwenzi awo, adzachita mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu, Lachinayi pa March 24, 2005, dzuwa litalowa.
Nkhani ya m’Baibulo idzafotokoza tanthauzo la mkate wosafufumitsa ndi vinyo wofiira zomwe zimagwiritsidwa ntchito pa mwambowu. (Mateyu 26:26-28) Nkhani imeneyi idzayankhanso mafunso ngati awa: Kodi Akristu ayenera kuchita kangati mwambo wa chikumbutso? Ndani amene ali oyenera kudya mkate ndi kumwa vinyo pa mwambowu? Ndani amene amapindula ndi imfa ya Yesu? Mwambo wofunikawu udzathandiza aliyense kuzindikira cholinga cha moyo ndi imfa ya Yesu.
Mudzalandiridwa ndi manja awiri pa mwambo umenewu wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu. Chonde funsani Mboni za Yehova kwanuko kuti mudziwe malo enieni osonkhanira ndi nthawi.