Kodi Ziphunzitso za Yesu Kristu Zimakukhudzani Motani?
Kodi Ziphunzitso za Yesu Kristu Zimakukhudzani Motani?
MALINGA ndi zomwe taona m’nkhani yapitayi, kodi pangakhale chifukwa chilichonse chokayikirira kuti ziphunzitso za Yesu zakhudza kwambiri anthu padziko lonse lapansi? Komano funso limene aliyense ayenera kudzifunsa ndi lakuti, “Kodi ziphunzitso za Yesu zandikhudza motani ineyo pandekha?”
Yesu anaphunzitsa nkhani zosiyanasiyana. Mfundo zofunika zopezeka m’ziphunzitso zakezo zingakhudze mbali iliyonse ya moyo wanu. Tiyeni tikambirane zimene Yesu anaphunzitsa zokhudza kuika zinthu zofunika patsogolo m’moyo, kupanga ubwenzi ndi Mulungu, kupanga ubwenzi wabwino ndi anthu anzathu, kuthetsa mavuto, ndiponso kupewa kuchita chiwawa.
Ikani Zinthu Zofunika Patsogolo M’moyo
Popeza kuti zochitika zomwe zimatithera nthawi komanso mphamvu zathu n’zochuluka m’dziko lotanganitsali, kawirikawiri mpata
wochitira zinthu zauzimu umasowa. Taganizirani za munthu wina wa zaka za m’ma 20 amene tingomutcha kuti Jerry. Jerry amakonda kwambiri kukambirana ndi anthu nkhani zauzimu ndipo amayamikira kwambiri zomwe iye amaphunzira m’makambiranowo, chotero akudandaula kuti: “Ndimasowa nthawi yokwanira yochitira zimenezi. Ndimagwira ntchito masiku asanu ndi limodzi mlungu uliwonse. Tsiku langa lopuma ndi Lamlungu lokha basi. Ndipo ndikamaliza ntchito zonse zofunikira, ndimakhala wotopa kwambiri.” Ngati inunso muli ndi vuto limeneli, zimene Yesu anaphunzitsa mu Ulaliki wa pa Phiri mungapindule nazo.Yesu anauza khamu la anthu omwe anasonkhana kudzamumvetsera kuti: “Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala? Yang’anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ayi, kapena sizimatema ayi, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi? . . . Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiyani? kapena, Tidzamwa chiyani? kapena, Tidzavala chiyani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimenezo; pakuti Atate wanu wa kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimenezo. Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” (Mateyu 6:25-33) Kodi tikuphunziranji pamenepa?
Yesu sanali kutanthauza kuti tizinyalanyaza zosowa zathu ndi za banja lathu. Baibulo limati: “Ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Komabe, Yesu analonjeza kuti ngati tiika zochita zathu m’dongosolo labwino, mwa kuika zinthu zauzimu patsogolo, Mulungu adzaonetsetsa kuti sitikusowa kanthu. Mawu a Yesuwa akutiphunzitsa mmene tingaikire zochita zathu m’dongosolo labwino. Kutsatira malangizo amenewa kumadzetsa chimwemwe, chifukwa “achimwemwe ali awo ozindikira kusowa kwawo kwauzimu.”—Mateyu 5:3, NW.
Pangani Ubwenzi ndi Mulungu
Anthu ozindikira kusowa kwawo kwauzimu amaona kuti n’kofunika kupanga ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Kodi timapanga bwanji ubwenzi wabwino ndi munthu? Timayesetsa kum’dziwa bwino munthu ameneyo. Timafunika kudekha kuti tiphunzire mmene amaganizira, makhalidwe ake, maluso ake, zimene wachitapo, zomwe amakonda, ndi zimene samakonda. Zilinso chimodzimodzi pofuna kupanga ubwenzi ndi Mulungu. M’pofunika kum’dziwa bwino. Popempherera ophunzira ake kwa Mulungu, Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.” (Yohane 17:3) Inde, kuti tipange ubwenzi ndi Mulungu m’pofunika kuti timudziwe bwino. Chomwe chingatithandize kum’dziwa mwa njira imeneyi ndi Baibulo, Mawu ouziridwa a Mulungu. (2 Timoteo 3:16) Chotero, tiyenera kupatula nthawi yophunzira Malemba.
