Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Ziphunzitso za Yesu Zakhudzira Anthu Padziko Lonse Lapansi

Mmene Ziphunzitso za Yesu Zakhudzira Anthu Padziko Lonse Lapansi

Mmene Ziphunzitso za Yesu Zakhudzira Anthu Padziko Lonse Lapansi

WOMASULIRA Baibulo, Edgar Goodspeed analemba kuti: “Zonse zimene Yesu ananena m’mauthenga abwino, kaya anazinena kumbali kapena pagulu, akanatha kuzinena m’maola awiri okha. Komabe ziphunzitso zochepa zomwezo, n’zogwira mtima ndiponso zolimbikitsa, moti n’zodziwikiratu kuti ndi Yesu yekha amene wasintha kwambiri miyoyo ya anthu padziko lonse lapansi chifukwa cha ziphunzitso zake.”

Pamene Yesu Kristu amatsiriza utumiki wake wapadziko lapansi m’chaka cha 33 C.E., panali amuna ndi akazi pafupifupi 120 omwe anali otsatira ake. (Machitidwe 1:15) Masiku ano, pali anthu oposa 2 biliyoni omwe amati ndi Akristu. Enanso miyandamiyanda amakhulupirira kuti Yesu anali mneneri. Ziphunzitso zake zakhudzadi anthu mochititsa chidwi kwambiri.

Atsogoleri omwe si achikristu nawonso amavomereza kuti ziphunzitso za Yesu zakhudza anthu padziko lonse lapansi. Mwachitsanzo, rabi wachiyuda, Hyman Enelow, analemba kuti: “M’mbiri ya zipembedzo, ndi Yesu yekha amene ali wotchuka kwambiri, wachikoka kwambiri, yemwenso anthu amuphunzira kwambiri.” Enelow ananenanso kuti: “Ndani angakwanitse kutchula zonse zimene anthu achita chifukwa cholimbikitsidwa ndi ziphunzitso za Yesu? Tikaganiza za chikondi chimene anasonyeza, mmene analimbikitsira anthu, ntchito zabwino zomwe anthu achita m’dzina lake, chiyembekezo ndi chimwemwe chomwe wapereka kwa anthu, palibenso wina amene angafanane naye m’mbiri ya anthu. Mwa anthu otchuka kwambiri ndi abwino onse amene akhalako m’mbiri ya anthu, palibe amene anali ndi chikoka ndiponso mphamvu padziko lonse ngati Yesu. Iye ndi munthu wochititsa chidwi kwambiri m’mbiri.” Ndipo mtsogoleri yemwe anali Mhindu, Mohandas K. Gandhi anati: “Palibenso wina amene wachita zambiri kwa anthu kuposa Yesu. Kunena zoona, palibe cholakwika chilichonse ndi Chikristu.” Komano anawonjezera kuti: “Vuto lili ndi inuyo Akristu. Simuyesa n’komwe kuchita zomwe mumaphunzitsa.”

Kwa nthawi yaitali, Matchalitchi Achikristu akhala akulephera kuchita zomwe Yesu anaphunzitsa. Wolemba mbiri ya Chikristu, Cecil John Cadoux, ananena kuti “pofika m’chaka cha 140 A.D., atsogoleri achikristu anali atadziwa kale kuti chizolowezi chotsatira makhalidwe abwino chikulowa pansi pang’ono ndi pang’ono.” Iye anati: “Kulowa pansi kumeneku kwa makhalidwe abwino omwe ankawatsatira m’Chikristu kalero, kunachititsa Akristuwo kutengera zochita zadziko mosavuta.”

Kulowa pansi kwa makhalidwe abwino kumeneku kunayamba kuwonjezereka modetsa nkhawa, mfumu Constantine ya Roma itakhala Mkristu m’zaka za m’ma 300. Cadoux analemba kuti: “Olemba mbiri aona ndipo ena a iwo amva chisoni kwambiri kuti Tchalitchi chinalola kuti zinthu ziwonongeke mwa kupanga mgwirizano ndi Constantine.” Kuchokera panthawiyo, anthu odzitcha Akristu, akhala akuchita zinthu zambiri zochititsa manyazi zonyozetsa dzina la Kristu.

Chotero mafunso ofunika kuwaganizira ndi akuti: Kodi Yesu ankaphunzitsa chiyani kwenikweni? Nanga ifeyo ziphunzitso zakezo ziyenera kutikhudza motani?

[Chithunzi patsamba 3]

“Palibenso wina amene wachita zambiri kwa anthu kuposa Yesu.”​—Mohandas K. Gandhi

[Chithunzi patsamba 3]

“Ndi Yesu yekha amene wasintha kwambiri miyoyo ya anthu padziko lonse lapansi.”​—Edgar Goodspeed

[Mawu a Chithunzi]

Culver Pictures