Komabe, kungodziwa kokha sikokwanira. M’pemphero lomwe lija, Yesu ananena kuti: “[Ophunzira ake] adasunga mawu anu.” (Yohane 17:6) Sitiyenera kungom’dziwa kokha Mulungu komanso tiyenera kumachita zinthu mogwirizana ndi zomwe tadziwazo. Kodi pangakhalenso njira ina yopangira ubwenzi ndi Mulungu kuposa imeneyi? Kodi n’zotheka kuti ubwenzi wathu ndi munthu upite patsogolo ngati tikuchita mwadala zinthu zosemphana ndi maganizo kapena mfundo zake za makhalidwe abwino? Chotero maganizo a Mulungu komanso mfundo zake za makhalidwe abwino n’zomwe ziyenera kutitsogolera pa chilichonse chimene tikuchita m’moyo wathu. Tiyeni tione mmene mfundo zake za makhalidwe abwino ziwiri zokha zimagwirira ntchito pa ubwenzi wathu ndi anthu ena.
Pangani Ubwenzi Wabwino ndi Ena
Nthawi ina, Yesu anasimba nkhani inayake pofuna kuphunzitsa anthu mfundo yofunika kwambiri yokhudza maubwenzi a anthu. Anafotokoza za mfumu yomwe inkafuna kuwerengerana chuma ndi antchito ake. Koma mmodzi wa iwo anali ndi ngongole yaikulu moti sakanatha kuibweza. Mfumuyo inalamula kuti wantchitoyo, mkazi wake ndi ana ake agulitsidwe kuti ngongoleyo ibwezedwe. Kapoloyu anagwada pansi ndi kuchonderera kuti: “Bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu.” Pomumvera chisoni, mbuye wakeyo anamukhululukira ngongole yonse. Koma kapolo ameneyu atangochoka, anakumana ndi kapolo mnzake yemwe anakongola tindalama tochepa kwa iye, ndipo anamuumiriza kuti abweze. Ngakhale kuti kapolo mnzakeyo anachonderera kuti am’chitire chifundo, mwini ndalama uja analamula kuti mnzakeyo aikidwe m’ndende kufikira atabweza ngongole yonse. Mfumu ija itamva zimenezi, inakwiya. Ndipo inati: “Kodi iwenso sukadam’chitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni?” Kenako inalamula kuti kapolo wosakhululukayo aikidwe m’ndende kufikira atabweza ngongole yonse ija. Pophunzitsa anthuwo mfundo yofunika m’nkhaniyi, Yesu anati: “Chomwechonso Atate wanga adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.”—Mateyu 18:23-35.
Popeza ndife anthu opanda ungwiro, timalakwitsa zinthu zambiri. Sitingakwanitse kubwezera Mulungu ngongole kapena kuti mangawa aakulu omwe tadziunjikira chifukwa chomulakwira. Chomwe tingachite ndicho kungopempha kuti atikhululukire basi. Ndipotu Yehova Mulungu ndi wokonzeka kutikhululukira zolakwa zathu zonse, ngati nafenso tingakhululukire abale athu machimo omwe atilakwira. Palitu phunziro lamphamvu pamenepa. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa athu.”—Mateyu 6:12.
Thetsani Mavuto mwa Kuona Chochititsa
Yesu anali katswiri pankhani ya kumvetsetsa chibadwa cha munthu. Malangizo ake othetsera mavuto analunjika pa choyambitsa vutolo. Taonani zitsanzo ziwiri zotsatirazi.
Yesu anati: “Munamva kuti kunanenedwa kwa iwo akale, Usaphe; koma yense wakupha adzakhala wopalamula mlandu: koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu.” (Mateyu 5:21, 22) Apa Yesu anasonyeza kuti chimene chimachititsa munthu kupha mnzake ndi zomwe zili mumtima mwa munthu wopha mnzakeyo, osati chiwawa chokhacho. Ngati anthu akanapewa kukulitsa mtima wa udani kapena mkwiyo, sipakanapezeka munthu wokonzera mnzake chiwembu. Kunena zoona, kuphana kukanachepa kwambiri ngati anthu akanagwiritsa ntchito chiphunzitso chimenechi.
Taonani mmene Yesu anafikira pa gwero la vuto lina limene likusautsa anthu kwambiri. Iye anauza khamu la anthulo kuti: “Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake. Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye.” (Mateyu 5:27-29) Yesu anaphunzitsa kuti vuto lalikulu limakhala mumtima mwa munthuyo osati kungochita chigololo kokhako. Vuto lake ndi chilakolako chimene chimam’chititsa khalidwe loipali. Munthu akapewa kumangoganizira zilakolako zosayenera ndi kuzichotseratu m’maganizo mwake, amapewa kuchita zinthu zoipa.
“Tabweza Lupanga Lako M’chimakemo”
Usiku umene Yesu anaperekedwa ndi kumangidwa, mmodzi wa ophunzira ake anasolola lupanga lake kuti amuteteze. Yesu anam’lamula kuti: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) M’mawa kutacha, Yesu anauza Pontiyo Pilato kuti: “Ufumu wanga suli wa dziko lino lapansi; ufumu wanga ukadakhala wa dziko lino lapansi, anyamata anga akadalimbika nkhondo, kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda; koma tsopano ufumu wanga suli wochokera konkuno.” (Yohane 18:36) Kodi zomwe anaphunzitsa pamenepa n’zothandiza?
Kodi Akristu oyambirira ankaona motani zimene Yesu anaphunzitsa zoletsa kuchita chiwawa? Buku lakuti The Early Christian Attitude to War limati: “Popeza kuti [ziphunzitso za Yesu] zinaletsa kuchita chiwawa ndi kuvulaza ena, n’zoonekeratu kuti kumenya nkhondo kunali kosaloleka. . . . Akristu oyambirira ankatsatira ziphunzitso za Yesu, ndipo anamvetsetsa kuti ziphunzitsozo zinatanthauza kuti ayenera kukhala oleza mtima ndi kupewa kudziteteza mwachiwawa. Anasonyezeratu kuti chipembedzo chawo ndi chamtendere. Sanali kugwirizana m’pang’ono pomwe ndi zoti anthu azichita nkhondo chifukwa chakuti pankhondo anthu amaphana mouma mtima.” Ngati onse amene amadzitcha Akristu akanatsatira chiphunzitso chimenechi, kunena zoona mbiri ya anthu ikanakhala yosiyana ndi yomwe ilipo panopa.
Mungapindule ndi Ziphunzitso Zonse za Yesu
Ziphunzitso za Yesu zomwe takambiranazi n’zochititsa chidwi, zosavuta kumva, komanso zamphamvu. Anthu angapindule ngati atadziwa bwino ziphunzitso zimenezi ndi kumazigwiritsa ntchito. *
Mboni za Yehova m’dera lanulo zidzasangalala kukuthandizani kuona mmene mungapindulire ndi ziphunzitso zanzeru zakuya kuposa ziphunzitso zina zilizonse za anthu. Tikukupemphani kuti muonane nawo kapena mulembe kalata pogwiritsa ntchito adiresi yomwe ili pa tsamba 2 m’maganizi ino.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 22 Kuti mumve ziphunzitso zonse za Yesu mwatsatanetsatane, werengani buku lakuti Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 5]
“Atate wanu wa kumwamba azidyetsa”
[Chithunzi patsamba 7]
Ziphunzitso za Yesu mungapindule nazo m’moyo wanu